Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 1/1 tsamba 11-20
  • “Limbitsani Mitima Yanu”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Limbitsani Mitima Yanu”
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chitsanzo cha Abrahamu cha Chikhulupiriro
  • Kumvetsera kwa Mulungu
  • Kulankhula ndi Mulungu
  • Mbiri ya Chikhulupiriro Lerolino
  • Kulitsani Chikhulupiriro Lerolino
  • Chiyembekezo Chidzakwaniritsidwa Posachedwa
  • Abulahamu Anali “Bwenzi” la Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Kodi Muli ndi Chikhulupiriro Chonga cha Abrahamu?
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Kodi Abulahamu Anali Ndani?
    Nsanja ya Olonda—2012
  • ‘Kuyenda mwa Chikhulupiriro Osati mwa Chionekedwe’
    Nsanja ya Olonda—1998
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 1/1 tsamba 11-20

“Limbitsani Mitima Yanu”

“Chikusoŵani chipiriro, kuti pamene mwachita chifuniro cha Mulungu, mukalandire lonjezano.”​—AHEBRI 10:36.

1, 2. (a) Kodi n’chiyani chimene chinachitikira Akristu ochuluka m’zaka za zana loyamba? (b) Kodi n’chifukwa chiyani sikovuta kuti chikhulupiriro chifooke?

MWA anthu onse amene analemba Baibulo, palibe amene anatchula chikhulupiriro kaŵirikaŵiri ngati mtumwi Paulo. Ndipo mochulukira, anali kunena za amene chikhulupiriro chawo chinafooka kapena chinafa. Mwachitsanzo, Humenayo ndi Alesandro “chikhulupiriro chawo chidatayika.” (1 Timoteo 1:19, 20) Dema anathaŵa Paulo chifukwa ‘anakonda dziko lino lapansi.’ (2 Timoteo 4:10) Ena, chifukwa cha zochita zawo zosakhala zachikristu ndi zosasamala, ‘anakana chikhulupiriro.’ Ena ananyengedwa ndi nzeru zonama ndipo ‘anataya chikhulupiriro.’​—1 Timoteo 5:8; 6:20, 21.

2 Kodi n’chifukwa chiyani Akristu odzozedwa amenewo analephera chonchi? Eya, “chikhulupiriro ndicho chikhazikitso cha zinthu zoyembekezeka, chiyesero cha zinthu zosapenyeka.” (Ahebri 11:1) Timasonyeza chikhulupiriro pazinthu zimene sitingazione. Chikhulupiriro sichifunika pazinthu zimene tikuziona. N’kosavuta kugwirira ntchito chuma chooneka kusiyana ndi chuma chauzimu chosaoneka. (Mateyu 19:21, 22) Zinthu zambiri zimene timaziona​—monga ngati “chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso”​—zimakopa mwamphamvu thupi lathu lopanda ungwiro ndipo zingafooketse chikhulupiriro chathu.​—1 Yohane 2:16.

3. Kodi Mkristu ayenera kukhala ndi chikhulupiriro chotani?

3 Komatu, “iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphoto iwo akumfuna Iye,” anatero Paulo. Mose anali ndi chikhulupiriro chonga chimenechi. Iye “anapenyerera chobwezera cha mphotho” ndipo “anapirira molimbika, monga ngati kuona wosaonekayo.” (Ahebri 11:6, 24, 26, 27) Mkristu amafunika chikhulupiriro chonga chimenechi. Monga momwe tinaonera m’nkhani yapitayo, Abrahamu anapereka chitsanzo chabwino pa mbali imeneyi.

Chitsanzo cha Abrahamu cha Chikhulupiriro

4. Kodi chikhulupiriro cha Abrahamu chinakhudza motani kukhala kwake ndi moyo?

4 Abrahamu anali ku Uri pamene Mulungu anamlonjeza kuti adzabereka mbewu imene idzadalitsa anthu amitundu yonse. (Genesis 12:1-3; Machitidwe 7:2, 3) Ndi lonjezo limeneli, Abrahamu anamvera Yehova, nasamukira choyamba ku Harana ndiyeno ku Kanani. Kumeneko, Yehova analonjeza kuti adzapereka dzikolo kwa mbewu ya Abrahamu. (Genesis 12:7; Nehemiya 9:7, 8) Komabe, zambiri zimene Yehova analonjeza zinali kudzakwaniritsidwa Abrahamu atamwalira. Mwachitsanzo, Abrahamu mwiniyo analibe malo akeake m’Kanani​—kupatula kokha phanga la Makipela, limene anagula kuti likhale manda. (Genesis 23:1-20) Mosasamala kanthu za zimenezo, iye anakhulupirira mawu a Yehova. Koposa zonse, anali kukhulupirira za “mudzi [wa m’tsogolo] wokhala nawo maziko, mmisiri wake ndi womanga wake ndiye Mulungu.” (Ahebri 11:10) Ndi chikhulupiriro choterocho chimene chinamchirikiza pamoyo wake wonse.

5, 6. Kodi chikhulupiriro cha Abrahamu chinayesedwa m’njira yotani mogwirizana ndi lonjezo la Yehova?

5 Zimenezi zikuoneka bwino makamaka pa lonjezo lakuti mbewu ya Abrahamu idzakhala mtundu waukulu. Kuti zimenezi zichitike, Abrahamu anafunika kukhala ndi mwana, komatu anadikirira nthaŵi yaitali kuti akhale naye. Sitikudziŵa kuti anali ndi zaka zingati pamene Mulungu anamlonjeza koyamba, koma pamene anayenda ulendo wautaliwo kupita ku Harana, Yehova anali asanampatsebe mwana. (Genesis 11:30) Anakhala ku Harana kwanthaŵi yaitali ndithu kotero kuti ‘anasonkhanitsa chuma ndi kubala miyoyo,’ ndipo pamene anasamukira ku Kanani, iye anali ndi zaka 75 ndipo Sara anali ndi zaka 65. Komabe, analibe mwana. (Genesis 12:4, 5) Pamene Sara anali ndi zaka zapakati pa ma 70, anaganiza kuti tsopano anali atakalamba kwambiri kwakuti sakanamubalira mwana Abrahamu. Motero, potsatira mwambo wa nthaŵi imeneyo, anapereka mdzakazi wake Hagara kwa Abrahamu, ndipo Abrahamu anabereka naye mwana. Koma ameneyu sanali mwana wolonjezedwayo. M’kupita kwa nthaŵi Hagara ndi mwana wake, Ismayeli, anadzachotsedwapo pakhomopo. Komabe, pamene Abrahamu anachonderera m’malo mwawo, Yehova analonjeza kudzadalitsa Ismayeli.​—Genesis 16:1-4, 10; 17:15, 16, 18-20; 21:8-21.

6 Panthaŵi yoikika ya Mulungu​—patapita nthaŵi yaitali kwambiri kuchokera pamene analonjezedwa kwanthaŵi yoyamba​—Abrahamu amene tsopano anali ndi zaka 100 ndi Sara amene anali ndi zaka 90 anabala mwana wamwamuna, Isake. Ziyenera kuti zinalidi zodabwitsa! Kwa nkhalamba zimenezi, zinali ngati kuti ndi chiukiriro pamene matupi awo ‘akufa’ anatulutsa moyo watsopano. (Aroma 4:19-21) Anadikira kwanthaŵi yaitali, koma pamene lonjezolo linakwaniritsidwa, kudikirirako kunalidi koyenerera.

7. Kodi chikhulupiriro chikugwirizana motani ndi chipiriro?

7 Chitsanzo cha Abrahamu chikutikumbutsa kuti chikhulupiriro sichiyenera kukhalapo kwanthaŵi yochepa chabe. Paulo anagwirizanitsa chikhulupiriro ndi chipiriro pamene analemba kuti: “Chikusoŵani chipiriro, kuti pamene mwachita chifuniro cha Mulungu, mukalandire lonjezano. . . . Ife si ndife a iwo akubwerera kuloŵa chitayiko; koma a iwo a chikhulupiriro cha ku chipulumutso cha moyo.” (Ahebri 10:36-39) Ambiri ayembekeza kwanthaŵi yaitali kuti lonjezo likwaniritsidwe. Ena ayembekeza kwamoyo wawo wonse. Chikhulupiriro chawo cholimba chawachirikiza. Ndipo monga Abrahamu, adzalandira mphotho m’nthaŵi yoikika ya Yehova.​—Habakuku 2:3.

Kumvetsera kwa Mulungu

8. Kodi lerolino timamvetsera motani kwa Mulungu, ndipo kodi n’chifukwa chiyani zimenezi zidzalimbitsa chikhulupiriro chathu?

8 Chikhulupiriro cha Abrahamu chinalimbikitsidwa ndi zinthu zosachepera pa zinayi, ndipo zinthu zomwezo zingatithandizenso ifeyo. Choyamba, anaonetsa kuti anali ‘kukhulupirira kuti Mulungu alipo’ mwa kumvera Yehova atalankhula. Motero, anali wosiyana ndi Ayuda a m’tsiku la Yeremiya, amene anali kukhulupirira Yehova koma osakhulupirira mawu ake. (Yeremiya 44:15-19) Lerolino, Yehova amatilankhula kupyolera mu Baibulo, Mawu ake ouziridwa, amene Petro anati ali ngati “nyali younikira m’malo a mdima . . . pa mtima yanu.” (2 Petro 1:19) Pamene tiŵerenga Baibulo ndi kumalimvetsa, timakhala ‘tikuleredwa m’mawuwo a chikhulupiriro.’ (1 Timoteo 4:6; Aroma 10:17) Ndiponso, m’masiku otsiriza ano, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” akupereka “zakudya [zauzimu] panthaŵi yake,” chitsogozo pa kugwiritsa ntchito mapulinsipulo a Baibulo ndi kumvetsetsa ulosi wa Baibulo. (Mateyu 24:45-47) Kumvetsera kwa Yehova kupyolera m’njira zimenezi ndi kofunika kwambiri kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba.

9. Kodi n’chiyani chimene chidzatsatirapo ngati tikukhulupiriradi chiyembekezo chachikristu?

9 Chikhulupiriro cha Abrahamu chinali chogwirizana kwambiri ndi chiyembekezo chake. “Anakhulupira nayembekeza . . . kuti iye akakhale kholo la mitundu yambiri ya anthu.” (Aroma 4:18) Ichi ndi chinthu chachiŵiri chimene chingatithandize. Tisaiwaletu kuti Yehova ali “wobwezera mphoto iwo akumfuna Iye.” Mtumwi Paulo anati: “Tigwiritsa ntchito ndi kuyesetsa, chifukwa chiyembekezo chathu tili nacho pa Mulungu wamoyo.” (1 Timoteo 4:10) Ngati timakhulupiriradi chiyembekezo chachikristu, moyo wathu wonse udzakhala ukusonyeza chikhulupiriro chathu, mofanana ndi mmene zinalili ndi Abrahamu.

Kulankhula ndi Mulungu

10. Kodi ndi pemphero lotani limene lidzalimbitsa chikhulupiriro chathu?

10 Abrahamu anali kulankhula ndi Mulungu, ndipo ichi ndi chinthu chachitatu chimene chinalimbitsa chikhulupiriro chake. Lerolino, ifenso tingalankhule ndi Yehova, pogwiritsa ntchito mphatso ya kupemphera mwa Yesu Kristu. (Yohane 14:6; Aefeso 6:18) Yesu anali atamaliza kufotokoza fanizo lomwe linagogomezera kufunika kwa kupemphera nthaŵi zonse pamene anafunsa kuti: “Mwana wa munthu pakudza Iye, adzapeza chikhulupiriro padziko lapansi kodi?” (Luka 18:8) Pemphero lolimbitsa chikhulupiriro silikhala lopanda nzeru komanso silikhala longoloŵeza pamtima. Limakhala latanthauzo kwambiri. Mwachitsanzo, pemphero lochokera mumtima ndi lofunika pamene tifunika kupanga zosankha zofunika kwambiri kapena pamene tapsinjika maganizo.​—Luka 6:12, 13; 22:41-44.

11. (a) Kodi Abrahamu analimbikitsidwa motani pamene anamuuza Mulungu za mumtima mwake? (b) Tikuphunziranji pachochitika cha Abrahamu?

11 Pamene Abrahamu anali kukalamba ndipo Yehova anali asanampatsebe mbewu yolonjezedwayo, anamfotokozera Mulungu dandaulo lake. Yehova anamkhazika mtima pansi. Chotsatirapo chake? Abrahamu “anakhulupirira Yehova, ndipo kunayesedwa kwa iye chilungamo.” Ndiyeno, Yehova anapereka chizindikiro kutsimikiziritsa mawu ake otonthozawo. (Genesis 15:1-18) Ngati timuuza Yehova za mumtima mwathu m’pemphero, kuvomereza zomwe iye akutitsimikizira m’Mawu ake, Baibulo, ndi kumumvera ndi chikhulupiriro chonse, ndiye kuti Yehova adzalimbitsanso chikhulupiriro chathu.​—Mateyu 21:22; Yuda 20, 21.

12, 13. (a) Kodi Abrahamu anadalitsidwa motani pamene anatsatira chitsogozo cha Yehova? (b) Kodi ndi zokumana nazo zotani zimene zidzalimbitsa chikhulupiriro chathu?

12 Chinthu chachinayi chimene chinalimbitsa chikhulupiriro cha Abrahamu chinali chichirikizo chimene Yehova anampatsa pamene anatsatira chitsogozo cha Mulungu. Pamene Abrahamu anapita kukapulumutsa Loti kwa mafumu oloŵerera, Yehova anampatsa chipambano. (Genesis 14:16, 20) Pamene anali kukhala monga wopempha malo m’dziko limene linali kudzakhala la mbewu yake, Yehova anamdalitsa mwakuthupi. (Yerekezerani ndi Genesis 14:21-23.) Yehova anatsogolera zoyesayesa za wantchito wake kuti apeze mkazi woyenera wa Isake. (Genesis 24:10-27) Inde, Yehova “anadalitsa Abrahamu m’zinthu zonse.” (Genesis 24:1) Motero chikhulupiriro chake chinalimbadi kwambiri ndipo unansi wake ndi Yehova Mulungu unakhaladi wathithithi kwakuti Yehova anamutcha kuti “bwenzi langa.”​—Yesaya 41:8; Yakobo 2:23.

13 Kodi lerolino ifeyo tingakhale ndi chikhulupiriro cholimba moterocho? Inde. Mofanana ndi Abrahamu, ngati ife timuyesa Yehova mwa kumvera malamulo ake, iye adzatidalitsanso, ndipo zimenezo zidzalimbitsa chikhulupiriro chathu. Mwachitsanzo, pa Lipoti la Chaka Chautumiki cha 1998 tingaone kuti anthu ambiri anadalitsidwa modabwitsa pamene anamvera lamulo lake la kulalikira uthenga wabwino.​—Marko 13:10.

Mbiri ya Chikhulupiriro Lerolino

14. Kodi Yehova anadalitsa motani ndaŵala ya Uthenga wa Ufumu Na. 35?

14 M’mbuyomo mu October 1997, ndaŵala ya padziko lonse ya Uthenga wa Ufumu Na. 35 inali yopambana kwambiri, chifukwa cha changu ndi kufunitsitsa kwa Mboni mamiliyoni ochuluka. Chitsanzo chake ndi zimene zinachitika ku Ghana. Pafupifupi makope mamiliyoni 2.5 anagaŵidwa m’zinenero zinayi, ndipo chotsatirapo chake chinali chakuti anthu pafupifupi 2,000 anapempha phunziro la Baibulo. Ku Cyprus Mboni ziŵiri zomwe zinali kugaŵira Uthenga wa Ufumu zinaona wansembe akuzitsatira. Patapita kanthaŵi, zinampatsa kope la Uthenga wa Ufumu. Iye anali atalilandira kale ndipo anati: “Ndinachita chidwi kwambiri ndi uthenga wake kwakuti ndimafuna kuthokoza anthu amene analilemba.” Ku Denmark, makope mamiliyoni 1.5 a Uthenga wa Ufumu anagaŵidwa ndipo panali zotsatirapo zabwino. Mkazi wina kumeneko amene amagwira ntchito yothandiza anthu anati: “Thirakitili lili ndi uthenga wa aliyense. Ndi losavuta kumva, ndipo limakopa, kukupatsa chikhumbo chofuna kumva zambiri. N’lolondoladi!”

15. Ndi zochitika ziti zimene zikusonyeza kuti Yehova anadalitsa zoyesayesa za kufikira anthu paliponse?

15 Mu 1998 panali kuyesayesa kofikira anthu osati kokha panyumba zawo komanso paliponsepo. Ku Côte d’Ivoire amishonale aŵiri anacheza m’sitima za pamadzi 322 pamene zinali m’madoko. Anagaŵira mabuku 247, magazini 2,284, mabolosha 500, ndi mathirakiti mazanamazana, kuphatikizaponso mavidiyo kuti amalinyerowo azionerera pamene ali panyanja. Ku Canada Mboni ina inapita ku galaja yokonza mabode a magalimoto. Mwiniwake anali wosangalatsidwa, ndipo mbaleyo anakhalamo maola anayi ndi theka, ngakhale kuti nthaŵi yeniyeni imene analalikira inali chabe ola limodzi kapena kuposerapo pamene ankayembekezera makasitomala. Pamapeto pake anagwirizana zomaphunzira nthaŵi ya 10:00 p.m. Komabe, nthaŵi zina anali kuyamba kuphunzira pakati pausiku ndipo anali kumaliza m’mbandakucha m’ma 2:00 koloko. Mwachionekere ndandanda yawoyo inali yovuta, koma inatulutsa zabwino. Munthuyo anaganiza zomatseka galaja yake pa Lamlungu kuti azipita kumisonkhano. Posakhalitsa iye ndi banja lake anali kupita patsogolo bwino kwambiri.

16. Ndi zochitika ziti zimene zikusonyeza kuti bolosha la Mulungu Amafunanji ndi buku la Chidziŵitso ndi zida zamphamvu pantchito ya kulalikira ndi kuphunzitsa?

16 Bolosha la Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? ndi buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha zidakali zida zamphamvu pantchito ya kulalikira ndi kuphunzitsa. Ku Italy mvirigo wina amene anali kudikira basi analandira kope la Uthenga wa Ufumu. Tsiku lotsatira, anafikiridwanso ndipo analandira bolosha la Mulungu Amafunanji. Kuchokera patsikulo, anali kukhala ndi phunziro la Baibulo kwa mphindi 10 kufika 15 tsiku lililonse pamalo okwerera basipo. Patatha mwezi umodzi ndi theka, anaganiza zochoka ku nyumba ya avirigo ndi kupita kwawo ku Guatemala kuti akapitirize kuphunzira. Ku Malaŵi Lobina, yemwe anali kupita kutchalitchi mwakhama, anakhumudwa ataona kuti ana ake ayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Komabe anawo anali kuwafotokozera amayi awo choonadi cha Baibulo pamene anali okhoza kutero. Mu June 1997, Lobina anaona buku la Chidziŵitso ndipo anakopeka ndi mawu akuti “Chidziŵitso Chotsogolera.” Mu July anavomera kukhala ndi phunziro la Baibulo. Mu August anafika pamsonkhano wachigawo ndipo anamvetsera mosamalitsa ku pologalamu yonse. Pofika ku mapeto a mwezi umenewo anali atasiya kupita kutchalitchi kwawo ndipo anayeneretsedwa kukhala wofalitsa wosabatizidwa. Anabatizidwa mu November 1997.

17, 18. Kodi mavidiyo a Sosaite akhala othandiza motani pa kuthandiza anthu kuti ‘aone’ zinthu zauzimu?

17 Mavidiyo a Sosaite athandiza anthu ambiri kuti ‘aone’ zinthu zauzimu. Ku Mauritius mwamuna wina anachoka m’tchalitchi chake chifukwa chakuti munalibe mgwirizano. Mmishonale wina anamsonyeza kugwirizana kwa Mboni za Yehova mwa kugwiritsa ntchito vidiyo ya United by Divine Teaching. Atachita chidwi, mwamunayo anati: “Inu Mboni za Yehova muli kale m’Paradaiso!” Anavomera kukhala ndi phunziro la Baibulo. Mlongo wina ku Japan anaonetsa mwamuna wake wosakhulupirira vidiyo ya Jehovah’s Witnesses​—The Organization Behind the Name ndipo inamsonkhezera kukhala ndi phunziro la Baibulo lokhazikika. Ataonerera vidiyo yakuti United by Divine Teaching, iye anafuna kukhala wa Mboni za Yehova. Vidiyo ya mbali zitatu yakuti The Bible​—A Book of Fact and Prophecy inamthandiza kugwiritsa ntchito mapulinsipulo a Baibulo m’moyo wake. Ndiyeno, vidiyo ya Jehovah’s Witnesses Stand Firm Against Nazi Assault inamsonyeza kuti Yehova amalimbikitsa anthu Ake pamene aukiridwa ndi Satana. Mwamunayo anabatizidwa mu October 1997.

18 Izi ndi zitsanzo zochepa chabe za zinthu zambirimbiri zimene tasangalala nazo m’chaka chautumiki chapitachi. Zikusonyeza kuti Mboni za Yehova zili ndi chikhulupiriro chantchito ndipo Yehova akulimbitsa chikhulupirirocho mwa kudalitsa ntchito yawo.​—Yakobo 2:17.

Kulitsani Chikhulupiriro Lerolino

19. (a) Kodi ndi motani mmene ife tilili pabwino kusiyana ndi Abrahamu? (b) Ndi anthu angati amene anasonkhana chaka chatha kuti akumbukire imfa ya nsembe ya Yesu? (c) Ndi mayiko ati amene anali ndi ziŵerengero zikuluzikulu za ofika pa Chikumbutso chaka chatha? (Onani tchati pamasamba 12 kufika 15.)

19 Ife lerolino tili pabwino m’njira zambiri kusiyana ndi mmene Abrahamu analili. Timadziŵa kuti Yehova anakwaniritsa malonjezo ake onse kwa Abrahamu. Ana a Abrahamu analandiradi dziko la Kanani, ndipo anakhaladi mtundu waukulu. (1 Mafumu 4:20; Ahebri 11:12) Komanso, zaka ngati 1,971 kuchokera pamene Abrahamu anachoka ku Harana, mbadwa yake, Yesu, anabatizidwa m’madzi ndi Yohane Mbatizi ndipo kenako mwa mzimu woyera ndi Yehova iyemwini kuti akhale Mesiya, Mbewu ya Abrahamu m’lingaliro lake lenileni lauzimu. (Mateyu 3:16, 17; Agalatiya 3:16) Pa Nisani 14, 33 C.E., Yesu anapereka moyo wake monga dipo kwa anthu amene adzasonyeza chikhulupiriro mwa iye. (Mateyu 20:28; Yohane 3:16) Tsopano anthu ochuluka akatha kudalitsidwa mwa iyeyu. Chaka chatha, anthu 13,896,312 anasonkhana pa Nisani 14 kuti akumbukire chochitika chodabwitsa chimenechi cha chikondi. Ndi chitsimikizirodi cha Yehova, Wosunga malonjezo Wamkulu!

20, 21. Kodi anthu a mitundu yonse anadzidalitsa motani mwa Mbewu ya Abrahamu m’zaka za zana loyamba, ndipo kodi akudzidalitsa motani lerolino?

20 M’zaka za zana loyamba, anthu ochuluka ochokera m’mitundu yonse​—kuyambira ndi Israyeli wakuthupi​—anakhulupirira Mbewu imeneyi ya Abrahamu ndipo anakhala ana odzozedwa a Mulungu, mamembala a “Israyeli wa Mulungu” watsopano wauzimu. (Agalatiya 3:26-29; 6:16; Machitidwe 3:25, 26) Anali atatsimikiziridwa za chiyembekezo cha moyo wauzimu wosafa kumwamba monga olamulira anzake a Ufumu wa Mulungu. Anthu 144,000 okha ndiwo adzadalitsidwa moteremu, ndipo amene adakalipo ndi ochepa chabe. (Chivumbulutso 5:9, 10; 7:4) Chaka chatha, anthu 8,756 anachitira umboni wakuti amakhulupirira kuti ali m’gulu limeneli mwa kudya zizindikiro paphwando la Chikumbutso.

21 Pafupifupi Mboni za Yehova zonse lerolino ndi za “khamu lalikulu” loloseredwa pa Chivumbulutso 7:9-17. Chifukwa chakuti amadzidalitsa mwa Yesu, ali ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi la paradaiso. (Chivumbulutso 21:3-5) Anthu 5,888,650 amene anali pantchito yolalikira mu 1998 ndi umboni wakuti khamuli ndi ‘lalikuludi.’ Zinalidi zokondweretsa kuona kuti kwanthaŵi yoyamba mayiko a Russia ndi Ukraine achitira lipoti ofalitsa oposa 100,000. Lipoti lochokera ku United States linalinso lochititsa chidwi kwambiri​—anali ndi ofalitsa 1,040,283 mu August! Awa ndi mayiko atatu chabe mwa mayiko 19 amene anachitira lipoti ofalitsa oposa 100,000 chaka chathachi.

Chiyembekezo Chidzakwaniritsidwa Posachedwa

22, 23. (a) Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kulimbitsa mitima yathu lerolino? (b) Kodi ndi motani mmene tingakhalire ngati Abrahamu, osati ngati anthu opanda chikhulupiriro amene Paulo anatchula?

22 Amene anafika pa Chikumbutso anakumbutsidwa kuti tafika pati m’kukwaniritsidwa kwa malonjezo a Yehova. Mu 1914, Yesu anaikidwa pampando monga Mfumu ya Ufumu wakumwamba wa Mulungu, kuyamba kukhalapo kwake m’mphamvu ya Ufumu. (Mateyu 24:3; Chivumbulutso 11:15) Inde, Mbewu ya Abrahamu tsopano ikulamulira kumwamba! Yakobo anauza Akristu a m’tsiku lake kuti: “Lezani mtima . . . limbitsani mitima yanu; pakuti kudza [“kukhalapo,” NW] kwake kwa Ambuye kuyandikira.” (Yakobo 5:8) Eya, kukhalapo kumeneko tsopano kulipodi! N’chifukwa chomvekadi cholimbitsira mitima yathu!

23 Chidaliro chathu mwa Mulungu chizikhalitsidwatu chatsopano nthaŵi zonse ndi phunziro la Baibulo lokhazikika ndi pemphero latanthauzo. Tisaleketu kukhala ndi madalitso a Yehova pamene tikumvera Mawu ake. Mwakutero tidzakhala ngati Abrahamu, osati ngati aja amene anawatchula Paulo kuti chikhulupiriro chawo chinafooka ndi kufa. Palibe chimene chidzatisiyitsa chikhulupiriro chathu choyeretsetsa. (Yuda 20) Tikupemphera kuti zimenezi zikhale motero kwa atumiki onse a Yehova m’chaka chautumiki cha 1999 ndi kupitirizabe mpaka m’tsogolo monse.

Kodi Mukudziŵa?

◻ Kodi lerolino tingamvetsere motani kwa Mulungu?

◻ Ndi mapindu otani amene amabwera ndi pemphero latanthauzo kwa Mulungu?

◻ Ngati momvera titsatira chitsogozo cha Yehova, kodi chikhulupiriro chathu chidzalimbitsidwa motani?

◻ Ndi mbali ziti za lipoti lachaka (masamba 12 kufika 15) zimene zakusangalatsani kwambiri?

[Tchati patsamba 12-15]

LIPOTI LA CHAKA CHAUTUMIKI CHA 1998 LA MBONI ZA YEHOVA PADZIKO LONSE

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

[Chithunzi patsamba 16]

Ngati timvetsera Mawu a Yehova, tidzapangitsa chidaliro chathu m’malonjezo ake kukhala chatsopano

[Chithunzi patsamba 18]

Chikhulupiriro chathu chimalimbitsidwa pamene tichita nawo utumiki

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena