Tikulandirani ku Msonkhano Wachigawo wa “Mantha Aumulungu”!
INDE, nthaŵi ya misonkhano yachigawo ya 1994 ya Mboni za Yehova ikuyandikira. Kuyambira June 1994 mpaka January 1995, programu ya msonkhano ya masiku atatu idzachitidwa m’mizinda mazana ambiri pa dziko lonse—kuyambira ku North America, kenako ku Eastern ndi Western Europe, Asia, Central ndi South America, Afirika, Australia, ndi zisumbu za m’nyanja.
Ndi mutu wotokosa maganizo chotani nanga—“Mantha Aumulungu”! Ameneŵa sali mantha oipa a munthu amene moyo wake uli pangozi koma kuwopa Mulungu, mantha amene amapereka mtendere wa maganizo ndi chisangalalo. Mwambi wa Baibulo umati: “Mphotho ya chifatso ndi kuopa Yehova, ndiy[o] chuma, ndi ulemu, ndi moyo.” (Miyambo 22:4) Kodi kuopa Mulungu kungabweretse motani “chuma, ndi ulemu, ndi moyo”? Zimenezo zidzaonekera bwino pamene mutu wa msonkhanowo udzafutukulidwa m’masiku atatu odzaza ndi nkhani, makambitsirano, zitsanzo, ndi drama.
Mtumwi Paulo analemba kuti sitiyenera ‘kuleka kusonkhana kwathu pamodzi.’ (Ahebri 10:25) Mboni za Yehova zimaona zimenezo mwamphamvu, zikumasonkhana nthaŵi zitatu pa mlungu kaamba ka phunziro la mpingo ndi kulambira. Komabe, msonkhano wachigawo wa pachaka uli wapadera. Izo zimauyembekezera mwachidwi ndi kulankhula za uwo kwa miyezi yambiri pambuyo pake. Tikuitanani mwaubwenzi, mosasamala kanthu za chipembedzo chanu, kudzagwirizana nawo pa msonkhano wawo ndi kusangalala ndi ubwenzi weniweni Wachikristu ndi chidziŵitso chofunika chauzimu. Chiŵalo cha mpingo wa Mboni za Yehova wa kwanuko chidzakhala chosangalala kukuuzani malo ndi nthaŵi imene msonkhano wakufupi nanu udzachitidwa.