Achititseni Kudzimva Olandiridwa pa Chikumbutso
1 M’zaka zingapo zapitazo, munthu 1 yekha pa anthu 5 opezeka pa Chikumbutso ndiye anali wofalitsa wa mbiri yabwino. Mwachionekere ndimmenenso zingakhalire chaka chino. Ena angapezekepo atalimbikitsidwa ndi wachibale kapena bwenzi limene limakhala mumzinda wina, pamene ena angakhale ataitanidwa ndi ofalitsa akumaloko. Komabe ena amene amapezekapo, ngakhale kuti ali obatizidwa, salinso okangalika muutumiki. Mowona mtima timalandira onse amene amasonyeza ulemu ku lamulo la Yesu lakuti: “Chitani ichi chikhale chikumbukiro changa.”—1 Akor. 11:24; Aroma 15:7.
2 Akalinde oikidwa ayenera kukhala atcheru kulandira aliyense, makamaka watsopano, pamene afika pa Nyumba Yaufumu. Komabe, tonsefe tingakhale ndi phande m’kulondola njira ya kuchereza alendo pa Chikumbutso. (Aroma 12:13) Motani?
3 Madzulo amenewo ofalitsa ena adzakhala otanganitsidwa kwambiri kunyamula okondwerera m’zoyendera zawo. Ena angakhoze kufika msanga ndi kuchingamira alendo obwera okha kuti awalonjere. Mlendo ataloŵa m’holo, mpatseni moni mwaubwenzi ndithu, ndipo yambitsani kukambitsirana naye. Mfunseni ngati adziŵa aliyense mumpingomo. Ngati amatero, msamalireni kufikira munthuyo atafika. (Yerekezerani ndi Luka 10:35.) Ngati palibe munthu aliyense amene adziŵa, bwanji osampempha kukhala nanu mkati mwa msonkhanowo? Fotokozani mmene vinyo ndi mkate zidzagwiritsidwira ntchito paprogramuyo. Mwina angafunikire chithandizo chanu posanthula malemba oŵerengedwa ndi wokamba nkhani.
4 Pamapeto a phwando la Chikumbutso, muuzeni kuti mwakondwa ndi kubwera kwake. Mwina angakhale ndi mafunso pa ntchito yathu amene mungayankhe. Chikondwerero chanu mwa iye chingayambitse kukambitsirana nkhani zina za Baibulo, mwina pa Nyumba Yaufumu kapena kwina kulikonse. Maphunziro abwino koposa ayambitsidwa ndi abale atcheru amene agwiritsira ntchito njira yabwino imeneyi. Asanachoke pa Nyumba Yaufumu, mdziŵikitseni kwa ena, ndipo muitanireni mwaubwenzi kuti akabwerenso.
5 Nkosangalatsa chotani nanga kulandira abale ndi alongo athu okondedwa amene akhala akupezeka pamisonkhano modumphadumpha kapena amene akhala osakangalika muutumiki kwanthaŵi yakutiyakuti! Mmalo mowafunsa chifukwa chake samapezeka, tangosonyezani chimwemwe chanu pakupezekapo kwawo. Mwinamwake kanthu kena kamene adzamva m’nkhani ya Chikumbutso kadzawasonkhezera kupendanso unansi wawo wodzipatulira ndi Yehova. Kuwalandira kwanu kwaubwenzi ndi nkhaŵa yanu yeniyeni imene musonyeza zingakhudze mitima yawo. Adziŵitseni kuti mukuyembekezera mwachidwi kuwaonanso.—Aroma 1:11, 12.
6 M’mipingo yochuluka nkhani yapoyera yapadera ya mutu wakuti “Chipembedzo Chowona Chikwaniritsa Zofunika za Chitaganya cha Anthu” idzakambidwa pa April 10. Tsimikizirani kuti onse opezeka paphwando la Chikumbutso aitanidwa ndi kuti adzathandizidwa kudzapezekapo. Tikhulupirira kuti awo amene adzapezeka pamisonkhano yapadera imeneyi adzadzimva olandiridwa ndi kuona mzimu wabwino wa mayanjano pakati pa anthu a Yehova.—Sal. 133:1.