Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 10/1 tsamba 7
  • Musaleke Kulengeza Uthenga Wabwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Musaleke Kulengeza Uthenga Wabwino
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Nkhani Yofanana
  • Ndimadalira Yehova Posankha Zochita
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
  • Chikondi Chigwirizanitsa Mabanja
    Nsanja ya Olonda—1989
  • “Mulungu Alibe Tsankhu”
    Nsanja ya Olonda—1994
Nsanja ya Olonda—1998
w98 10/1 tsamba 7

Olengeza Ufumu Akusimba

Musaleke Kulengeza Uthenga Wabwino

PAMENE anthu a ku Ulaya oyendera malo anafika ku Gulf of Venezuela ndi ku Nyanja ya Maracaibo nthaŵi yoyamba, m’gombelo munali nyumba zambiri zofolera zomangidwa pansanja pamwamba pa madzi osazamawo. Zimenezo zinawakumbutsa mzinda wa Venice, ku Italy, kumene anthu anamanga nyumba zawo m’mbali mwenimweni mwa madzi. Ndiye chifukwa chake oyendera malo amenewo olankhula Chisipanya anatcha malowo kuti Venezuela, liwu lotanthauza “Venice Wamng’ono.”

Lerolino, m’dziko lokongola limeneli mukuchitikanso programu yomanga ya mtundu wina, yauzimu. Kumeneko Mboni za Yehova zili pantchito yaikulu yodzala mbewu za Ufumu pampata uliwonse wabwino. Kututa kwauzimu kumene kwatsatirapo kukudzetsa chitamando chachikulu kwa “Mwini zotuta,” Yehova Mulungu.​—Mateyu 9:37, 38.

Pamene woyang’anira wina woyendayenda anachezera mpingo wina m’chigawo cha Zulia kumpoto chakumadzulo kwa Venezuela, Mboni za kumeneko zinalinganiza kuti iye ndi mkazi wake akaone kachisumbu kena kapafupi kotchedwa Toas. Ataima pamzere mmamaŵa poyembekezera boti lopita ku kachisumbuko, mkazi wa woyang’anira woyendayendayu, Mery, anapempha mnzake, mlongo mpainiya wanthaŵi zonse, kuti alankhule ndi antchito ena a pabotipo. Mlongo mpainiyayo anavomera.

Atafikira makanika wina, Mery anamsonyeza buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Anamsonyeza mutu wakuti “Kumanga Banja Lolemekeza Mulungu,” umene anaoneka kuti anaukonda mwamunayo. Kenako Mery anafotokoza kuti mwa kugwiritsira ntchito bukulo, angakhale ndi phunziro la Baibulo m’nyumba mwake. Mwamunayo analandira bukulo, ndipo makonzedwe anapangidwa akuti wina akamchezere kunyumba kwake.

Posapita nthaŵi kenako, kunali msonkhano wapadera wa tsiku limodzi kumeneko. Mery anadabwa kwambiri kuona makanikayo, Senor Nava, ali pamsonkhanowo, pamodzi ndi mkazi wake ndi ana ake aang’ono aakazi aŵiri! Mery anafunsa mkaziyo kuti akuliona bwanji phunziro lawo la banja la Baibulo. Yankho lake linali lodabwitsa zedi.

“Ndikuthokoza Yehova kuti taphunzira choonadi,” mkaziyo anatero. Ndiyeno anafotokoza. “Mutalankhula ndi amuna anga, anali atangondisiya kumene ndi kukwatira mkazi wina. Analinso kumwa kwadzaoneni. Nthaŵi zina ataledzera, anali kundisautsa, zinthu zimene anthu ochepawo apachisumbu sanakondwere nazo. Anali kukhulupiriranso mizimu. Komabe, chidziŵitso cha m’Baibulo chimene anapeza paphunzirolo chawathandiza kusinthiratu moyo wawo. Anasiya zochita zawo zonse zoipa. Makolo awo, amene ndi Akatolika achita chidwi kwambiri ndi kusintha kumeneku. Iwo ngokondwa kuti tsopano iwo ndi mwamuna ndiponso tate wodalirika.”

Senor Nava anabatizidwa mu 1996 ndipo panopo akutumikira monga mtumiki wanthaŵi zonse. Mkazi wawo, Jenny, anabatizidwa mu 1997. Bwanamkubwa wa tauniyo anachita chidwi kwambiri ndi kusintha kwa makanika wa boti ameneyu moti iyenso anapempha kukhala ndi phunziro la Baibulo. Alongowo ngokondwa chotani nanga kuti sanaleke kulengeza uthenga wabwino poyembekezera boti pamzere mmaŵawo!

[Zithunzi patsamba 7]

Kuuzako makanika wa boti uthenga wabwino kunali ndi zotsatirapo zosangalatsa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena