Kodi Mukukumbukira?
Kodi mwapeza makope a Nsanja ya Olonda aposachedwapa kukhala okupindulitsani? Pamenepo bwanji osayesa chikumbukiro chanu ndi mafunso otsatirapowa:
▫ Kodi nchifukwa ninji Mboni za Yehova zimapitirizabe kufikira anansi awo?
Mboni za Yehova izo eni zimafuna dalitso la Mulungu kupyolera mu Ufumu wolonjezedwa, ndipo chifukwa cha kukonda kwawo anansi, zimafuna dalitso limodzimodzilo kukhala pa iwo. Motero, potsanzira chitsanzo cha Yesu, zimakakamizika ndi chikondi chopanda dyera kufikira anansi awo. (Mateyu 6:9, 10; 22:37-39)—8/15, masamba 8, 9.
▫ Kodi nchifukwa ninji kukhulupirira chisinthiko kuli nkhani ya chikhulupiriro?
Asayansi sanaonepo kusintha kwa majini kwa mwadzidzidzi—ngakhale kopindulitsa—kukumatulutsa mitundu yatsopano ya moyo, komabe ochirikiza chisinthiko amanena kuti umu ndimo mmene mtundu wa zolengedwa zatsopano unakhalirako. Ochirikiza chisinthiko sanaonepo kuyambika kwa moyo kuchokera ku zinthu zosakhala zamoyo, komabe amaumirira kunena kuti ndi mmene moyo unayambira.—9/1, tsamba 5.
▫ Kodi ndimotani mmene tingagonjetsere bwino koposa kulefulidwa kumene kungadze chifukwa cha zoletsa m’moyo?
Mulimonse mmene mkhalidwe wathu ungakhalire, ngati tisumika maganizo athu pa zimene tingathe kuchita m’malo movutika mtima ndi zimene sitingathe kuchita, moyo udzakhala wokhutiritsa kwambiri, ndipo tidzapeza chisangalalo mu utumiki wa Mulungu. (Salmo 126:5, 6)—9/1, tsamba 28.
▫ Kodi ndi ati amene ali mapindu a kukhululukira?
Kukhululukira ena kumachirikiza maunansi abwino (Aefeso 4:32); kumadzetsa osati mtendere wokha ndi anthu anzathu komanso mtendere wamaganizo (Aroma 14:19; Akolose 3:13-15); kukhululukira ena kumalambula njira yakuti machimo athu akhululukidwe (Mateyu 6:14); ndiponso, kumatithandiza kukumbukira kuti ife enife tifunikira kukhululukiridwa. (Aroma 3:23)—9/15, tsamba 7.
▫ Kodi ndimotani mmene chitsanzo cha mneneri Amosi chimatithandizira mu ntchito yathu yolalikira?
Mofanana ndi Amosi, ife sitimasintha kapenanso kuchepetsa mphamvu ya uthenga wa Mulungu. M’malo mwake, momvera timaulengeza mosasamala kanthu za mmene udzayambukirira omvetsera athu.—9/15, tsamba 17.
▫ Kodi ndi mikhalidwe iti ya Mulungu imene tiyenera kutsanzira?
Iŵiri yaikulu ndiyo luso la kulinganiza la Yehova ndi chimwemwe chake. (1 Akorinto 14:33; 1 Timoteo 1:11) Mikhalidwe imeneyi ya Mulungu njolinganizika, kotero kuti palibe umodzi wa iyo umene umakulitsidwa kuposa wina.—10/1, tsamba 10.
▫ Kodi ndi ati amene ali ena a masitepe otsimikizirika amene makolo akutenga kuthandiza ana awo kutumikira Yehova?
Mfungulo yofunika ndiyo kuyamba msanga. Mikhalidwe yokhomerezeka ndi maphunziro olandiridwa mkati mwa zaka zaubwana adzakhalako moyo wonse. (Miyambo 22:6) Nkofunika kuwaphunzitsa kumvera ndi kulemekeza Yehova ndi kulambira kwake pamisonkhano yonse. Makolo achipambano amaphunzira kuzindikira zikhoterero zoipa, ndipo amathandiza anawo kuwongolera zimenezi. (Miyambo 22:15) Potsirizira pake, yambani msanga kuika zonulirapo zateokrase kaamba ka mwana wanu zimene moyenerera angafikire.—10/1, masamba 27-8.
▫ Kodi ndi mbali yapadera yotani ya chikhululukiro cha Yehova imene tiyenera kuyesa kusonyeza?
Yehova amakhululukira ndi kuiŵala komwe. (Yeremiya 31:34) Zimenezi nzovuta kwa zolengedwa zaumunthu kuchita. Kufunika kwa kuchita motero kunagogomezeredwa ndi Yesu, monga momwe kwalembedwera pa Mateyu 6:14, 15.—10/15, masamba 25-6.
▫ Kodi nziti zimene zili zopinga zitatu pa kukhala kwathu achifundo?
Chifukwa cha chibadwa chathu cha uchimo, mikhalidwe ya nsanje ingazike mizu. Ngati tichitira nsanje munthu wina, kodi tingamchitire chifundo motani? Kupenyerera chiwawa kuli chopinga chinanso. Kumeneku kumatipangitsa kukhala opanda chifundo kulinga kwa anthu ena ovutika. Ndiponso, munthu wodzikonda mwachionekere amakhala wopanda chifundo. (1 Yohane 3:17)—11/1, masamba 19, 20.
▫ Kodi ndi maphunziro otani amene angaphunziridwe m’nkhani ya Malemba yonena za Yobu?
Cholembedwa cha Yobu chimatipangitsa kuzindikira kwambiri za machenjera a Satana ndipo chimatithandiza kuona mmene ulamuliro wachilengedwe chonse wa Yehova umayambukirira umphumphu waumunthu. Monga Yobu, onse amene amakonda Mulungu ayenera kuyesedwa. Nafenso tingapirire monga momwe Yobu anachitira, kusonyeza Satana kukhala wonama, ndi kulandira madalitso a Ufumu wa Mulungu.—11/15, tsamba 20.
▫ Kodi ndimotani mmene tcheyamani wa bungwe la akulu angasonyezere mkhalidwe wa kuŵerengera mkulu aliyense?
Paliponse pamene pali pothekera tcheyamani ayenera kupereka mfundo zokambitsirana pasadakhale kupatsa mkulu aliyense nthaŵi ya kulingalira kosamalitsa ndi kwapemphero pa mfundo iliyonse yondandalikidwa. Pamsonkhano wa akulu, iye sadzayesa kulamulira malingaliro a akulu ena koma adzawalimbikitsa kusonyeza “ufulu wa kulankhula” pankhani zimene akukambitsirana. (1 Timoteo 3:13, NW)—12/1, tsamba 30.