Kuyesetsa Kukhala “Wantchito Wopanda Chifukwa Cha Kuchita Manyazi”
YOSIMBIDWA NDI ANDRÉ SOPPA
Nkhondo Yadziko II inali mkati, kuchititsa imfa za anthu zosaneneka ndi kusweka mtima pomalizira pake. Monga wopereka masiginala wa m’Gulu Lankhondo Lapamadzi la Germany amene ndinali pafupi ndi Narvik, ku Norway, ndinadzionera ndekha nkhanza ya munthu kwa munthu mnzake. Usiku, m’munsi mwa maphedi a m’mbali mwa nyanja, kukongola kwa kuwala kwakuthambo kotchedwa northern lights kumene kumaonekera m’madera a kumpoto kwa dziko lapansi kunandipangitsa kusinkhasinkha kwambiri za moyo. Ndinali wotsimikiza kuti Mulungu amene analenga zinthu ngati zimenezi sindiye akuchititsa nkhondo zoipazo.
NDINABADWA mu 1923 m’mudzi wina waung’ono wa Lassoth (kumene tsopano ndi ku Poland), kufupi ndi malire a dziko la Czech, ndipo ndinakulira m’banja losauka laulimi. Makolo anga anali Akatolika amphamvu, ndipo chipembedzo chinali chofunika kwambiri m’miyoyo yathu. Komabe, ndidakali wamng’ono ndinayamba kuchikayikira chipembedzo changa. M’mudzi mwathu, munali mabanja atatu achiprotesitanti, ndipo Akatolika anali kusala mabanjawa. Sindinali kumvetsa chifukwa chochitira zimenezi. Kusukulu anali kutiphunzitsa katekisima. Koma tsiku lina nditafunsa wansembe kuti afotokoze Utatu, yankho limene anandipatsa linali zikoti khumi. Komabe, chimene chinachitika ndili ndi zaka 17 n’chimene chinandipangitsa kumva kuti tchalitchi chandigwiritsa mwala. Makolo awo a amayi anga anamwalira motsatizana mosiyana ndi mwezi umodzi pakati, ndipo amayi analibe ndalama zokwanira zoti alipirire mapemphero akutchalitchi a maliro aŵiri. Choncho amayiwo anafunsa wansembe ngati angadzamlipire bwino lake. “Makolo anu anali ndi katundu, si choncho?” ndilo linali yankho lake. “Mgulitseni ndi kugwiritsa ntchito ndalama zake pamaliro.”
Zaka zingapo zimenezo zisanachitike, Hitler atayamba kulamulira mu 1933, anatiletseratu kulankhula Chipolishi; tinafunikira kulankhula Chijeremani. Aja amene anakana, kapena amene analephera kuphunzira Chijeremani, anali kusoŵa pang’onopang’ono—anatumizidwa ku misasa yachibalo, tinamva choncho pambuyo pake. Ngakhale mudzi wathu unasinthidwa dzina n’kupatsidwa lachijeremani, Grünfliess. Pamene ndinali ndi zaka 14 ndinasiya sukulu, ndipo chifukwa chakuti sindinali m’gulu la Achinyamata a Hitler, ndinavutika kupeza ntchito. Koma m’kupita kwa nthaŵi, ndinalembedwa monga wophunzira kusula zitsulo. Nkhondo itayamba, m’tchalitchi munali mapemphero opempherera Hitler ndi asilikali achijeremani. Ndinali kusinkhasinkha ngati mapemphero ofananawo opempha chilakiko anali kuperekedwanso kumbali inayo.
Kutumikira m’Gulu Lankhondo Lapamadzi la Germany
Mu December 1941, ndinaloŵa Gulu Lankhondo Lapamadzi la Germany, ndipo kuchiyambi kwa 1942, ndinatumizidwa ku gombe la Norway kukagwira ntchito pachombo cha azondi. Tinapatsidwa ntchito yoperekeza zombo zonyamula asilikali, zida zankhondo, kapena katundu wamba zoyenda pakati pa Trondheim ndi Oslo. Mpanyanjapo pamene ndinamva oyendetsa zombo aŵiri akukambirana za mapeto a dziko lapansi monga momwe Baibulo likuneneratu. Ngakhale kuti ankachita mantha kulankhula momasuka, iwo anandiuza kuti makolo awo ankagwirizana ndi Mboni za Yehova koma kuti iwowo sanatsatire chitsanzo chawo. Imeneyi inali nthaŵi yoyamba kuti ndimve za Mboni za Yehova.
Nkhondoyo itatha, Abulitishi anatigwira kukhala akaidi ndipo anakatisiya m’manja mwa Aamereka kuti atibwezere ku Germany. Ife amene midzi yakwathu tsopano inali m’dera la Soviet anatitumiza kundende ya ku Liévin, kumpoto kwa France, kukagwira ntchito m’migodi ya malasha. Mmenemu munali mu August 1945. Ndikukumbukira kufunsa mmodzi mwa alonda athu achifalansa chipembedzo chake. “Katolika,” anayankha. Popeza kuti inenso ndinali Mkatolika, ndinamfunsa zimene tinalakwirana. “Palibe chifukwa chofunira kumvetsa. Basi ndi mmene zilili,” anayankha motero. Kwa ine zinali zodabwitsa kuti anthu a chipembedzo chimodzi azimenyana ndi kuphana.
Kuunika Mumgodi wa Malasha
Patsiku langa loyamba mumgodi, ndikugwira ntchito pamodzi ndi antchito a komweko, munthu wina wotchedwa Evans Emiot anandigaŵira masangweji. Anali atakhala m’France zaka zambiri ndithu, koma kwawo kunali ku Ohio, ku United States. Anandiuza za dziko limene simudzakhala nkhondo. Kukoma mtima kwake kunandidabwitsa. Sanandide ngakhale kuti ndinali Mjeremani ndipo iye Mmereka. Sitinaonanenso mpaka kuchiyambi cha 1948 pamene anandipatsa kabuku kakuti “The Prince of Peace” (Kalonga wa Mtendere). Mpamene ndinaphunzira tsono za Mulungu wokonda ubwino amene amada nkhondo—Mulungu amene ndinali kumganizira ndikamayang’ana kuwala kwakuthambo kuja. Ndinafunitsitsa kupeza chipembedzo chimene chinali kuphunzitsa zimenezi. Koma popeza kuti Evans anali kugwira ntchito kumbali ina ya mgodi, sindinathe kuonana naye. Ndinazungulira mosaphula kanthu m’timagulu tonse tosiyanasiyana tachipembedzo m’ndendemo, ndikumafunsa ngati akudziŵa zilizonse ponena za kabukuko.
Pomalizira pake, mu April 1948, ndinamasulidwa m’ndende ndipo ndinakhala wantchito womasuka. Lamlungu lotsatira, ndinadabwa kumva kulira kwa kabelu mumsewu. Ndinakondwatu kwambiri kuona Evans! Anali pamodzi ndi gulu la Mboni za Yehova zomwe zinavala mabolodi kumbuyo ndi kutsogolo olengeza nkhani yapoyera. Mboni yomwe inali kuliza belulo ndi Marceau Leroy, amene tsopano ndi wa m’Komiti ya Nthambi ku France. Anandipereka kwa Mpolishi wina wolankhula Chijeremani wotchedwa Joseph Kulczak, amene anavutika m’misasa yachibalo chifukwa cha chikhulupiriro chake. Anandipempha kuti ndipite kumisonkhano madzulowo. Sindinamve zambiri zomwe zinali kunenedwa, koma pamene onse amene analipo anakweza mikono yawo, ndinafunsa munthu amene ndinayandikana naye kuti akuchitiranji zimenezo. “Ndiwo amene akufuna kupita ku Dunkerque mlungu wamaŵa kukalalikira.” “Kodi ndingapite nawo?” ndinafunsa motero. “Kulekeranji, mutha kupita!” anandiyankha. Choncho Lamlungu lotsatira ndinali kulalikira kunyumba ndi nyumba. Ngakhale kuti si onse amene tinakumana nawo amene anamvetsera, ndinasangalala kwambiri ndipo posapita nthaŵi ndinali kulalikira mokhazikika.
Kuphunzira Kuletsa Ukali Wanga
Posapita nthaŵi, Mboni zinayamba kulalikira m’mudzi mmene munali kukhala Ajeremani omasulidwa kundende. Zimenezi zinandivuta, popeza kuti ambiri mmenemo anali kundidziŵa kuti ndine waukali. Wina atanyozera zimene ndikumuuza, ndinali kumuopseza kuti: “Ngati susamala uloŵa nazo m’mavuto zimenezi.” Nthaŵi ina yake ndidakali kugwira ntchito mumgodi, ndinammenya wina amene anatonza Yehova.
Komabe, mothandizidwa ndi Yehova, ndinatha kusintha umunthu wanga. Tsiku lina, tikulalikira m’mudziwu, gulu la amuna amene anali atamwa kwambiri moŵa anali kusautsa Mboni zina. Podziŵa kuti ndine wamtima wapachala, abale amene ndinali nawo anayesa kundiletsa kuti ndisaloŵerepo, koma mmodzi mwa amunawo anayamba kubwera kwa ine moopseza nayamba kuvula jekete lake. Ndinatsika panjinga, kumpatsa iyeyo kuti aigwire, ndi kuika manja anga m’matumba. Anadabwa nazo kwambiri zimenezi moti anamvetsera zimene ndinanena. Ndinamuuza kuti apite kunyumba kukagona ndiyeno afike kudzamvetsera nkhani yapoyera. Ndithudi, pa 3:00 p.m., anali atafika! M’kupita kwa nthaŵi, amene anali akaidi ngati 20 analandira uthengawo. Ineyo ndinabatizidwa mu September 1948.
Zochita Zambiri Koma Zopindulitsa
Ndinapatsidwa udindo wosamalira magawo amene tinayenera kukalalikirako ndi kupeza malo kumene kungakhalire nkhani zapoyera. Kuti ndichite zimenezi ndinkayenda makilomita ngati 50 pa kanjinga kanga kamoto, ndisanapite kukagwira shifiti yausiku kumigodi. Ndiyeno pa mapeto a mlungu, tinkapita kugawolo pa basi ndi kusiya ofalitsa aŵiri kapena anayi pamodzi ndi wokamba nkhani. M’mizinda ikuluikulu, titapeza malo abwino, tinali kusanjikiza masutukesi athu kuti akhale thebulo la wokamba nkhani. Nthaŵi zambiri, tinali kuvala mabolodi kumbuyo ndi kutsogolo polengeza mutu wa nkhani yapoyera imene tinali kuitanirako anthu.
Mu 1951 mpamene ndinadziŵana ndi Jeannette Chauffour, Mboni ina ya ku Reims. Tinangokondana nthaŵi yomweyo, ndipo patapita chaka chimodzi, pa May 17, 1952, tinakwatirana. Tinasamukira ku Pecquencourt, mzinda wa migodi woyandikana ndi Douai. Komabe, posapita nthaŵi ndinayamba kudwaladwala. Anandipeza ndi silicosis, matenda ochititsidwa ndi kugwira ntchito m’migodi, koma sindinathe kupeza ntchito yamtundu wina. Choncho mu 1955, pamsonkhano wamitundu yonse ku Nuremberg, Germany, titapemphedwa kukathandiza mpingo wina waung’ono ku Kehl, tauni yaing’ono ya maindasitale ambiri kumtsinje wa Rhine, tinali omasuka kusamukira kumeneko. Panthaŵiyo, kunali ofalitsa 45 okha mumpingomo. Pazaka zisanu ndi ziŵiri zimene tinagwira ntchito ndi mpingo umenewu, chiŵerengero cha ofalitsa chinawonjezeka kufika pa 95.
Mwayi Wowonjezeka wa Utumiki
Poona kuti mpingo uja wakhazikika, tinapempha Sosaite kuti ititumize monga apainiya apadera ku France. Mosayembekezeka, tinatumizidwa ku Paris. Miyezi isanu ndi itatu imene tinathera kumeneko inali yosangalatsa kwambiri. Ineyo ndi Jeannette tinali ndi mwayi wochititsa maphunziro a Baibulo 42 onse pamodzi. Asanu mwa ophunzira athu anabatizidwa ifeyo tidakali komweko, m’kupita kwa nthaŵi 11 enanso analandira choonadi.
Popeza tinali kukhala ku Latin Quarter, nthaŵi zambiri tinali kukumana ndi mapolofesa a pa Sorbonne. Polofesa wina wa filosofi wopuma pantchito amene anali kuchita machiritso achikhulupiriro anaphunzira Baibulo nakhala mmodzi wa Mboni za Yehova m’kupita kwa nthaŵi. Tsiku lina ndinayamba kukambirana za Baibulo ndi injiniya wina wa zomangamanga amene anali kugwirizana kwambiri ndi aphunzitsi achijezwiti. Anabwera kunyumba kwathu nthaŵi ya 3 koloko masana ndi kuchokako 10 koloko usikuwo. Koma tinadabwa kuti anabweranso kunyumba kwathu patangopita ola limodzi ndi theka. Anali atalankhula ndi Mjezwiti wina amene analephera kuyankha mafunso ake okhudza ulosi wa Baibulo. Pa 1 koloko m’bandakucha anapita kunyumba kwawo, nabweranso pa 7 koloko. M’kupita kwa nthaŵi, iyenso anakhala mmodzi wa Mboni za Yehova. Ludzu lotero la choonadi linandilimbikitsa kwambiri ineyo ndi mkazi wanga.
Titatumikira ku Paris, ndinapemphedwa kukatumikira monga woyang’anira woyendayenda kummaŵa kwa France. Tinasangalala zedi kuchezera mipingo yolankhula Chifalansa ndi Chijeremani, kulimbikitsa abale. Pochezera mpingo wa Rombas, ku Lorraine, ndinakumana ndi Stanislas Ambroszczak. Iye anali Mpolishi amene, m’nkhondo, anatumikira m’chombo cha pansi pa nyanja cha mayiko olimbana ndi Germany ndipo anamenya nkhondo m’madzi a ku Norway. Tinali adani panyanja imodzimodzi. Tsopano tinali abale ogwirira ntchito pamodzi kutumikira Mulungu wathu, Yehova. Nthaŵi ina pamsonkhano waukulu ku Paris, ndinaona munthu amene ndinamzindikira. Anali mkulu wa msasa kumene ndinali mkaidi kumpoto kwa France. Tinakondwera kwambiri kugwirira ntchito pamodzi pamsonkhanopo! Imeneyo ndiyo mphamvu ya Mawu a Mulungu; imasintha adani akale kukhala abale ndiponso mabwenzi apamtima!
Mwachisoni, titakhala m’ntchito yoyendayenda kwa zaka 14, ndinasiya chifukwa cha kudwaladwala kwanga. Komabe, ineyo ndi mkazi wanga tinali otsimikiza mtima kupitirizabe kutumikira Yehova mulimonse mmene tingathere. Choncho tinapeza nyumba yokhalamo ndi kuloŵa ntchito m’tauni ya Mulhouse, kummaŵa kwa France, ndipo tinakhala apainiya (alaliki a nthaŵi zonse).
Chinanso chosangalatsa kwambiri pazaka zonsezi chakhala kumanga nawo Nyumba za Ufumu. Mu 1985, ndinapemphedwa kulinganiza gulu lomanga nyumba kummaŵa kwa France. Mwa kugwiritsa ntchito amisiri aluso ndi kuphunzitsa anthu odzipereka modzifunira, tinakwanitsa kupanga gulu limene lamanga kapena kukonzanso maholo oposa 80, kuwapanga kukhala oyenerera kulambira kwa Yehova. Ndipo ndinasangalalatu kwambiri, mu 1993, kumanga nawo Nyumba Yamsonkhano ndi Nyumba za Ufumu zisanu ku French Guiana, South America!
Kulimbikirabe Pamavuto
Nditha kunena motsimikizira kuti pazaka 50 zapitazi za ntchito yateokalase, moyo wanga wakhala ndi zinthu zambiri zosangalatsa ndiponso mwayi wochuluka wa utumiki. Mwachisoni, mu December 1995 mkazi wanga wokondedwa, amene ndinakhala naye zaka 43, anamwalira. Pamene kuli kwakuti nthaŵi imeneyi inali yachisoni chachikulu—ndipo ndidakalirabe mpaka pano—Yehova amandipatsa nyonga, ndiponso abale ndi alongo anga auzimu andisonyeza chikondi ndi kundipatsa chichirikizo zimene zikuchepetsa chisoni m’kupita kwa nthaŵi.
Ndikukumbukirabe bwino lomwe mawu a mbale wina wodzozedwa pamsonkhano waukulu ku Munich, Germany, mu 1963. “André,” iye anatero, “usayang’ane kulamanzere kapena kulamanja. Abale amene anali m’misasa yachibalo anayesedwa. Tsopano ifeyo tiyenera kupitiriza. Sitiyenera kudzimvera chisoni. Choncho tiyeni tilimbikirebe!” Ndakhala ndikukumbukirabe zimenezi. Tsopano pamene sinditha kuchita zambiri chifukwa cha thanzi lofooka ndi ukalamba, mawu opezeka pa Ahebri 6:10 amanditonthoza nthaŵi zonse: “Mulungu sali wosalungama kuti adzaiŵala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera ku dzina lake.” Inde, kuchita utumiki wa Yehova ndiwo mwayi waukulu koposa umene aliyense angakhale nawo. Pazaka 50 zapitazi, cholinga changa chinali, ndipo chidakali, kukhala “wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi.”—2 Timoteo 2:15.
[Chithunzi patsamba 22]
Mtundu wa boti limene ndinali kutumikiramo m’maphedi a m’mbali mwa nyanja ku Norway
[Chithunzi patsamba 23]
Kulalikira panjinga kumpoto kwa France
[Chithunzi patsamba 23]
Masutukesi osanjikizana ndiwo anali thebulo la wokamba nkhani
[Zithunzi patsamba 24]
Ineyo ndi mkazi wanga, Jeannette, pachikwati chathu mu 1952