Anachita Chifuniro cha Yehova
Buthu Limene Linalankhula Molimba Mtima
MKATI mwa zaka za zana la khumi B.C.E., unansi wa pakati pa Israyeli ndi Aramu unaipa. Kumenyana kunali kofala kwakuti pamene zaka zitatu zinapita popanda chiwawa, inali mbiri yosaiŵalika.—1 Mafumu 22:1.
Chinthu chowopsa kwenikweni panthaŵiyo chinali magulu olanda zinthu a Aaramu, ena amene anali opangidwa ndi mazana a asilikali. Asilikali ameneŵa ankakwerera ndi kulanda Aisrayeli, kutenga mokakamiza ndi kutengera ambiri kuukapolo—ngakhale ana.
Mkati mwa kukwerera kwina, “buthu” lina analitenga mwankhanza kulisiyanitsa ndi banja lake lowopa Mulungu. (2 Mafumu 5:2) Atalipititsa ku Aramu, analikakamiza kukhala pakati pa amene mwinamwake analichititsa mantha ndipo achilendo—anthu amene ankalambira dzuŵa, mwezi, nyenyezi, mitengo, zomera, ndipo ngakhale miyala. Mmene analili osiyana kwambiri nanga ndi banja lake ndi mabwenzi ake, amene analambira Mulungu mmodzi yekha woona, Yehova! Komabe, ngakhale ku malo achilendo ameneŵa, mtsikanayu anasonyeza kulimba mtima kwapadera ponena za kulambira Yehova. Chifukwa cha zimenezi, anasintha moyo wa mkulu wina wotchuka wogwira ntchito pansi pa mfumu ya Aramu. Tiyeni tione mmene zinachitikira.
Kulankhula Molimba Mtima
Nkhani ya m’Baibulo siimatchula dzina la buthuli. Linadzakhala mdzakazi wa mkazi wa Namani, kazembe wamphamvu wa khamu la nkhondo la Mfumu Benihadadi II. (2 Mafumu 5:1) Ngakhale kuti analemekezedwa kwambiri, Namani anali ndi nthenda yonyansa ya khate.
Mwinamwake makhalidwe aulemu a mtsikanayu anasonkhezera mkazi wa Namani kufunsira kwa iye. Mkaziyo angakhale atafunsa mtsikanayu kuti, ‘Kodi odwala khate amawachitiranji ku Israyeli?’ Wantchito wachiisrayeli ameneyu sanachite manyazi kunena mopanda mantha kuti: “Mbuye wanga akadakhala kwa mneneri ali m’Samariya, akadamchiritsa khate lake.”—2 Mafumu 5:3.
Mawu a mtsikanayu sanawanyalanyaze monga zinthu zachibwana. M’malo mwake, ananenedwa kwa Mfumu Benihadadi, amene anatumiza Namani ndi ena paulendo wa makilomita 150 kupita ku Samariya kukafunafuna mneneriyu.—2 Mafumu 5:4, 5.
Kuchiritsidwa kwa Namani
Namani ndi anthu ake anapita kwa Mfumu Yehoramu ya Israyeli, ali ndi kalata yomdziŵikitsa yochokera kwa Benihadadi ndi mtulo woyenera wa ndalama. Mosadabwitsa, Mfumu Yehoramu yolambira mwana wang’ombeyo siinasonyeze chikhulupiriro chimene mtsikana wantchitoyo anasonyeza mwa mneneri wa Mulungu. M’malo mwake, anaganiza kuti Namani wabwera kudzayambitsa mkangano. Pamene mneneri wa Mulungu Elisa anamva za mantha a Yehoramu, pomwepo anatumiza uthenga wopempha kuti mfumu itumize Namani ku nyumba kwake.—2 Mafumu 5:6-8.
Pamene Namani anafika panyumba ya Elisa, mneneriyo anatumiza mthenga amene anamuuza kuti: “Kasambe m’Yordano kasanu ndi kaŵiri, ndi mnofu wako udzabwerera momwe, nudzakhala wokonzeka.” (2 Mafumu 5:9, 10) Namani anapsa mtima. Akumayembekezera chisonyezero chozizwitsa ndi chodzionetsera, anafunsa kuti: “Nanga Abana ndi Faripara, mitsinje ya Damasiko, siiposa kodi madzi onse a m’Israyeli? ndilekerenji kukasamba m’mwemo, ndi kukonzeka?” Namani anachoka panyumba ya Elisa mwaukali. Koma pamene antchito a Namani anakambitsirana naye, anagonja pomalizira pake. Atasamba kasanu ndi kaŵiri m’mtsinje wa Yordano, “mnofu wake unabwera monga mnofu wa mwana wamng’ono, nakonzeka.”—2 Mafumu 5:11-14.
Atabwerera kwa Elisa, Namani anati: “Taonani, tsopano ndidziŵa kuti palibe Mulungu padziko lonse lapansi, koma kwa Israyeli ndiko.” Namani anaŵinda kuti “sadzaperekanso nsembe yopsereza kapena yophera kwa milungu ina, koma kwa Yehova.”—2 Mafumu 5:15-17.
Maphunziro kwa Ife
Namani sakanapita kwa mneneri Elisa ngati buthu la ntchito silikanalankhulapo molimba mtima. Lerolino, achichepere ambiri akuchita mofananamo. Kusukulu, angakhale ozingidwa ndi ophunzira amene sakufuna kutumikira Mulungu. Ngakhale zili choncho, iwo amalankhula za zimene amakhulupirira. Ena amayamba kuchita zimenezo pamsinkhu waung’onodi kwambiri.
Talingalirani za Alexandra, mtsikana wazaka zisanu wa ku Australia. Pamene anayamba sukulu, amayi wake anapanga makonzedwe akukafotokozera mphunzitsi wake zikhulupiriro za Mboni za Yehova. Koma amake Alexandra anadabwitsidwa. “Ndikudziŵa kale za zikhulupiriro zanu zingapo, limodzinso ndi zimene Alexandra adzachita ndi zimene sadzachita pasukulu,” mphunzitsiyo anatero. Amayi wa Alexandra anadabwa, popeza panalibe ana ena a Mboni pasukulupo. “Alexandra anatiuza,” anafotokoza motero mphunzitsiyo. Inde, buthuli linali litakhala kale ndi makambitsirano aluso ndi mphunzitsi wake.
Achichepere otere amalankhula molimba mtima. Motero amachita mogwirizana ndi Salmo 148:12, 13 kuti: “Anyamata ndiponso anamwali; okalamba pamodzi ndi ana: alemekeze dzina la Yehova; pakuti dzina lake lokha ndi lokwezeka; ulemerero wake uli pamwamba pa dziko lapansi ndi thambo.”