Kuchokera ku Nsanjika za Mumzinda Kumka ku Chipululu cha Tundra—Pitani Komwe Kuli Anthu
MVULA kapena chipale chofeŵa kapena matalala kapena mimbulu kapena mikango ya m’mapiri kapena anthu ankhanza sizinafooketse kutsimikiza mtima kwawo. Iwo anathamanga kudutsa mtunda wa makilomita 3,000 paliŵiro lodabwitsa, kudutsa mitunda yopanda mitengo, mitsinje yothamanga mwamphamvu, ndi zigwa zakuya kuti apereke makalata ofunika mwamsanga ku West Coast. Kodi iwo anali ayani?
Anali apakavalo achinyamata opanda mantha a pony express.a Kodi nchiyani chinapangitsa amuna achinyamata ameneŵa kutsimikiza mtima choncho? Mwinamwake kuvuta kwa ntchitoyo, kusangalatsa kwake, ndi chikhutiro chake atafikitsa makalatawo. Komanso, wapakavalo aliyense anali kunyamula Baibulo m’chikwama chake pamodzi ndi makalata ofunika kwambiri.
Patapita zaka zoposa zana limodzi, kutsimikiza mtima kwakukulu, changu, ndi kudzipereka zikusonyezedwa ndi olengeza Ufumu odzipereka oposa 113,000 m’dziko lonse la Canada. Kodi nchiyani chikuwasonkhezera? Kukonda Mulungu ndi anansi awo kumawasonkhezera kupereka choonadi cha Ufumu mwa mabuku ndiponso mwa mawu apakamwa. Choonadi chopatsa moyo chimenechi nchofunika mwamsanga kwambiri kuposa makalata alionse operekedwa ndi a pony express. Inde, ndi uthenga wamtengo wapatali wonena za Ufumu, wopezeka m’Baibulo Lopatulika, buku limodzimodzilo limene linali kukhala m’zikwama za apakavalo a pony express.—Miyambo 2:21, 22; Yesaya 2:2-4; 61:2; Mateyu 22:37-39; 24:14.
Osonkhezeredwa ndi Kukonda Yehova ndi Anthu
Mboni za Yehova zimakonda kukambitsirana ndi anthu ponena za Ufumu. Mudzawapeza akuchita zimenezi m’nyumba zosanja za m’mizinda, kumidzi yakutali ya ku tundra, pamabwalo a ndege, m’misewu ndi m’malo ena apoyera, ndi patelefoni. Nchifukwa chiyani amachita zimenezi m’malo osiyanasiyana amenewo?
Kusintha kwa makhalidwe kochititsidwa ndi mkhalidwe wa zachuma ndi kuchuluka kwa anthu kumapangitsa kuti kupeza anthu panyumba kukhale kovuta kwambiri. Nthaŵi zambiri, onse aŵiri mwamuna ndi mkazi wake amagwira ntchito kuti asamalire zofunika zazikulu zakuthupi za banja, ndipo kaŵirikaŵiri amanyalanyaza zofunika zauzimu. Pokhala pakati pa zovuta ndi kupsinjika maganizo kumeneku, iwo, mofulumira akufunikira uthenga wotonthoza wachiyembekezo. Mboni za Yehova zikuchitapo kanthu mwachimwemwe. Mochenjera ndiponso mwachifundo, iwo amatsegula mpata wobweretsera uthenga wabwino kwa anthu a mtundu uliwonse m’njira yosangalatsa ndiponso yodzutsa chidwi.—1 Timoteo 2:3, 4.
M’Zinenero Zina: Pamene Yesu analamula otsatira ake kuti ‘amuke ndi kuphunzitsa anthu,’ iye anawasiyira mpata wochitapo kanthu ndiponso wa kukhala otsimikiza mtima popereka uthenga wa chiyembekezo kwa anthu a zinenero zonse. (Mateyu 28:19) Mofanana ndi maiko ambiri, dziko la Canada lakhala lolukana ndi zikhalidwe ndi zinenero zosiyanasiyana, ndipo alengezi ambiri a Ufumu asintha malinga ndi mkhalidwe umenewo mwa kuphunzira zinenero zatsopano.
Mwachitsanzo, mwamuna wina ndi mkazi wake, atumiki a nthaŵi zonse ku Edmonton, Alberta, anaona kuti afunikira kufikira anthu olankhula Chitchaina chachimandarini mumzinda wakwawo. Komabe, choyamba banjalo linafunikira kuphunzira chinenerocho, choncho analankhula ndi wophunzira wapayunivesite wolankhula Chimandarini. Analola kuwaphunzitsa chinenerocho ndiponso panthaŵi imodzimodziyo kuphunzira choonadi cha m’Baibulo kwa iwo. Zinali zochitika zosangalatsa chotani nanga! Pamiyezi 24 yokha alengezi a Ufumu aŵiri odzipereka ameneŵa anali okhoza kuphunzitsa bwino m’Chimandarini. Panthaŵi imodzimodziyo, mphunzitsi wawo amenenso anali wophunzira wawo anayenerera kubatizidwa nkukhala Mkristu.
Zochitika ngati zimenezi zikuchitikanso m’mizinda ina pamene alengezi a Ufumu, mosonkhezeredwa ndi chikondi, akuphunzira zinenero monga Chipolishi, Chirasha, ndi Chiviyetinamu.
Pamsewu: Monga apakavalo a pony express a m’zaka za zana lathalo, amene ankakhala okha paulendo, alengezi ena a Ufumu mkati mwenimweni mwa British Columbia amayendanso okha. Nthaŵi yawo yochuluka imathera pantchito yawo yolembedwa yoyendetsa malole amphamvu onyamula mitengo yamatabwa kudutsa m’misewu ya m’tchire kupita kokachekera matabwa. Zimenezi zimafuna kuti nthaŵi zonse azilankhula ndi enanso oyendetsa malole pawailesi yotchedwa CB (citizens band), kufunsana za kayendedwe ka galimoto zina ndi mkhalidwe wa misewu.
Mwaluso, alengezi a Ufumu ameneŵa amagwiritsira ntchito mawailesi awo a CB m’njira yapadera. Iwo amayambitsa makambitsirano pa CB mwa kutchula nkhani zimene zikuchitika. Kenako, mwaluso, amafotokoza za m’Baibulo. Nthaŵi inayake woyendetsa lole wina anayankhapo pa zimene Baibulo limanena pankhani ya chiyembekezo cha akufa. (Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15) Imfa ya dalaiva mnzake m’ngozi ya pamsewu waukulu inamsautsa mtima kwambiri. Mosangalala, analola kukhala ndi phunziro la Baibulo ndipo tsopano amamveka akulengeza uthenga wabwino kwa antchito anzake ndi mabwenzi ake. Ndiponso, anasangalala kuti phunziro la Baibulo linayambidwa ndi mkazi wamasiye wa bwenzi lake limene linamwalira. Ndi mphotho yabwino chotani nanga ya kuchitapo kanthu popereka uthenga wopatsa moyo wa choonadi m’njira yachilendo imeneyi!
Pandege: Pofuna kupereka uthenga wamtengo wapatali wa choonadi, alengezi achangu a Ufumu amapita kumene kuli anthu ‘kuloŵa m’mudzi’ pandege zazing’ono. (Mateyu 10:11, 12) Chakumbuyoku, magulu aŵiri apandege, mosonkhezeredwa ndi changu chofuna kulengeza uthenga wabwino ndiponso mwa kugwiritsira ntchito ndalama za m’thumba mwawo, anauluka kupita kwa anthu omwazikana m’chipululu chotakasuka kwambiri cha tundra. Ndege iliyonse inayenda mtunda wa makilomita pafupifupi 3,000 ndipo inatera m’midzi 14 yosiyanasiyana, kutsala mtunda wa makilomita 250 kuti afike m’dera lozizira koposa la dziko lapansi. Alengezi ogwira ntchito mosatopa ameneŵa anapitiriza kwa masiku asanu ndi aŵiri athunthu kuti afikire anthu okhala kutali kwambiri.
Ndipo kodi zinali zopindulitsa? Tangolingalirani za mmene anthu ameneŵa anasangalalira ndi uthenga wa m’Baibulo. Atumiki owachezerawo anathandizira kukhutiritsa chosoŵa chofunika kwambiri chauzimu pamene anafotokoza za zimene Yehova akulinga kudzachita padziko lapansi laparadaiso mtsogolomu posachedwapa. (Mateyu 5:3) Patapita nthaŵi yaitali onyamula uthenga amenewo atachoka, anthu oona mtima a m’midzi imeneyo adzakhala akuŵerenga mabaibulo ndi mabuku ofotokoza Baibulo okwanira 542 ndi magazini 3,000 amene anawagaŵira.—Yerekezerani ndi Machitidwe 12:24.
Patelefoni: Anthu zikwizikwi okhala m’mizinda amakhala m’nyumba zosanja zotetezeredwa ndi tekinoloji yamakono. Ngakhale zili motero, alengezi odzipereka a Ufumu amachitabe ntchito yawo mwachangu ndiponso mochenjera. Kodi amatha motani kupita kumene kuli anthu? Pamene kuli kwakuti amakonda kulankhula ndi anthu maso ndi maso, nthaŵi zambiri foni ya intercom imene imakhala pofikira alendo m’nsanjika zimenezo amaigwiritsira ntchito kulankhula nawo. Ngati zimenezi nzosatheka, iwo amagwiritsira ntchito zala zawo, kufikira anthu patelefoni.
Tsiku lina mmaŵa mkazi wachikulire anayankha telefoni yake. Atalonjeredwa mwachidule ndiponso mwaulemu, anafunsidwa ngati akuona kuti padzakhala nthaŵi pamene anthu adzatha kuyenda m’misewu usiku popanda choopsa. Malemba anaŵerengedwa omtsimikizira kuti kudzakhala mtendere wochuluka mtsogolo. (Salmo 37:10, 11; Danieli 2:44; Mateyu 6:9, 10) Iye analola kuti mlungu wotsatira panthaŵi yofananayo adzakambitsirane patelefoni ponena za chifukwa chimene tiyenera kukhulupirira malonjezo a Mulungu. Atachita phunziro la Baibulo patelefoni kwa mwezi umodzi, kuŵerenga ndime za m’chofalitsa chofotokoza Baibulo ndi kufunsa mafunso oyenerera, mlengezi wa Ufumu anathokozedwa ndi mkaziyo pokhala ndi maulaliki ambiri osiyanasiyana mlungu uliwonse. Inali nthaŵi yomfotokozera za buku lophunziramo ndi kumgaŵira kope lake. Makonzedwe anapangidwa akuti aŵiriwo aonane maso ndi maso. Ndithudi, Mboni za Yehova zasonyeza kukonda kwawo anthu, ndipo anthu akulabadira, pozindikira kuti Yehova ali ndi alaliki achikristu ameneŵa.—Yerekezerani ndi 1 Akorinto 14:25.
Mwa Mabuku: Alengezi a Ufumu m’chigawo cha anthu olankhula Chifrenchi cha Quebec nawonso akupita kumene kuli anthu. Mtumiki wina woyendayenda anati: “Kwa zaka zambiri abale ankaona kuti sakuphula kanthu chifukwa cha chitsutso choopsa cha a tchalitchi. Koma chifukwa cha kugwira ntchito mosatopa kwa abale ndiponso mwa kufikira anthu mobwerezabwereza, Baibulo, limene linali buku losadziŵika kwa anthu ambiri, ndipo limene linali kuŵerengedwa ndi kagulu kakang’ono, tsopano limapezeka m’nyumba zambiri.”
Pali zotsatirapo zosangalatsa pamene alengezi atsopano akubadwa mwa anthu osiyanasiyana a ku Quebec, kuphatikizapo madokotala. Ndi mmene zinalili ndi dokotala wina. Mkazi wake, amene ndi mlengezi wa Ufumu, anali kukambitsirana naye za chiyembekezo cha m’Baibulo nthaŵi zambiri. Mkulu wochenjera wa mumpingo anachitapo kanthu mwa kuitanira dokotalayo kumsonkhano wampingo panthaŵi imene brosha lakuti Kodi Mwazi Ungapulumutse Motani Moyo Wanu? linali kuphunziridwa. Iye anabwera ndiponso anayankhapo. Atachita chidwi ndi mkhalidwe wa makambitsirano amenewo ndi kuya kwake kwauzimu, analola kukhala ndi phunziro lakelake la Baibulo. Tsopano iyenso ali mlengezi wa Ufumu.
Kugwiritsira ntchito bwino magazini kwachita zambiri pokopera anthu ku Baibulo. Iweyo sumadziŵa kuti ndi nkhani iti imene idzakopera munthu ku choonadi. Mlengezi wina wa Ufumu anagaŵira kope lachingelezi la Galamukani! kwa mnansi wake amene sanafune kumvetsera uthenga koma amene anali kukonda nkhani za tizilombo. Chithunzithunzi cha mu Galamukani! wachingelezi wa November 22, 1992, pankhani yakuti “Chagas’ Disease—A Kiss of Death” chinamchititsa chidwi. Atasangalala ndi zimene anaŵerenga, anapempha magazini ena. Phunziro la Baibulo linayambidwa, ndipo pamiyezi isanu ndi umodzi yokha iye anali kulalikira kwa ena.
Pamalo Apoyera: Malamulo a ku Canada amapereka ufulu wakulankhula pamalo apoyera, monga pamabwalo andege. Pa Halifax International Airport, alengezi a Ufumu mochenjera amafikira apaulendo amene akudikira ndege ina, kuyamba kukambitsirana nawo. Iwo amagwiritsira ntchito mafunso abwino otsogolera makambitsirano ku Baibulo. Popeza kuti amanyamula Baibulo lokwana m’thumba ndi mabuku, iwo amasamalira zosoŵa zauzimu. Madokotala, asayansi, maloya, oyendetsa ndege, atsogoleri achipembedzo, apolisi, oyendetsa matola, mainjiniya, aphunzitsi, asilikali, ndi andale ochokera kumaiko osiyanasiyana ndiwo ena mwa amene amva uthenga wa Ufumu m’njira imeneyi ndipo anyamula mbewu za choonadi zomwe zakakulira kumalo akutali.—Akolose 1:6.
Tsiku lina mmamaŵa pabwalo landege, mwamuna wina analandira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Kenako, analankhulira pansipansi ngati mokayikira kuti: “Ayi ndithu, Mboni za Yehova!” Kodi ananeneranji zimenezo? Mwamunayo anali Msilamu wodzipereka amene anali atangopemphera kumene mumzikiti wa pabwalo landege. Iye anali kuchonderera Mulungu kuti ampatse luntha, nzeru, ndi kumsonyeza choonadi. Anadabwa kuona kuti yankho lamwamsanga la pemphero lake linali Mboni za Yehova.
Ndithudi, alengezi olimba mtima a Ufumu ku Canada samalola kalikonse kuwatsekereza popereka uthenga wamtengo wapatali umenewo wa Ufumu. Iwo samalola zinenero zachilendo, misewu yoipa yafumbi, midzi yakutali, kapena nyumba zosanja zotetezeredwa kwambiri kuti ziwatsekereze. Iwo ngotsimikiza mtima kupereka uthenga wa moyo wa Mulungu kwa anthu oona mtima ofunafuna choonadi. Mogwirizana ndi ubale wapadziko lonse lapansi wa antchito anzawo, iwo, mosadzikonda, amamvera lamulo la Yesu lakuti ‘amuke ndi kuphunzitsa anthu.’—Mateyu 28:19.
[Mawu a M’munsi]
a Pony express inali kampani yonyamula makalata ku United States imene inakhalako kwa nyengo yaifupi ya miyezi 18 yokha kuyambira mu 1860 mpaka 1861.
[Bokosi patsamba 27]
Alengezi a Ufumu Achipambano Amagwiritsira Ntchito Telefoni
Ena anena kuti: “Dzina langa ndine [tchulani dzina]. Ndakhala ndikulankhula ndi anansi anu mwachidule ponena za mmene pangakhalire mtendere. Kodi mukuganiza kuti dziko lonse lapansi lidzakhalapo ndi mtendere? [Yembekezerani yankho.] Kuti ndikumasuleni, ndingakuuzeni kuti sindikufufuza zilizonse kapena kugulitsa zilizonse. M’malo mwake, ndakhala ndikugaŵana ndi ena lingaliro la m’Malemba Opatulika lonena kuti kwenikweni ndi Mulungu amene adzabweretsa mtendere.” Ndiyeno makambitsirano angapitirize mwa kukambitsirana mfundo zachidule za m’Malemba.”
Ena anena kuti: “Muli bwanji? Dzina langa ndine [tchulani dzina]. Ndine wantchito wodzifunira wa m’dera lanuli. Ndakhala ndikumvetsera malingaliro a anansi anu. Ambiri akudera nkhaŵa poona kuwonjezereka kwa chiwawa ndi upandu m’dera lathuli. Kodi inunso zimakudetsani nkhaŵa? [Yembekezerani yankho.] Kodi mukuganiza kuti padzakhala nthaŵi pamene anthu padziko lonse lapansi adzamva kukhala osungika?” Yembekezerani yankho, ndiyeno pitirizani ndi uthenga wa m’Malemba.