Midzi Yopulumukirako—Makonzedwe Achifundo A Mulungu
“Midzi isanu ndi umodzi imene ndiyo yopulumukirako . . . kuti aliyense adamupha munthu osati dala athaŵireko.”—NUMERI 35:15.
1. Kodi Mulungu amauona motani moyo ndi liwongo la mwazi?
YEHOVA MULUNGU amaona moyo wa munthu kukhala wopatulika. Ndipo moyo uli m’mwazi. (Levitiko 17:11, 14) Chotero, Kaini, munthu woyamba kubadwa pa dziko lapansi, anakhala ndi liwongo la mwazi pamene anapha mphwake Abele. Nchifukwa chake, Mulungu anauza Kaini kuti: “Mawu a mwazi wa mphwako andifuulira ine kunthaka.” Mwazi umene unaipitsa nthaka pamalo omwe anaphedwerapo unapereka umboni wakachetechete koma wamphamvu wa moyo umene unadulidwa mwankhanza. Mwazi wa Abele unafuulira Mulungu kuti abwezere chilango.—Genesis 4:4-11.
2. Kodi kulemekeza moyo kwa Yehova kunagogomezeredwa motani pambuyo pa Chigumula?
2 Kulemekeza moyo wa munthu kwa Mulungu kunagogomezeredwa pamene Nowa wolungama ndi banja lake anatuluka m’chingalaŵa monga opulumuka Chigumula cha dziko lonse. Nthaŵiyo Yehova anawonjezera chakudya cha munthu akumaphatikizapo nyama koma osati mwazi. Ndiponso analamula kuti: “Mwazi wanu wa miyoyo yanu ndidzafuna; padzanja la zinyama zonse ndidzaufuna: ndi padzanja la munthu, padzanja la mbale wake wa munthu ndidzaufuna moyo wa munthu. Amene akhetsa mwazi wa munthu, ndi munthunso mwazi wake udzakhetsedwa: chifukwa m’chifanizo cha Mulungu iye anampanga munthu.” (Genesis 9:5, 6) Yehova anazindikira kuyenera kumene wachibale wapafupi wa wophedwayo anali nako kwa kupha iye amene anamupha atakumana naye.—Numeri 35:19.
3. Kodi Chilamulo cha Mose chinagogomezera chiyani pa kupatulika kwa moyo?
3 M’Chilamulo chimene Israyeli anapatsidwa mwa mneneri Mose, kupatulika kwa moyo kunagogomezeredwa mobwerezabwereza. Mwachitsanzo, Mulungu analamula kuti: “Usaphe.” (Eksodo 20:13) Kulemekeza moyo kunaonekeranso pa zimene Chilamulo cha Mose chinanena pa imfa yokhudza mkazi wapakati. Chilamulo chinanena kuti iye kapena mwana wake wosabadwa akafa chifukwa cha kumenyana kwa amuna aŵiri, oweruza anafunikira kupenda mikhalidwe ndi kuona ngati zinali zadala, koma chilango chake chinkakhala “moyo kulipa moyo.” (Eksodo 21:22-25) Komabe, kodi panali njira ina imene Mwisrayeli wopha munthu akanapeŵera zotsatirapo za mbanda yake?
Kodi Kunali Kuteteza Apandu Opha Anzawo?
4. Kodi ndi malo otani othaŵirako apandu amene akhalako kumbuyoku kunja kwa Israyeli?
4 M’mitundu ina kunja kwa Israyeli, opha anzawo ndi apandu ena anali ndi malo othaŵirako. Zinali choncho m’malo onga kachisi wa Artemi, mulungu wachikazi m’Efeso wakale. Ponena za malo ngati amenewo, kwanenedwa kuti: “Akachisi ena anali malo osonkhezera apandu; ndipo nthaŵi zambiri panafunika kuchepetsa chiŵerengero cha malo othaŵirako apandu. Ku Atene boma linavomereza malo oŵerengeka okha monga othaŵirako apandu (mwachitsanzo, kachisi wa Theseus wa akapolo); m’nthaŵi ya Tiberiyo magulu a apandu mu akachisi anakhala owopsa kwambiri kwakuti ndi mizinda yochepa yokha imene inaloledwa kukhala ndi Malo Othaŵirako Apandu (m’chaka cha 22).” (The Jewish Encyclopedia, 1909, Voliyumu II, tsamba 256) Pambuyo pake, matchalitchi a Dziko Lachikristu anakhala malo othaŵirako apandu, koma zimenezi zinachititsa kuti boma lilandidwe mphamvu ndi kuperekedwa kwa ansembe ndipo zimenezi zinapinga chilungamo. Potsiriza pake kugwiritsira ntchito molakwa malowo kunachititsa makonzedwewa kutha.
5. Kodi pali umboni wotani wakuti Chilamulo sichinalole kuchitira chifundo munthu amene anapha mnzake chifukwa chosasamala?
5 Kwa Aisrayeli, anthu opha dala anzawo analibe kothaŵira. Ngakhale wansembe Wachilevi amene anali kutumikira pa guwa la nsembe la Mulungu anafunika kutengedwa ndi kuphedwa chifukwa chopha mnzake mwachiŵembu. (Eksodo 21:12-14) Ndiponso, Chilamulo sichinalole kuchitira chifundo wina amene anapha mnzake chifukwa chosasamala. Mwachitsanzo, munthu anafunika kumanga kampanda ku tsindwi latyatyatya la nyumba yake yatsopano. Akanapanda kutero, liwongo la mwazi likanakhala panyumbayo ngati wina akanagwa ku tsindwiko ndi kufa. (Deuteronomo 22:8) Ndiponso, ngati mwini ng’ombe yokonda kutunga ena anachenjezedwa koma sanaisunge nyamayo ndipo inapha wina, mwini ng’ombeyo anali ndi liwongo la mwazi ndipo anayenera kuphedwa. (Eksodo 21:28-32) Umboni wina wakuti Mulungu amalemekeza moyo kwambiri umasonyezedwa ndi mfundo yakuti aliyense wakupha mbala anali kukhala ndi liwongo la mwazi ngati anachita zimenezo masana pamene akanatha kuona mbalayo ndi kuidzindikira. (Eksodo 22:2, 3) Pamenepa, nkwachionekere kuti malamulo olungama a Mulungu sanalole kuti anthu opha dala anzawo apeŵe chilango cha imfa.
6. Kodi lamulo la “moyo kulipa moyo” linakwaniritsidwa motani m’Israyeli wakale?
6 Ngati munthu anaphedwa mu Israyeli wakale, mwazi wake unafunika kulipsira. Lamulo la “moyo kulipa moyo” linakwaniritsidwa pamene wopha mnzakeyo anaphedwa ndi “wolipsa mwazi.” (Numeri 35:19) Wolipsirayo anali mwamuna wachibale wapafupi wa wophedwayo. Nanga bwanji za akupha anthu mwangozi?
Makonzedwe Achifundo a Yehova
7. Kodi Mulungu anawapangira makonzedwe otani aja amene anapha mnzawo mwangozi?
7 Aja amene anapha wina mwangozi, Mulungu mwachikondi anawakonzera midzi yopulumukirako. Ponena za imeneyi, Mose anauzidwa kuti: “Nena ndi ana a Israyeli, nuti nawo, Pakuwoloka inu Yordano kuloŵa m’dziko la Kanani, muikire midzi ikukhalireni midzi yopulumukirako; kuti wakupha mnzake wosati dala athaŵireko. Ndipo midziyo ikukhalireni yakupulumuka wolipsa; kuti wakupha mnzake asafe, kufikira ataima pamaso pa msonkhano amweruze. Ndipo midziyo muipereke ikukhalireni midzi isanu ndi umodzi yopulumukirako. Mupereke midzi itatu tsidya lino la Yordano, ndi midzi itatu mupereke m’dziko la Kanani, ndiyo yopulumukirako . . . kuti aliyense adamupha munthu osati dala athaŵireko.”—Numeri 35:9-15.
8. Kodi midzi yopulumukirako inali kuti, ndipo kodi opha anthu mwangozi anathandizidwa motani kufikako?
8 Pamene Aisrayeli analoŵa m’Dziko Lolonjezedwa, iwo momvera anakhazikitsa midzi isanu ndi umodzi yopulumukirako. Itatu mwa midzi imeneyi—Kedesi, Sekemu, ndi Hebroni—inali kumadzulo kwa Mtsinje wa Yordano. Kummaŵa kwa Yordano kunali midzi yopulumukirako ya Golani, Ramoti, ndi Bezeri. Midzi isanu ndi umodzi yopulumukirako inali pamalo osavuta kufikapo m’mbali mwa misewu yosamalidwa bwino. Pamalo oyenera m’mbali mwa misewu imeneyi, panali zikwangwani zolembedwa kuti “kopulumukira.” Zikwangwani zimenezi zinaloza kumene mudzi wopulumukirako unali, ndipo wakupha munthu mwangozi anathaŵira ku umene unali pafupi naye kupulumutsa moyo wake. Kumeneko anatetezedwa kwa wolipsa mwazi.—Yoswa 20:2-9.
9. Kodi nchifukwa ninji Yehova anapereka midzi yopulumukirako, ndipo inaperekedwa kaamba ka phindu la ayani?
9 Kodi nchifukwa ninji Mulungu anakonza midzi yopulumukirako? Inakonzedwa kuti dziko lisaipitsidwe ndi mwazi wosachimwa ndi kuti liwongo la mwazi lisakhale pa anthu. (Deuteronomo 19:10) Kodi midzi yopulumukirako inakonzedwa kaamba ka phindu la ayani? Chilamulo chinati: “Midzi isanu ndi umodzi imene ndiyo yopulumukirako ana a Israyeli, ndi mlendo, ndi wokhala pakati pawo; kuti aliyense adamupha munthu osati dala athaŵireko.” (Numeri 35:15) Chotero, kuti atsate chilungamo ndi zolinga zake polola chifundo, Yehova anauza Aisrayeli kukhazikitsa midzi yopulumukirako opha anzawo mwangozi amene anali (1) mbadwa za Israyeli, (2) alendo mu Israyeli, kapena (3) odzakhala m’dziko pakati pawo ochokera kumaiko ena.
10. Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti midzi yopulumukirako inali makonzedwe achifundo opangidwa ndi Mulungu?
10 Ndi bwino kudziŵa kuti ngakhale ngati munthu anali wakupha mnzake mwangozi, anafunika kuphedwa molingana ndi lamulo la Mulungu lakuti: “Amene akhetsa mwazi wa munthu, ndi munthunso mwazi wake udzakhetsedwa.” Chotero, kunali kokha mwa makonzedwe achifundo a Yehova Mulungu kuti wakupha mnzake mwangozi azithaŵira ku umodzi wa midzi yopulumukirako. Mwachionekere, anthu ambiri anamchitira chifundo aliyense amene anali kuthaŵa wolipsa mwazi, pakuti onse anali kudziŵa kuti nawonso akanachita tchimo longa limenelo mwangozi nafuna kopulumukira ndi chifundo.
Kuthaŵira Kopulumukirako
11. Mu Israyeli wakale, kodi munthu anali kuchita chiyani akapha wantchito mnzake mwangozi?
11 Mwina fanizo lingakuthandizeni kumvetsetsa makonzedwe achifundo a Mulungu a kopulumukirako. Tinene kuti munali kutema mitengo m’Israyeli wakale. Ndiyeno nkhwangwa ndikuguluka mumpini ndi kutema wantchito mnzanu nafa. Kodi mukanachita chiyani? Eya, Chilamulo chinali ndi makonzedwe a mkhalidwe umenewu. Mosakayikira, mukanagwiritsira ntchito makonzedwe otsatirawa amene Mulungu anapereka: “Mlandu wa munthu wakupha mnzake wakuthaŵirako [ku mudzi wopulumukirako] nakhala ndi moyo ndiwo: wakupha mnzake osati dala, osamuda kale lonse; monga ngati munthu analoŵa kunkhalango ndi mnzake kutema mitengo, ndi dzanja lake liyendetsa nkhwangwa kutema mtengo, ndi nkhwangwa iguluka m’mpinimo, nikomana ndi mnzake, nafa nayo; athaŵire ku wina wa midzi iyi, kuti akhale ndi moyo.” (Deuteronomo 19:4, 5) Komabe, ngakhale ngati munafika m’mudzi wopulumukiramowo, simukanakhala womasuka pamlandu wonse wa zimene zinachitika.
12. Kodi nchiyani chinali kuchitika pambuyo poti wopha munthu mwangozi wafika ku mudzi wopulumukirako?
12 Ngakhale kuti akanakulandirani bwino, mukanafunikira kufotokoza mlandu wanu kwa akulu pachipata cha mudzi wopulumukirakowo. Pambuyo poloŵa m’mudziwo, akanakubwezani kukaweruzidwa ndi akulu oimira mpingo wa Israyeli pazipata za mudzi woyang’anira dera kumene munapherako mnzanu. Kumeneko mukanakhala ndi mwaŵi wosonyeza kuti munalibe liwongo.
Pamene Opha Anzawo Anali Kuweruzidwa
13, 14. Kodi ndi zinthu zina ziti zimene akulu anali kufuna kudziŵa poweruza mlandu wa wopha munthu?
13 Pamlandu wanu pamaso pa akulu okhala pachipata cha mudzi woyang’anira deralo, inu mosakayikira mukanazindikira ndi chiyamikiro kuti iwo anasumika kwambiri maganizo pa khalidwe lanu lakumbuyo. Akuluwo akanapenda mosamala unansi wanu ndi wakufayo. Kodi munamuda munthuyo, kumlalira, ndi kumupha dala? Ngati zinali choncho, akuluwo akanakuperekani kwa wolipsa mwazi, ndipo mukanafa. Amuna athayo ameneŵa anayenera kudziŵa chofunika cha Chilamulo chakuti ‘achotse liwongo la mwazi wosachimwa m’Israyeli.’ (Deuteronomo 19:11-13) Momwemonso, pankhani yachiweruzo lerolino, akulu Achikristu afunikira kudziŵa bwino Malemba, kuwatsatira pamene akulingalira za mzimu ndi khalidwe la wochita cholakwa zimene iye anasonyeza kumbuyoku.
14 Pokufunsani mokoma mtima, akulu a mudziwo akanafuna kudziŵa ngati munaŵenderera wakufayo. (Eksodo 21:12, 13) Kodi munambisalira pomukantha? (Deuteronomo 27:24) Kodi munapsa naye mtima kwambiri kwakuti munaganiza zochita chiŵembu cha kumupha? Ngati munatero, mukanayenera kufa. (Eksodo 21:14) Akuluwo makamaka akanafuna kudziŵa ngati munali kudana ndi munthu wakufayo. (Deuteronomo 19:4, 6, 7; Yoswa 20:5) Tinene kuti akuluwo anakupezani wopanda liwongo nakubwezerani ku mudzi wopulumukirako. Ha, mukanayamikira chotani nanga chifundo chosonyezedwacho!
Moyo m’Mudzi Wopulumukiramo
15. Kodi ndi ziletso zotani zimene zinaikidwa pa wakupha munthu mwangozi?
15 Wopha munthu mwangozi anafunikira kukhala m’mudzi wopulumukiramo kapena mkati mwa malire a mtunda wa mikono 1,000 (pafupifupi mafiti 1,450) kunja kwa malinga ake. (Numeri 35:2-4) Ngati anadutsa malirewo, akanakumana ndi wolipsa mwazi. Zimenezo zitachitika, wolipsayo akanapha wopha mnzakeyo ndipo iyeyo sakanalangidwa. Komanso wopha mnzake sanamangidwe unyolo kapena kuikidwa m’ndende. Pokhala nzika ya mudzi wopulumukirako, anafunikira kuphunzira umisiri, kukhala wantchito, ndi kukhala munthu wothandiza anthu ena.
16. (a) Kodi wopha munthu mwangozi anali kukhala nthaŵi yotani m’mudzi wopulumukiramo? (b) Kodi nchifukwa ninji imfa ya mkulu wa ansembe inatheketsa wopha munthu kuchoka m’mudzi wopulumukiramo?
16 Kodi wopha mnzake mwangozi anafunikira kukhala nthaŵi yotani m’mudzi wopulumukiramo? Mwinamwake moyo wake wonse. Mulimonse mmene zikanakhalira, Chilamulo chinati: “Akadakhala m’mudzi wake wopulumukiramo kufikira atafa mkulu wa ansembe; koma atafa mkulu wa ansembe wakupha munthuyo abwere ku dziko lakelake.” (Numeri 35:26-28) Kodi nchifukwa ninji imfa ya mkulu wa ansembe inalola wakupha munthu mwangozi kuchoka m’mudzi wopulumukiramo? Eya, mkulu wa ansembe anali mmodzi wa anthu otchuka kwambiri pamtunduwo. Chotero imfa yake inali chochitika chapadera kwambiri kwakuti inali kudziŵika kwa mafuko onse a Israyeli. Chifukwa chake onse othaŵa amene anali m’midzi yopulumukirako anali kubwerera kwawo osakhala pangozi kwa olipsa mwazi. Chifukwa? Chifukwa chakuti Chilamulo cha Mulungu chinanena kuti mpata wakuti wolipsayo aphe uja amene anapha mnzake unatha pa imfa ya mkulu wa ansembe, ndipo aliyense anadziŵa zimenezi. Ngati wachibaleyo analipsira imfayo pambuyo pa zimenezo, anali kukhala wakupha munthu ndipotu anali kupatsidwa chilango cha kupha munthu.
Zotulukapo Zake Zachikhalire
17. Kodi zotulukapo zake za ziletso zoikidwa pa wakupha munthu mwangozi zingakhale zinali zotani?
17 Kodi zotulukapo zake za ziletso zoikidwa pa wopha munthu mwangozi zingakhale zinali zotani? Ziletsozo zinali kumkumbutsa kuti anapha mnzake. Mosakayikira, iye pambuyo pake anaona moyo wa munthu kukhala wopatulika nthaŵi zonse. Ndiponso, sakanaiŵala konse kuti anasonyezedwa chifundo. Pokhala atasonyezedwa chifundo, iye akanafunadi kukhala wachifundo kwa ena. Makonzedwe a midzi yopulumukirako ndi ziletso zake anapindulitsanso anthu onse. Motani? Anawasonyezadi bwino lomwe kuti iwo sanayenera kukhala osasamala kapena onyalanyaza moyo wa munthu. Choncho Akristu ayenera kukumbukira kuti afunika kupeŵa kusasamala kumene kungachititse imfa ya ngozi. Ndiyenonso, makonzedwe achifundo a Mulungu a midzi yopulumukirako ayenera kutisonkhezera kusonyeza chifundo ngati kuteroko kuli koyenera.—Yakobo 2:13.
18. Kodi makonzedwe a Mulungu a midzi yopulumukirako anali opindulitsa m’njira zotani?
18 Makonzedwe a Yehova Mulungu a midzi yopulumukirako analinso opindulitsa m’njira zina. Anthu sanapange timagulu tolanga apandu tolondalonda wopha munthu poganiza kuti iye anali waliwongo ngakhale asanaweruzidwe. M’malo mwake, anamuyesa wopanda liwongo la kupha munthu dala, ndipo anamthandiza kuthaŵa. Ndiponso, makonzedwe a midzi yopulumukirako anali osiyana kwambiri ndi makonzedwe amasiku ano a kuika opha anthu m’ndende, kumene anthu amawachirikiza ndi ndalama zawo ndi kumenenso nthaŵi zambiri amakhala apandu oipitsitsa chifukwa cha kuyanjana kwawo ndi amaliwongo ena. M’makonzedwe a midzi yopulumukirako, sipanafunikire kumanga, kusamalira, ndi kulonda ndende zamalinga zotchingidwa ndi zitsulo, ndi zodya ndalama kumene akaidi nthaŵi zambiri amafuna kuthaŵa. M’malo mwake, wopha mnzake anafunafuna “ndende” nakhala komweko mkati mwa nthaŵi yoikika. Anafunikiranso kukhala wantchito, motero akumachita kanthu kena kuthandiza anthu anzake.
19. Kodi pakubuka mafunso otani ponena za midzi yopulumukirako?
19 Indedi, makonzedwe a Yehova a midzi yopulumukirako m’Israyeli otetezera opha anthu mwangozi anali achifundo. Makonzedwe ameneŵa anachirikizadi ulemu kaamba ka moyo. Komabe, kodi midzi yopulumukirako yakale ili ndi tanthauzo kwa anthu okhala m’zaka za zana la 20? Kodi tingakhale ndi liwongo la mwazi kwa Yehova Mulungu koma osazindikira kuti tifunikira chifundo chake? Kodi midzi yopulumukirako m’Israyeli ili ndi tanthauzo lamakono lililonse kwa ife?
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi Yehova amauona motani moyo wa munthu?
◻ Kodi ndi makonzedwe achifundo otani amene Mulungu anapangira opha anthu mwangozi?
◻ Kodi wakupha munthu analoŵa motani m’mudzi wopulumukiramo, ndipo anayenera kukhalamo nthaŵi yotani?
◻ Kodi zotulukapo zake za ziletso zoikidwa pa wakupha munthu mwangozi zingakhale zinali zotani?
[Mapu patsamba 12]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Midzi yopulumukirako mu Israyeli inali pamalo osavuta kufikapo
KEDESI Mtsinje wa Yordano GOLANI
SEKEMU RAMOTI
HEBRONI BEZERI