Kodi Ana Anu Mungawatetezere Motani?
ATAPHUNZIRA pasukulu ina yoyandikana nayo kwa zaka zambiri, Wernera anayamba maphunziro apamwamba pamodzi ndi achinyamata ena 3,000 ku São Paulo, Brazil. Kwa nthaŵi yoyamba, iye anaona ophunzira anzake akugulitsa ndi kumwa mankhwala osokoneza bongo. Pokhala wamng’ono, ophunzira ena aakulu posapita nthaŵi anayamba kumkakamiza kuchita miyambo yonyansa ndiponso yangozi yoloŵera gulu lawo.
Nayenso mlongo wa Werner, Eva analinso ndi mavuto. Pofuna kuyesetsa monga momwe angathere, anali kuŵerenga kwambiri moti nyonga yake inatheratu ndiponso anazungulira mutu. Monga achinyamata ena omasinkhuka, Werner ndi Eva anali kufunikira zonse ziŵiri chitetezo chakuthupi ndi chamalingaliro. Kodi ana anu akufunikira thandizo lotani? Kodi mungawakonzekeretse motani moyo wauchikulire? Ndithudi, kodi ana anu mukuwafunira tsogolo lotani?
Si Zinthu Zakuthupi Zokha Zimene Amafunikira
Tangolingalirani za ntchito imene makolo ali nayo pofuna kutetezera ana awo lerolino. Chifukwa cha kuwonongeka kwa moyo wa banja ndiponso kuwonjezereka kwa umphaŵi, m’maiko ambiri ana ongokhala mumsewu akuchuluka. Kulemba ana ntchito yakalavula gaga kukuchitika chifukwa cha kulephera kutetezera ana kuti ena asawadyere masuku pamutu. Mankhwala osokoneza bongo akuwononganso achinyamata ambiri. Mwachitsanzo, pamene wachinyamata wina ku Brazil anamwerekera ndi mankhwala osokoneza bongo, mtendere unatheratu panyumba pawo. Kuwonjezera pa kusautsika mtima kwa makolo ake, iwo anavutika ndi kuti apeze ndalama zompezera chithandizo choti asiye khalidweli, ndiponso anthu opanda chifundo ogulitsa mankhwala osokoneza bongowo anabwera kudzafuna malipiro awo.
Komabe, mosasamala kanthu za mavuto a m’moyo, makolo ambiri akulimbikira kupezera ana awo osati kokha chakudya, zovala, ndi pogona ayi komanso kuwatetezera ku chiwawa, mankhwala osokoneza bongo, ndi mavuto ena. Akuchita bwino, koma kodi nzokhazo zimene ayenera kuchita? Bwanji ponena za kuwatetezera ku zinthu zimene zingawononge malingaliro awo kapena uzimu wawo? Ambiri akudziŵa kuti kuchita bwino ukholo kumaphatikizapo kuthandiza ana pamavuto awo osankha mabwenzi ndi zosangulutsa. Komabe, kodi makolo angapeŵe motani kupereka chitetezo chomkitsa kapena kukhala olekerera mopambanitsa? Tikukupemphani kusanthula mayankho opezeka m’nkhani yotsatira.
[Mawu a M’munsi]
a Maina asinthidwa m’nkhani ino.