“Mwandisinthitsa Malingaliro Anga pa Mboni za Yehova”
MMENEMO ndi mmene mmodzi wa oyang’anira ndende ku Poland ananenera pankhani yonena za ntchito ya Mboni za Yehova, yofotokozedwa m’kope lathu la October 15, 1998. Nkhaniyo, “Pamene Mitima Yonga Mwala Imvetsera,” inafotokoza za chipambano cha Mboni za Yehova m’ntchito yolalikira kwa akaidi a m’ndende ya ku Wołów, Poland.
Magazini ya Nsanja ya Olonda yotchulidwa pamwambayi isanatulutsidwe, msonkhano wapadera wakuti adzaigaŵire kwa akaidiwo unachitika ku ndendeyo ya ku Wołów pa September 13, 1998. Oitanidwa ku msonkhano umenewu anaphatikizapo Mboni za kumaloko, akaidi obatizidwa ndi ena okondwerera, ndi oyang’anira ndendeyo angapo. Zotsatirazi ndi zina mwa zimene opezeka pa msonkhanowo ananena.
Jerzy, mmodzi wa Mboni za Yehova amene anabatizidwa ali m’ndende zaka zoposa zisanu zapitazo, anati: “Ndasangalala kwambiri, chifukwa lerolino ndingathe kuŵerenga za kuyesayesa kumene abale a m’mipingo yapafupi achita pofuna kutithandiza.” Iye anawonjezera kuti: “Ndikuyesetsa kuti ndisinthe, ndipo ndikutha kuona mmene Yehova akundiumbira.”
Mkaidi wina, yemwe dzina lake ndi Zdzisław, ponena za ntchito yochitira umboni m’ndendeyo anati: “Pakali pano, akaidi anayi akukonzekera ubatizo, ndipo okondwerera atsopano akupitiriza kumapezeka pa misonkhano m’holo yathu. Nkhani imeneyi ndi chisonkhezero cha mphamvu kwa ife kuti tipititse patsogolo ntchito yolalikira m’gawo limeneli.” Ndi chinthu cholimbikitsa kwambiri polingalira kuti Zdzisław adakali ndi zaka 19 zokhala m’ndende!
Ataŵerenga nkhani yonena za ndende ya ku Wołów, mmodzi wa oyang’anira ndende anati: “Tachitiridwa ulemu waukulu. Sindinaganizepo kuti nkhani yonena za ndende ino ingafalitsidwe motero m’zinenero 130 padziko lapansi. Ndimasangalala ndi anthu inu, ndipo ndikuyamikira zoyesayesa zanu m’malo mwa akaidi onse.” Woyang’anira wina anawonjezera kuti: “Mwandisinthitsa malingaliro anga pa Mboni za Yehova. M’mbuyomu, ndimakulingalirani kukhala anthu ouma khosi m’zachipembedzo. Ndaona tsopano kuti ndinu anthu a choonadi.”
Mkulu wa ndende ya Wołów, Marek Gajos anamwetulira nati: “Poyamba tinali kuganiza kuti simudzaphulapo kanthu kwenikweni. Tinali kukulingalirani kukhala chipembedzonso china chofuna kuwongolera akaidi pogwiritsa ntchito Baibulo. Komabe, poona zotsatira za ntchito yanu, talingalira za kugwirizana nanu. Mwakhala mukubwera kuno mosatopa kwa zaka zisanu ndi zinayi tsopano, ndipo ndikukuyamikani kwambiri pa zimene mwachitapo kale.”
Komabe, kodi nkhaniyi inalandiridwa motani ndi anthu onse a pandende ya Wołów? Panali chisangalalo chachikulu kwambiri, moti magazini onse amene anali ndi Mboni za m’ndendezo anatha. Oyang’anira ndende nawonso, anasonyeza chisangalalo mwa kupemphanso makope ena 40. Kuti akwanire, abale a mipingo yakufupi anathandiza mwa kutumizira abale akundendewo makope 100 owonjezera. Nthaŵi yomweyonso, chiŵerengero cha anthu osonkhana a m’ndende chinawonjezereka.
Woyang’anira ndende wina, Piotr Choduń amene wakhala akugwirizana ndi Mboni za Yehova, anati: “Tinaganiza za kukhoma nkhaniyi pa mabolodi onse a chidziŵitso m’ndende yathu. Tili ndi chikhumbo choti akaidi onse amene sanayambe kuphunzira nanu Baibulo aŵerenge magaziniyi.”
Chitsanzo chabwino cha Mboni ndi kuyesayesa kwawo kudzipereka m’ntchito yolalikira zikupitirizabe kutulutsa zabwino. Kuphatikiza pa akaidi 15 amene anabatizidwa, oyang’anira ndende aŵiri anapatulira miyoyo yawo kwa Yehova ndipo woyang’anira ndende winanso wapempha kuti azikhala ndi phunziro la Baibulo. Inde, abale amene akulalikira ku ndende ya ku Wołów akulemekeza Yehova Mulungu chifukwa cha chipambano chawo.—Yerekezani ndi 1 Akorinto 3:6, 7.
[Chithunzi patsamba 28]
Mboni zitatu ndi mkaidi pa mwambo wopereka magazini m’holo yamisonkhano ya m’ndende