Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 6/15 tsamba 20-25
  • Londolani Mtendere Waumulungu m’Moyo wa Banja

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Londolani Mtendere Waumulungu m’Moyo wa Banja
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Moyo wa Banja Uli pa Vuto
  • Nchifukwa Ninji Banja Lili pa Vuto?
  • Mapulinsipulo Ofunika Anayi
  • Musaleke Kulondola Mtendere Waumulungu
  • Mangirani Banja Lanu Mtsogolo Mokhalitsa
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
  • Kodi Pali Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja?
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
  • Kodi Nyumba Yanu Iri Malo a Mpumulo ndi Mtendere?
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Sangalalani ndi Moyo Wabanja
    Sangalalani ndi Moyo Wabanja
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 6/15 tsamba 20-25

Londolani Mtendere Waumulungu m’Moyo wa Banja

“Mpatseni Yehova, inu, mafuko a mitundu ya anthu, mpatseni Yehova ulemerero ndi mphamvu.”​—SALMO 96:7.

1. Kodi Yehova anayambitsa banja ndi chiyambi chotani?

YEHOVA anayambitsa moyo wa banja ndi chiyambi cha mtendere ndi chimwemwe pamene anakwatitsa mwamuna ndi mkazi woyamba. Ndithudi, Adamu anakondwera kwambiri kwakuti anasonyeza chisangalalo chake m’ndakatulo yoyamba kulembedwa nati: “Uyu tsopano ndiye fupa la mafupa anga, ndi mnofu wa mnofu wanga; ndipo adzatchedwa Mkazi, chifukwa anamtenga mwa mwamuna.”​—Genesis 2:23.

2. Kodi cholinga cha Mulungu chinali chotani ponena za ukwati kuwonjezera pakupatsa ana ake aumunthu chimwemwe?

2 Pamene Mulungu anayambitsa ukwati ndi kakonzedwe ka banja, anali ndi zochuluka m’maganizo osati chabe kupatsa chimwemwe ana ake aumunthuwo. Anafuna kuti iwo achite chifuniro chake. Mulungu anauza okwatirana oyamba aja kuti: “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pa nsomba za m’nyanja, ndi pa mbalame za m’mlengalenga, ndi pa zamoyo zonse zakukwaŵa padziko lapansi.” (Genesis 1:28) Inali ntchito yofupa kwenikweni. Akanakhala osangalala chotani nanga Adamu, Hava, ndi ana awo amtsogolo ngati okwatirana oyambawo akanamvera ndi kuchita chifuniro cha Yehova!

3. Kodi chofunika nchiyani kuti mabanja akhale opembedza Mulungu?

3 Ngakhale lero, mabanja amakhala achimwemwe kwambiri pamene achitira pamodzi chifuniro cha Mulungu. Ndipo ndi madalitso aulemerero otani nanga omwe ali mtsogolo mwa mabanja omverawo! Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chipembedzo chipindula zonse, popeza chikhala nalo lonjezano la ku moyo uno, ndi la moyo ulinkudza.” (1 Timoteo 4:8) Mabanja okhala ndi moyo wa kupembedza koona amatsatira mapulinsipulo a Mawu a Yehova ndi kuchita chifuniro chake. Amalondola mtendere waumulungu napeza chimwemwe mu “moyo uno.”

Moyo wa Banja Uli pa Vuto

4, 5. Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti moyo wa banja tsopano uli pa vuto kuzungulira dziko lonse?

4 Ndithudi, mtendere ndi chimwemwe sizimapezeka m’mabanja onse. Potchula za kufufuza kochitidwa ndi bungwe lofufuza kakhalidwe ka anthu lotchedwa Population Council, The New York Times inati: “M’maiko osauka ndi olemera omwe, moyo wa banja ukusintha kwambiri.” Wolemba kufufuzako anati: “Lingaliro lakuti banja ndilo mgwirizano wokhazikika ndi waumodzi mmene tate ndiye wopeza ndalama ndipo mayi ndiye wosamalira mwachifundo lili loto chabe. Zenizeni nzakuti mikhalidwe monga amayi osakwatiwa, kukwera kwa zisudzulo, [ndi] mabanja aang’ono . . . ikufalikira padziko lonse.” Chifukwa cha mikhalidwe imeneyi, mamiliyoni a mabanja sali okhazikika, alibe mtendere ndi chimwemwe, ndipo ambiri akupasuka. Mu Spain, chiŵerengero cha zisudzulo chinakwera kuchokera pa 1 pa maukwati 100 alionse kufika pa 1 pa maukwati 8 alionse pofika kuchiyambi kwa ma 1990​—chiwonjezeko chachikulu patangopita zaka 25 zokha. Malipoti akunena kuti England ali ndi chiŵerengero chapamwamba koposa cha zisudzulo mu Ulaya​—4 pa maukwati 10 alionse amalephereka. Dzikolo laonanso kukwera kwa chiŵerengero cha mabanja a kholo limodzi.

5 Zikuoneka kuti anthu ena sakhozanso ngakhale kuyembekezera kuti akasudzulane kukhoti. Ambiri amathamangira ku “Kachisi Wolekanitsa Zigwirizano” pafupi ndi Tokyo, Japan. Kachisi wachishintho ameneyu amalandira mapempho ofuna chisudzulo ndi akuthetsa maunansi ena osafunikira. Wopembedza aliyense amalemba pempho lake pathabwa lopsapsala, nalikoloŵeka m’bwalo la kachisiyo, ndi kupempherera yankho. Nyuzipepala ya ku Tokyo ikunena kuti pamene kachisiyo anakhazikitsidwa ngati zaka zana limodzi zapitazo, “akazi a [amuna] amalonda olemera akumaloko analemba mapemphero opempha kuti amuna awo asiye zibwenzi zawo kuti abwerere kwa iwo.” Komabe, lerolino mapempho ambiri amakhala ofuna chisudzulo, osati kubwererana. Mosakayikira, moyo wa banja uli pa vuto kuzungulira dziko lonse. Kodi zimenezi ziyenera kudabwitsa Akristu? Iyayi. Chifukwa Baibulo limatiuza zimene zikuchititsa banja kukhala pa vuto lero.

Nchifukwa Ninji Banja Lili pa Vuto?

6. Kodi 1 Yohane 5:19 akusonyezanji ponena za vuto la banja lero?

6 Chimodzi cha zifukwa zoika banja pa vuto lero ndi ichi: “Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Kodi tingayembekezere chabwino kwa woipayo, Satana Mdyerekezi? Iye ali woipa, wabodza wa makhalidwe onyansa. (Yohane 8:44) Ndicho chifukwa chake dziko lake lamwerekera m’chinyengo ndi chisembwere, zimene zimasakaza kwambiri moyo wa banja! Kunja kwa gulu la Mulungu, kuli chisonkhezero chausatana chimene chingawononge kakonzedwe ka ukwati ka Yehova ndi kuthetsa mtendere m’moyo wa banja.

7. Kodi mabanja angayambukiridwe motani ndi mikhalidwe imene anthu ambiri amasonyeza m’masiku ano otsiriza?

7 Chifukwa china chochititsa mavuto m’banja amene tsopano akusautsa anthu chasonyezedwa pa 2 Timoteo 3:1-5. Ulosi wa Paulo wolembedwa pamenepo umasonyeza kuti tikukhala mu “masiku otsiriza.” Mabanja sangakhale amtendere ndi achimwemwe ngati a m’banjamo ali “odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudyerekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiŵembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu; akukhala nawo maonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana.” Banja silingakhale lachimwemwe kwenikweni ngakhale ngati mmodzi yekha mwa iwo alibe chikondi chachibadwidwe kapena ngati ali wosakhulupirika. Kodi banja lingakhale lamtendere motani ngati wina m’banjamo ali waukali ndi wosayanjanitsika? Ndiponso, kodi mtendere ndi chimwemwe zingakhalemo bwanji m’banja ngati anthu ake ali okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu? Imeneyi ndiyo mikhalidwe ya anthu m’dzikoli, lolamuliridwa ndi Satana. Ndicho chifukwa chake chimwemwe m’banja nchovuta kupeza masiku ano otsiriza!

8, 9. Kodi khalidwe la ana lingayambukire motani chimwemwe cha banja?

8 Chifukwa chinanso chimene mabanja ambiri alibire mtendere ndi chimwemwe ndicho ana opulupudza. Pamene Paulo ananeneratu za mikhalidwe m’masiku otsiriza, anati ana ambiri adzakhala osamvera akuwabala. Ngati ndinu mwana, kodi khalidwe lanu limachititsa banja lanu kukhala pamtendere ndi chimwemwe?

9 Ana ena alibe khalidwe labwino. Mwachitsanzo, mnyamata wina analembera atate wake kalata yamwano iyi: “Ngati simupita nane ku Alexandria sindidzakulemberaninso kalata, kapena kulankhula nanu, kapena kutsazikana nanu, ndipo ngati mupita ku Alexandria sindidzagwiranso dzanja lanu kapena kukupatsaninso moni. Izi nzimene zidzachitika ngati simupita nane . . . Koma nditumizireni [zeze], chonde. Ngati simutero, sindidzadya kanthu ndipo sindidzamwa kanthu. Ndi zomwezo!” Kodi umenewu ukumveka monga mkhalidwe wamakono? Kalata ya mnyamata imeneyi kwa atate wake inalembedwa m’Aigupto wakale zaka zoposa 2,000 zapitazo.

10. Kodi achinyamata angathandize motani mabanja awo kulondola mtendere waumulungu?

10 Mkhalidwe wa mnyamata wachiigupto ameneyo sunali wodzetsa mtendere pabanja. Koma pali zinthu zoipa kuposa chimenechi zimene zikuchitika m’mabanja masiku ano otsiriza. Komabe, achinyamata inu mukhoza kuthandiza banja lanu kulondola mtendere waumulungu. Motani? Mwa kumvera uphungu wa Baibulo uwu: “Ana inu, mverani akubala inu m’zonse, pakuti ichi Ambuye akondwera nacho.”​—Akolose 3:20.

11. Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kukhala atumiki a Yehova okhulupirika?

11 Bwanji ponena za inu makolo? Mwachikondi, thandizani ana anu kukhala atumiki okhulupirika a Yehova. “Phunzitsa mwana poyamba njira yake,” imatero Miyambo 22:6. “Ndipo ngakhale atakalamba sadzachokamo.” Polandira chiphunzitso chabwino cha Malemba ndi pokhala ndi chitsanzo chabwino cha makolo, anyamata ndi atsikana ambiri samachoka panjira yoyenera pamene akula. Koma zambiri zimadalira pamtundu wake ndi mlingo wa chiphunzitso cha Baibulo ndi pamtima wake wachinyamatayo.

12. Kodi nchifukwa ninji nyumba yachikristu iyenera kukhala yamtendere?

12 Ngati onse m’banja lathu akuyesa kuchita chifuniro cha Yehova, tiyenera kusangalala ndi mtendere waumulungu. Nyumba yachikristu iyenera kudzala ndi ‘ana a mtendere.’ Luka 10:1-6 amasonyeza kuti Yesu anali kuganiza za anthu oterowo pamene anatumiza ophunzira ake 70 monga atumiki ndi kuwauza kuti: “M’nyumba iliyonse mukaloŵamo muthange mwanena, Mtendere ukhale pa nyumba iyi. Ndipo mukakhala mwana wa mtendere mmenemo, mtendere wanu udzapumula pa iye.” Pamene atumiki a Yehova amayenda mwamtendere kunyumba ndi nyumba ndi “uthenga wabwino wa mtendere,” amakhala akufunafuna ‘ana a mtendere.’ (Machitidwe 10:34-36; Aefeso 2:13-18) Ndithudi, banja lachikristu la ana a mtendere liyenera kukhaladi lamtendere.

13, 14. (a) Kodi Naomi anakhumba kuti Rute ndi Olipa apeze chiyani? (b) Kodi nyumba yachikristu iyenera kukhala malo ampumulo a mtundu wanji?

13 Nyumba iyenera kukhala malo a mtendere ndi mpumulo. Mkazi wamasiye wokalambayo, Naomi, anali ndi chiyembekezo chakuti Mulungu adzapatsa apongozi ake amasiye aang’onowo, Rute ndi Olipa, mpumulo ndi chitonthozo zimene zimadza mwa kukhala ndi mwamuna wabwino ndi nyumba yabwino. Naomi anati: “Yehova akuloleni mupeze mpumulo yense m’nyumba ya mwamuna wake.” (Rute 1:9) Ponena za chikhumbo cha Naomi, katswiri wina wamaphunziro analemba kuti m’nyumba zoterozo Rute ndi Olipa “akanapeza chimasuko ku mavuto ndi nkhaŵa. Akanapeza mpumulo. Akanakhala malo amene akanapitiriza kukhalamo, mmene malingaliro a chifundo cha mtima wawo akanakhutiritsidwa ndi kupumula. Mphamvu yapadera ya mawu achihebri . . . ikusonyezedwa bwino lomwe mwa mkhalidwe wa mawu ogwirizana nawo a mu [Yesaya 32:17, 18].”

14 Chonde onani zimene zikunenedwa pa Yesaya 32:17, 18. Pamenepo timaŵerenga kuti: “Ntchito ya chilungamo idzakhala mtendere; ndi zotsata chilungamo zidzakhala mtendere [“bata,” NW] ndi kukhulupirika [“chisungiko,” NW] ku nthaŵi zonse. Ndipo anthu anga adzakhala m’malo a mtendere, ndi mokhala mokhulupirika ndi mopuma mwa phe.” Nyumba yachikristu iyenera kukhala mopuma mwa phe, mwa chilungamo, bata, chisungiko, ndi mtendere waumulungu. Koma bwanji ngati pabuka mayesero, kusamvana, kapena mavuto ena? Pamenepo tifunikira kudziŵa chinsinsi chopezera chimwemwe cha banja.

Mapulinsipulo Ofunika Anayi

15. Kodi mungachilongosole motani chinsinsi chopezera chimwemwe cha banja?

15 Banja lililonse padziko lapansi lakhala ndi dzina chifukwa cha Yehova Mulungu, Mlengi wa mabanja onse. (Aefeso 3:14, 15) Choncho aja ofuna chimwemwe cha m’banja ayenera kufuna chitsogozo chake ndi kumtamanda, monga momwe anachitira wamasalmo: “Mpatseni Yehova, inu, mafuko a mitundu ya anthu, mpatseni Yehova ulemerero ndi mphamvu.” (Salmo 96:7) Chinsinsi cha chimwemwe cha banja chili m’Mawu a Mulungu, Baibulo, ndi m’kugwiritsira ntchito mapulinsipulo opezeka mmenemo. Banja limene limagwiritsira ntchito mapulinsipulo ameneŵa lidzakhala lachimwemwe ndipo lidzasangalala ndi mtendere waumulungu. Tsono tiyeni tipende anayi a mapulinsipulo ofunika ameneŵa.

16. Kodi kudziletsa kuyenera kuchitanji m’moyo wa banja?

16 Limodzi la mapulinsipulo ameneŵa limafuna izi: Kudziletsa nkofunika pa mtendere waumulungu m’moyo wa banja. Mfumu Solomo ananena kuti: “Wosalamulira mtima wake akunga mudzi wopasuka wopanda linga.” (Miyambo 25:28) Kulamulira mtima wathu​—kudziletsa​—nkofunika ngati tikufuna kukhala ndi banja lamtendere ndi lachimwemwe. Ngakhale kuti tili opanda ungwiro, tiyenera kudziletsa, kumene kuli chipatso cha mzimu woyera wa Mulungu. (Aroma 7:21, 22; Agalatiya 5:22, 23) Mzimuwo udzatipatsa kudziletsa ngati tiupempherera mkhalidwe umenewu, kugwiritsira ntchito uphungu wa Baibulo wonena za mkhalidwewo, ndi kuyanjana ndi ena ousonyeza. Kachitidwe kameneka kadzatithandiza ‘kuthaŵa dama.’ (1 Akorinto 6:18) Kudziletsa kudzatithandizanso kukana chiwawa, kupeŵa kapena kugonjetsa uchidakwa, ndi kuchita modekha kwambiri ndi mikhalidwe yovuta.

17, 18. (a) Kodi 1 Akorinto 11:3 amagwira ntchito motani pa moyo wa banja lachikristu? (b) Kodi kulemekeza umutu kumadzetsa bwanji mtendere waumulungu pabanja?

17 Pulinsipulo lina lofunika linganenedwe mwa njira iyi: Kulemekeza umutu kudzatithandiza kulondola mtendere waumulungu m’mabanja athu. Paulo analemba kuti: “Ndifuna kuti mudziŵe, kuti mutu wa munthu yense ndiye Kristu; ndi mutu wa mkazi ndiye mwamuna; ndipo mutu wa Kristu ndiye Mulungu.” (1 Akorinto 11:3) Izi zikutanthauza kuti mwamuna ndiye amatsogolera m’banja, mkazi wake amamthandiza mokhulupirika, ndipo ana amamvera makolo awo. (Aefeso 5:22-25, 28-33; 6:1-4) Mkhalidwe wotero umakulitsadi mtendere waumulungu m’moyo wa banja.

18 Mwamuna wachikristu ayenera kukumbukira kuti umutu wa m’Malemba sindiwo kupondereza. Ayenera kutsanzira Yesu, Mutu wake. Ngakhale kuti iye anali kudzakhala “mutu pamtu pa zonse,” Yesu “sanadza kutumikiridwa koma kutumikira.” (Aefeso 1:22; Mateyu 20:28) Mofananamo, mwamuna wachikristu amachita umutu m’njira yachikondi imene imamkhozetsa kusamalira bwino banja lake. Ndipo mkazi wachikristu amakonda kugwirizana ndi mwamuna wake. Monga “womthangata,” amasonyeza mikhalidwe imene mwamuna wake alibe ndi kumpatsa chichirikizo chofunikira. (Genesis 2:20; Miyambo 31:10-31) Kuchita bwino umutu kumathandiza amuna ndi akazi kuchitirana mwaulemu ndipo kumasonkhezera ana kukhala omvera. Inde, kulemekeza umutu kumakulitsa mtendere waumulungu m’moyo wa banja.

19. Kodi nchifukwa ninji kulankhulana kwabwino kuli kofunika kuti m’banja mukhale mtendere ndi chimwemwe?

19 Pulinsipulo lofunika lachitatu linganenedwe motere: Kulankhulana kwabwino nkofunika kuti mukhale mtendere ndi chimwemwe m’banja. Yakobo 1:19 amatiuza kuti: “Munthu aliyense akhale wotchera khutu, wodekha polankhula, wodekha pakupsa mtima.” A m’banja afunikira kukambitsirana ndi kumvetserana chifukwa kulankhulana kwa m’banja kuyenera kukhala kwa mbali ziŵiri. Ngakhale pamene tinena zoona, timapweteka wina m’malo mwa kumthandiza ngati tilankhula mwaukali, monyada, kapena mopanda chifundo. Mawu athu ayenera kukhala achisomo, “okoleretsa.” (Akolose 4:6) Mabanja amene amatsatira mapulinsipulo a Malemba ndi kulankhulana bwino amalondola mtendere waumulungu.

