Chisungiko Chenicheni—Chonulirapo Chovuta Kuchifikira
ARNOLD anali mwana amene ankakonda chidole chake chansalu cha nyalugwe. Kulikonse kumene ankapita, anamka nacho—kokaseŵera, panthaŵi yachakudya, pokagona. Kwa iye, nyalugweyo anampatsa chimwemwe, chisungiko. Tsiku lina, panali vuto. Nyalugweyo anasoŵa!
Pamene Arnold anali kulira, amayi wake, atate wake, ndi abale ake aakulu atatu anafufuza nyumba yawo yaikuluyo kuti apeze nyalugweyo. M’kupita kwa nthaŵi mmodzi wa iwo anampeza m’drowo. Mwachionekere, Arnold anali atamuika mmenemo ndi kuiŵala pomwepo kumene anali. Anambwezera nyalugweyo, ndipo Arnold anapukuta misozi yake. Anasangalala ndi kumvanso kukhala wosungika.
Mmene zikanakhalira bwino nanga ngati mavuto onse akanathetsedwa m’njira yosavuta motero—monga mwa kungopeza chidole cha nyalugwe m’drowo! Komabe, kwa anthu ambiri, mafunso onena za chisungiko ngovuta ndi ocholoŵana kwambiri kuposa zimenezo. Kungoti pafupifupi kulikonse, anthu amadzifunsa kuti, ‘Kodi ndidzachitiridwa upandu kapena chiwawa? Kodi ndili pangozi ya kuchotsedwa pantchito yanga? Kodi banja langa nlotsimikizira kukhala ndi chakudya chokwanira? Kodi ena adzandipeŵa chifukwa cha chipembedzo changa kapena fuko langa?’
Chiŵerengero cha anthu amene alibe chisungiko nchachikulu. Malinga ndi United Nations, anthu pafupifupi mamiliyoni zikwi zitatu samangosoŵa mankhwala a matenda a masiku onse komanso mankhwala ofunika kwambiri. Anthu oposa pa mamiliyoni chikwi chimodzi ali mu umphaŵi waukulu. Pafupifupi mamiliyoni chikwi chimodzi, ngakhale kuti akugwira ntchito, alibe ntchito zokhazikika. Chiŵerengero cha othaŵa kwawo chikukula. Podzafika kumapeto a 1994, pafupifupi munthu mmodzi mwa 115 alionse padziko lapansi anakakamizika kuthaŵa kwawo. Moyo wa anthu ambirimbiri ukuwonongeka chifukwa cha malonda a anamgoneka a padziko lonse opanga ndalama zokwanira $500 biliyoni pachaka amene amabala machitidwe osaŵerengeka aupandu ndi achiwawa. Nkhondo imawononga moyo wa anthu ambirimbiri. Mu 1993 mokha, maiko 42 anali ndi nkhondo zazikulu, pamene kuli kwakuti 37 ena anali ndi chiwawa cha zandale.
Nkhondo, umphaŵi, upandu, ndi zinthu zina zowopseza chisungiko cha anthu nzoloŵanaloŵana, ndipo zikuwonjezereka. Palibe njira zothetsera mavuto oterewa zonga kungopeza nyalugwe m’drowo. Kwenikweni, anthu sadzawathetsa konse.
“Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye,” akuchenjeza motero Mawu a Mulungu, Baibulo. Nangano, ndi mwa yani mmene tingakhulupirire? Lembali limapitiriza kuti: “Wodala munthu amene akhala naye Mulungu wa Yakobo kuti amthandize, chiyembekezo chake chili pa Yehova, Mulungu wake; amene analenga zakumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zili m’mwemo.”—Salmo 146:3-6.
Kodi nchifukwa ninji tingadalire mwa Yehova kuti adzabweretsa chisungiko padziko lino lapansi? Kodi nkotheka kukhala ndi moyo wosungika ndi wachimwemwe tsopano? Kodi ndi motani mmene Mulungu adzachotsera zopinga chisungiko cha anthu?