Kodi Mukukumbukira?
Kodi mwasangalala kuŵerenga makope aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Ngati ndi choncho, mudzakupeza kukhala kokondweretsa kukumbukira zotsatirazi:
▫ Kodi nchifukwa ninji azondi Achiisrayeli anasankha kukagona kunyumba ya Rahabi mkazi wadama?
Azondi Achiisrayeli anakhala ndi moyo mogwirizana ndi Chilamulo cha Mulungu, chotero sanagone m’nyumba ya Rahabi kaamba ka zifukwa zachisembwere. Mwinamwake analingalira kuti kukhala kwawo m’nyumba ya mkazi wadama kukachepetsa kunyumwira kukhala kwawo mumzindamo. Kumangidwa palinga kwa nyumba yake kukachititsanso kuthaŵa kwawo kukhala kosavuta. Koma koposa zonse, Yehova anawatsogolera kwa wochimwa amene mtima wake unayambukiridwa bwino ndi mbiri ya zochita za Mulungu ndi Aisrayeli kwakuti iye analapa nasintha njira zake.—12/15, masamba 24-5.
▫ Kodi mkwiyo umayambukira motani thanzi lathu?
Zofufuza zikusonyeza kuti mkwiyo umatulutsa mahomoni a kupsinjika. Kukwiyakwiya kungachititse kusiyana m’milingo ya cholesterol yotetezera ndi yaupandu, kukumatiika paupandu wa nthenda ya mtima.—12/15, tsamba 32.
▫ Kodi ndi malingaliro otani amene adzatithandiza kuwonjezera kugaŵira kwathu magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!?
Khalani ozindikira kufunika kwa Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!; perekani ulaliki wosavuta; khalani wokhoza kusintha mwa kukonzekera maulaliki achidule angapo; khazikitsani chonulirapo chaumwini.—1/1, masamba 24-5.
▫ Kodi nchifukwa ninji Mose ali chitsanzo chabwino chateokratiki choyenera ife kuchitsanzira?
Mose anafuna chitsogozo cha Yehova pa zinthu. Sanadzifunire ulemerero koma anadera nkhaŵa ndi ulemerero wa Yehova. Anali ndi chikhulupiriro champhamvu ndipo sanaiŵale konse kuti Yehova anali Wolamulira weniweni wa mtundu wa Israyeli.—1/15, tsamba 11.
▫ Kodi ndi njira zina zotani mmene chiphunzitso chaumulungu chimalakikira?
Chiphunzitso chaumulungu chimalakika mwa kupereka kwa anthu a Yehova kumvetsetsa komawonjezereka kwa chowonadi. Chimabweretsa anthu m’kuunika kwauzimu, ndipo chimasonyeza ofatsa mmene angalambirire Mulungu “mu mzimu ndi chowonadi.” (Yohane 4:24) Chiphunzitso chaumulungu chimalakanso ziyeso ndi dziko loipa.—2/1, masamba 10-12.
▫ Kodi nchiyani chimene chili mfungulo ya kupereka uphungu kwachipambano?
Mfungulo ndiyo kupereka ulemu woyenerera kwa munthu wina ndi kuyenera kwake kuchitiridwa mwaulemu. Chifukwa chake, phungu Wachikristu ayenera kukhala wokoma mtima ndi wotsimikiza komabe ayenera kupatsa ulemu munthu wolandira uphunguyo.—2/1, tsamba 28.
▫ Kodi ndimotani mmene tchalitchi cha Roma Katolika chinafikira pa kulandira chiphunzitso cha Kutengeredwa Kumwamba kwa Mariya?
M’zaka za zana loyamba pambuyo pa imfa ya Yesu, lingaliro la Kutengedwera Kumwamba kwa Mariya linali lachilendo m’maganizo mwa Akristu. Komabe, chiphunzitso cha Utatu chitakhala chiphunzitso chovomerezedwa cha tchalitchi, Mariya anayamba kuikidwa pamalo olemekezeka mowonjezereka. Nthanthi ya Kutengeredwa Kumwamba sinalandiridwe kukhala chiphunzitso choikidwa kufikira pa November 1, 1950, pamene Papa Pius XII analengeza kuti: “Tikuchilengeza kukhala chiphunzitso choikidwa chovumbulidwa ndi Mulungu.”—Munificentissimus Deus.—2/15, masamba 26-7.
▫ Mu Yeremiya chaputala 24, kodi mitanga iŵiri ya nkhuyu, nkhuyu zabwino ndi zoipa, inaimira chiyani?
Poyamba nkhuyu zabwino zinaimira Ayuda amene anatengedwa ukapolo ku Babulo, amene otsalira akabwerera ku Yuda. Nkhuyu zoipa zinaimira Mfumu Zedekiya ndi awo amene anapandukira Mfumu Nebukadinezara mosasamala kanthu kuti anachita lumbiro m’dzina la Mulungu. Mofananamo, timapeza m’nthaŵi zamakono otsalira a Israyeli wauzimu, amene atulutsa zipatso zabwino m’miyoyo yawo, mosiyana ndi atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu, amene atulutsa zipatso zoipa.—3/1, masamba 14-16.
▫ Kodi a Quartodecimans anali ayani, ndipo nchifukwa ninji ali ofunika kwa Akristu lerolino?
Pambuyo pa nthaŵi ya atumwi, panali ena amene anachita phwando la Chakudya Chamadzulo cha Ambuye pa Nisani 14 chaka chilichonse, kutsatira dongosolo la atumwi. Iwo anadziŵika monga “Osunga Tsiku Lakhumi ndi Chinayi,” kapena Quartodecimans. Zimenezi nzofunika lerolino, popeza zimasonyeza kuti ngakhale pambuyo pa kufa kwa atumwi, panali ena amene anamamatira ku njira yoyenera yokumbukirira imfa ya Yesu kamodzi pa chaka pa Nisani 14.—3/15, masamba 4-5.
▫ Kodi William Whiston anali yani?
Anali wophunzira wanzeru kwambiri wa m’zaka za zana la 18 wa ku England, mnzake wa Bwana Isaac Newton. Whiston anatembenuza Malemba Achigiriki Achikristu, anatsutsa poyera chiphunzitso cha Utatu, ndipo anali mphunzitsi wa zakuthambo ndi masamu. Koma mosakayikira Whiston amakumbukiridwa kwambiri chifukwa cha kutembenuza kwake m’Chingelezi zolemba za wolemba mbiri Wachiyuda Flavius Josephus.—3/15, masamba 26-8.
▫ Kodi munthu anapangidwa motani m’chifanizo cha Mulungu? (Genesis 1:27)
Munthu anapangidwa ndi luso la kusonyeza mikhalidwe yapamwamba ya Mulungu ya chikondi, chilungamo, nzeru, ndi mphamvu—limodzinso ndi mikhalidwe ina.—4/1, tsamba 25.