Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 10/1 tsamba 26-28
  • Lamulo la Mkhalidwe Kapena Kutchuka—Kodi Mumatsogozedwa Nchiyani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Lamulo la Mkhalidwe Kapena Kutchuka—Kodi Mumatsogozedwa Nchiyani?
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chikhumbo cha Kugwirizana ndi Ena
  • Zitsenderezo za Kugwirizana ndi Ena
  • Khamu Lingakhale Lolakwa
  • Malamulo a Mkhalidwe a Baibulo Ngabwino Kwambiri
  • Pamene Onse Adzachita Zoyenera
  • Achichepere Achikristu Khalani Olimba M’chikhulupiriro
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Khamu Lalikulu Kwambiri
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
  • “Ndinaona Khamu Lalikulu la Anthu”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • Kumbukirani Maprinsipulo Achikristu
    Nsanja ya Olonda—1988
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1993
w93 10/1 tsamba 26-28

Lamulo la Mkhalidwe Kapena Kutchuka​—Kodi Mumatsogozedwa Nchiyani?

NORIHITO wa m’giredi lachisanu ndi chimodzi anali kutenga mbali m’maseŵera. Mwadzidzidzi, iyeyu anayang’anizana ndi chosankha choti apange. Ophunzira onse anafunikira kutenga mbali m’dzoma lautundu. Kodi iye akayenera kugwirizana ndi ophunzira anzake m’chochitika chimenechi chamwambo?

Norihito anali ataphunzira m’Baibulo kuti kugwirizana mumchitidwe wa kulambira mulungu wina mmalo mwa Yehova kunali kolakwa. (Eksodo 20:4, 5; Mateyu 4:10) Iye anadziŵanso kuti Akristu ayenera kukhala auchete m’nkhani za ndale zadziko. (Danieli 3:1-30; Yohane 17:16) Chotero ngakhale kuti anzake ophunzira nawo anamlimbikitsa kugwirizana nawo, iye anakana molimba mtima koma mwaulemu. Kodi inu mukanachitanji mukanakhala m’mkhalidwe wofananawo?

Chikhumbo cha Kugwirizana ndi Ena

Malemba amasonyeza kuti anthu analengedwa ndi Mulungu kuti akhale oyanjana ndi ena, kugwirizana ndi ena, ndi kusangalala kuchitira zinthu pamodzi. Kufuna kukhala ndi anzako, kukhala wovomerezedwa, kukhala wogwirizana ndi ena nkwachibadwa. Malingaliro otero amapangitsa moyo kukhala wokondweretsa ndipo amachilikiza mtendere ndi chimvano m’kuchita zinthu zathu ndi ena.​—Genesis 2:18; Salmo 133:1; 1 Petro 3:8.

Chikhumbo chachibadwa cha kufuna kukhala ogwirizana ndi ena chimasonyezedwa mwamphamvu m’kugwirizana kumene kumaonedwa m’zitaganya za anthu ena ngakhale lerolino. Mwachitsanzo, ana a ku Japan amaphunzitsidwa kuyambira paubwana wawo kukhala ozindikira ndi kugwirizana ndi zosankha za unyinji. Mwambo wawo umawaphunzitsa kuti limodzi la thayo lawo lalikulu koposa ndilo kugwirizana ndi chitaganya. “Nzika za ku Japan nzokhoza kuchitira zinthu pamodzi m’timagulu koposa nzika Zakumadzulo,” anatero Edwin Reischauer, amene kale anali kazembe wa United States ku Japan ndi wachidwi ndi zizoloŵezi za nzika za ku Japan. Ananenanso kuti: “Pamene nzika Zakumadzulo zimasonyeza kudzigangira ndi kudzisankha, nzika zochuluka za ku Japan zimakhala zokhutira ndi kugwirizana m’kavalidwe, khalidwe, njira ya moyo, ndipo ngakhale kuganiza mogwirizana ndi kagulu kawo.” Komabe, kufuna kugwirizana ndi ena, sikuli kwa nzika za ku Japan zokha. Kumapezeka padziko lonse.

Zitsenderezo za Kugwirizana ndi Ena

Ngakhale kuti kuchita zimene munthu angathe kuti agwirizane ndi ena kuli kokhumbika, muli upandu m’kugwirizana wamba ndi zimene zili zotchuka. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti zimene zili zotchuka kwa anthu kaŵirikaŵiri nzotsutsana ndi zimene Mulungu amavomereza. “Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo,” limatiuza motero Baibulo. (1 Yohane 5:19) Satana amagwiritsira ntchito njira iliyonse imene ali nayo mochenjera​—kukondetsa zinthu zakuthupi, makhalidwe oluluza, tsankho lautundu, liuma lachipembedzo, kukonda fuko, ndi zina zotero​—kusonkhezera unyinji wa anthu ndi kuwachotsa kwa Mulungu. Kwenikweni, kugwirizana ndi machitachita amenewo kungachititse munthu kukhala wotsutsana ndi Yehova Mulungu ndi zifuno zake. Ndicho chifukwa chake Akristu akulangizidwa kuti: “Musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.”​—Aroma 12:2.

Pokhala ndi moyo m’dongosolo ili la zinthu, Akristu amatsenderezedwa mosalekeza kuti agwirizane ndi ena pazimene zili zotchuka. Makamaka achichepere ndiwo amene ali paupandu ponena za nkhaniyi. Chikhumbo cha kuoneka ndi kuchita zinthu mofanana ndi anzawo akusukulu nchamphamvu kwambiri. Pamafunika kulimba mtima kuti iwo afotokozere anzawo chifukwa chake sakhalira ndi phande m’machitachita ena. Komabe, kulephera kwawo kufotokoza molimba mtima, kungatanthauze tsoka lauzimu kwa iwo.​—Miyambo 24:1, 19, 20.

Nawonso achikulire amayang’anizana ndi zitsenderezo kumalo awo a ntchito. Iwo angayembekezeredwe kukhala ndi phande m’zochitika zina za mayanjano ataŵeruka ntchito kapena pamaholide ena. Kukana kuchita mogwirizana ndi ena kungawasonyeze kukhala onyada ndi osagwirizanika, kukumachititsa mkhalidwe wovuta pamalo antchito. Ena angadzione kukhala oumirizika kugwira ntchito kwa maola ambiri kokha chifukwa chakuti ena akuchita motero ndipo nawonso akuyembekezeredwa kutero. Kugonjera m’nkhani zotero kungakhale kowavulaza mwauzimu ndiponso kungawalepheretse kukwaniritsa mathayo awo ena.​—1 Akorinto 15:33; 1 Timoteo 6:6-8.

Zitsenderezo za kugwirizana ndi ena zimakhalapo ngakhale pamene sitili kusukulu kapena kuntchito. Nakubala wina Wachikristu anasimba kuti panthaŵi ina analeka kupereka chilango kwa mwana wake, ngakhale kuti chinali chofunika kwambiri, kokha chifukwa chakuti anaona kuti akazi ena amene analipo sakanagwirizana nacho.​—Miyambo 29:15, 17.

Khamu Lingakhale Lolakwa

Baibulo limatipatsa uphungu wochuluka womvekera bwino pamene tifika pankhani ya kutsatira zochita za khamu. Mwachitsanzo, mtundu wa Israyeli unauzidwa kuti: “Usatsata unyinji wa anthu kuchita choipa; kapena usachita umboni kumlandu, ndi kupatukira kutsata unyinji ndi kukhotetsa mlandu.” (Eksodo 23:2; yerekezerani ndi Aroma 6:16.) Uphungu umenewu sunatsatiridwe nthaŵi zonse. Atangotuluka kumene mu Igupto, pamene Mose anachoka, anthu ena anasonkhezera Aroni ndi mtundu wonse kupanga mwana wang’ombe wagolidi ndi kumlambira ‘m’madyerero a Yehova.’ Anthuwo anadya ndi kumwa ndi kusangalala ndi nyimbo ndi kuvina pamene anali kupereka nsembe kwa mwana wang’ombe wagolidi. Chifukwa cha mchitidwe wa chilakolako choipa ndi wa kupembedza fano umenewu, pafupifupi atsogoleri awo 3,000 anaphedwa. Koma enanso ambiri anakanthidwa ndi mliri wa Yehova chifukwa cha kutsatira wamba kwawo khamu la anthu.​—Eksodo 32:1-35.

Nkhani ina ya kutsatira khamu lokhala ndi cholinga choipa inachitika m’zaka za zana loyamba mogwirizana ndi imfa ya Yesu Kristu. Atasonkhezeredwa ndi atsogoleri achipembedzo ansanje, anthu ambiri anagwirizana m’kufuula kuti Yesu aphedwe. (Marko 15:11) Pamene Petro anatchula za tchimo lawo lalikulu pa Pentekoste pambuyo pa chiukiriro ndi kukwera kumwamba kwa Yesu, ambiri “analaswa mtima” ndi kuzindikira zimene anachita m’kutsatira khamu.​—Machitidwe 2:36, 37.

Malamulo a Mkhalidwe a Baibulo Ngabwino Kwambiri

Monga momwe zochitika zimenezi zimasonyezera bwino lomwe, kutsatira wamba zinthu zotchuka kungadzetse zotulukapo zowopsa. Nkwabwino kwambiri chotani nanga mmene kuliri kutsatira Baibulo ndi kulola malamulo ake a mkhalidwe kutitsogolera! “Monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, momwemo njira zanga zili zazitali kupambana njira zanu, ndi maganizo anga kupambana maganizo anu,” Yehova amatero. (Yesaya 55:9) M’nkhani za makhalidwe ndi maunansi a anthu​—indedi, m’zosankha zonse za moyo​—mwasonyezedwa mobwerezabwereza kuti kutsatira njira za Yehova nkwabwino kwambiri koposa kutsatira zimene zili zotchuka. Ndiko mfungulo ya njira yachimwemwe ndi yabwinopo.

Mwachitsanzo, talingalirani chokumana nacho cha Kazuya. Ngakhale kuti anaphunzirapo Baibulo panthaŵi ina, anapitiriza kutsatira njira ya anthu yotchuka​—akumamenyera nkhondo kulemera ndi kupeza chipambano. Zoyesayesa zake za kukondweretsa omlemba ntchito ndi kuti alingaliridwe bwino ndi antchito anzake kaŵirikaŵiri zinamchititsa kukamwa moŵa ndi ena kufikira mbandakucha. Iye anafikira kukhala munthu wovuta, wosapirira, ndi wamtima wapachala. Njira ya moyo wake yomkitsayo mofulumira inamdwalitsa sitoroko, imene inampuŵalitsa mbali imodzi. Pamene anali gone kuti achire pambedi wa kuchipatala, anayamba kulingalira zimene anaphunzira m’Baibulo ndi mmene analiri kukhalira ndi moyo. Anasankha kuti imeneyi inali nthaŵi yakuyamba kugwiritsira ntchito zimene anaphunzira. Analeka ntchito yake yaumanijala ndi kusintha mabwenzi ake. Anayesayesanso mwakhama kuvala umunthu Wachikristu ndi kusintha lingaliro lake pachuma chakuthupi. Monga chotulukapo, makhalidwe ake anasintha, ndipo thanzi lake linaongokera. Potsirizira pake, anapatulira moyo wake kwa Yehova ndi kubatizidwa.

Kuti munthu apambane m’kutsatira njira yosakondedwa ndi khamu, ayenera kudziŵa malamulo a mkhalidwe oloŵetsedwamo ndi kukhutiritsidwa kuti ngolondola. Zimene Masaru anakumana nazo zikusonyeza zimenezi kukhala choncho. Pamene anali m’giredi lachisanu ndi chimodzi, kusukulu ya pulaimale, anasankhidwa ndi anzake a m’kalasi kuti akhale wodzasankhidwa kukhala prezidenti wa bungwe la ophunzira. Mwamanyazi iye akukumbukira kuti chifukwa cha kusadziŵa mokwanira malamulo a Baibulo oloŵetsedwamo, anali wosakhoza kufotokozera anzake a m’kalasi chifukwa chake sakanavomereza malo antchito yandalewo. Kuopa kwake anthu kunamlepheretsa kufotokoza kuti anali Mkristu. Iye anangozolika mutu akumalira nabwereza kunena kuti, “Sindingathe kutero.”

Chokumana nacho chovuta chimenechi chinamchititsa kufufuza kuti adziŵe chifukwa chake Mkristu samaloŵa m’machitachita andale. (Yerekezerani ndi Yohane 6:15.) Pambuyo pake, pamene anali kusekondale, mkhalidwe wofananawo unabuka. Komabe, panthaŵiyi, iye anali wokonzekera kufotokoza mokhutira maganizo za kaimidwe kake kwa mphunzitsi wake. Mphunzitsiyo anavomera zimene ananena, monga momwe anachitiranso anzake a m’kalasi amene anamfunsa za zikhulupiriro zake zochokera m’Baibulo.

Pamene Onse Adzachita Zoyenera

M’dziko latsopano limene likudzalo pansi pa ulamuliro wa Kristu, chinthu choyenera ndicho chidzakhala chotchuka kuchita. Kufikira nthaŵiyo, tifunikira kukhala maso pachisonkhezero cha kugwirizana ndi ena kuti tichite zimene zili zotchuka. Tingathe kupeza chilimbikitso m’chilangizo cha Paulo chakuti: “Popeza tizingidwa nawo mtambo waukulu wotere wa mboni, titaye cholemetsa chilichonse, ndi tchimoli limangotizinga, ndipo tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira.”​—Ahebri 12:1.

Pamene mukumana ndi mikangano ndi zovuta, kodi mudzachitanji? Kodi mudzalola kuopa anthu kukugonjetsani m’kuchita zimene zili zotchuka kwa onse? Kapena kodi mudzatembenukira ku Mawu a Mulungu, Baibulo, ndi kutsatira malamulo ake a mkhalidwe? Kulondola njira yotsirizirayo sikudzakupindulitsani kokha tsopano lino komanso kudzakupatsani chiyembekezo cha kukhala pakati pa “iwo amene alikuloŵa malonjezano mwa chikhulupiriro ndi kuleza mtima.”​—Ahebri 6:12.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena