Kodi Mwambo Uyenera Kuwombana ndi Choonadi?
MARTIN LUTHER anakhulupiriradi kuti zimene anali kudziŵa zinali zoona. Iye anaganiza kuti Baibulo linamchirikiza. Komabe, Copernicus, katswiri wa zakuthambo Wachipolishi, anaganiza kuti chikhulupiriro chamwambo cha panthaŵiyo chinali cholakwika.
Chikhulupiriro chotani? Chakuti dziko lapansi linali pakati pa chilengedwe chonse ndipo zinthu zonse zimayenda molizungulira. Copernicus anati choonadi chinali chakuti dziko lapansi lenilenilo limayenda mozungulira dzuŵa. Luther anakana zimenezi, akumati: “Anthu amamvetsera wopenda nyenyezi watsopano amene anayesayesa kusonyeza kuti dziko lapansi limazungulira, m’malo mwa miyamba kapena thambo, dzuŵa ndi mwezi.”—History of Western Philosophy.
ZIKHULUPIRIRO zamwambo kaŵirikaŵiri zawombana ndi zinthu zoona, ndi choonadi. Ndipo zingasonkhezere anthu kuchita zinthu zoipa.
Komabe, zimenezi sizitanthauza kuti mwambo umawombana ndi choonadi nthaŵi zonse. Kwenikweni, mtumwi Paulo analimbikitsa Akristu a m’tsiku lake kutsatabe miyambo imene anawapatsa akumati: “Ndikutamandani . . . kuti musunga miyambo monga ndinapereka kwa inu.”—1 Akorinto 11:2; onaninso 2 Atesalonika 2:15; 3:6.
Kodi Paulo anatanthauzanji ndi mawuwo “miyambo”? Insight on the Scriptures, Voliyumu 2, tsamba 1118, imati liwu Lachigiriki la “mwambo” limene anagwiritsira ntchito, pa·raʹdo·sis, limatanthauza chinthu “choperekedwa kwa wina mwa kulankhula kapena mwa kulemba.” Liwu Lachingelezi limatanthauza “chidziŵitso, ziphunzitso, kapena machitachita zimene ana analandira kwa makolo kapena zimene zakhala maziko a kalingaliridwe kapena kachitidwe ka zinthu zina zake.”a Chifukwa chakuti miyambo imene mtumwi Paulo anapereka inali ndi magwero abwino, Akristu anachita bwino kuisunga.
Koma nzodziŵikiratu kuti mwambo ungakhale woona kapena wonama, wabwino kapena woipa. Mwachitsanzo, wafilosofi Wachibritishi Bertrand Russell anathokoza anthu ngati Copernicus a m’zaka za zana la 16 amene anali oona mtima ndi olimba mtima kwakuti nkukayikira zikhulupiriro zamwambo. Iwo “anazindikira kuti zimene anakhulupirira chiyambire nthaŵi zamakedzana zingakhale zinali zonama.” Kodi inunso mwaiona nzeru yake ya kusangotsatira mwambo mwaumbuli?—Yerekezerani ndi Mateyu 15:1-9, 14.
Nanga bwanji za zikhulupiriro ndi miyambo yachipembedzo? Kodi tinganene kuti zili zolondola ndiponso zabwino? Kodi tingadziŵe bwanji? Nanga tiyenera kuchita chiyani ngati tapeza kuti miyambo yachipembedzo imawombanadi ndi choonadi? Nkhani yotsatira idzayankha mafunso ameneŵa.
[Mawu a M’munsi]
a Yofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Mawu a Chithunzi patsamba 2]
Chikuto: Jean-Leon Huens © National Geographic Society
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
Universität Leipzig