Miyambo ya Chipembedzo—Kulambira Mulungu m’Chowonadi?
“SALGA, salga, salga” (“Tulukani, tulukani, tukukani”). Kulira kodandaulako kumachokera ku manda kwa mdima pa chisumbu cha Janitzio mu Nyanja ya Pátzcuaro, Mexico. Kumeneko m’Mwenye wodzipereka wa Tarascan apembedzera mnansi wake womwalira ndi thandizo la pemphero lolembedwa. “Lolani Korona Woyera adule unyolo womwe wakumangani,” iye achonderera tero.
Liri Tsiku Lokumbukira Akufa. Kuchokera ku maora a kum’mawa, akazi ndi ana akongoletsa manda a mabanja awo ndi maluŵa ndi mafelemu a mitengo okongoletsedwa. Iwo aika zopereka za zipatso ndi mikate kutsogolo kwa mandawo. Ndipo tsopano iwo alimba mtima mu kuzizira kwa usiku kupereka mapemphero kapena kuyang’anira kwa kachetechete m’kuwala kwa chizimezime kwa zikwi za makandulo oyatsidwa m’malo mwa akufawo.
Chomwe chikuwoneka chachilendo kapena ngakhale chozizwitsa kwa woyang’anira wa kunja chiri kwa anthuwa mwambo wa chipembedzo wolemekezedwa kwa nthaŵi yaitali: chikondwerero cha Chikatolika cha Tsiku la Miyoyo Yonse. M’maiko a ku Latin America ambiri, mwambo umasonyeza kuti zikwi za okhulupirira amapita kumanda ndi kupereka mapemphero olembedwa ndi mphatso kaamba ka akufa awo.
Latin America irinso ndi miyambo yochuluka ponena za mafano a chipembedzo. Mafano a Kristu ndi Mariya ali ofala, akumakongoletsa nyumba zambiri ndi nyumba za malonda. Kwerani basi ndipo inu mosakaikira mudzawona zithunzi zazing’ono za Mariya zosonyezedwa pamwamba pa mpando wa woyendetsa. Mafano a Mariya, okongoletsedwa ndi magetsi a mitundumitundu omawala m’malo mwa makandulo, amaikidwa ngakhale pakati moyang’anizana ndi njira yapakati yopitamo anthu m’basi.
Mu Colombia zithunzi zazikulu za Kristu ndi za Mariya zimayang’ana pansi kuchokera pa mapiri atatli pamwamba pa mizinda yambiri. Malo apamwamba koposa otchuka a Monserrate ali ofikiridwa ndi tchalitchi chomwe chiri chodzaza ndi mafano olemekezedwa koposa. Mkati mwa milungu yoyera, zikwi za nzika za ku Bogotá zimakwera ku phiri la miyala limeneli, ena akumakwawa pa mawondo ochekeka ndi a kukha mwazi.
Mafano, mitanda, mapwando—izi ziri mbali ya miyambo ya chipembedzo yomwe yakhala mbali yokhazikitsidwa ya moyo kaamba ka anthu m’dziko lonse. Miyambo imeneyi yapatsiridwa kuchokera ku mibadwo kupita ku mibadwo, ndipo anthu amayedzamira m’kuwona iyo monga yopatulika.
Kulambira m’Chowonadi?
Pamene kuli kwakuti mwinamwake ambiri ali okhutiritsidwa kutsatira miyamboyo mosakaikira, kwa ambiri odzinenera kukhala akristu miyambo imeneyo imapangitsa tsoka losokoneza. Ndiko nkomwe, anali Yesu Kristu iyemwini amene ananena kuti: “Olambira owona adzalambira Atate mu mzimu ndi m’chowonadi.” (Yohane 4:23) Komabe, miyambo yambiri ya chipembedzo iri mwachiwonekere yotengedwa kuchokera, kapena chifupifupi mozizwitsa yofanana ndi, miyambo ya chipembedzo yosakhala ya Chikristu. Mwachitsanzo, Tsiku la Miyoyo Yonse limafanana kotheratu ndi phwando la chiBudda la “Ullambana,” tsiku loikidwa pambali kaamba ka “kulongosola kwa chisoni cha ana kwa makolo omwalira ndi kumasulidwa kwa mzimu kuchokera ku ukapolo ku dziko iri.” (The New Encyclopædia Britannica, yofalitsidwa mu 1976, Micropædia, Volyumu 1, tsamba 260) Kodi atsatiri a miyambo yoteroyo ndithudi akulambira m’chowonadi?
Ena amatsutsa kuti kuvomerezedwa kokha kwa miyambo mu tchalitchi kumalungamitsa iwo. Unatero Msonkhano Wachiŵiri wa Vatican mu 1965: “Sikuli kokha kuchokera ku Malemba oyera kumene Tchalitchi chimatenga chitsimikiziro chake ponena za chirichonse chomwe chavumbulidwa. Chotero ponse paŵiri mwambo wopatulika ndi Malemba opatulika ziyenera ulandirika ndi kulemekezedwa ndi lingaliro lofananalo la kudzipereka ndi ulemu.”
Bwanji, ngakhale ndi tero, ngati pali kuwombana kokulira pakati pa miyambo yopangidwa ndi anthu ndi Malemba owuziridwa ndi Mulungu? M’kuyankha, tiyeni titenge kayang’anidwe kosamalitsa pa miyambo m’chiwunikiro cha uphungu wa Baibulo.