Otsimikiza Mtima Kutumikira Yehova!
“SUYENERA kumapita kukalalikira!” “Anzako asamabwere pano!” Akazi ambiri Achikristu amva mawu ameneŵa ndi ena ofanana nawo kuchokera kwa amuna awo. Koma pamene amuna ameneŵa akugwira ntchito m’magulu ankhondo, akazi awo amayang’anizana ndi chitokoso chapadera pa chikhulupiriro chawo. (Yesaya 2:4; Yohane 17:16) Pamenepo, kodi ndimotani mmene akazi Achikristu oterowo angakhozere kukhalabe amphamvu mwauzimu ndi okangalika muutumiki Waufumu?
Kukhulupirika kwa Yehova Mulungu limodzi ndi kutsimikiza mtima kwaumwini zidzawathandiza kupirira. “Ndiganiza kuti kunali kutsimikiza mtima kwanga kolimba,” akulongosola motero Yvonne, mkazi wa msilikali. “Ndinadziŵa kuti payenera kukhala njira zopeŵera chitsutso cha mwamuna wanga.” Ndithudi, zinalipo.
Mkazi wina Wachikristu, wokwatiwa ndi mkulu wankhondo, akusimba mmene kutsimikiza mtima kwake kumachititsira zinthu kukhala zosavuta kwa mwamuna wake. Iye akulongosola kuti: “Amadziŵa ndandanda yanga ndi yake, ndipo anthu ankhondo amayamikira zimenezo.” Komabe, kupitiriza kwake utumiki wa Yehova sikuli kokhweka.
Kugonjetsa Kusungulumwa
Kaŵirikaŵiri akazi a asilikali amakumana ndi chitokoso cha kusamuka atangodziŵitsidwa kwa masiku ochepa ngati akufuna kutsagana ndi amuna awo kumalo akutali ndi kwawo. Ndiyeno, pamene ali mmalo achilendowo, kumakhala kosavuta kudzimva opatulidwa. Koma zimenezi siziyenera kuchitika. Amene amatumikira Yehova ali ndi mwaŵi. Kodi ndi mwaŵi wotani? Malinga ndi kunena kwa mtumwi Petro Wachikristu, uli “gulu lonse la abale.” Tsopano, zomafika chiŵerengero cha mamiliyoni, Mboni za Yehova za m’maiko 231 zimachita monga banja lalikulu Lachikristu, “ubale.” Mumazipeza pafupifupi kulikonse.—1 Petro 2:17, NW, mawu amtsinde.
Susan, anachoka mwadzidzidzi kudera lakwawo, nafika kumalo a asilikali apandege kumene mwamuna wake anagaŵiridwa. Pokhala watsopano m’chikhulupiriro ndi wotsenderezedwa ndi mwamuna wake wosakhulupirira kuti asiye kutenga mbali muutumiki Wachikristu, iye akusimba kuti: “Ndinapita mofulumira ku misonkhano yakumaloko, ndipo kumeneko ndinali wokhoza kukhala ndi kulankhula ndi alongo ena. Ndinganene mowonadi kuti kuyanjana kumeneko nkomwe kunandilimbikitsa.”
Nthaŵi zina kusungulumwa kungachititse tondovi. Ngakhale panthaŵiyo, mbiri yabwino imapereka chithandizo. Glenys, mlongo wa ku England amene anatsagana ndi mwamuna wake pamene anatumizidwa kudziko lina, akusimba kuti: “Pamene ndinachita tondovi kwambiri, mwadzidzidzi, munthu wina amene ndinamdziŵa zaka zambiri zapitazo pamene nanenso ndinali m’gulu la nkhondo anandilembera kalata ndi kunena kuti anabatizidwa posachedwapa monga mmodzi wa Mboni za Yehova. Zimenezo zinandipatsa chilimbikitso panthaŵi yoyenera.”
Jane, amene anapita ndi mwamuna wake ku Kenya, anapeza kuti misonkhano Yachikristu inali yothandiza, ngakhale kuti inali kuchititsidwa m’zinenero zimene sanali kumva. “Ndinadziŵa kuti kuno nkumene Yehova anafuna kuti ndikhale,” analongosola motero. “Ndinali ndi abale anga, ndipo anali ngati mankhwala auzimu. Anandilandira, ndipo ndinaona ngati kuti tinali abanja limodzi.”
Jane ali mmodzi wa ambiri amene ali m’mikhalidwe imeneyi amene anapeza abale auzimu amene sanadziŵe kuti anali nawo!—Marko 10:29, 30.
Kuchirimika Poyang’anizana ndi Chitsutso
“Musalingalire kuti ndinadzera kuponya mtendere pa dziko lapansi,” Yesu anachenjeza motero. “Sindinadzera kuponya mtendere, koma lupanga.” (Mateyu 10:34) Kodi anatanthauzanji? Ngakhale m’banja, mmene mumayembekezeredwa kukhala mtendere, mungakhale “kuponya lupanga kwa mwadzidzidzi,” akutero A. T. Robertson mu Word Pictures in the New Testament. Yesu ananena kuti: “Apabanja ake a munthu adzakhala adani ake.” (Mateyu 10:36) Mawu ameneŵa amakhala owona chotani nanga pamene mnzanu wamuukwati amada chowonadi!
Pamene Diane anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, mwamuna wake, mkulu wa gulu lankhondo la mlengalenga, anakwiya kwambiri. Kodi zimenezi zinali ndi chiyambukiro chotani pa ukwati wawo? “Kunali ngati kuti chopinga chinali kubwera pakati pathu,” akulongosola motero Diane. “Tinali achimwemwe muukwati wathu. Mwadzidzidzi sitinali kulankhulana.” Pamenepo, kodi anachita motani? “Chikhulupiriro changa ndi kutsimikiza mtima ndizo zinandithandiza, limodzi ndi chithandizo cha Yehova ndi mzimu wake.” Diane anatsanzira chitsanzo cha m’Baibulo cha mneneri Danieli.
Pamene anali muukapolo ku Babulo ndi kupatsidwa chakudya chosayenera mtumiki wa Mulungu, Danieli “anatsimikiza mtima kuti asadzidetse ndi chakudya cha mfumu.” Inde, Danieli anapanga chosankha modziŵa. Anagamula mumtima mwake kusadzidetsa mwa kudya chakudya chimenecho. Iye anasonyeza kulimba kotani nanga pamene “anapempha mkulu wa adindo amlole asadzidetse”! Chotulukapo chake? Yehova anadalitsa kaimidwe kake kotsimikiza mtima.—Danieli 1:8, 9, 17.
Mofananamo lerolino mwamuna wotsutsa angalamule kuti mkazi wake aleke kufika pamisonkhano yampingo. Kodi mkaziyo ayenera kuchita motani? Jane anapezeka mumkhalidwe umenewu. Iye akulongosola kuti: “Sindinagonjere konse chitsenderezocho. Ndinadziŵa kuti sipafunikira kulolera molakwa. Ndinayenera kusonyeza mmene misonkhano inaliri yofunika kwa ine.” Yehova anadalitsa chosankha chake pamene anapitiriza kufikapo.
“Mwamuna wanga anayesa kundiletsa kupita ku misonkhano, koma zimenezo sizinachitike kwanthaŵi yaitali,” akusimba choncho Glenys. “Ndinapitabe. Pamene ndinabwerera kunyumba, nthaŵi zina anandimenya, ndipo nthaŵi zina sanandilankhuze.” Komabe, iye analimbikira, akumapemphera mobwerezabwereza. Ndiponso, akulu a mpingo aŵiri anapemphera naye mokhazikika, zimene zinamlimbikitsa kwambiri kupitirizabe kusonkhana.—Yakobo 5:13-15; 1 Petro 2:23.
Nthaŵi zina akuluakulu akuntchito kwa mwamunayo angamkakamize kuletsa mkazi wake kulalikira mbiri yabwino. Diane anapeza kuti anayenera kumuuza momvekera bwino mwamuna wake zinthu zake zofunika kwambiri. Iye anati: “Ndinakonzekera kulandira zotulukapo za kupitiriza kwanga kulalikira.” Kaimidwe kameneka nkofanana motani nanga ndi ka atumwi! (Machitidwe 4:29, 31) Komabe, iye anali wochenjera m’kulalikira kwake. Akusimba kuti: “Ndinali kuitana anthu kudzamwa khofi ndi kugaŵira onse opezekapo buku la Coonadi.”—Mateyu 10:16; 24:14.
Kumvera Popanda Kulolera Molakwa
Ngakhale kuti amavutika ndi mavuto a m’banja, akazi Achikristu amayang’ana mtsogolo ndi kudalira Yehova. Zimenezi zimawathandiza kukhala ndi lingaliro lachikatikati. Amapatsa amuna awo chichirikizo chilichonse chimene angathe popanda kulolera molakwa chikhulupiriro chawo. Mwakutero, amatsatira uphungu wouziridwa wa Petro wakuti: “Akazi inu, mverani amuna anu a inu nokha.” (1 Petro 3:1) Mu The Amplified New Testament, uphungu wa mtumwi umenewu umati: “Dzigonjetsereni nokha kukhala achiŵiri ndi odalira pa iwo, ndipo dzisintheni molingana nawo.” Onani mmene Jane analabadirira uphungu umenewu. Iye akulongosola kuti: “Mwamuna wanga anandiuza kuti zimene ndinafuna kuchita siziyenera kusokoneza ntchito yake. Chotero ndinayesa kupeza njira zomuthandizira.”
Motero akazi ena Achikristu avomereza kupita kumapwando kumene amuna awo aitanidwa. Koma amagamulabe kusalolera molakwa chikhulupiriro chawo. Jane anapatula nthaŵi ya kulankhula ndi mwamuna wake za nkhaniyi. Iye analongosola mokoma mtima kuti anali wofunitsitsa kufikako koma sanafune kuti kukhalapo kwake kuchititse manyazi mwamunayo. “Ndinadziŵa kuti nthaŵi zina onse opezekapo amayembekezeredwa kuima ndi kumwa kulemekeza munthu wina. Ndinali nditaphunzira kuti ulemu uyenera kuperekedwa kwa Yehova yekha, ndipo kumwa kolemekeza munthu sikunali kusonyeza ulemu chabe. Mwamuna wanga anazindikira mmene mkhalidwewo ukaipira, chotero anangoti: ‘Usabwere!’ Ndinamvera.”
Kumbali ina, Glenys anatsagana ndi mwamuna wake ku chochitika choterocho, koma anayang’ana akuluakulu amene anakhala kumutu kwa thebulo. Pamene anawaona akukonzekera kumwa kopereka ulemu kwa munthu, anatuluka mochenjera kupita kuchimbudzi! Inde, akazi ameneŵa anadzisintha koma sanalolere molakwa konse.
‘Kukodwa Popanda Mawu’
“Ngati ndiwongolera maluso anga monga mkazi, mwamuna wanga adzaona kuti chowonadi chikundisintha,” analingalira motero Yvonne. Chotero anaŵerenga mobwerezabwereza mutu wa m’buku la Moyo wa Banja wakuti “Mkazi Amene Ali Wokondedwa Kwambiri.”a “Ndinapereka chisamaliro chachikulu ku nkhani ya pansi pakamutu kakuti ‘Olira, Olongoloza’! Koma ndinapeza kuti pamene ndinayesa kwambiri kulankhula ndi mwamuna wanga, zinthu zinavuta kwambiri.” Komabe, pomalizira pake anapambana kuthandiza mwamuna wake kutumikira Yehova. Motani? Mwa kugwiritsira ntchito lamulo lopezeka pa 1 Petro 3:1, lakuti amuna ‘akakodwe popanda mawu.’
Njira imene akazi Achikristu amasamalira mabanja awo imathandiza kukopera ena ku Chikristu. Diane akusimba kuti: “Ndinayesa kupangitsa chowonadi kukhala chokopa kwambiri. Pamene ndinapita kumisonkhano, mwamuna wanga anali kudzimva kukhala wopatulidwa, chotero ndinatsimikiza kulangiza ana kusonyeza khalidwe labwino koposa pamene tinabwerera kunyumba. Ndinayesanso kupereka chisamaliro chowonjezereka kwa iye tikabwerera.” Mwapang’onopang’ono mkhalidwe wa maganizo wa mwamuna wake unasintha pamene anavomereza chisamaliro chachifundo cha banja lake.
Atumiki anzathu a Yehova angathandizenso. Jane akusimba kuti mwamuna wake anakonda kucheza ndi amishonale amene anakumana nawo ku Kenya. “Iwo anapalana naye ubwenzi ndipo anali kulankhula za maseŵera a mpira, ndipo anali ochereza kwambiri. Nthaŵi zambiri, tinaitanidwa kukadya ku nyumba za amishonale zosiyanasiyana.” Mwamuna wake analongosola pambuyo pake kuti: “Ndinayamba kuona chikhulupiriro cha Jane ndi lingaliro losiyana kwambiri. Mabwenzi ake anali anthu anzeru kwambiri omwe anakhoza kulankhula pa nkhani zosiyanasiyana.” Mofananamo, mwamuna wa Diane anasintha lingaliro lake la chowonadi. Pamene galimoto lomwe anali kuyendetsa linafa, Mboni yachichepere inabwera kudzamuthandiza. Iye akuti: “Zimenezo zinandisangalatsa kwambiri.”
Ndithudi, si amuukwati onse amene amakopedwa kulandira chowonadi. Pamenepo chiyani? Yehova amapereka chithandizo kutheketsa okhulupirika kupirira. (1 Akorinto 10:13) Talingalirani za chilimbikitso cha Glenys kwa awo amene ali m’mikhalidwe yofanana ndi yake: “Musakayikire konse kuti Yehova ndiye Amene anayambitsa ukwati ndipo amafuna kuti okwatirana akhale pamodzi. Chotero mosasamala kanthu za zimene mwamuna angachite kapena chitsutso chimene mungalandire kuchokera kwa okuzingani, Yehova sadzakulolani kugwedezeka.” Ngakhale kuti mwamuna wake sanayambe kulambira Yehova, mkhalidwe wake wamaganizo kulinga kwa iye ndi chowonadi waongokera.
‘Fesani ndi Misozi; Tutani Mokondwera’
Ndithudi, akazi Achikristu ameneŵa ali otsimikiza mtima kutumikira Yehova. Ngati muli m’mikhalidwe yofananayo, pangani zimenezi kukhala chosankha chanunso. Kumbukirani uphungu wakuti: “Muziopa Yehova Mulungu wanu; mumtumikire iyeyo; mummamatire iye.”—Deuteronomo 10:20.
“Iye amene ayendayenda nalira, ponyamula mbewu yakufesa; adzabweranso ndithu ndi kufuula mokondwera, alikunyamula mitolo yake.” (Salmo 126:6) “Umakhetsa misozi yambiri pamene uyesa kusonyeza mnzako wamuukwati chowonadi, kaya popanda mawu kapena mwa kulankhula,” ikuvomereza motero Mboni ina. “Koma pomalizira pake umalira mokondwera chifukwa chakuti ngakhale ngati salandira chowonadi, Yehova amakudalitsa chifukwa cha kuyesayesa kumene umapanga.”
Onse amene amatumikira Yehova mokhulupirika mosasamala kanthu za chitsutso cha panyumba ayenera kuyamikiridwadi. Iwo amayenerera chichirikizo ndi chikondi. Asungebe kaimidwe kawo kosalolera molakwa, otsimikiza mtima kutumikira Yehova!
[Mawu a M’munsi]
a Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc. (1981).
[Chithunzi patsamba 28]
Kuphunzira mwapemphero kumalimbikitsa kutsimikiza mtima Kwachikristu