Misonkhano Yautumiki ya October
Mlungu Woyambira October 3
Mph. 10: Zilengezo za pamalopo ndi Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu. Kumbutsani onse kubwera ndi kope lawo la brosha la Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira pa Msonkhano Wautumiki wa mlungu wotsatira.
Mph. 17: “Tsopano Ndiyo Nthaŵi.” Mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo ndemanga za pamutu waung’ono wakuti “Londolani Zonulirapo Zauzimu” pamasamba 4 ndi 5 a Utumiki Wathu Waufumu wa November 1993.
Mph. 18: “Khalani Ofunitsitsa Kugaŵira Sabusikripishoni mu October.” Kambitsiranani ndi omvetsera. Khalani ndi zitsanzo ziŵiri zokonzedwa bwino zosonyeza mmene masabusikripishoni angagaŵiridwire. Ofalitsa ayenera kukhala ndi masilipi a sabusikripishoni pamene ali mu utumiki wakumunda.
Nyimbo Na. 212 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira October 10
Mph. 10: Zilengezo za pamalopo. Lipoti la maakaunti ndi ziyamikiro zilizonse za zopereka.
Mph. 20: “Makolo—Khalani Ochirikiza!” Nkhani yokambidwa ndi mkulu yozikidwa pa nkhani zitatu zoyambirira mu Galamukani! wa August 8, 1994. Gwiritsirani ntchito nkhanizo m’mikhalidwe ya kumaloko. Mwachidule funsani kholo limene lingakhale litalankhulapo ndi aphunzitsi kapena akuluakulu a sukulu. Gogomezerani mmene makolo angakhalire ochirikiza kwa ana awo.
Mph. 15: “Kugwiritsira Ntchito Brosha Latsopano Mogwira Mtima.” Kambitsiranani nkhaniyo ndi omvetsera. Sonyezani mbali zazikulu za broshalo, ndipo perekani malingaliro osonyeza mmene lingagwiritsidwire ntchito pothandiza ofedwa.
Nyimbo Na. 108 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira October 17
Mph. 10: Zilengezo za pamalopo. Mbiri Yateokratiki. Lengezani makonzedwe a utumiki wakumunda a Tsiku la Magazini lapadera pa October 29.
Mph. 15: Tisaleme Pakuchita Zabwino. Nkhani yokambidwa ndi mkulu. Kutopa kwauzimu kungachepetse chimwemwe ndi changu chathu mu utumiki wa Yehova. Kambitsiranani njira zina zopezeranso nyonga yathu yauzimu mwa kugwiritsira ntchito malingaliro operekedwa mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 1986, patsamba 19 (m’bokosi). Gogomezerani kuchirikiza ndi mtima wonse ntchito za mpingo.
Mph. 20: “Thandizani Mwachikondi Awo Amene Amasonyeza Chikondwerero.” Kambitsiranani ndi omvetsera. Konzani zitsanzo ziŵiri zogwiritsira ntchito maulaliki osonyezedwa. Fotokozani za kufunika kwa kusunga cholembedwa cha awo amene alonjeza kulembetsa patsiku lakutilakuti.
Nyimbo Na. 156 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira October 24
Mph. 12: Zilengezo za pamalopo. Fotokozani mfundo zili m’bokosi lakuti “Matrakiti Ogaŵiridwa—Kodi Ayenera Kuchitiridwa Lipoti?”
Mph. 15: Kodi Muli ndi Oda Yoikika? Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! ali zithandizo zazikulu pofalitsa uthenga wa Ufumu. Tiyenera kuwagaŵira pampata uliwonse. Utumiki Wathu Waufumu wa May 1984 unalangiza kuti wofalitsa aliyense akhale ndi “oda ya magazini yotsimikizirika . . . ya chiŵerengero choikika cha kope lililonse.” Ngati sititero tidzakhala tilibe makope atsopano ogaŵira ndipo tidzangodalira pa matrakiti kapena mabrosha. Ndi bwino kuti chiŵalo chilichonse cha banja chikhale ndi oda yoikika. Pangani maoda pa kaunta ya magazini. Tsimikizirani kuti mukutenga magaziniwo mlungu uliwonse. Tchulani mapindu amene amakhalapo chifukwa cha kukhala ndi oda yoikika.
Mph. 18: “Funafunani Ufumu wa Mulungu Choyamba—Mwa Kupereka Nsembe za Chitamando Nthaŵi Zonse.” Mafunso ndi mayankho. Tchulani zonulirapo zina zopindulitsa zimene tingakalimire mwaumwini. Kambitsiranani njira zimene tingakhozere kuthandiza nazo ena kuchita zambiri.
Nyimbo Na. 171 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira October 31
Mph. 12: Zilengezo za pamalopo. Ndi maholide amene adzakhalako m’December, limbikitsani onse kulingalira za kulembetsa kukhala apainiya othandiza. Perekani malingaliro onena za mmene tingapezere nthaŵi yokwanira yochitira zimenezo.
Mph. 15: Zosoŵa za pamalopo. Kapena mkulu akambe nkhani yozikidwa pa mutu wakuti “Kodi Mungasonyeze Kuleza Mtima?” ya mu Nsanja ya Olonda ya May 15, 1994, masamba 21-3.
Mph. 18: Gaŵirani New World Translation mu November. Popeza kuti anthu ambiri ali ndi Baibulo kale, tifunikira kusonyeza chifukwa chake New World Translation ili yoposa. Tembenukirani m’buku la “All Scripture Is Inspired of God and Beneficial” (pamasamba 327-8, ndime 1-6). Fotokozani chifukwa chake dzina la Yehova lagwiritsiridwa ntchito, ndipo perekani zitsanzo kusonyeza ubwino wa kugwiritsira ntchito chinenero chamakono. Sonyezani mbali zothandiza zimene zili kumapeto kwa Baibulolo, zonga “Bible Words Indexed,” zimene zingagwiritsiridwe ntchito kupezera mwamsanga malemba odziŵika. Mbali ya “Table of the Books of the Bible” imasonyeza amene analemba buku lililonse, kumene linalembedwera, ndi pamene linalembedwa, limodzinso ndi utali wa nthaŵi imene zolembedwazo zinachitikiramo. Tembenukirani m’buku la Kukambitsirana (patsamba 53, pamutu waung’ono wakuti “Ulosi wa Baibulo umalongosola tanthauzo la mikhalidwe ya dziko”), ndipo fotokozani mmene mungayambire makambitsirano a Malemba ozikidwa pa Yohane 17:3 ndi Salmo 37:10, 11, 29. Konzani kuti wofalitsa wokhoza asonyeze mmene New World Translation ndi buku la Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? zingagaŵiridwire m’gawo lakumaloko.
Nyimbo Na. 136 ndi pemphero lomaliza.