Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 7/1 tsamba 28-29
  • Kutchula Dzina la Mulungu ku Israyeli

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kutchula Dzina la Mulungu ku Israyeli
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi N’kulakwa Kutchula Dzina la Mulungu?
    Galamukani!—1999
  • Chifukwa Chake Tiyenera Kudziwa Dzina la Mulungu
    Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha
  • Mmene Mungadziŵire Dzina la Mulungu
    Galamukani!—2004
  • Tanthauzo la Dzina la Mulungu Ndiponso Mmene Tingaligwiritsire Ntchito
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 7/1 tsamba 28-29

Kutchula Dzina la Mulungu ku Israyeli

KWA zaka mazana angapo Chiyuda chosunga mwambo chaletsa anthu ake kutchula dzina la Mulungu lakuti Yehova. Malinga ndi mmene Mishnah imanenera, aliyense wotchula dzina la Mulungu “alibe malo m’dziko likudzalo.”​—Sanhedrin 10:1.a

Pa January 30, 1995, yemwe anali rabi wamkulu wa a Sephardi ku Israyeli anatchula mwadala dzina la Mulungu. Anachita zimenezi pamene anali kulakatula tikkun, pemphero la kulapa la ophunzira Cabala. Pemphero limeneli limaperekedwa kuti mwina Mulungu angabwezeretse mgwirizano m’chilengedwe, umene malinga ndi olambira ake, unasokonezeka ndi makamu a mizimu yoipa. Nyuzipepala yakuti Yedioth Aharonoth ya pa February 6, 1995, inati: “Pemphero limeneli ndi lamphamvu kwambiri moti mawu ake amangopezeka m’kabuku kapadera kamene sagulitsa kwa anthu.” Kutchula kotere dzina la Mulungu amati kumachititsa pemphero kukhala ndi mphamvu yapadera.

Kusangalatsa kwake n’koti Baibulo limalamula atumiki a Mulungu kugwiritsa ntchito dzina lake lakuti Yehova. (Eksodo 3:15; Miyambo 18:10; Yesaya 12:4; Zefaniya 3:9) M’malembo oyambirira achihebri a m’Baibulo, dzina limeneli limapezeka pafupifupi nthaŵi zokwana 7,000. Komabe, Baibulo limachenjeza za kugwiritsira ntchito molakwa dzina la Mulungu. Lamulo lachitatu pa Malamulo Khumi limati: “Usatchule dzina la Yehova Mulungu wako pachabe; chifukwa Yehova sadzamuyesa iye wosachimwa, amene atchula pachabe dzina lakelo.” (Eksodo 20:7) Kodi ndi motani mmene dzina la Mulungu lingatchulidwire pachabe? Ndemanga ya The Jewish Publication Society imati liwu lachihebri lotembenuzidwa kuti “pachabe” lingaphatikizepo osati “kupeputsa” kokha dzina la Mulungu komanso “kulakatula madalitso opanda pake.”

Ndiyeno kodi tikkun, pemphero la kulapa la ophunzira Cabala, tingalione motani? Kodi linayamba bwanji? M’zaka za zana la 12 ndi 13 C.E, Chiyuda chotsata zinsinsi, chotchedwa Cabala, chinayamba kufalikira. M’zaka za zana la 16, Isaac Luria, mrabi, anaphatikiza “tikkunim” m’pemphero la ophunzira Cabala. Dzina la Mulungu linali kutchulidwa monga chithumwa chokhala ndi mphamvu yapadera, ndipo analiphatikiza m’pemphero la ophunzira Cabala. Kodi muganiza kuti n’koyenera kugwiritsa ntchito motere dzina la Mulungu?​—Deuteronomo 18:10-12.

Mulimonse mmene muyankhire funso limeneli, mungavomereze kuti kutchula dzina la Mulungu poyera ku Israyeli wamakono chinali chinthu chosachitikachitika. Koma Mulungu iye mwini ananeneratu kuti: “Tsiku lomwelo mudzati, Muyamikire Yehova, bukitsani dzina lake, mulalikire machitidwe ake mwa mitundu ya anthu, munene kuti dzina lake lakwezedwa. Muimbire Yehova; pakuti wachita zaulemerero; chidziŵike ichi m’dziko lonse.”​—Yesaya 12:4, 5.

Chosangalatsa n’chakuti ku Israyeli, monganso mayiko ena oposa 230 padziko lonse lapansi, Mboni za Yehova zikuyesetsa kuthandiza anasi awo kupeza chidziŵitso cholongosoka cha Yehova. Izo zikukhulupirira kuti enanso ambiri adzafikira pozindikira tanthauzo la malemba monga la Salmo 91:14 lakuti: “Popeza andikondadi [akutero Yehova] ndidzam’pulumutsa; ndidzam’kweza m’mwamba, popeza adziŵa dzina langa.”

[Mawu a M’munsi]

a Mishnah ndi buku la ndemanga zowonjezera pa malamulo a m’Malemba, zozikidwa pa ziphunzitso za arabi (aphunzitsi) otchedwa Tannaim. Linalembedwa chakumapeto kwa zaka za zana lachiŵiri ndi kumayambiriro kwa zaka za zana lachitatu C.E.

[Chithunzi patsamba 28]

Kuno ku Negeb, anthu a Yehova akudziŵikitsa dzina lake ndi Mawu ake

[Chithunzi patsamba 29]

Chikwangwani chosonyeza dzina la Mulungu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena