Mboni za Yehova Padziko Lonse—India
INDIA! Chigawo chachikulu cha kontinenti chimenechi ndicho kwawo kwa munthu mmodzi aliyense pa anthu asanu ndi mmodzi a pa pulanetili. Muli zinenero ndi malankhulidwe zoposa 1,000 zonse pamodzi, m’dziko limeneli la zosiyanasiyana. Anthu ake ambiri ndiwo Ahindu, okwanira 83 peresenti, pamene kuli kwakuti 11 peresenti ndiwo Asilamu, ndipo mbali yotsala imapangidwa ndi Asikhi, Abuda, Ajaini, ndi odzitcha kuti Akristu.
Mboni za Yehova zakhala ndi chipambano chapadera ku India m’zaka zaposachedwapa. Zapeza anthu onga nkhosa amene akufuna kuima mochirimika kumbali ya Ufumu wa Yehova, ngakhale kuti pali zitsenderezo zosiyanasiyana ndi chitsutso.
Mwachitsanzo, msungwana wina wa m’banja la Ahindu osunga mwambo anapunduka chifukwa cha poliyo kuyambira pa ubwana. Mavuto amene anakumana nawo anamchititsa kuganiza za Mulungu ndi chifuno cha moyo. Anafunafuna yankho m’zipembedzo zambiri komabe sanapeze chitonthozo. Chotero, anataya chikhulupiriro chake m’zipembedzo zonse, koma osati mwa Mulungu.
Panthaŵiyi Mboni zina ziŵiri zinafikira msungwanayu mu utumiki wawo wa kunyumba ndi nyumba. “Ndinagwetsa misozi pamene ndinawamva akuŵerenga Chivumbulutso 21:4,” akukumbukira motero. Analandira zofalitsidwa zambiri za Watch Tower Society ndipo anavomera phunziro la Baibulo lapanyumba ngakhale kuti amake anatsutsa. Msungwanayo anasintha moyo wake kwambiri, anachirimika molimba mtima pa kutsutsidwa ndi achibale ake, ndipo anakhala Mboni yobatizidwa. Iye akuti: “Ndachoka patali, ndipo zinali zovuta. Koma Yehova Mulungu nthaŵi zonse wakhala nane ndi kundipatsa mtendere waukulu ndi chimwemwe.”
Kuchirimika pa Kulambira Koyera pa Sukulu
Mlongo wina wachichepere anapemphedwa ndi mphunzitsi wake kupita ku tchalitchi cha Katolika pamodzi ndi a m’kalasi onse. Mlongoyo anakana mwaulemu, akumanena kuti anali mmodzi wa Mboni za Yehova ndipo sangalambire wina aliyense kapena kanthu kena kalikonse kusiyapo Yehova. Mphunzitsiyo anati pamene ena onse adzapita kutchalitchi, nayenso adzayenera kupita. Koma mlongoyo anachirimika nati popeza kuti anthu amene adzapita kutchalitchiko sadzapemphera kwa Yehova, sangathe kuona chomwe angakhalire pakati pawo.
Chifukwa cha kuchirimika kwa msungwanayo, mphunzitsi wake anafuna kudziŵa zambiri. Chotero tsiku lotsatira mlongoyo anampatsa nkhani ina ya mu Nsanja ya Olonda yonena za kulambira Yehova. Atachita chidwi ndi zimene anaŵerenga, mphunzitsiyo anamchotsa m’zochitika zonse za chipembedzo kusukulu. Mlongoyo anagaŵira magazini khumi kwa iye ndi aphunzitsi ena.
Kumvera Lamulo la Mulungu la Mwazi Kufupidwa
Posachedwapa viral fever inabuka monga mliri m’mbali zina za boma la Kerala. Nthenda imeneyi imawononga impso kotheratu ndipo imachititsa kuti munthu akhale pamakina a dialysis. Kaŵirikaŵiri mwazi umagwiritsiridwa ntchito. Mu mzinda wina anthu 14 anagonekedwa m’chipatala chifukwa cha nthenda imeneyi. Mmodzi wa odwala ameneŵa anali Mboni, mkulu wa mumpingo wakumaloko. Anauzidwa kuti mankhwala okha amene analipo anali a kuthira mwazi. Mkuluyo anafotokoza zikhulupiriro zake za m’Malemba ndipo anakana mwazi mwamphamvu. (Machitidwe 15:28, 29) Atakangana naye kwambiri madokotala anati adzafa chifukwa cha kukana kwake kuthiridwa mwazi.
Odwala 13 enawo anathiridwa mwazi. Mwatsoka, onsewo anafa m’masiku oŵerengeka. Mbaleyo ndiye yekha anapulumuka! Akuluakulu achipatala anadabwa kwambiri. Antchito za m’chipatala anachita chidwi kwambiri ndi ziŵalo za mpingo zodzamzonda nthaŵi zonse. Atatuluka m’chipatala, mbaleyo anapita kukathokoza madokotala, koma iwo anati: “Mutithokozeranji? Thokozani Mulungu wanu, Yehova. Iye ndiye Amene wakupulumutsani. Chonde mutipempherere nafenso kwa Mulungu wanu, Yehova.”
[Bokosi patsamba 24]
ZIŴERENGERO ZA DZIKOLO
Chaka Chautumiki cha 1994
CHIŴERENGERO CHAPAMWAMBA CHA OCHITIRA UMBONI: 14,271
KUGAŴA: Mboni 1 pa anthu 65,266
OFIKA PACHIKUMBUTSO: 38,192
AVAREJI YA OFALITSA AUPAINIYA: 1,780
AVAREJI YA MAPHUNZIRO A BAIBULO: 12,453
CHIŴERENGERO CHA OBATIZIDWA: 1,312
CHIŴERENGERO CHA MIPINGO: 410
OFESI YA NTHAMBI: LONAVLA
[Chithunzi patsamba 25]
Ofesi ya nthambi, Lonavla
[Chithunzi patsamba 25]
Kuchitira umboni za msonkhano wa “Mbiri Yabwino Yosatha” mu 1963
[Chithunzi patsamba 25]
Kulalikira kwa wamalonda kunja kwa Red Fort mu Delhi