Matrakiti ogaŵiridwa—Kodi Ayenera kuchitiridwa Lipoti?
1 Matrakiti amagaŵiridwa kwaulere kwa anthu amene asonyeza chikondwerero. Zoona, kuti wofalitsa apeze matrakiti ameneŵa ku mpingo, amapereka ndalama. Komabe, kuteroko sikumatanthauza kuti tiyeneranso kupempha ndalama yogulira kwa okondwererawo. Malemba amatilimbikitsa kutumikira Yehova ndi chuma chathu. (2 Akor. 9:13) Kugaŵira matrakiti aulere kwa okondwerera kumasonyeza chikondi chathu pa Yehova ndi anthu anzathu.—Mat. 22:37-39.
2 Kodi kuli kofunika kupereka lipoti ku mpingo la chiŵerengero cha matrakiti amene tagaŵira muutumiki wakumunda? Buku la Uminisitala Wathu (tsa. 102, ndime 1 mpaka tsa. 104, ndime 1), limasonyeza bwino lomwe zimene ziyenera kulembedwa palipoti pa kamutu kakuti “Lipoti Lanu Lautumiki Wakumunda.” Ena apereka lipoti la matrakiti ogaŵiridwa monga mabrosha kapena magazini. Alembi a mipingo nawonso atumiza zimenezi ku Sosaite. Nthaŵi zina, ofalitsa ena apempha chopereka pogaŵira matrakiti aulere ameneŵa. Zimenezi sizolondola.
3 Tikugogomezera zolimba kuti pali mapindu ambiri ngati nthaŵi zonse timamatira ku malangizo a gulu koposa kutsatira maganizo ndi malingaliro athuathu ponena za mmene zinthu ziyenera kuchitidwira. (1 Akor. 4:6) Gwiritsirani ntchito matrakiti okongolawo mogwira mtima kuperekera umboni wabwino ndipo motero kuthandiza ena kuphunzira za Ufumu wa Mulungu. Iwo angasiidwe kwa anthu okondwerera amene akana chogaŵira cha nthaŵi zonse kapena amene sakhoza kupereka chopereka.