Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp19 No. 2 tsamba 3
  • Mukamaona Kuti Simungathenso Kupirira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mukamaona Kuti Simungathenso Kupirira
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2019
  • Nkhani Yofanana
  • Moyo Ukafika Povuta
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
  • Munthu Amene Mumamukonda Akamwalira
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2019
  • Pakachitika Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2019
  • Kodi Mungatani Mutakumana Ndi Vuto Lalikulu?
    Galamukani!—2014
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2019
wp19 No. 2 tsamba 3
Mtsikana akulira ali kuntchito

Mukamaona Kuti Simungathenso Kupirira

MOYO umakoma zinthu zonse zikamayenda bwino. Koma bwanji ngati titakumana ndi mavuto amene tikuona kuti sitingathe kuwapirira?

Mwachitsanzo, ku United States kutawomba mphepo yamkuntho, katundu wambiri wa Sallya anawonongeka. Iye anati: “Ndinasowa mtengo wogwira, moti ndinkaona kuti sindingathenso kupirira.”

Vuto lina lingakhale imfa ya munthu amene timam’konda. Janice yemwe amakhala ku Australia anati: “Ana anga aamuna awiri atamwalira, ndinamva ululu woopsa mumtima mwanga. Ndinapemphera kwa Mulungu kuti: ‘Chonde, sindithanso kupirira. Ndiloleni ndingofa chifukwa sindikufunanso kukhala ndi moyo.’”

Nayenso Daniel anasokonezeka maganizo atazindikira kuti mkazi wake wachita chigololo. Iye anati: “Mkazi wanga atavomera kuti anachitadi zimenezi, zinangokhala ngati ndabayidwa ndi mpeni mumtimamu. Kwa miyezi ingapo ndinkamvabe ululu umenewu.”

Nsanja ya Olonda ino ifotokoza zimene zingatithandize kupirira

  • Pakachitika ngozi zadzidzidzi

  • Munthu amene timamukonda akamwalira

  • Mwamuna kapena mkazi wathu akakhala wosakhulupirika

  • Ngati tikudwala kapena kudwazika matenda aakulu

  • Ngati tikuona kuti bola kungofa

Choyamba, tiyeni tione zimene zingatithandize pakachitika ngozi zadzidzidzi.

a Munkhanizi mayina ena asinthidwa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena