Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 3/1 tsamba 24
  • Anthu a Mulungu Adzipereka Mofunitsitsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anthu a Mulungu Adzipereka Mofunitsitsa
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Nyumba ya Ufumu Yanu Mumaiona Bwanji?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Malo Olambirira Yehova
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
  • Mmene Anthu Akuwonjezekera Pakufunika Nyumba Zina Mwamsanga
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Ntchito Yomanga Yomwe Imalemekeza Yehova
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulira
Nsanja ya Olonda—1995
w95 3/1 tsamba 24

Olengeza Ufumu Akusimba

Anthu a Mulungu Adzipereka Mofunitsitsa

DZINA lake linali Yosefe, ndipo anali nzika ya chisumbu cha Kupro. Anali pakati pa Akristu a m’zaka za zana loyamba amene anagulitsa minda ndi nyumba zawo kuti achirikize ndi ndalama kupitita patsogolo kwa Chikristu. Chifukwa cha mkhalidwe wake wachikondi ndi kuoloŵa manja, anadziŵidwa kukhala Barnaba, kutanthauza kuti “Mwana wa Chitonthozo.”​—Machitidwe 4:34-37, NW.

Kukondwerera ena kwapadera kumeneko nthaŵi zonse kwakhala chizindikiro cha olambira oona a Yehova. Mboni za Yehova lerolino zimachita chimodzimodzi, monga momwe kwasonyezedwera ndi chokumana nacho chotsatirachi chochokera ku Solomon Islands.

Gulu la Mboni zoposa 60 la ku Australia ndi New Zealand linapita ku Honiara, likulu la Solomon Islands pa Guadalcanal. Linadza kudzathandiza kumanga Nyumba Yosonkhaniramo misonkhano yaikulu Yachikristu. Kunangotenga milungu iŵiri kuti aimike nyumbayo yokhala ndi malo okhala anthu pafupifupi 1,200!

Pafupifupi panthaŵi yofananayo, boma lina la tauni yaing’ono ya Munda lakumaloko, pa chisumbu cha New Georgia, linapatsa malo mpingo wa Mboni za Yehova pakati penipeni pa tauniyo. Izo zinafuna kumanga Nyumba Yaufumu, malo olambirira. Ndipo inali yofunika kwambiri kwa iwo. Ankasonkhana m’chipinda chochezera cha nyumba ina yaing’ono yofoleredwa ndi masamba, koma analibe ndalama zomangira Nyumba Yaufumu.a Mpingowo unapangidwa makamaka ndi anthu okalamba ndi odwala ndi ana, ndipo panalibe amene anadziŵa ntchito yomanga.

Pafupifupi makilomita 380 pa chisumbu cha Guadalcanal, Mboni mu mzinda wa Honiara zinadzipereka mofunitsitsa. (Salmo 110:3) Izo zinalingalira kuti: “Ngati abale athu akumaiko ena anali ofunitsitsa kutimangira Nyumba Yosonkhaniramo m’milungu iŵiri, ife ndithudi tingathandize abale athu ku Munda ndi kuwamangira Nyumba Yaufumu m’milungu iŵiri.”

Zimenezo nzimene zinachitika. Tsiku lina bwato lowolotsa lodzazidwa ndi Mboni zogwira ntchito modzifunira zokondwera linafika ku Munda. Amuna ndi akazi, achikulire ndi achichepere, onsewo anadzitanganitsa kutsitsa katundu wawo ndi kukonzekera kuyamba kumanga ndi matabwa, simenti, malata, ndi milimo ina imene inali itafika ku Munda pasadakhale.

Ntchitoyo itangoyamba, mipope inaleka kutulutsa madzi chifukwa cha mkuntho woipa kwambiri mu mzindawo. Komabe, zimenezi sizinakhale vuto lalikulu. Mbonizo zinakumba chitsime chimene chinapereka madzi mkati mwa ntchito yomanga yonseyo. Bwanji nanga za chakudya cha antchito onse? Zimenezonso sizinali vuto. Antchito odzifunira a ku Honiara anatumizidwa ndi chakudya chochuluka choperekedwa ndi mipingo ya ku Honiara. Anabweretsanso ophika awo!

Anansi anapenyerera kuchitika kwa ntchitoyo mosakhulupirira. Mmodzi wa iwo anati: “Kuno zinthu sizimachitika m’masiku oŵerengeka chabe. Zimatenga zaka.” Mnansi wina, mtsogoleri wachipembedzo, anavomereza kuti tchalitchi chake chakhala chikumangidwa kwa zaka 20 zapitazo ndi kuti sichinathebe. Mosiyana ndi zimenezo, Nyumba Yaufumu ya Mboni za Yehova yatsopanoyo ku Munda inamalizidwa m’masiku khumi okha!

[Mawu a M’munsi]

a Nyumba yofoleredwa ndi masamba yopangidwa ndi milimo yamtchire kapena ya m’nkhalango. Feremu yake imapangidwa ndi mitengo, ndipo denga ndi chipupa zimakutidwa ndi mikwamba yopangidwa ndi makhwatha a kanjedza opindiridwa patimitengo ndi olukidwa ndi luzi.

[Mapu patsamba 24]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

South Pacific Ocean

SOLOMON ISLANDS

Munda

GUADALCANAL

Honiara

[Mapu]

AUSTRALIA

NEW ZEALAND

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena