Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 7/15 tsamba 4-6
  • Kodi Ana Anu Mukuwafunira Tsogolo Lotani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ana Anu Mukuwafunira Tsogolo Lotani?
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ngati Makolo Akhaladi Osamala
  • Athandizeni Kusankha Ntchito Yabwino
  • Kodi Mungasamalire Motani Zosoŵa za Mumtima Mwawo?
  • Njira Zosamalirira Zosoŵa Zawo Zauzimu
  • Pamene Ana Onse Adzakhala Osungika
  • Makolo, Muzithandiza Ana Anu Kuti Azikonda Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Phunzitsani Mwana Wanu Kuyambira Paukhanda Wake
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
  • Makolo Phunzitsani Ana Anu Mwachikondi
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Makolo, Pezerani A M’banja Lanu Zosowa Zawo
    Nsanja ya Olonda—2005
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 7/15 tsamba 4-6

Kodi Ana Anu Mukuwafunira Tsogolo Lotani?

KODI ana anu mumawaona monga mphatso ya mtengo wapatali? (Salmo 127:3) Kapena kodi mumaona kuti kuwalera kwangokhala ngati chinthu chosatsimikizika chowonongetsa ndalama? M’malo modzetsa phindu landalama, kulera ana kumadya ndalama mpaka pamene adzayamba kudzichirikiza okha. Monga momwe kuyendetsa chuma chopatsidwa kumafunira kulinganiza bwino, kulera ana mwachipambano kumafunaso zomwezo.

Makolo osamala amafuna kuthandiza ana awo kukhala ndi chiyambi chabwino m’moyo. Ngakhale kuti zinthu zoipa ndiponso zomvetsa chisoni zingachitike m’dziko lino, makolo angayesetse kutetezera ana awo. Lingalirani za Werner ndi Eva, otchulidwa m’nkhani yoyambayo.a

Ngati Makolo Akhaladi Osamala

Werner akusimba kuti m’malo mochita mphwayi, makolo ake anali ofunitsitsadi kudziŵa zimene zikuchitika kusukulu. “Ndinayamikira kwambiri malingaliro othandiza amene iwo anandipatsa, ndipo ndinali kumva kuti akundisamaladi ndipo akundichirikiza. Pokhala makolo, anali ndi malamulo okhwima ndithu, koma ndinadziŵa kuti ali mabwenzi anga enieni.” Ndipo pamene Eva anakhumudwa kwambiri ndi maphunziro ake moti anachita tondovi ndipo sanali kupeza tulo, makolo ake, Francisco ndi Inez, anatheranso nthaŵi yaitali ndithu kulankhula naye ndi kumthandiza kuti awongolere maganizo ake ndiponso kuti ayambe kusamalira zinthu zauzimu.

Kodi Francisco ndi Inez, anachita motani kuti atetezere ana awo ndi kuwakonzekeretsa moyo wauchikulire? Eya, kuyambira panthaŵi imene anawo anali makanda, makolo achikondi ameneŵa anali kukhala nawo pazochita zawo zatsiku ndi tsiku nthaŵi zonse. M’malo mongocheza ndi akulu anzawo, Inez ndi Francisco anali kukhala ndi ana awo kulikonse kumene anali kupita. Monga makolo achikondi, iwo anapatsanso mwana wawo wamwamuna ndi wamkazi chitsogozo chabwino. Inez anati: “Tinawaphunzitsa kusamalira nyumba, kugwiritsira ntchito bwino ndalama, ndi kusamalira zovala zawo. Ndipo tinathandiza aliyense wa iwo kusankha ntchito yakuthupi ndiponso kusamalira bwino maudindo awo pamodzi ndi zinthu zauzimu.”

Nkofunika chotani nanga kudziŵa ana anu ndi kuwatsogoza monga makolo! Tiyeni tisanthule mbali zitatu mmene mungachitire zimenezi: (1) Thandizani ana anu kusankha ntchito yabwino yakuthupi; (2) akonzekeretseni kupirira zovuta zakusukulu ndi zakuntchito; (3) asonyezeni mmene angasamalirire zofunika zawo zauzimu.

Athandizeni Kusankha Ntchito Yabwino

Popeza kuti ntchito ya munthu yakuthupi simangokhudza mkhalidwe wake wazandalama wokha komanso imamdyera nthaŵi yaikulu, kuchita bwino ukholo kumaphatikizapo kusanthula zimene mwana aliyense amakonda ndiponso zimene amatha kuchita. Popeza kuti palibe munthu wachikumbumtima chabwino amene amafuna kukhala chothodwetsa kwa ena, makolo ayenera kuganiza mofatsa za mmene angakonzekeretsere mwana wawo kudzichirikiza yekha ndi banja lake. Kodi mwana wanu wamwamuna kapena wamkazi ayenera kuphunzira umisiri wina kuti adzizipezera zofunika m’moyo? Monga kholo losamaladi, yesetsani mosaleka kuthandiza mwana wanu kukulitsa mikhalidwe monga chikhumbo cha kulimbikira pogwira ntchito, kukhala wofunitsitsa kuphunzira, ndi kukhala bwino ndi ena.

Lingalirani za Nicole. Iye anati: “Ndinali kugwira ntchito ndi makolo anga pantchito yawo yoyeretsa. Iwo anati gawo lina la malipiro anga likhale losamalirira zosoŵa zapanyumba ndi kugwiritsira ntchito ndalama zotsalazo mmene ndikufunira kapena kuzisunga. Zimenezi zinandipangitsa kudzimva kukhala waudindo kwambiri, zimene zinandithandiza kwambiri pambuyo pake.”

Mawu a Mulungu, Baibulo, safotokoza za mtundu wa ntchito yakuthupi imene munthu ayenera kusankha. Koma amapereka zitsogozo zothandiza. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo anati: “Ngati munthu safuna kugwira ntchito, asadyenso.” Polembera Akristu a ku Tesalonika, ananenanso kuti: “Tikumva za ena mwa inu kuti ayenda dwachedwache, osagwira ntchito konse, koma ali ochita mwina ndi mwina. Koma oterewa tiwalamulira ndi kuwadandaulira mwa Ambuye Yesu Kristu, kuti agwire ntchito pokhala chete, nadye chakudya cha iwo okha.”​—2 Atesalonika 3:10-12.

Komabe, moyo si kungopeza ntchito ndi kupanga ndalama basi. M’kupita kwa nthaŵi, awo amene amangokhumba kutchuka sadzakhala okhutira ndipo adzazindikira kuti ‘akungosautsa mtima.’ (Mlaliki 1:14) M’malo molimbikitsa ana awo kukhumba kutchuka ndi kulemera, makolo amachita bwino kuwathandiza kuona nzeru ya mawu ouziridwa a mtumwi Yohane akuti: “Musakonde dziko lapansi, kapena za m’dziko lapansi. Ngati wina akonda dziko lapansi, chikondi cha Atate sichili mwa iye. Pakuti chilichonse cha m’dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma kudziko lapansi. Ndipo dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi zonse.”​—1 Yohane 2:15-17.

Kodi Mungasamalire Motani Zosoŵa za Mumtima Mwawo?

Monga kholo, bwanji osakhala monga mphunzitsi wa anthu ochita maseŵero olimbitsa thupi? Iye samangosumika maganizo pa kuthandiza amaseŵerowo kukhala aliŵiro kwambiri kapena kuti azilumpha kwambiri chabe. Ayenera kuti amayesetsanso kuwathandiza kuchotsa mantha aliwonse, kukulitsa chidaliro chawo. Nanga inuyo mungawalimbikitse motani ana anu, kuwamangirira, ndi kuwasonkhezera?

Lingalirani za Rogério, wachinyamata wazaka 13. Kuwonjezera pa kuvutika mtima kwake chifukwa cha kusintha kwa thupi lake, iye anapsinjika mtima chifukwa cha kusagwirizana kwa makolo ake ndi kusasamalidwa kwake. Kodi pali thandizo lotani kwa achinyamata monga iye? Ngakhale kuti simungathe kutetezera ana anu ku nkhaŵa zonse ndi zisonkhezero zoipa, musasiye ntchito yanu yaukholo. Popanda kukhala wotetezera monkitsa, phunzitsani ana anu mukumawamvetsa, nthaŵi zonse mukumakumbukira kuti mwana aliyense ngwosiyana ndi ena. Mwa kusonyeza kukoma mtima ndi chikondi, mungayesetse kupangitsa wachinyamata kudzimva kuti ngwosungika. Zimenezi zidzapangitsanso kuti akadzakula adzakhale wodzidalira ndiponso wodzilemekeza.

Mosasamala kanthu za chipambano chimene makolo anu anali nacho posamalira zosoŵa za mumtima mwanu, zinthu zitatu zingakuthandizeni kukhala kholo lothandizadi: (1) Musatengeke kwambiri ndi mavuto anu moti nkunyalanyaza mavuto ooneka ngati aang’ono a ana anu; (2) yesetsani kukambitsirana nawo mwa njira yosangalatsa ndiponso kambitsiranani zinthu zothandiza masiku onse; (3) asonkhezereni kukhala ndi maganizo abwino pothetsa mavuto ndi pochita zinthu ndi anthu ena.

Pokumbukira zaka zaunyamata wake, Birgit anati: “Ndinaphunzira kuti sungasinthe anthu kuti akhale monga momwe ukufunira. Amayi anga anandiphunzitsa kuti ndikaona khalidwe lina mwa anthu ena limene sindinakonde, zimene ndingachite ndizo kupeŵa kukhala monga iwo. Anandiuzanso kuti nthaŵi yabwino koposa yosinthira zochita zanga ndiyo pamene ndidakali mwana.”

Komabe, ana anu amafunanso zina kuwonjezera pantchito ndi mtima wokhazikika. Dzifunseni kuti ‘Kodi ukholo ndimauona monga udindo wopatsidwa ndi Mulungu?’ Ngati mumauona motero, mudzasamalira zosoŵa zauzimu za ana anu.

Njira Zosamalirira Zosoŵa Zawo Zauzimu

Pa Ulaliki wake wa pa Phiri, Yesu Kristu anati: “Achimwemwe ali awo ozindikira kusoŵa kwawo kwauzimu, popeza kuti ufumu wakumwamba uli wawo.” (Mateyu 5:3, NW) Kodi pamafunikanji kuti musamalire zosoŵa zauzimu? Ana amapindula kwambiri pamene makolo apereka chitsanzo chabwino posonyeza chikhulupiriro mwa Yehova Mulungu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Wopanda chikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa [Mulungu]; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna Iye.” (Ahebri 11:6) Koma kuti chikhulupiriro chikhale chatanthauzo lenileni, pemphero nlofunika. (Aroma 12:12) Ngati muzindikira zosoŵa zanu zauzimu, mudzapempha thandizo la Mulungu, monga momwe anachitira atate wa mwana amene anadzakhala Woweruza wodziŵika bwino wa Israyeli, Samsoni. (Oweruza 13:8) Simudzalekezera pa pemphero ayi komanso mudzafunafuna thandizo m’Mawu ouziridwa a Mulungu, Baibulo.​—2 Timoteo 3:16, 17.b

Mosasamala kanthu za ntchito yanu yovuta yopereka chitsogozo chabwino, kusamalira zosoŵa za mumtima, ndi kuwathandiza mwauzimu, ukholo ungakhale wofupa. Atate wina wa ana aŵiri ku Brazil anati: “Sindingathe nkuyerekezera kuti ndilibe anawa. Pali zabwino zambiri zimene timachitira nawo limodzi.” Pofotokoza chifukwa chimene anawo akuchitira bwino, amayi awo anawonjezera kuti: “Nthaŵi zonse timakhala limodzi, ndipo timayesa kuchita zinthu zosangalatsa ndiponso zodzetsa chimwemwe. Ndiponso, chofunika kwambiri, nthaŵi zonse timawapempherera.”

Priscilla akukumbukira mmene makolo ake anamsonyezera chikondi ndi kuleza mtima nthaŵi zonse patakhala vuto. “Anali mabwenzi anga enieni ndipo anandithandiza pa zilizonse,” iye akutero. “Monga mwana wawo, ndinadzimvadi kuti akunditenga monga ‘cholandira cha kwa Yehova.’” (Salmo 127:3) Monga momwe makolo ena ambiri amachitira, bwanji osapangana ndi ana anu za nthaŵi yoŵerengera pamodzi Baibulo ndi zofalitsa zachikristu? Kuphunzira nkhani za m’Baibulo ndi mapulinsipulo ake mumkhalidwe wosangalatsa kungathandize ana anu kukhala achidaliro ndi kukhala ndi chiyembekezo chabwino cha zamtsogolo.

Pamene Ana Onse Adzakhala Osungika

Ngakhale kuti lerolino tsogolo la ana ambiri likuoneka ngati lopanda zabwino, Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti dziko lapansi lidzakhala malo achisungiko okhalapo mtundu wa anthu. Tangolingalirani za nthaŵi m’dziko latsopano lolonjezedwalo la Mulungu pamene makolo sadzadera nkhaŵa za chisungiko cha ana awo! (2 Petro 3:13) Ingoyerekezerani kuti mukuona kukwaniritsidwa kwakukulu kwa ulosiwu: “Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wa nkhosa, ndipo nyalugwe adzagona pansi ndi mwana wa mbuzi; ndipo mwana wa ng’ombe ndi mwana wa mkango ndi choŵeta chonenepa pamodzi; ndipo mwana wamng’ono adzazitsogolera.” (Yesaya 11:6) Ngakhale lerolino, chisungiko chauzimu chofotokozedwa m’mawuwo chikupezeka mophiphiritsira pakati pa amene akutumikira Yehova. Mutakhala pakati pawo, mudzapeza chisamaliro chachikondi cha Mulungu. Ngati mumakondadi Mulungu, mungakhale wotsimikiza kuti iye akumvetsa mmene mukumverera monga kholo ndipo adzakuthandizani kulimbana ndi nkhaŵa ndi mayesero amene mungakumane nawo. Phunzirani Mawu ake ndipo khalani ndi chiyembekezo mu Ufumu wake.

Thandizani ana anu kuti akapeze moyo wosatha mwa kupereka chitsanzo chabwino. Ngati muthaŵira kwa Yehova Mulungu, tsogolo lanu ndi la ana anu lidzaposa ndi zimene mukuganizira. Mungakhale ndi chidaliro chonga cha wamasalmo amene anaimba kuti: “Udzikondweretsenso mwa Yehova; ndipo Iye adzakupatsa zokhumba mtima wako.”​—Salmo 37:4.

[Mawu a M’munsi]

a Maina asinthidwa m’nkhani ino.

b Onani mitu 5 mpaka 7 m’buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena