Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w15 2/1 tsamba 16
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mulungu Adzakhazikitsa Boma Lolamulira Dziko Lonse Lapansi?
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Boma la Mulungu la Mtendere
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
    Nsanja ya Olonda—2014
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
w15 2/1 tsamba 16

KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO

Kodi zidzatheka kukhala ndi boma limodzi lolamulira dziko lonse?

Anthu a mitundu yonse, ogwirizana chifukwa akulamulidwa ndi boma limodzi

Kodi boma lolamulira dziko lonse lidzathandiza bwanji kuti anthu a mitundu yonse azigwirizana? Yesaya 32:1, 17; 54:13

Kodi mukuganiza kuti zinthu zingakhale bwanji patakhala boma limodzi lolamulira dziko lonse lapansi? Masiku ano anthu ambiri ali pa umphawi wadzaoneni, pomwe ena ndi olemera kwambiri. Koma patakhala boma limodzi lolamulira dziko lonse, lingamaonetsetse kuti anthu onse ali ndi zimene amafunikira. Kodi mukuganiza kuti anthu angathe kukhazikitsa boma loterolo?​—Werengani Yeremiya 10:23.

Kuyambira kale, maboma akhala akulephera kuthandiza nzika zawo, makamaka anthu osauka. Komanso maboma ena amapondereza anthu awo. (Mlaliki 4:1; 8:9) Koma Mulungu Wamphamvuyonse watilonjeza kuti adzakhazikitsa boma limene lidzalowe m’malo mwa maboma onse. Wolamulira wa boma, kapena kuti Ufumu umenewu, adzaonetsetsa kuti nzika zake zonse zili ndi zofunikira.​—Werengani Yesaya 11:4; Danieli 2:44.

Kodi Ufumu wa Mulungu udzachita zotani?

Yehova Mulungu wasankha Mfumu yoyenera kulamulira dziko lonse yemwe ndi Mwana wake, Yesu. (Luka 1:31-33) Yesu ali padziko lapansi, ankakonda kuthandiza anthu. Choncho akamadzalamulira dziko lonse adzathandizanso anthu a mitundu yonse.​—Werengani Salimo 72:8, 12-14.

Koma kodi anthu onse angafune kuti Yesu akhale Mfumu yawo? Ayi. Komabe, Yehova ndi woleza mtima. (2 Petulo 3:9) Iye akupereka kwa anthu oterewa mwayi woti aphunzire zokhudza Yesu n’cholinga choti avomereze kuti adzakhale Mfumu yawo. Posachedwapa, Yesu adzachotsa anthu oipa n’kubweretsa mtendere pa dziko lonse.​—Werengani Mika 4:3, 4.

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 8 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova

Likupezekanso pa webusaiti yathu ya www.jw.org/ny

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena