Pamene Mwambo Uwombana ndi Choonadi
NGOZI—MADZIŴA SAALI AKUMWA. Mwina tazoloŵera kuona machenjezo otero. M’madera ambiri anthu amasamala za madzi amene amamwa chifukwa adziŵa kuti akasupe ena a madzi akuipitsidwa ndi poizoni imene yatchedwa “mankhwala a mfiti.” Chifukwa cha kuipitsa kumeneku, kufufuza kwina kumatero, madzi angakhale “opereka tizilombo ta matenda ndi . . . mankhwala oipitsa” m’malo mokhala “ochirikiza moyo ndi kuutetezera.”—Water Pollution.
Kuipitsa Madzi a Choonadi
Miyambo yowombana ndi choonadi ili ngati akasupe a madzi oipa. Ife mosadziŵa tingaumirire miyambo—chidziŵitso, malingaliro, zikhulupiriro, kapena chikhalidwe zimene mbadwo wina unalandira kwa wina—imene kwenikweni, yakhala yoipitsidwa ndi “mankhwala a mfiti” a malingaliro ndi mafilosofi onama ndi osocheza. Mofanana ndi madzi oipa, zimenezi zingativulaze kwambiri—kutivulaza mwauzimu.
Ngakhale ngati tikhulupirira kuti zikhulupiriro zathu zachipembedzo zamwambo zili zozikidwa pa Baibulo, ife tonse tiyenera kupatula nthaŵi ya kuzipenda mosamalitsa. Kumbukirani kuti pamene Martin Luther anaumirira chikhulupiriro chamwambo cha m’tsiku lake natsutsa Copernicus, anakhulupirira kuti Baibulo linamchirikiza. Komabe, Luther analephera kutsanzira chitsanzo chabwino cha Abereya akale amene ‘anali mfulu posanthula m’Malembo masiku onse ngati zinthu zinali zotero.’—Machitidwe 17:10, 11.
Talingalirani za ngozi imene zikhulupiriro zamwambo zinadzetsa pa Ayuda ena m’tsiku la Yesu. Iwo anakhulupirira ndi mtima wonse kuti miyambo yawo inali yoona. Pamene ananena kuti ophunzira a Yesu sanasunge miyamboyo, Yesu anawafunsa kuti: “Inunso mulumphiranji lamulo la Mulungu chifukwa cha miyambo yanu?” (Mateyu 15:1-3) Kodi chinalakwika nchiyani? Yesu anasonyeza vuto lawo pamene anagwira mawu mneneri Yesaya kuti: ‘Alambira [Mulungu] kwachabe, ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu.’—Mateyu 15:9; Yesaya 29:13.
Inde, m’malo mwa choonadi chochokera kwa Mulungu, iwo anatenga malingaliro a anthu kapena, zoipa koposa, a ziŵanda. Mwachitsanzo, Insight on the Scriptures, Voliyumu 1, tsamba 506, imafotokoza kuti: “Panthaŵiyo Afarisi anaphunzitsa kuti munthu atangoti chuma chake ndi ‘korban,’ kapena mphatso yopatulidwa kwa Mulungu, sakanachigwiritsira ntchito kuthandizira makolo ake, ngakhale ngati anali osoŵa motani, pamene iye yekha akanagwiritsira ntchito chuma chimenecho kufikira imfa yake ngati anafuna kutero.” Nzeru yaumunthu imene inaipitsa madzi a choonadi inali ndi zotulukapo zoipa mwauzimu pa Ayuda. Ndipo ambiri anakana Mesiya wawo yemwe anamuyembekezera nthaŵi yaitali.
Dziko Lachikristu Liwonjezera Kuipitsa
Chivulazo chauzimu chonga chimenecho chinachitika pambuyo pa imfa ya Yesu. Ambiri omwe anati anali otsatira ake anagwiritsira ntchito miyambo ya pakamwa monga maziko a ziphunzitso zawo zatsopano. Malinga ndi kunena kwa Cyclopedia of Biblical, Theological, and Ecclesiastical Literature, yolembedwa ndi McClintock ndi Strong, otchedwa Akristu ena anakhulupirira kuti miyambo yotero inali “malangizo a pakamwa a atumwi amene matchalitchi oyamba Achikristu analandira kwa iwo, kupyola m’nyengo za atumwi, ndi kusungidwa oyera kufikira m’nthaŵi yawo.”—Kanyenye ngwathu.
Kwenikweni yambiri ya miyambo imeneyi inali malingaliro odetsedwa ndi olakwika. Monga momwe Cyclopedia imeneyo ikufotokozera, mafilosofi atsopano ameneŵa sanali “osemphana chabe ndi miyambo ina, komanso ndi zolemba zenizeni za atumwi zimene anali nazo.” Zimenezi sizinali zachilendo konse. Mtumwi Paulo anali atachenjeza Akristu kuti: “Penyani kuti pasakhale wina wakulanda inu ngati chuma, mwa kukonda nzeru kwake, ndi chinyengo chopanda pake, potsata mwambo wa anthu, potsata zoyamba za dziko lapansi, osati potsata Kristu.”—Akolose 2:8.
Momwemonso, zikhulupiriro zamwambo lerolino zili ‘zosemphana ndi zolemba zenizeni za atumwi.’ Dziko Lachikristu laipitsa madzi a choonadi ndi zikhulupiriro zambiri zouziridwa ndi ziŵanda, zonga Utatu, moto wa helo, kusafa kwa moyo wa munthu, utundu, ndi kupembedza mafano.a (1 Timoteo 4:1-3) Mbiri imachitira umboni za nthenda zakuuzimu zimene anthu okhulupirira ziphunzitso za ziŵanda zimene zakhala ziphunzitso zamwambo za Dziko Lachikristu adwala.—Yerekezerani ndi Yesaya 1:4-7.
Ndipotu, kuipitsa choonadi kotero kwachitika kuchokera pachiyambi cha munthu. Satana wapitiriza ndi njira imene anayamba m’Edene ya kuipitsa maganizo a anthu mwa mabodza ake ndi chinyengo. (Yohane 8:44; 2 Akorinto 11:3) Pamene banja la anthu linafalikira pa dziko lonse lapansi pambuyo pa Chigumula cha m’tsiku la Nowa, anthu a m’mitundu yonse anayamba kumwa pa akasupe a chidziŵitso chaumunthu oipitsidwa dala ndi mafilosofi ndi malingaliro ouziridwa ndi ziŵanda.
Zotulukapo za Kuipitsa Kwauzimu
Kodi kuipitsa kwauzimu kotero kungachititse zoipa zotani? Tingaziyerekeze ndi mmene madzi oipa amakhudzira thanzi lathu. Katswiri wina akuti: “Anthu pafupifupi 200 miliyoni amadwala schistosomiasis (likodzo) [matenda a nkhono, amene amachititsa kuchepa mwazi m’thupi, kusapeza bwino, kudwaladwala, ndipo ngakhale imfa], ochititsidwa ndi madzi oipa okhudza khungu. Anthu 500 miliyoni ali ndi trachoma, imodzi ya zochititsa khungu zambiri, chifukwa chosamba madzi akuda. . . . Anthu pafupifupi mamiliyoni zikwi ziŵiri alibe madzi abwino akumwa.” (Our Country, the Planet) Anthu miyandamiyanda apunduka mwauzimu, akhala akhungu, ndipo ngakhale kufa chifukwa chotsatira miyambo yoipitsidwa ndi ziphunzitso zonama zauchiŵanda.—1 Akorinto 10:20, 21; 2 Akorinto 4:3, 4.
Mwachitsanzo, ambiri ngosokonezeka kapena ali akhungu ponena za kugwirizana kwa Yesu Kristu ndi Atate wake, Yehova Mulungu. Ena omwe anati anali Akristu anayamba kutsatira mwambo wa kusaikamo dzina lopatulika la Mulungu, Yehova, m’Malemba Achigiriki Achikristu. George Howard akunena zotsatirazi mu Journal of Biblical Literature: “Malinga ndi kuganiza kwathu, kuchotsa Tetragrama[toni] kumeneku kunasokoneza maganizo Akristu Akunja ponena za kugwirizana kwa ‘Ambuye Mulungu’ ndi ‘Ambuye Kristu.’”
Talingaliraninso msokonezo, kuwopa akufa, ndi mantha ochititsidwa ndi chikhulupiriro chopanda malemba chakuti moyo wa munthu sumafa. (Yerekezerani ndi Mlaliki 9:5; Ezekieli 18:4.) Kodi ndi anthu angati amene ali mu ukapolo wa kulambira makolo kapena amene amakhala amantha nthaŵi zonse kuti akufa adzabwera kudzawavulaza? Chikhulupiriro chimenechi chalimbikitsa anthu ngakhale kudzipha ndi kupha anzawo.
Ajapani ambiri amaganiza kuti pa imfa mizimu yawo yotulukayo imakakumana m’moyo wa pambuyo pa imfa. Chifukwa chake, makolo ena amene amadzipha, amaganiza kuti ndi bwinonso kupha ana awo. An English Dictionary of Japanese Ways of Thinking imafotokoza kuti: “Ku Japan kudzipha sikumatsutsidwa nthaŵi zambiri, koma kaŵirikaŵiri kumaonedwa monga njira yabwino yopepesera kaamba ka machimo aakulu a munthu . . . Mwachionekere ngakhale kudzipha kwa banja lonse kungasimbidwe mwa mawu ochirikiza.”
Yesani Miyamboyo
Polingalira za ngozi zimene kutsatira mwaumbuli zikhulupiriro zamwambo ndi chikhalidwe kuli nazo, kodi tiyenera kuchitanji? Chakumapeto kwa zaka za zana loyamba, mtumwi Yohane analangiza Akristu anzake motere: ‘Okondedwa, musamakhulupirira [mawu ouziridwa alionse, NW], koma yesani [mawu ouziridwa] [monga momwe mungapimire madzi kuona ngati ali bwino] ngati achokera kwa Mulungu: popeza aneneri onyenga ambiri anatuluka kuloŵa m’dziko lapansi.’ (1 Yohane 4:1; onaninso 1 Atesalonika 5:21.) Kodi mungadziŵe bwanji ngati mwambo uli woipa? Mufunikira ulamuliro wina wake, muyezo wina wake wa kuyera, kuti muyese zimene mumakhulupirira.
Ulamuliro umenewo ndiwo Baibulo. Yesu Kristu anati: “Patulani iwo m’choonadi; mawu anu ndi choonadi.” (Yohane 17:17) Iye anatinso: “Ikudza nthaŵi, ndipo tsopano ilipo, imene olambira oona adzalambira Atate mumzimu ndi m’choonadi.” (Yohane 4:23) Mwa kugwiritsira ntchito Mawu ouziridwa a Mulungu, mungapeze madzi oyera a choonadi m’malo mwa madzi oipa a mafilosofi a anthu ndi auchiŵanda.—Yohane 8:31, 32; 2 Timoteo 3:16.
Kumbukirani, ngakhale poizoni waung’ono kwambiri ungakhale wangozi. Nthaŵi zina pamapita zaka kuti zotulukapo zake zionekere. “Madzi oipa,” akutero Shridath Ramphal, yemwe kale anali pulezidenti wa World Conservation Union, “akhala wakupha wowopsa koposa padziko lonse. Anthu osachepera zikwi makumi aŵiri ndi zisanu amafa tsiku lililonse chifukwa chowagwiritsira ntchito.” Miyambo yoipitsidwa mwauzimu njowopsa kuposa zimenezo.
Kodi kulimba mtima kwanu mukhoza kumasuka nako ku zikhulupiriro zamwambo zimene mungakhale mutazitsatira kwa zaka zambiri ngati mwapeza kuti zikuwombana ndi choonadi? Labadirani machenjezo. Dzichinjirizeni inu nokha ndi banja lanu mwa kutsimikiza kuti miyambo yanu ikugwirizana ndi Mawu oyera a Mulungu a choonadi.—Salmo 19:8-11; Miyambo 14:15; Machitidwe 17:11.
[Mawu a M’munsi]
a Kuti mupeze umboni wakuti ziphunzitso zotero sizozikidwa pa Baibulo, onani Kukambitsirana za m’Malemba. Bukuli limafalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Chithunzi patsamba 7]
Mawu a Mulungu a choonadi ali ngati mtsinje wa madzi oyera abwino