Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 11/15 tsamba 8-9
  • Mboni za Yehova Padziko Lonse—New Zealand

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mboni za Yehova Padziko Lonse—New Zealand
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Mu New Zealand—Tsiku Loyenera Kukumbukira
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Mboni za Yehova Padziko Lonse—Bahamas
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Yehova Wandisamalira Bwino
    Nsanja ya Olonda—1992
Nsanja ya Olonda—1995
w95 11/15 tsamba 8-9

Mboni za Yehova Padziko Lonse​—New Zealand

KODI zisumbu zingatamande Yehova? Inde, malinga ndi kunena kwa Yesaya 42:10: “Imbirani Yehova nyimbo yatsopano, ndi matamando ake kuchokera ku malekezero a dziko lapansi; . . . zisumbu ndi okhala mommo.” Zisumbu zimene zimapanga New Zealand zimatamandadi Yehova. Dziko lotchuka ndi nyanja zake, mathiriro, mapiri aatali, mitsinje ya madzi oundana, magombe, nkhalango za mvula zokongoletsedwa ndi ma fern, ndi malo odyera zifuyo obiriŵira, New Zealand amalankhula bwino kwambiri za ulemerero ndi ukulu wa Mlengi wakumwamba ndi dziko lapansi.

Kungoyambira pa chiyambi cha zaka za zana lino, nzika zowonjezereka za New Zealand zawonjezera mawu awo pa kutamanda Yehova mwa kutembenukira kwa iye pa kulambira koyera ndi kuuza ena uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Posachedwapa, Mboni ina imene inamva chokumana nacho china chabwino chonena za kuchitira umboni kwa achibale inasankha kuyesayesa zimenezi kwa a m’banja lake. Anapereka mphatso ya makope a buku lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi kwa a m’banja lake angapo. Kodi nchiyani chimene chinachitika? Iye akusimba kuti mlongo wake mmodzi ndi mbale wake mmodzi tsopano akuphunzira Baibulo, mdzukulu wake wabatizidwa kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova, ndipo tsopano ena akumvetsera kwambiri choonadi cha Mawu a Mulungu. Iye akali ndi munda waukulu woti agwiremo ntchito; kuwonjezera pa makolo ake, iyeyo ali ndi abale ake asanu ndi mmodzi ndi alongo ake asanu ndi anayi!

Kutamanda Yehova kumachitikanso pamene Mboni zichita mogwirizana pomanga Nyumba za Ufumu. Mwachitsanzo, wolemba nkhani m’nyuzipepala Roy Perkins analemba mu Opotiki News ya May 17, 1994 kuti: “Pokhala wosakhulupirira, ndinachita chidwi kwambiri ndi ntchito ndi zoyesayesa za antchito onse odzipereka amene anathera nthaŵi yochuluka ndi kuyesayesa pantchitoyo chifukwa cha kukonda Mulungu wawo.

“Pa maola onse a ntchito yochitidwa pa kutha kwa mulungupo sindinaonepo kapena kumvapo mkangano wa antchito . . . Akazi anakwera pa nsanja zomangira nyumba akumagwira ntchito limodzi ndi anzawo achimuna, akumapala ndi kusalaza makoma, kutukula, kunyamula zinthu, zonsezo zikumachitidwa mwamtendere ndi mwachimwemwe.

“Ndipo panalibe mphindi imene inawawanyidwa ndi aliyense chifukwa cha kusuta fodya. Anthu onsewo mosasamala kanthu za zimene anali kuchita anagwira ntchito mumpweya woyera ndi wabwino kusiyapo za nkhungu ya penti ndi fumbi la njerwa.”

Bungwe la akulu la Mpingo wa Opotiki linalemba kuti: “Ntchito yonseyo inachititsa chidwi anthu a m’tauniyo. Zichita ngati kuti aliyense akulankhula za ntchitoyo. Maphunziro a Baibulo angapo ayambidwa. Makamaka phunziro lina limene latikondweretsa ndilo la banja lina lokonda chipembedzo kwambiri limene kwa zaka zambiri lapempha kuti tisalifikire. Iwo anafika pamalopo tsiku lililonse ndiyeno ku msonkhano. Pambuyo pake mwamuna anati, ‘Ndikutha kuona kuti ndinu anthu a Mulungu. M’moyo wanga wonse, ndakhala ndikulakalaka kuchokera pansi pa mtima kuyanjana ndi anthu onga ameneŵa.’”

Chaka chotsatira, wolemba nkhani wina wa Otago Daily Times ananena mawu otsatirapowa ponena za Nyumba Yaufumu yomangidwa mofulumira ku Dunedin: “Chinali chochita chapadera, chitsanzo chapadera cha chisonkhezero ndi kudzithandiza.” Nyuzipepala imodzimodziyo inanena kuti: “Anthu a mu mzinda anapenyerera mosirira pamene chinyumbacho chinali kumangidwa pamaso pawo, ndipo mwina ambiri anali kusinkhasinkha za kusintha zinthu kwina ndi ntchito zabwino zimene zingachitidwe ngati antchito odzipereka ofanana ndi iwo a mzimu waukulu wogwirizana angakhalepo. Nyumba ya Ufumu ili chizindikiro chonyaditsa cha zoyesayesa zomangirira zopindulitsa.”

Pakati pa mazana ambiri amene anafika pamalo omangawo, mwamuna wina ananena kuti Mboni zinali kumanga “matchalitchi” pamene kuli kwakuti chipembedzo chake chinali kuwagulitsa chifukwa cha kuchepa kwa ziŵalo zake. “Mukanayembekezera miyezi ina khumi ndi iŵiri, mukanagula tchalitchi chathu chimodzi,” anatero. “Tifunikira kugulitsapo chimodzi chifukwa chakuti sitingathe kulipirira. Komatu, anthunu mulibe abusa owalipira malipiro. . . . Ndiyenso nyumba zanu nzamtengo wotsika pozisamalira, osati nyumba zazitali zokhala ndi nsonga zimene zili zosatheka kuzisamalira.”

Mwachionekere, zisumbu zingatamandedi Mulungu. Zitamando za Yehova zipitirizebetu kumveka m’dziko lokongola limeneli la mu Pacific​—ndi padziko lonse!

[Bokosi patsamba 9]

ZIŴERENGERO Za DZIKOLO:

Chaka Chautumiki cha 1994

CHIŴERENGERO CHAPAMWAMBA CHA OCHITIRA UMBONI: 12,867

KUGAŴA: Mboni 1 pa anthu 271

OFIKA PA CHIKUMBUTSO: 24,436

AVAREJI YA OFALITSA AUPAINIYA: 1,386

AVAREJI YA MAPHUNZIRO A BAIBULO: 7,519

CHIŴERENGERO CHA OBATIZIDWA: 568

CHIŴERENGERO CHA MIPINGO: 158

OFESI YA NTHAMBI: MANUREWA

[Chithunzi patsamba 9]

Apainiya akupita kumunda m’ma 1930

[Chithunzi patsamba 9]

Nyumba za nthambi ku Manurewa

[Chithunzi patsamba 9]

Kulalikira uthenga wa Ufumu ku Devonport, Auckland

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena