Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 5/15 tsamba 4-7
  • Chisungiko Chenicheni—Tsopano Ndiponso Kosatha

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chisungiko Chenicheni—Tsopano Ndiponso Kosatha
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chisungiko cha Atumiki a Mulungu
  • Zimene Mulungu Amachitira Anthu Ake
  • Chisungiko Chenicheni kwa Onse?
  • Pomalizira Pake​—Chisungiko Chenicheni Chosatha!
  • Mtsogolo Mosungika Mmene Mungamupezere
    M’tsogolo Mosungika—M’mene Mungamupezere
  • Mtendere Weniweni ndi Chisungiko Zayandikira!
    Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?
  • Kodi Nchisungiko cha Mtundu Wotani Chimene Mumachikhumba?
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Kuyang’ana Kuposa pa “Mtendere ndi Chisungiko” Zaumunthu
    Nsanja ya Olonda—1991
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 5/15 tsamba 4-7

Chisungiko Chenicheni​—Tsopano Ndiponso Kosatha

PALIBE kukayikira kulikonse kuti Yehova Mulungu angapereke chisungiko kwa anthu ake. Iye ndiye “Wamphamvuyonse.” (Salmo 68:14) Dzina lake lapaderalo limatanthauza kuti “Amachititsa Kukhalako.” Zimenezi zimamdziŵikitsa kukhala Yekhayo m’chilengedwe chonse amene akhoza kugonjetsa chopinga chilichonse kuti akwaniritse malonjezo ake ndi chifuniro chake. Mulungu iye mwini akuti: “Momwemo adzakhala mawu anga amene atuluka mkamwa mwanga, sadzabwerera kwa ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula mmene ndinawatumizira.”​—Yesaya 55:11.

Mulungu amapereka chisungiko kwa amene amamdalira. Mawu ake amatsimikizira zimenezi. “Dzina la Yehova ndilo linga lolimba,” inatero Mfumu Solomo yanzeruyo mouziridwa ndi Mulungu. “Wolungama athamangiramo napulumuka.” Inanenanso kuti: “Wokhulupirira Yehova adzapulumuka.”​—Miyambo 18:10; 29:25.

Chisungiko cha Atumiki a Mulungu

Nthaŵi zonse Yehova wapereka chisungiko kwa amene amamdalira. Mwachitsanzo, mneneri Yeremiya anali ndi chitetezo cha Mulungu. Pamene magulu ankhondo a Babulo analalira Yerusalemu wampatukoyo, anthu ‘anadya chakudya monga mwa muyeso, ndi mosamalira.’ (Ezekieli 4:16) Mkhalidwewo unadzaipa kwambiri kwakuti akazi ena anaphika ana awo ndi kuwadya. (Maliro 2:20; 4:10) Ngakhale kuti panthaŵiyo Yeremiya anali atamangidwa chifukwa cha kulalikira kwake mopanda mantha, Yehova anatsimikizira kuti “[a]nampatsa mkate wofuma ku msewu wa oumba mikate, mpaka unatha mkate wonse wa m’mudzi.”​—Yeremiya 37:21.

Pamene Yerusalemu anagonjetsedwa ndi Ababulo, Yeremiya sanaphedwe kapena kutengeredwa ku Babulo monga wandende. M’malo mwake, “kapitao [wachibabulo] wa alonda anampatsa iye phoso ndi mtulo, namleka amuke.”​—Yeremiya 40:5.

Zaka mazana angapo pambuyo pake Yesu Kristu anatsimikizira atumiki a Mulungu kuti: “Musadere nkhaŵa, ndi kuti, Tidzadya chiyani? kapena, Tidzamwa chiyani? kapena, Tidzavala chiyani? Pakuti anthu akunja azifunitsa zonse zimenezo; pakuti Atate wanu wakumwamba adziŵa kuti musoŵa zonse zimenezo. Koma muthange mwafuna ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.”​—Mateyu 6:31-33.

Kodi zimenezi zikutanthauza kuti atumiki a Yehova adzakhala ndi chitetezo cha Mulungu pa masoka onse a masiku ano? Ayi, sizili choncho. Okhulupirika amayambukiridwa ndi zinthu zoipa. Akristu oona amadwala, amakumana ndi chizunzo, amachitiridwa upandu, amafa m’ngozi, ndipo amavutika m’njira zina.

Ngakhale kuti pakali pano Yehova sakupereka chisungiko chotheratu pa chivulazo, nkhani zimasonyeza kuti amagwiritsira ntchito mphamvu zake kupatsa atumiki ake zofunika ndi kuwatetezera. Akristu amatetezeredwanso ku mavuto ambiri chifukwa chakuti amagwiritsira ntchito mapulinsipulo a Baibulo m’moyo wawo. (Miyambo 22:3) Ndiponso, ali ndi chisungiko cha gulu lapadziko lonse la abale ndi alongo achikondi auzimu, amene amathandizana m’nthaŵi zovuta. (Yohane 13:34, 35; Aroma 8:28) Mwachitsanzo, poyankha pempho lochonderera la abale awo a ku Rwanda wosakazidwa ndi nkhondoyo, Mboni za Yehova ku Ulaya mwamsanga zinasonkha zopereka ndi kuwatumizira matani 65 a zovala ndi mankhwala, zakudya, ndi zofunika zina zokwanira ndalama $1,600,000.​—Yerekezerani ndi Machitidwe 11:28, 29.

Ngakhale kuti Yehova amalola ziyeso kugwera Akristu oona, iwo ngotsimikizira kuti adzawapatsa nyonga, thandizo, ndi nzeru kuti apirire. Polembera okhulupirira anzake, mtumwi Paulo anati: “Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene munthu akhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.”​—1 Akorinto 10:13.

Zimene Mulungu Amachitira Anthu Ake

Lerolino, mamiliyoni a anthu amasangalala kuchita chifuniro cha Mulungu. Samakakamizidwa kutumikira Mulungu; iwo amatero chifukwa chakuti amamdziŵa ndi kumkonda. Choteronso, chifukwa chakuti Yehova amakonda atumiki ake okhulupirika, walinganiza kusanduliza dziko lapansi kukhala paradaiso mmene anthu omvera adzakhala ndi mtendere, thanzi labwino, ndi chisungiko kosatha.​—Luka 23:43.

Mulungu adzachita zimenezi mwa boma lakumwamba, lokhala ndi Mfumu yake yoikidwa, Yesu Kristu monga Wolamulira wake. (Danieli 7:13, 14) Baibulo limanena za bomali monga “Ufumu wa Mulungu” ndiponso monga “ufumu wakumwamba.” (1 Akorinto 15:50; Mateyu 13:44) Ufumu wa Mulungu udzaloŵa m’malo maboma aumunthu onse. M’malo mokhala ndi maboma ambiri padziko lapansi, padzakhala boma limodzi lokha. Lidzalamulira m’chilungamo padziko lonse lapansi.​—Salmo 72:7, 8; Danieli 2:44.

Yehova akuitanira onse kudzakhala mu Ufumuwu. Njira imodzi imene akuchitiramo zimenezi ndiyo mwa kugaŵiridwa kwakukulu kwa Baibulo, buku limene limafotokoza zimene Ufumuwo udzachitira anthu. Baibulo ndilo buku logaŵiridwa koposa padziko lonse lapansi, ndipo tsopano likupezeka, lathunthu kapena mbali yake ina, m’zinenero zoposa 2,000.

Mwachikondi Yehova Mulungu amathandiza anthu kumvetsa zimene Baibulo limaphunzitsa ponena za Ufumu. Amachita zimenezo mwa kulangiza ndi kutumiza anthu kuti akafotokoze Malemba kwa ena. Mboni za Yehova zoposa mamiliyoni asanu tsopano zikulengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu m’maiko oposa 230.

Chisungiko Chenicheni kwa Onse?

Kodi onse adzalandira chiitano cha kukhala nzika za Ufumu wa Mulungu mwa kulabadira miyezo yake yolungama? Ayi, chifukwa chakuti anthu ambiri safuna kuchita chifuniro cha Mulungu. Amakana zoyesayesa zowathandizira kusintha moyo wawo kuti ukhale wabwino. Zoonadi, amadzisonyeza kukhala ngati amene Yesu ananena kuti: “Unalemera mtima wa anthu awa, ndipo m’makutu awo anamva mogontha, ndipo maso awo anatsinzina; kuti asaone konse ndi maso, asamve ndi makutu, asazindikire ndi mtima wawo, asatembenuke, ndipo [asa]wachiritse [Mulungu].”​—Mateyu 13:15.

Kodi ndi motani mmene chisungiko chenicheni chingakhalire konse padziko lapansi pakati pa awo amene amakana kukhala mogwirizana ndi njira zolungama za Mulungu? Sichingakhalepo. Anthu osadziŵa Mulungu amawopseza chisungiko cha amene amafuna kutumikira Yehova.

Mulungu samakakamiza anthu kusintha, komanso sadzalekerera kuipa kunthaŵi zonse. Ngakhale kuti Yehova modekha akupitirizabe kutumiza Mboni zake kukaphunzitsa anthu za njira ndi zifuniro zake, sadzapitiriza kuchita zimenezo kwanthaŵi yaitali. Yesu Kristu ananeneratu kuti: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.”​—Mateyu 24:14.

Kodi “chimaliziro” chidzatanthauzanji kwa amene amakana miyezo ya Mulungu? Chidzatanthauza kuweruzidwa ndi kuwonongedwa kwawo. Baibulo limanena za “kubwezera chilango kwa iwo osamdziŵa Mulungu, ndi iwo osamvera uthenga wabwino wa Ambuye wathu Yesu; amene adzamva chilango, ndicho chionongeko chosatha.”​—2 Atesalonika 1:6-9.

Pomalizira Pake​—Chisungiko Chenicheni Chosatha!

Pambuyo pa kuwonongedwa kwa amene amakana njira za Yehova zamtendere, Ufumu wa Mulungu udzadzetsa nyengo ya ulemerero ya chisungiko kaamba ka ubwino wa olungama a padziko lapansi. (Salmo 37:10, 11) Ha, mmene dziko lapansi latsopanolo lidzakhalira losiyana kwambiri nanga ndi limene tikukhalamo tsopano!​—2 Petro 3:13.

Sikudzakhalanso njala. Aliyense adzakhala ndi zakudya zambiri. Baibulo limanena kuti ‘anthu onse adzakhala ndi phwando la zinthu zonona.’ (Yesaya 25:6) Sikudzakhalanso kupereŵera kwa chakudya, popeza “m’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri.”​—Salmo 72:16.

Anthu sadzakhalanso m’zithando ndi m’mashantetauni. Pansi pa Ufumu wa Mulungu, onse adzakhala ndi nyumba zabwino, ndipo adzadya chakudya cholimidwa m’minda yawo. Baibulo limalonjeza kuti: “Iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzawoka minda yamphesa, ndi kudya zipatso zake.”​—Yesaya 65:21.

M’malo mwa ulova wowanda, kudzakhala ntchito zopindulitsa, ndipo anthu adzaona zotulukapo zake zabwino. Mawu a Mulungu amati: “Osankhidwa anga adzasangalala nthaŵi zambiri ndi ntchito za manja awo. Iwo sadzagwira ntchito mwachabe.”​—Yesaya 65:22, 23.

Pansi pa ulamuliro wa Ufumu, anthu sadzadwala ndi kufa. Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti: “Wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.”​—Yesaya 33:24.

Mu Paradaiso wapadziko lapansi amene adzakhalako posachedwapa, kuvutika ndi zopweteka, chisoni ndi imfa, zidzachotsedwapo. Inde, ngakhale imfa! Anthu adzakhala ndi moyo kosatha mu Paradaiso! Baibulo limatiuza kuti Mulungu “adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.”​—Chivumbulutso 21:4.

Mu ulamuliro wa Yesu Kristu, “Kalonga wa Mtendere,” moyo padziko lapansi pomalizira pake udzakhaladi wosungika. Indedi, chisungiko cha padziko lonse chidzakhalako mu ulamuliro wolungama ndi wachikondi wa boma limodzi​—Ufumu wa Mulungu.​—Yesaya 9:6, 7; Chivumbulutso 7:9, 17.

[Mawu Otsindika patsamba 4]

“Chisungiko chaumunthu chimasonyeza chikhulupiriro ponena za maŵa, . . . [chikhulupiriro pa] kukhazikika kwa mkhalidwe wa zandale ndi zachuma.”​—Mkazi wa ku Asia

[Mawu Otsindika patsamba 5]

“Zimene kwenikweni zimakupangitsa kumva kukhala wopanda chisungiko ndizo chiwawa ndi kupulupudza.”​—Mwamuna wa ku South America

[Mawu Otsindika patsamba 6]

“Sindinamve kukhala wosungika pamene . . . anatiukira. Ngati dziko lili pankhondo, kodi anthu angamve bwanji kukhala osungika?”​—Mwana wa sukulu ya pulaimale ku Middle East

[Mawu Otsindika patsamba 7]

“Ndidzamva kukhala wosungika pamene ndidzadziŵa kuti ndingayende m’makwalala usiku popanda kugwiriridwa chigololo.”​—Mtsikana wapasukulu mu Afirika

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena