Mawu a Mulungu Ali ndi Mphamvu
1 Baibulo lasonkhezera kwambiri miyoyo ya anthu mamiliyoni ambiri. Zimene limanena zili zosonkhezera kwambiri kuposa chilichonse chimene munthu anganene. (Aheb. 4:12) Taonani zimene latichitira. Zoonadi, phindu lake nlosayerekezereka.
2 Mboni za Yehova zili ophunzira Baibulo ndi achirikizi ake oposa. Tiyenera kuona kuŵerenga Baibulo monga mbali yaikulu ya ndandanda yathu ya nthaŵi zonse yateokratiki, tikumakuika pamalo oyamba mmalo mwa wailesi yakanema ndi zosangulutsa zina zonse.
3 Kupangeni Kukhala Chizoloŵezi cha Nthaŵi Zonse: Anthu a Yehova afika pa kuzindikira chisonkhezero champhamvu chimene kuŵerenga Baibulo nthaŵi zonse kungakhale nacho. Kwa zaka zambiri chikwangwani chachikulu pa imodzi ya nyumba za fakitale yathu ku Brooklyn chakhala chikulimbikitsa odutsa m’njira ndi mawu akuti “Ŵerengani Mawu a Mulungu Baibulo Loyera Tsiku ndi Tsiku.” Ziŵalo zatsopano za banja la Beteli zimafunikira kuŵerenga Baibulo lonse m’chaka chawo choyamba cha utumiki wa pa Beteli.
4 Mosasamala kanthu za ndandanda yanu yopanikizika, kodi mukuyendera limodzi ndi kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu kosonyezedwa mu Ndandanda ya Sukulu Yautumiki Wateokratiki? Ngati mwapeza vuto kuchita zimenezi, bwanji osayesayesa kuwongolera m’November? Kuŵerenga Baibulo kwa mwezi wonse kuli pa Masalmo 95-109, kumene kudzafuna kuŵerenga pafupifupi masamba atatu kapena anayi pa mlungu. Ena asankha kuŵerenga pang’ono tsiku lililonse, mwinamwake mmamaŵa kapena asanakagone usiku. Mulimonse mmene mungachitire zimenezo, chinthu chofunika nchakuti mutute mapindu oyenera opezeka mwa kuŵerenga Mawu a Mulungu nthaŵi zonse.
5 Gaŵirani Baibulo m’November: Anthu ambiri adakali kulemekeza Baibulo ndipo amakonda kumvetsera pamene tiliŵerenga. M’November tidzakhala tikugaŵira New World Translation ndi buku lakuti Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? Zimenezi zikupereka mpata wabwino kwambiri wosonyezera oona mtima phindu la Mawu a Mulungu. Khalani wachisangalalo pochita zimenezo.
6 Konzani ndemanga zolingaliridwa bwino zofotokoza mbali zapadera za New World Translation zimene zidzadzutsa chikondwerero cha anthu kuti aiwombole. Sonyezani phindu lake lothandiza. Mungasonyeze nkhani imodzi m’chigawo cha “Bible Topics for Discussion” ndi kuigwirizanitsa ndi buku la Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? Kapena mungasonyeze phindu la mpambo wamasamba 92 wa mawu a m’Baibulo mwa kusonyeza mmene umathandizira woŵerenga kupeza malemba ozoloŵereka. Ofalitsa ena angafune kusonyeza “Appendix” kapena “Table of the Books of the Bible” mwa kusonyeza phindu lake m’phunziro la Baibulo.
7 Musaiŵale kutchula kuti New World Translation ili m’Chingelezi chamakono, motero ili yosavuta kumva. Malemba ake ena amene ali osangalatsa kuwayerekezera ndi a King James Version ndiwo 1 Akorinto 10:25 ndi 16:22. New World Translation imagwiritsira ntchito dzina la Mulungu, Yehova, nthaŵi 7,210.
8 Inde, Baibulo lili Mawu a Mulungu. Ngati tiliŵerenga, kulikhulupirira, ndi kugwiritsira ntchito uphungu wake m’miyoyo yathu, tidzapeza mapindu ochuluka. Linalembedwera kutilangiza ndi kutipatsa chiyembekezo. (Aroma 15:4) Nkofunika kuti tizilifufuza masiku onse ndi kuti tikhale okonzekera kuligwiritsira ntchito kuphunzitsira ena.