20. Kodi nchifukwa ninji munganene kuti chikondi nchofunika pofuna kupeza mtendere wa banja?

20 Pulinsipulo lachinayi ndi ili: Chikondi nchofunika pa mtendere ndi chimwemwe cha banja. Chikondi cha mwamuna ndi mkazi chimachita mbali yaikulu muukwati, ndipo chikondi chozama chingakule pakati pa onse m’banja. Koma chofunika koposa ndicho chikondi chosonyezedwa ndi liwu lachigiriki lakuti a·gaʹpe. Ichi ndicho chikondi chimene timakonda nacho Yehova, Yesu, ndi mnansi wathu. (Mateyu 22:37-39) Mulungu anasonyeza chikondi chimenechi kwa anthu mwa ‘kupatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.’ (Yohane 3:16) Nkwabwino chotani nanga kuti tikhoza kusonyeza mtundu umenewo wa chikondi kwa awo a m’banja lathu! Chikondi chachikulu chimenechi ndicho “chomangira cha mtima wamphumphu.” (Akolose 3:14) Chimamanga pamodzi okwatirana ndi kuwasonkhezera kuchita chimene chili chabwino kopambana kwa wina ndi mnzake ndi kwa ana awo. Pamene mavuto abuka, chikondi chimawathandiza kusamalira zinthu mogwirizana. Tingakhale otsimikiza za chimenechi chifukwa “chikondi . . . sichitsata za mwini yekha, . . . chikwirira zinthu zonse, chikhulupirira zinthu zonse, chiyembekeza zinthu zonse, chipirira zinthu zonse. Chikondi sichitha nthaŵi zonse.” (1 Akorinto 13:4-8) Alidi achimwemwe mabanja amene chikondi chawo nchomangika pa chikondi cha kwa Yehova!

Musaleke Kulondola Mtendere Waumulungu

21. Kodi nchiyani chingakulitse mtendere ndi chimwemwe m’banja lanu?

21 Mapulinsipulo amenewo limodzinso ndi ena ochokera m’Baibulo akufotokozedwa m’zofalitsa zimene Yehova wapereka mwachifundo chake kupyolera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45) Mwachitsanzo, chidziŵitso choterocho chimapezeka m’buku la masamba 192 lakuti Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja, limene linatuluka pa Misonkhano Yachigawo ya Mboni za Yehova yakuti “Amithenga a Mtendere Waumulungu,” imene inachitika kuzungulira dziko lonse mu 1996/97. Kuphunzira Malemba kwa munthu payekha ndi kwa banja mwa kugwiritsira ntchito bukulo kungadzetse mapindu ambiri. (Yesaya 48:17, 18) Inde, kugwiritsira ntchito uphungu wa m’Malemba kungakulitse mtendere ndi chimwemwe m’banja lanu.

22. Kodi moyo wa banja lathu tiyenera kuuzika pachiyani?

22 Yehova wasungira mabanja ochita chifuniro chake zinthu zabwino zodabwitsa, choncho tiyenera kumtamanda ndi kumtumikira. (Chivumbulutso 21:1-4) Lolani kuti banja lanu lizike moyo wawo pa kulambira Mulungu woona. Ndipo Atate wathu wakumwamba wachikondi, Yehova, akudalitseni ndi chimwemwe pamene mukulondola mtendere waumulungu m’moyo wanu wa banja!

Kodi Mungayankhe Motani?

◻ Kodi chofunika nchiyani kuti mabanja akhale opembedza Mulungu?

◻ Kodi nchifukwa ninji mabanja ali pa vuto lero?

◻ Nanga chinsinsi chopezera chimwemwe cha banja nchiyani?

◻ Kodi ndi mapulinsipulo ena ati amene adzatithandiza kupeza mtendere ndi chimwemwe m’banja?

[Chithunzi patsamba 24]

Kulankhulana kwabwino kumathandiza kulondola mtendere waumulungu m’moyo wa banja

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena