Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w14 6/15 tsamba 8-11
  • Kodi Tingathandize Bwanji Akhristu Amene Banja Lawo Latha?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Tingathandize Bwanji Akhristu Amene Banja Lawo Latha?
  • Nsanja ya Olonda—2014
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • AMAVUTIKA MAGANIZO KWAMBIRI
  • AMAVUTIKA KUTI AYAMBE KUONA ZINTHU MOYENERA
  • AMASOWA WOCHEZA NAYE NDIPO AMADZIKAYIKIRA
  • Zimene Mungachite Ngati Banja Lanu Latha
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Mmene Kutha Kwa Banja Kumakhudzira Ana
    Mfundo Zothandiza Mabanja
  • Chisudzulo—Zotulukapo Zake Zoŵaŵa
    Galamukani!—1992
  • Zinthu Zinayi Zimene Muyenera Kudziwa Musanathetse Banja
    Galamukani!—2010
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2014
w14 6/15 tsamba 8-11

Kodi Tingathandize Bwanji Akhristu Amene Banja Lawo Latha?

Mlongo akulimbikitsa mnzake amene banja lake latha

Masiku ano mabanja ambiri akutha. Mwinanso inu mukudziwa anthu ena amene mabanja awo anatha. Kafukufuku wina wa ku Poland anasonyeza kuti anthu ambiri azaka 30 amene akhala pa banja zaka zitatu kapena 6 amathetsa mabanja awo. Koma si anthu azaka 30 okha amene amachita zimenezi.

Bungwe lina la ku Spain loona za mabanja linati: “Kafukufuku wasonyeza kuti hafu ya anthu [ku Ulaya] amene akwatirana adzathetsa mabanja awo.” Ndi mmene zililinso kumayiko ena olemera.

AMAVUTIKA MAGANIZO KWAMBIRI

Mlangizi wina wa anthu am’banja ku Ulaya anati: “Banja likafika pakutha zimakhala kuti zinthu zinasokonekera kale. Zinthu ngati zimenezi zikachitika zimakhala zopweteka kwambiri.” Ananenanso kuti: “Munthu amavutika maganizo, amakwiya, amadziimba mlandu, amakhumudwa, amataya mtima ndiponso amachita manyazi.” Ena mpaka amafika pofuna kudzipha. Anapitiriza kuti: “Ndiyeno likatha kubwalo la milandu, mavuto enanso amayamba. Munthu amayamba kuona kuti ali yekhayekha ndipo amadzifunsa kuti: ‘Kodi panopa anthu akundiona bwanji? Kodi ndiye ndizichita chiyani pa moyo wanga?’”

Pokumbukira zimene zinachitika zaka zingapo zapitazo, mlongo wina dzina lake Ewa anati: “Banja lathu litatha, ndinkachita manyazi kwambiri chifukwa aneba anga ndi anzanga akuntchito ankauzana kuti, ‘Awotu banja lawo lija linatha.’ Ndinkakwiya kwambiri ndi zimene zinkandichitikira. Mwamuna wanga anandisiya ndi ana awiri moti ndinkachita zinthu ngati mayi komanso bambo.”a M’bale wina dzina lake Adam, anali mkulu wodalirika kwa zaka 12. Koma banjalo litatha, iye anati: “Munthune ndimamva ngati ndanyozeka kwabasi ndipo nthawi zina ndimakwiya nazo moti ndimangofuna nditamakhala pandekha basi.”

AMAVUTIKA KUTI AYAMBE KUONA ZINTHU MOYENERA

Banja likatha anthu ena amavutika kwambiri kuti ayambenso kuona zinthu moyenera ngakhale patapita zaka zambiri. Mwina angamaganize kuti anthu ena alibe nawonso ntchito. Katswiri wina woona za kutha kwa mabanja ananena kuti: “Anthuwo amayenera kusintha mmene amachitira zinthu n’kuphunzira kulimbana ndi mavuto paokha.”

Stanisław anati: “Banja lathu litatha, mkazi wanga wakale ankandikaniza kuona tiana tanga tiwiri. Izi zinandichititsa kuganiza kuti palibe amene amandikonda komanso kuti ngakhale Yehova wandisiya. Ndinafika poona kuti bola kungofa. Koma kenako ndinazindikira kuti ndinali kuona zinthu molakwika.” Mlongo wina dzina lake Wanda yemwe banja lake linatha n’kusiyidwa ndi ana 4 ankadera nkhawa kwambiri za tsogolo lake ndi anawo. Iye anati: “Ndinkaona kuti pakapita nthawi anzathu, ngakhale abale ndi alongo, adzasiya kutiganizira ndiponso kutithandiza. Koma panopa m’pamene ndikuzindikira kuti abale ankandithandiza kwambiri pamene ndinkayesetsa kulera ana anga ndi kuwaphunzitsa kuti azitumikira Yehova.”

Ndemanga za anthuwa zikusonyeza kuti anthu ena amavutika kwambiri maganizo mabanja awo akatha. Mwina angayambe kuganiza kuti ndi opanda pake ndiponso kuti palibe amene angawakonde. Komanso akhoza kumangotola ena zifukwa. Ndiyeno angayambe kuganiza kuti mumpingo mulibe anthu achikondi. Koma zimene zinachitikira Stanisław ndi Wanda zikusonyeza kuti anthu amene mabanja awo anatha amazindikira patapita nthawi kuti abale ndi alongo awo amawakonda. Akhristu amathandiza m’njira zikuluzikulu ngakhale kuti mwina anthu amene akuthandizidwawo, poyamba sangazindikire.

AMASOWA WOCHEZA NAYE NDIPO AMADZIKAYIKIRA

Koma chimene tiyenera kudziwa n’chakuti ngakhale titayesetsa bwanji kuwathandiza, anthu amene banja lawo latha nthawi zina amavutikabe chifukwa chosowa mnzawo. Nthawi zambiri, alongo osiyidwa amaganiza kuti palibenso amene angawakonde. Mlongo wina dzina lake Alicja anati: “Panopa padutsa zaka 8 kuchokera pamene banja lathu linatha. Koma nthawi zina ndimadzikayikirabe. Maganizo amenewa akandibwerera ndimadzimvera chisoni n’kupita kwandekha kukalira.”

Zimene tanenazi zimachitikira anthu ambiri amene banja lawo latha. Koma Baibulo limanena kuti si bwino kudzipatula. Munthu akayamba kudzipatula akhoza kuyamba kuchita “zosemphana ndi nzeru zonse zopindulitsa.” (Miy. 18:1) Koma munthu amene akusowa mnzakeyo ayenera kusamala kuti asakhale ndi chizolowezi chofunsira nzeru kapena kudandaulira munthu amene si mwamuna kapena mkazi mnzake. Tikutero chifukwa chakuti akhoza kuyamba kukopana.

Akhristu anzathu amene banja lawo linatha akhoza kuvutika kwambiri chifukwa chosowa wocheza nawo, kudera nkhawa za tsogolo lawo komanso kumva kuti palibe amene angawakonde. Zimene anthuwo amaganiza si zachilendo koma n’zovuta kupirira. Choncho tizitsanzira Yehova powamvetsa komanso kupitiriza kuwathandiza. (Sal. 55:22; 1 Pet. 5:6, 7) Dziwani kuti iwo adzayamikira kwambiri chilichonse chimene tingachite powathandiza. Tikachita zimenezi tidzakhala anzawo enieni.—Miy. 17:17; 18:24.

a Mayina ena asinthidwa.

Kodi Tiziona Bwanji Nkhani Yothetsa Banja?

Atumiki a Yehova sathetsa banja mwachisawawa. Izi zili choncho chifukwa timatsatira zimene Malemba amanena. Mwachitsanzo, pa Malaki 2:16 Mulungu ananena kuti: “Ndimadana ndi zakuti anthu azithetsa mabanja.” Malinga ndi Malemba, munthu akhoza kuthetsa banja pokhapokha ngati mwamuna kapena mkazi wake wachita dama. Choncho kungakhale kulakwa kwambiri kukonza zothetsa banja popanda chifukwa cha m’Malemba pongofuna kuti mukwatirane ndi munthu wina.—Gen. 2:22-24; Deut. 5:21; Mat. 19:4-6, 9.

Koma ngati banja latha, mwina chifukwa chakuti wina sanakhulupirike, abale ndi alongo amathandiza kwambiri. Iwo amatsanzira Yehova pochita zonse zimene angathe kuti athandize anthu olungama amene ali ndi “mtima wosweka.”—Sal. 34:15, 18; Yes. 41:10.

KODI TINGAWATHANDIZE BWANJI?

Mwina inuyo mungafune kuthandiza anthu amene akuvutika chifukwa choti banja lawo latha. Koma kodi mungawathandize bwanji? Onani mfundo za m’Baibulo zimene zili m’munsimu komanso zimene Akhristu ena achita pothandiza anthu oterewa.

Khalani ozindikira. (Miy. 16:20, 23)

Banja likatha, anthu ena safuna kufotokoza zonse zimene zinachititsa kuti lithe. Komanso nthawi zambiri kulankhulalankhula za mavutowo sikuthandiza kwenikweni ndiponso sikuthetsa nkhawa. (Miy. 12:25; Aroma 12:15) M’bale wina dzina lake Michał anathandiza kwambiri Adam amene tamutchula m’nkhani ija. Michał ananena kuti n’zotheka kukhala wozindikira komanso kumvetsera mwachifundo mavuto a anthu oterewa popanda kumva zonse zimene zinachitika. Iye anati: “Ndinathandiza Adam kudziwa kuti nthawi zina akapanikizika ndi nkhawa akhoza kulankhula zinthu zina zimene pambuyo pake angaone kuti sanachite bwino kuzinena.” Choncho Michał anamuthandiza kudziwa kuti cholinga chake si chofuna kumva zonse zimene zinachitika. Komabe ankamumvetsera bwinobwino akamalankhula. Nthawi zina mawu ochepa amene tinganene misonkhano isanayambe kapena itatha angakhale othandiza kwambiri. Mwina tingawafunse kuti: “Kaya pano zili bwanji? Muyenera kuti mukuvutikabe. Pakakhala zina muzindiuza, ndizikuthandizani.”

Muzisonyeza kuti mumawaganizira. (Afil. 2:4)

Mirosław anati: “Ine ndi mkazi wanga tinakonza nthawi yoti tizithandiza mlongo wina amene banja lake linatha. Mwachitsanzo, tinakakonza loko wa chitseko chake. Tinamutenganso kuti akaonane ndi dokotala.” Zimenezi zingaoneke ngati zazing’ono koma zinamuthandiza kwambiri. Mlongoyo anayambanso kuchita zinthu bwinobwino ngati kale. Chosangalatsa kwambiri n’chakuti anadzayamba upainiya ndiponso mwana wake wazaka 11 anabatizidwa.

Banja likuthandiza mlongo amene banja lake latha

Muziwatsimikizira kuti Yehova akudziwa bwino mavuto awo.

Ngati munthuyo akudzikayikira mungamutsimikizire kuti Mulungu amaona mtumiki wake aliyense kukhala wofunika kwambiri. Ifetu ndife “ofunika kwambiri kuposa mpheta zochuluka.” Yehova amaona kuti aliyense wa ife ndi wapadera ndiponso wamtengo wapatali. (Mat. 10:29-31) Iye “amayesa mitima” choncho amamvetsa bwino zimene anthu omwe mabanja awo anatha akukumana nazo. Sadzasiya atumiki ake okhulupirika. (Miy. 17:3; Sal. 145:18; Aheb. 13:5) Muzisonyeza kuti mumakonda anthuwo. Muziwatsimikiziranso kuti Mulungu amayamikira kwambiri zimene iwo akuchita chifukwa chokonda choonadi ndiponso kufuna kumutumikira.—Afil. 2:29.

Alimbikitseni kusonkhana.

Anthu ena akapanikizika zimawavuta kuti apite ku misonkhano. Koma misonkhano imakonzedwa kuti itilimbikitse ndipo imatilimbikitsadi. (1 Akor. 14:26; Sal. 122:1) Choncho zimakhala bwino kwambiri ngati akulu akuyesetsa kulimbikitsa anthu oterewa. Wanda amene tamutchula uja anati: “Sitiiwala zimene akulu anachita potithandiza.”

Alimbikitseni kuti azipemphera, kuphunzira Baibulo paokha komanso kusinkhasinkha n’cholinga choti ubwenzi wawo ndi Mulungu ulimbe. (Yak. 4:8)

Yehova ndi Mulungu Wamphamvuyonse ndipo amakhala kumwamba koma amaganizira ‘munthu amene ali wosautsidwa, wosweka mtima ndiponso wonjenjemera ndi mawu ake.’ Anthu amene banja lawo latha tiyenera kuwatsimikizira mfundo imeneyi. Tiziwathandizanso kuona ubwino wolimbitsa ubwenzi wawo ndi Mulungu popemphera ndi kuphunzira Baibulo paokha.—Yes. 66:2.

Apempheni kuti muyende nawo mu utumiki kapena mukonzekere limodzi misonkhano.

Abale awiri akulalikira limodzi

Izi zingathandize munthuyo kuyamba kuchita zinthu bwinobwino pa moyo wake. Mlongo wina dzina lake Marta anathandiza mlongo amene anali wakhama kwambiri koma yemwe ankavutika maganizo banja lake litatha. Marta anati: “Ndimayenda naye limodzi mu utumiki ndipo timasangalala kwambiri tikakwaniritsa zolinga zathu. Nthawi zina timakonzekeranso limodzi misonkhano ndipo kenako timaphika kenakake kuti tidye.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena