Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w12 11/1 tsamba 8-9
  • Funso Lachitatu: N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Ndizivutika?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Funso Lachitatu: N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Ndizivutika?
  • Nsanja ya Olonda—2012
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Baibulo Limanena Zotani?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
  • Nkhani Zimene Zili M’magaziniyi
    Galamukani!—2020
  • Mavuto
    Galamukani!—2015
  • N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola kuti Anthu Azivutika?
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2012
w12 11/1 tsamba 8-9

Funso Lachitatu: N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Ndizivutika?

ABAMBO ake a Ian anali chidakwa. Ngakhale kuti bambo a Ian ankapezera banja lawo zofunika pa moyo, Ian ankasowa chikondi cha bambo ake. Iye anati: “Bambo anga sindinkawakonda chifukwa anali chidakwa komanso ankachitira nkhanza mayi anga.” Ian atakula anayamba kukayikira ngatidi kuli Mulungu. Iye anati: “Ngati kulidi Mulungu, ‘n’chifukwa chiyani amalola kuti anthu azivutika?’”

N’chifukwa chiyani anthu amafunsa funso limeneli?

Ngakhale mutakhala kuti simukukumana ndi mavuto ambiri pa moyo wanu, zimakukhudzani mukaona anthu osalakwa akuvutika. Komabe, mofanana ndi Ian, zimakukhudzani kwambiri zikakhala kuti inuyo ndi amene mukuvutika, kapena ndi m’bale wanu amene akuvutika, akudwala kapenanso wamwalira.

Kodi anthu ena amayankha bwanji funsoli?

Anthu ena amakhulupirira kuti Mulungu amalola kuti zoipa zizitichitikira n’cholinga choti tikhale odzichepetsa komanso achikondi. Anthu ena amaganiza kuti anthu amavutika chifukwa cha machimo amene anachita pa nthawi imene anali ndi moyo asanabadwe moyo uno.

Kodi mayankho amenewa akusonyeza kuti anthu ambiri ali ndi maganizo otani?

Mulungu alibe nazo kanthu za mavuto a anthu ndipo zimenezi zimachititsa kuti zikhale zovuta kumukonda. Mulungu ndi wankhanza.

Kodi Baibulo limaphunzitsa chiyani pa nkhaniyi?

Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti Mulungu si amene amachititsa kuti anthufe tizivutika. Baibulo limati: “Munthu akakhala pa mayesero asamanene kuti: ‘Mulungu akundiyesa.’ Pakuti Mulungu sangayesedwe ndi zinthu zoipa ndipo iye sayesa munthu ndi zinthu zoipa.” (Yakobo 1:13) Choncho maganizo onena kuti Mulungu ndi amene amachititsa kuti tizivutika si ogwirizana ndi zimene Baibulo limafotokoza zokhudza Mulungu. N’chifukwa chiyani tikutero?

Khalidwe lalikulu la Mulungu ndi chikondi. (1 Yohane 4:8) Pofuna kutsindika mfundo imeneyi Baibulo limamufotokoza Mulungu monga mayi woyamwitsa. Mulungu anafunsa kuti: “Kodi mayi angaiwale mwana wake woyamwa, osamvera chisoni mwana wochokera m’mimba mwake? Ngakhale amayi amenewa akhoza kuiwala, koma ine sindidzakuiwala.” (Yesaya 49:15) Kodi mukuganiza kuti pali mayi wachikondi amene angavulaze dala mwana wake? N’zodziwikiratu kuti palibe. Mayi aliyense wachikondi amayesetsa kuthandiza mwana wake kuti asavutike. N’chimodzimodzinso ndi Mulungu. Iye sachititsa kuti anthu osalakwa azivutika.—Genesis 18:25.

Koma ngakhale kuti Mulungu sachititsa kuti anthu azivutika, anthu osalakwa amavutikabe. Komabe mwina mungadzifunse kuti, ‘Ngati Mulungu amatikonda ndipo ali ndi mphamvu zothetsera mavuto, n’chifukwa chiyani sakuchotsa zinthu zimene zimayambitsa mavuto?’

Pali zifukwa zomveka zimene zapangitsa Mulungu kulola kuti tizivutika. Taganizirani chifukwa chimodzi chimene iye walolera kuti anthu azivutika. Nthawi zambiri anthu ndi amene amachititsa kuti anthu ena azivutika. Olamulira ambiri ankhanza safuna kusintha zochita zawo zoipa. Choncho kuti Mulungu athetse mavuto ena amene ali padzikoli, ayenera kuwononga anthu oipawa.

Pofotokoza chifukwa chimene Mulungu sanawonongerebe anthu ochita zoipa, mtumwi Petulo analemba kuti: “Yehova sakuchedwa kukwaniritsa lonjezo lake, ngati mmene anthu ena amaonera kuti akuchedwa, koma akuleza nanu mtima, pakuti safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe, koma amafuna kuti anthu onse alape.” (2 Petulo 3:9) Kuleza mtima kumene Yehova Mulungu amasonyeza, ndi umboni wakuti iye ndi wachikondi komanso wachifundo.

Komabe posachedwapa Yehova Mulungu adzawononga oipa. Iye ‘adzabwezera masautso kwa amene amasautsa’ anthu osalakwa. Anthu amene amachititsa kuti anzawo azivutika, Mulungu “adzawaweruza kuti alandire chilango cha chiwonongeko chamuyaya.”—2 Atesalonika 1:6-9.

Ian, yemwe tinamutchula poyamba uja, anapeza mayankho ogwira mtima a mafunso ake okhudza chifukwa chake anthu amavutika. Zimene anaphunzirazi, zinamuthandiza kuti asinthe zimene ankakhulupirira. Mungawerenge nkhani yake patsamba 13.

Kuti mudziwe zifukwa zimene Mulungu walolera kuti anthu azivutika komanso zimene adzachite pothetsa mavuto, werengani mutu 11 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Mungathenso kukopera bukuli pa Webusaiti yathu iyi: www.jw.org.

Zimene Yesu Ananena Zokhudza Mavuto Amene Ali Padzikoli

Yesu sanaimbe Mulungu mlandu chifukwa cha mavuto amene analipo pa nthawi yake. M’malomwake iye anachita zotsatirazi:

Anasonyeza kuti Mulungu salanga anthu osalakwa pochititsa kuti azivutika. Yesu anachiritsa odwala, olumala komanso akhungu. (Mateyu 15:30) Zozizwitsa zimene anachita zimatiphunzitsa mfundo ziwiri zofunika izi: Choyamba, Yesu anagwiritsa ntchito mphamvu za Mulungu pochepetsa mavuto a anthu osati kuwayambitsa. Chachiwiri, Yesu ankachiritsa anthu chifukwa choti ankawachitira chifundo. Mwachitsanzo, ataona anthu akuvutika, “anagwidwa ndi chifundo.” (Mateyu 20:29-34) Yesu anasonyeza bwino mmene Atate wake amamvera anthu akamavutika. Choncho zimene Yesu anachita komanso kulankhula zimatiphunzitsa kuti Mulungu amamva chisoni akaona anthu akuvutika ndipo ndi wofunitsitsa kudzathetsa mavuto onse.—Yohane 14:7, 9.

Anasonyeza kuti Satana Mdyerekezi ndi amene amayambitsa mavuto ambiri amene anthu amakumana nawo. Ponena za Satana, Yesu anati: “Iyeyo ndi wopha anthu chiyambire kupanduka kwake.” (Yohane 8:44) Yesu ananenanso kuti Satana Mdyerekezi ndi “wolamulira wa dzikoli” komanso ndi “amene akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.”—Yohane 12:31; Chivumbulutso 12:9.

Anatipatsa chiyembekezo choti posachedwapa mavuto onse adzatha. Yesu anaphunzitsa otsatira ake kupemphera kuti: “Atate wathu wakumwamba, . . . Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.” (Mateyu 6:9, 10) Ufumu wa Mulungu ukadzayamba kulamulira padziko lapansili, mavuto onse adzatha.

M’masomphenya amene Yesu anaonetsa mtumwi Yohane, iye anasonyeza mmene anthu adzasangalalire Ufumu wa Mulungu ukadzayamba kulamulira padziko lapansi. Pa nthawi imeneyo, Mulungu “adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”—Chivumbulutso 1:1; 21:3, 4.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena