Zamkatimu
October 15, 2011
Magazini Yophunzira
NKHANI ZOPHUNZIRA MILUNGU YA:
November 28, 2011–December 4, 2011
Kodi Zimene Mumachita pa Nthawi Yosangalala Zimakhala Zopindulitsa?
TSAMBA 8
December 5-11, 2011
Malangizo Anzeru kwa Anthu Amene Sali Pabanja Ndiponso Amene Ali Pabanja
TSAMBA 13
December 12-18, 2011
Khulupirirani Yehova, “Mulungu Amene Amatitonthoza M’njira Iliyonse”
TSAMBA 23
December 19-25, 2011
TSAMBA 27
Cholinga cha Nkhani Zophunzira
NKHANI YOPHUNZIRA 1 TSAMBA 8-12
Kaya tikukhala kuti, kutsatira mfundo za m’Baibulo kungatithandize kusankha zosangalatsa zabwino. Nkhaniyi itithandiza kuunika bwino zosangalatsa zomwe timakonda.
NKHANI YOPHUNZIRA 2 TSAMBA 13-17
Zimene munthu wasankha pa nkhani yoti akhale pa banja kapena ayi sizimangokhudza mmene moyo wake udzakhalire koma zimakhudzanso ubwenzi wake ndi Yehova. Nkhaniyi isonyeza mmene atumiki a Mulungu kaya apabanja kapena ayi angagwiritse ntchito uphungu wa m’Baibulo wopezeka pa 1 Akorinto chaputala 7 pa moyo wawo.
NKHANI ZOPHUNZIRA 3, 4 TSAMBA 23-31
M’masiku otsiriza ano, atumiki a Yehova komanso anthu ena akukumana ndi mavuto ambiri. Kodi ndi mavuto ati amene amakumana nawo? Kodi tingapeze kuti thandizo? Nkhani ziwirizi zisonyeza mmene Yehova limodzi ndi anthu ake akuthandizira anthu m’masiku ovuta ano.
M’MAGAZINI INO MULINSO NKHANI IZI
3 N’chifukwa Chiyani Tiyenera—‘Kukhalabe Maso’?
18 Kutumikira Yehova Kwandibweretsera Chimwemwe
32 Mafunso Ochokera kwa Owerenga
[Mawu a Chithunzi patsamba 2]
Globe: Courtesy of Replogle Globes