Ndandanda ya Sukulu Yautumiki Wateokratiki ya 1995
MALANGIZO
Mu 1995 otsatiraŵa ndiwo amene adzakhala makonzedwe pochititsa Sukulu Yautumiki Wateokratiki.
MABUKU OPHUNZIRIDWA: Baibulo Lopatulika [bi053], Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona [uw-CN], Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu [om-CN], Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako [gt-CN], ndi Kukambitsirana za m’Malemba [rs-CN] adzakhala maziko a nkhani zogaŵiridwa.
Sukuluyo idzayamba ndi nyimbo, pemphero, ndi mawu amalonje, ndiyeno kupitiriza motere:
NKHANI NA. 1: Mphindi 15. Nkhani imeneyi iyenera kukambidwa ndi mkulu kapena mtumiki wotumikira, ndipo idzatengedwa m’buku la Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona kapena Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu. Pamene itengedwa m’buku la Uminisitala Wathu, nkhaniyi iyenera kukambidwa monga nkhani yachilangizo ya mphindi 15 popanda kupenda kwa pakamwa; pamene itengedwa m’buku la Ogwirizana m’Kulambiridwa, iyenera kukambidwa monga nkhani yachilangizo ya mphindi 10 mpaka 12 yotsatiridwa ndi kupenda kwa pakamwa kwa mphindi 3 mpaka 5, mwakugwiritsira ntchito mafunso osindikizidwa m’bukulo. Cholinga chake sichiyenera kukhala cha kungokamba nkhaniyo koma kusumika chisamaliro pa phindu lenileni la chidziŵitso chimene chikufotokozedwacho, ikumagogomezera mfundo zomwe zidzakhala zothandiza kwambiri mpingowo. Mutu wosonyezedwa uyenera kugwiritsiridwa ntchito. Onse akulimbikitsidwa kukonzekera bwino lomwe pasadakhale kotero kuti akapindule mokwanira ndi nkhani imeneyi.
Abale opatsidwa nkhani imeneyi ayenera kukhala osamala kusunga nthaŵi. Uphungu wamseri ungaperekedwe ngati uli wofunikira kapena ngati utapemphedwa pasadakhale ndi wokamba nkhaniyo.
MFUNDO ZAZIKULU ZOCHOKERA M’KUŴERENGA BAIBULO: Mphindi 6. Mbaliyi iyenera kusamaliridwa ndi woyang’anira sukulu kapena mkulu wina kapena mtumiki wotumikira amene akagwiritsira ntchito nkhaniyo mogwira mtima kuzosoŵa zapamalopo. Siyenera kukhala chabe kufotokozedwa kwachidule kwa mbali yoŵerenga yogaŵiridwayo. Fotokozani mawu oyamba a machaputala onse ogaŵiridwa kwa timphindi 30 mpaka 60. Cholinga chachikulu ndicho kuthandiza omvetsera kuzindikira chifukwa chake ndi mmene chidziŵitsocho chiliri chaphindu kwa ife. Ndiyeno woyang’anira sukulu adzapempha ophunzira kumwazikana kupita kumakalasi awo osiyanasiyana.
NKHANI NA. 2: Mphindi 5. Uku nkuŵerengedwa kwa Baibulo kwa mbali yogaŵiridwa kochitidwa ndi mbale. Nkhaniyi idzakambidwa m’sukulu yaikulu limodzinso ndi m’timagulu tinato. Kaŵirikaŵiri mbali zoŵerenga zimakhala zazifupi mokwanira kulola wophunzira kulongosola mwachidule chidziŵitsocho m’ndemanga zotsegulira ndi zomalizira. Mbiri yakale, tanthauzo la ulosi kapena la chiphunzitso, ndi mmene malamulo a mkhalidwe angagwiritsiridwire ntchito zingaphatikizidwe. Mavesi onse ogaŵiridwa ayenera kuŵerengedwadi mosaima. Ndithudi, pamene mavesi oŵerengedwawo sali ondondozana, wophunzira angatchule vesi lopitirizira kuŵerengako.
NKHANI NA. 3: Mphindi 5. Nkhaniyi idzagaŵiridwa kwa alongo. Mitu ya nkhani imeneyi idzatengedwa m’buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Wophunzira wogaŵiridwa nkhaniyi ayenera kukhala wodziŵa kuŵerenga. Pokamba nkhaniyi, wophunzira angakhale pansi kapena kuimirira. Wothandiza mmodzi adzasankhidwa ndi woyang’anira sukulu, komabe othandiza owonjezereka angathe kugwiritsiridwa ntchito. Alongo ogaŵiridwa nkhaniyi angafunikire kusintha mutu ndi nkhaniyo kuti iyenerane ndi mpangidwe woyenerera, makamaka wokhudza utumiki wakumunda kapena umboni wamwamwaŵi. Nkhaniyo ndiyo iyenera kupatsidwa chisamaliro chachikulu kuposa mpangidwewo.
NKHANI NA. 4: Mphindi 5. Yogaŵiridwa kwa mbale kapena mlongo. Nkhaniyi idzatengedwa m’buku la Kukambitsirana za m’Malemba. Pamene igaŵiridwa kwa mbale, iyenera kukhala nkhani yokambidwira omvetsera onse. Kaŵirikaŵiri kudzakhala bwino kuti mbaleyo akonzekere nkhani yake akumalingalira omvetsera ake m’Nyumba Yaufumu kotero kuti idzakhaledi yopatsa chidziŵitso ndi yopindulitsa kwa amene adzamvetsera. Pamene igaŵiridwa kwa mlongo, nkhaniyo iyenera kuperekedwa monga momwe kwafotokozedwera ponena za Nkhani Na. 3.
UPHUNGU NDI NDEMANGA: Pambuyo pa nkhani ya wophunzira aliyense, woyang’anira sukulu adzapereka uphungu wachindunji, osati kwenikweni motsatira mfundo za uphungu wopita patsogolo zondandalikidwa pasilipi ya Uphungu wa Kulankhula. M’malomwake, iye ayenera kusumika chisamaliro m’mbali zomwe wophunzirayo afunikira kuwongolera. Ngati wophunzira wolankhulayo amapeza “B” yekha ndipo palibe mkhalidwe wa kulankhula wolembedwa kuti “W” kapena “L,” pamenepo phunguyo ayenera kukweteza pabokosilo, pamene “B,” “W,” kapena “L” mwachibadwa akaonekera, mkhalidwe wa kulankhula umene wophunzirayo ayenera kugwirirapo ntchito m’nthaŵi yotsatira. Iye adzadziŵitsa wophunzirayo ponena za zimenezi tsiku lomwelo limodzinso ndi kusonyeza mfundo ya uphungu yotsatira pasilipi ya wophunzira ya Gawo la Sukulu Yautumiki Wateokratiki (S-89). Okamba nkhani ayenera kukhala kutsogolo. Zimenezi zidzasungitsa nthaŵi ndi kukhozetsa woyang’anira sukulu kupereka uphungu wake mwachindunji kwa wophunzira aliyense. Ngati nthaŵi ilola pambuyo pa kupereka uphungu wa pakamwa, ndemanga zingaperekedwe ndi phunguyo ponena za chidziŵitso ndi nsonga zopindulitsa zomwe sizinatchulidwe ndi ophunzirawo. Woyang’anira sukulu adzafunikira kukhala wosamala kuti sakugwiritsira ntchito zoposa mphindi ziŵiri kupereka uphungu ndi ndemanga zina zachidule pambuyo pankhani ya wophunzira aliyense. Ngati kanthu kena kofunika mumfundo zazikulu za Baibulo kasiyidwa, uphungu wamseri ungaperekedwe.
KUKONZEKERA NKHANI: Asanakonzekere nkhani yogaŵiridwa, wophunzira ayenera kuŵerenga mosamalitsa mfundo za mu Bukhu Lolangiza la Sukulu zokhudza mkhalidwe wa kulankhula umene adzagwirirapo ntchito. Ophunzira opatsidwa nkhani yachiŵiri angasankhe mutu wogwirizana ndi chigawo cha m’Baibulo chimene chiti chiŵerengedwe. Nkhani zinazo zidzakambidwa mogwirizana ndi mutu wosonyezedwa pandandanda yosindikizidwa.
KUSUNGA NTHAŴI: Palibe nkhani imene iyenera kudya nthaŵi, ngakhalenso uphungu ndi ndemanga za phungu siziyenera kutero. Nkhani Na. 2 mpaka 4 ziyenera kuimitsidwa mwaluso pamene nthaŵi ikwana. Wopatsidwa thayo la kupereka chizindikiro cha kuima ayenera kutero nthaŵi yomweyo. Ngati abale opereka Nkhani Na. 1 ndi mfundo zazikulu za Baibulo adya nthaŵi, ayenera kupatsidwa uphungu wamseri. Onse afunikira kusamala kwambiri nthaŵi yawo. Programu yonse: njamphindi 45, kupatulapo nyimbo ndi pemphero.
KUPENDA KOLEMBA: Panthaŵi ndi nthaŵi padzakhala kupenda kolemba. Pokonzekera, pendani mfundo zogaŵiridwa ndi kutsiriza ndandanda ya kuŵerenga Baibulo. Baibulo lokha lingagwiritsidwe ntchito mkati mwa kupenda kumeneku kwa mphindi 25. Nthaŵi yotsalayo idzagwiritsiridwa ntchito kukambitsirana mafunso ndi mayankho. Wophunzira aliyense adzachonga pepala lake. Woyang’anira sukulu adzakambitsirana mayankho ndi omvetsera ndi kupereka chisamaliro pamafunso ovuta kwambiri, akumathandiza onse kumvetsetsa bwino mayankhowo. Ngati, pachifukwa chinachake, mikhalidwe ya pamalopo ikupanga kukhala koyenera, kupenda kolemba kungachitidwe mlungu wotsatira m’malo mwa umene wasonyezedwa pandandanda.
MIPINGO YAIKULU: Mipingo yokhala ndi ophunzira olembetsa m’sukulu 50 kapena kuposa pamenepo ingafune kulinganiza magulu ena owonjezereka a ophunzira kukamba nkhani zondandalitsidwazo pamaso pa alangizi ena. Ndithudi, anthu osabatizidwa amene akukhala ndi moyo mogwirizana ndi malamulo a mkhalidwe Achikristu angalembetsenso m’sukulu ndi kupatsidwa magawo a nkhanizi.
OSAPEZEKAPO: Onse mumpingo akhoza kusonyeza chiyamikiro kaamba ka sukulu imeneyi mwa kuyesayesa kupezekapo paprogramu iliyonse ya mlungu ndi mlungu, mwa kukonzekera magawo awo bwino lomwe, ndiponso mwa kutengamo mbali m’mbali ya mafunso. Tikhulupirira kuti ophunzira onse adzaona magawo awo mwamphamvu. Ngati wophunzira sanapezekepo panthaŵi yomwe waikidwa, wina wodzipereka angathe kutenga gawolo, akumapanga kuyesayesa kulikonse kothekera komwe akulingalira kukhala koyenera m’nthaŵi ya kudziwitsidwa yochepayo. Kapena woyang’anira sukulu angathe kukamba nkhaniyo limodzi ndi kutengamo mbali koyenera kwa omvetsera.
NDANDANDA
Jan. 2 Kuŵerenga Baibulo: Salmo 119:113-176
Na. 1: Kudziŵikitsa Khamu Lalikulu (uw-CN mas. 103-4 ndime 1-4)
Na. 2: Salmo 119:161-176
Na. 3: Phunziro m’Chifundo (gt-CN mutu 40)
Na. 4: Mankhwala: Pamene Amaletsedwa kwa Akristu (rs-CN mas. 248-9)
Jan. 9 Kuŵerenga Baibulo: Masalmo 120 mpaka 130
Na. 1: Mikhalidwe Imene Nkhosa Zina Ziyenera Kusonyeza (uw-CN tsa. 105 ndime 5)
Na. 2: Salmo 122:1–123:4
Na. 3: Yesu Ali Phata la Mkangano (gt-CN mutu 41)
Na. 4: Chifukwa Chake Akristu Amapeŵa Chamba (rs-CN mas. 250-1, kamutu koyamba)
Jan. 16 Kuŵerenga Baibulo: Masalmo 131 mpaka 136
Na. 1: Chifukwa Chake Khamu Lalikulu Lidzapulumuka Chisautso Chachikulu (uw-CN mas. 106-9 ndime 6-13)
Na. 2: Salmo 132:1-18
Na. 3: Yesu Adzudzula Afarisi (gt-CN mutu 42)
Na. 4: Kodi Nchifukwa Ninji Akristu Amapeŵa Fodya? (rs-CN mas. 251-3 ndime 1)
Jan. 23 Kuŵerenga Baibulo: Masalmo 137 mpaka 140
Na. 1: Chifukwa Chake Pali Oloŵa Ufumu Oŵerengeka Chabe Padziko Lapansi Lerolino (uw-CN mas. 110-12 ndime 1-7)
Na. 2: Salmo 137:1–138:8
Na. 3: Mafanizo Asanu Ali m’Bwato (gt-CN mutu 43 ndime 1-8)
Na. 4: Mitundu Sidzasokoneza Chifuno cha Mulungu Ponena za Dziko Lapansi (rs-CN mas. 131-2)
Jan. 30 Kuŵerenga Baibulo: Masalmo 141 mpaka 145
Na. 1: Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu (om-CN tsa. 5 ndime 1 mpaka tsa. 8 ndime 1)
Na. 2: Salmo 144:1-15
Na. 3: Mmene Ophunzira Akupindulira ndi Ziphunzitso za Yesu (gt-CN mutu 43 ndime 9-19)
Na. 4: Kodi Yehova Adzawononga Dziko Lapansi ndi Moto? (rs-CN mas. 132-3)
Feb. 6 Kuŵerenga Baibulo: Masalmo 146 mpaka 150
Na. 1: Lingaliro Loyenera Kulinga ku Uminisitala (om-CN tsa. 8 ndime 2 mpaka tsa. 12)
Na. 2: Salmo 148:1-14
Na. 3: Yesu Adalitsa Ophunzira Ake ndi Malangizo Owonjezereka (gt-CN mutu 43 ndime 20-31)
Na. 4: Ziŵalo za Yerusalemu Watsopano Sizidzabwerera Padziko Lapansi Pambuyo pa Kuwonongedwa kwa Oipa (rs-CN tsa. 134)
Feb. 13 Kuŵerenga Baibulo: Miyambo 1 ndi 2
Na. 1: Kupindula mwa Kugonjera Kwateokratiki (om-CN mutu 2)
Na. 2: Miyambo 2:1-19
Na. 3: Yesu Atontholetsa Namondwe Wochititsa Mantha (gt-CN mutu 44)
Na. 4: Kodi Chifuno Choyambirira cha Mulungu Kaamba ka Dziko Lapansi Chinasintha? (rs-CN tsa. 135)
Feb. 20 Kuŵerenga Baibulo: Miyambo 3 ndi 4
Na. 1: Kuzindikira Ntchito ya Kristu m’Kakonzedwe ka Mulungu (om-CN mutu 3)
Na. 2: Miyambo 3:1-18
Na. 3: Munthu Wogwidwa ndi Ziŵanda Akhala Wophunzira (gt-CN mutu 45)
Na. 4: Kodi Tingalimbikitse Motani Odwala? (rs-CN tsa. 79)
Feb. 27 Kuŵerenga Baibulo: Miyambo 5 ndi 6
Na. 1: Kodi Amadziŵa Motani Kuti Ali Ana Auzimu? (uw-CN mas. 112-16 ndime 8-14)
Na. 2: Miyambo 6:1-19
Na. 3: Anakhudza Chovala Chake (gt-CN mutu 46)
Na. 4: Mmene Tingalimbikitsire Oferedwa (rs-CN tsa. 80)
Mar. 6 Kuŵerenga Baibulo: Miyambo 7 ndi 8
Na. 1: Kudziŵikitsa Gulu Looneka la Yehova (uw-CN mas. 117-20 ndime 1-7)
Na. 2: Miyambo 8:22-36
Na. 3: Misozi Isanduka Chikondwerero Chachikulu (gt-CN mutu 47)
Na. 4: Chilimbikitso kwa Amene Akuzunzidwa Chifukwa cha Kuchita Chifuniro cha Mulungu (rs-CN mas. 80-1)
Mar. 13 Kuŵerenga Baibulo: Miyambo 9 ndi 10
Na. 1: Mbali ya m’Malemba ya Bungwe Lolamulira (uw-CN mas. 120-22 ndime 8-12)
Na. 2: Miyambo 10:16-32
Na. 3: Mosasamala Kanthu za Zozizwitsa Zake, Yesu Akanidwa (gt-CN mutu 48)
Na. 4: Kodi Mungalimbikitse Motani Otaya Mtima Chifukwa cha Chisalungamo? (rs-CN tsa. 81)
Mar. 20 Kuŵerenga Baibulo: Miyambo 11 ndi 12
Na. 1: Kupenda Chiyamikiro Chathu cha Gulu la Mulungu (uw-CN mas. 123-4 ndime 13, 14)
Na. 2: Miyambo 11:1-14
Na. 3: Ulendo Wachitatu Wokalalikira ku Galileya (gt-CN mutu 49)
Na. 4: Kodi Pali Chilimbikitso Chotani kwa Opanikizika ndi Mavuto Azachuma? (rs-CN mas. 81-2)
Mar. 27 Kuŵerenga Baibulo: Miyambo 13 ndi 14
Na. 1: Kodi Nkumvetsereranji Uphungu? (uw-CN mas. 125-7 ndime 1-4)
Na. 2: Miyambo 14:1-16
Na. 3: Kukonzekeretsa Ophunzira Ake Kuyang’anizana ndi Chitsutso (gt-CN mutu 50)
Na. 4: Chilimbikitso kwa Olefuka ndi Zophophonya (rs-CN tsa. 82)
Apr. 3 Kuŵerenga Baibulo: Miyambo 15 ndi 16
Na. 1: Tsatirani Chitsanzo cha Awo Amene Analabadira Uphungu (uw-CN mas. 127-8 ndime 5, 6)
Na. 2: Miyambo 15:1-16
Na. 3: Kupha Mwambanda pa Phwando la Tsiku Lakubadwa (gt-CN mutu 51)
Na. 4: Chisinthiko: Vuto la Sayansi (rs-CN mas. 99-100)
Apr. 10 Kuŵerenga Baibulo: Miyambo 17 ndi 18
Na. 1: Kulitsani Mikhalidwe Yamtengo Wapatali (uw-CN mas. 128-31 ndime 7-14)
Na. 2: Miyambo 18:1-15
Na. 3: Yesu Adyetsa Zikwi Zambiri Mozizwitsa (gt-CN mutu 52)
Na. 4: Chisinthiko ndi Cholembedwa cha Zokwiriridwa Zakale (rs-CN mas. 101-2)
Apr. 17 Kuŵerenga Baibulo: Miyambo 19 ndi 20
Na. 1: Chikondi Chimadziŵikitsa Akristu Oona (uw-CN mas. 132-3 ndime 1-5)
Na. 2: Miyambo 19:8-23
Na. 3: Pamene Yesu Akuyenda pa Madzi (gt-CN mutu 53)
Na. 4: Kugometsa Zitsutso Zofala za Achisinthiko (rs-CN mas. 104-5)
Apr. 24 Kupenda Kolemba. Malizani Salmo 119:113 mpaka Miyambo 20
May 1 Kuŵerenga Baibulo: Miyambo 21 ndi 22
Na. 1: Chochita Pamene Mavuto Abuka (uw-CN tsa. 134 ndime 6-9)
Na. 2: Miyambo 22:1-16
Na. 3: Mkate Wochokera Kumwamba—Mphatso Yochokera kwa Yani? (gt-CN mutu 54)
Na. 4: Kodi Nchifukwa Ninji Anthu Ambiri Alibe Chikhulupiriro? (rs-CN mas. 67-8)
May 8 Kuŵerenga Baibulo: Miyambo 23 ndi 24
Na. 1: Samalirani Mavuto Mwamalemba (uw-CN mas. 135-8 ndime 10-17)
Na. 2: Miyambo 24:1-16
Na. 3: Chifukwa Chake Ambiri Akuleka Kutsatira Yesu (gt-CN mutu 55)
Na. 4: Kodi Munthu Angapeze Motani Chikhulupiriro? (rs-CN mas. 68-9 ndime 1)
May 15 Kuŵerenga Baibulo: Miyambo 25 ndi 26
Na. 1: Gwiritsirani Ntchito Kudzipereka Kwaumulungu Panyumba (uw-CN mas. 139-41 ndime 1-5)
Na. 2: Miyambo 25:1-13
Na. 3: Kodi Chimaipitsa Munthu Nchiyani? (gt-CN mutu 56)
Na. 4. Chikhulupiriro m’Chiyembekezo cha Dongosolo Latsopano Lolungama Chimatsimikiziridwa ndi Ntchito (rs-CN mas. 69-70)
May 22 Kuŵerenga Baibulo: Miyambo 27 ndi 28
Na. 1: Mmene Mpingo Umalinganizidwira ndi Kulamuliridwira (om-CN tsa. 21 ndime 1 mpaka tsa. 24 ndime 3)
Na. 2: Miyambo 28:1-14
Na. 3: Yesu Achitira Chifundo Okanthidwa (gt-CN mutu 57)
Na. 4: Kodi Aneneri Onyenga Angadziŵike Motani? (rs-CN mas. 32-3 ndime 1)
May 29 Kuŵerenga Baibulo: Miyambo 29 mpaka 31
Na. 1: Mpingo Lerolino Umatsatira Chitsanzo cha Atumwi (om-CN tsa. 25 ndime 1 mpaka tsa. 27 ndime 3)
Na. 2: Miyambo 31:10-31
Na. 3: Yesu Awongolera Kusamvana (gt-CN mutu 58)
Na. 4: Aneneri Oona Nthaŵi Zina Sanamvetsetse Ndimotani Ndipo Ndiliti Pamene Zinthu Zonenedweratu Zikachitika (rs-CN tsa. 33, kamutu kachiŵiri mpaka tsa. 34 ndime 1)
June 5 Kuŵerenga Baibulo: Mlaliki 1 mpaka 3
Na. 1: Kodi Ndani Amayeneretsedwa Kuŵeta Gulu? (om-CN tsa. 28 mpaka tsa. 31 ndime 1)
Na. 2: Mlaliki 3:1-9, 18-22
Na. 3: Kodi Yesu Kwenikweni Ndani? (gt-CN mutu 59)
Na. 4: Mawu a Mneneri Woona Amachirikiza Kulambira Koona (rs-CN tsa. 34, kamutu koyamba)
June 12 Kuŵerenga Baibulo: Mlaliki 4 mpaka 6
Na. 1: Kwaniritsani Mbali Yanu m’Kakonzedwe ka Banja ka Mulungu (uw-CN mas. 142-4 ndime 6-13)
Na. 2: Mlaliki 5:1-8, 18-20
Na. 3: Kuoneratu Ulemerero wa Ufumu wa Kristu (gt-CN mutu 60)
Na. 4: Aneneri Oona Amadziŵikitsidwa ndi Zipatso Zotulutsidwa (rs-CN tsa. 35 mpaka tsa. 36 ndime 2)
June 19 Kuŵerenga Baibulo: Mlaliki 7 mpaka 9
Na. 1: Zifukwa Zamalemba Zimene Sitilili Pansi pa Chilamulo cha Mose (uw-CN mas. 146-8 ndime 1-6)
Na. 2: Mlaliki 7:1-12
Na. 3: Mphamvu ya Chikhulupiriro (gt-CN mutu 61)
Na. 4: Chifukwa Chimene Zolakwa za Mboni za Yehova Sizimazipangitsa Kusayenerera Kukhala Aneneri Oona (rs-CN tsa. 36 ndime 3 mpaka tsa. 37 ndime 2)
June 26 Kuŵerenga Baibulo: Mlaliki 10 mpaka 12
Na. 1: Ziyeneretso za Oyang’anira (om-CN tsa. 32 ndime 1 mpaka tsa. 34 ndime 3)
Na. 2: Mlaliki 12:1-14
Na. 3: Phunziro la Kudzichepetsa (gt-CN mutu 62)
Na. 4: Mulungu Samaikiratu Pamene Munthu Aliyense Adzafa (rs-CN tsa. 114, mutu woyamba)
July 3 Kuŵerenga Baibulo: Nyimbo ya Solomo 1 mpaka 4
Na. 1: Kuthandiza Amuna Kuyenerera Monga Oyang’anira (om-CN tsa. 35 ndime 1 mpaka tsa. 38 ndime 1)
Na. 2: Nyimbo ya Solomo 2:1-14
Na. 3: Chenjerani ndi Kukhumudwitsa Ena (gt-CN mutu 63)
Na. 4: Sizonse Zimene Zimachitika Zimene Zili Chifuniro cha Mulungu (rs-CN tsa. 115 mpaka tsa. 116, kamutu kachiŵiri)
July 10 Kuŵerenga Baibulo: Nyimbo ya Solomo 5 mpaka 8
Na. 1: Kalimirani Ntchito ya Woyang’anira (om-CN tsa. 38 ndime 2 mpaka tsa. 40 ndime 3)
Na. 2: Nyimbo ya Solomo 8:1-14
Na. 3: Phunziro la Kukhululukira (gt-CN mutu 64)
Na. 4: Mulungu Samadziŵiratu ndi Kulinganiziratu Kanthu Kalikonse (rs-CN tsa. 116, kamutu kachitatu)
July 17 Kuŵerenga Baibulo: Yesaya 1 mpaka 3
Na. 1: Mathayo a Amuna Oikidwa ndi Mzimu (om-CN tsa. 41 ndime 1 mpaka tsa. 45 ndime 2)
Na. 2: Yesaya 1:1-13
Na. 3: Ulendo Wakachetechete wa ku Yerusalemu (gt-CN mutu 65)
Na. 4: Mphamvu ya Mulungu ya Kudziŵiratu ndi Kulinganiziratu Zochitika (rs-CN tsa. 117 ndime 2-5)
July 24 Kuŵerenga Baibulo: Yesaya 4 mpaka 7
Na. 1: Chikhulupiriro Nchofunika Kaamba ka Chikhululukiro ndi Chipulumutso (uw-CN mas. 148-50 ndime 7-10)
Na. 2: Yesaya 6:1-13
Na. 3: Ngozi ku Phwando la Misasa (gt-CN mutu 66)
Na. 4: Chifukwa Chake Mulungu Sanagwiritsire Ntchito Kudziŵiratu Kwake Ponena za Adamu (rs-CN tsa. 118)
July 31 Kuŵerenga Baibulo: Yesaya 8 mpaka 10
Na. 1: Mapindu a Kudziŵa Chilamulo (uw-CN mas. 150-1 ndime 11-13; tsa. 153 ndime 14)
Na. 2: Yesaya 9:1-12
Na. 3: Chifukwa Chake Maofesala Akulephera Kugwira Yesu (gt-CN mutu 67)
Na. 4: Mulungu Sanalinganiziretu Yakobo, Esau, Kapena Yudasi (rs-CN tsa. 119 ndime 1-3)
Aug. 7 Kuŵerenga Baibulo: Yesaya 11 mpaka 13
Na. 1: Ziphunzitso Zamaziko m’Chilamulo cha Mose: “Mathayo Kulinga kwa Mulungu” (uw-CN tsa. 152)
Na. 2: Yesaya 11:1-10
Na. 3: Chiyambi Chaumulungu cha Yesu ndi Mtsogolo Mwake Kumwamba (gt-CN mutu 68 ndime 1-11)
Na. 4: Kodi ndi Mwanjira Yotani Mmene Mpingo Wachikristu Unalinganizidwiratu? (rs-CN tsa. 119, kamutu kachitatu mpaka tsa. 120 ndime 1)
Aug. 14 Kuŵerenga Baibulo: Yesaya 14 mpaka 17
Na. 1: Ziphunzitso Zamaziko m’Chilamulo cha Mose: “Machitachita Achipembedzo Oletsedwa” (uw-CN tsa. 152)
Na. 2: Yesaya 14:3-20
Na. 3: Choonadi Chimene Chimamasula Anthu (gt-CN mutu 68 ndime 12-16)
Na. 4: Kodi Nkati Kamene Kali Kaonedwe Kamalemba ka Kupenda Nyenyezi? (rs-CN mas. 120-1)
Aug. 21 Kuŵerenga Baibulo: Yesaya 18 mpaka 22
Na. 1: Ziphunzitso Zamaziko m’Chilamulo cha Mose: “Mu Ukwati ndi Moyo wa Banja” (uw-CN tsa. 152)
Na. 2: Yesaya 21:1-17
Na. 3: Nkhani ya Utate (gt-CN mutu 69)
Na. 4: Kodi Pali Zifukwa Zomveka Zotani Zokhulupirira Mulungu? (rs-CN tsa. 307, kamutu koyamba)
Aug. 28 Kupenda Kolemba. Malizani Miyambo 21 mpaka Yesaya 22
Sept. 4 Kuŵerenga Baibulo: Yesaya 23 mpaka 26
Na. 1: Ziphunzitso Zamaziko m’Chilamulo cha Mose: “Ntchito Zophatikizapo Anthu Ena” (uw-CN tsa. 152)
Na. 2: Yesaya 25:1-12
Na. 3: Kuchiritsa Munthu Wobadwa Wosaona (gt-CN mutu 70)
Na. 4: Kuipa ndi Kuvutika Sizimatsimikizira Kusakhalako kwa Mulungu (rs-CN tsa. 307, kamutu komaliza mpaka tsa. 308, kamutu koyamba)
Sept. 11 Kuŵerenga Baibulo: Yesaya 27 mpaka 29
Na. 1: Moyo ndi Mwazi Nzopatulika (uw-CN mas. 154-6 ndime 1-6)
Na. 2: Yesaya 28:1-13
Na. 3: Munthu Wopemphapempha Akwiyitsa Afarisi (gt-CN mutu 71)
Na. 4: Mulungu ndi Munthu Weniweni Wokhoza Kukhala ndi Malingaliro (rs-CN tsa. 309 ndime 1-7)
Sept. 18 Kuŵerenga Baibulo: Yesaya 30 mpaka 33
Na. 1: Kugwiritsira Ntchito Mwazi m’Zamakhwala ndi Thayo la Mkristu (uw-CN mas. 156-60 ndime 7-12)
Na. 2: Yesaya 32:1-8, 16-20
Na. 3: Yesu Atuma Okwanira 70 (gt-CN mutu 72)
Na. 4: Mulungu Alibe Chiyambi (rs-CN tsa. 309, kamutu kachitatu)
Sept. 25 Kuŵerenga Baibulo: Yesaya 34 mpaka 37
Na. 1: Akristu Oona Sali Mbali ya Dziko (uw-CN mas. 161-3 ndime 1-6)
Na. 2: Yesaya 35:1-10
Na. 3: Kodi Ndani Kwenikweni Amene Ali Mnansi Wathu? (gt-CN mutu 73)
Na. 4: Kugwiritsira Ntchito Dzina la Mulungu Nkofunika Kaamba ka Chipulumutso (rs-CN tsa. 310, kamutu koyamba)
Oct. 2 Kuŵerenga Baibulo: Yesaya 38 mpaka 40
Na. 1: Zimene Kusakhala Mbali ya Dziko Kumafuna kwa Akristu (uw-CN mas. 163-8 ndime 7-16)
Na. 2: Yesaya 40:12-26
Na. 3: Uphungu wa Yesu kwa Marita (gt-CN mutu 74 ndime 1-5)
Na. 4: Kodi Zipembedzo Zonse Nzabwino? (rs-CN tsa. 310, kamutu kachiŵiri)
Oct. 9 Kuŵerenga Baibulo: Yesaya 41 mpaka 43
Na. 1: Pitirizani Kulankhula Mawu a Mulungu Molimbika Mtima (uw-CN mas. 169-71 ndime 1-7)
Na. 2: Yesaya 43:1-15
Na. 3: Kufunika kwa Kukhala Akhama m’Pemphero (gt-CN mutu 74 ndime 6-9)
Na. 4: Kodi Yesu Ali “Mulungu” Wamtundu Wotani? (rs-CN tsa. 311, kamutu koyamba)
Oct. 16 Kuŵerenga Baibulo: Yesaya 44 mpaka 46
Na. 1: Kupindula ndi Chitsanzo cha Atumwi (uw-CN tsa. 172 ndime 8)
Na. 2: Yesaya 46:1-13
Na. 3: Chilabadiro Choyenera ku Zozizwitsa za Yesu (gt-CN mutu 75)
Na. 4: Kulaka Zitsutso za Kukhulupirira Mulungu (rs-CN tsa. 311, ndime 5, mpaka tsa. 313, ndime 1)
Oct. 23 Kuŵerenga Baibulo: Yesaya 47 mpaka 49
Na. 1: Kulalikira Molimba Mtima ndi Mozindikira (uw-CN mas. 173-5 ndime 9-13)
Na. 2: Yesaya 48:1-11, 16-19
Na. 3: Yesu Avumbula Afarisi ndi Achilamulo (gt-CN mutu 76)
Na. 4: Chifukwa Chake Anthu Alephera Kukhazikitsa Boma Lolungama (rs-CN tsa. 62 mpaka tsa. 63, ndime 4)
Oct. 30 Kuŵerenga Baibulo: Yesaya 50 mpaka 53
Na. 1: Kumbukirani Kuti Tsiku la Yehova Layandikira (uw-CN mas. 176-7 ndime 1-4)
Na. 2: Yesaya 52:1-15
Na. 3: Yesu Afotokoza Nkhani ya Choloŵa (gt-CN mutu 77)
Na. 4: Chifukwa Chake Zoyesayesa za Anthu Zakudzetsa Mpumulo Sizingapambane (rs-CN tsa. 63, kamutu kachiŵiri, mpaka tsa. 64, kamutu kachiŵiri)
Nov. 6 Kuŵerenga Baibulo: Yesaya 54 mpaka 57
Na. 1: Khalani Maso ku Zochitika Zokwaniritsa Chizindikiro (uw-CN mas. 178-9 ndime 5, 6)
Na. 2: Yesaya 55:1-13
Na. 3: Yesu Afulumiza Ophunzira Ake Kukhala Okonzekera Kaamba ka Kubweranso Kwake (gt-CN mutu 78)
Na. 4: Ufumu wa Mulungu Ndiwo Yankho Lokha la Zosoŵa Zenizeni za Mtundu wa Anthu (rs-CN tsa. 65, kamutu koyamba)
Nov. 13 Kuŵerenga Baibulo: Yesaya 58 mpaka 62
Na. 1: Ntchito Yaikulu Yolekanitsa—Umboni Wakuti Mapeto Ali Pafupi (uw-CN mas. 179-83 ndime 7-14)
Na. 2: Yesaya 60:4-17
Na. 3: Mtundu Wotayika, Koma Osati Wonse (gt-CN mutu 79 ndime 1-5)
Na. 4: Maulosi a Baibulo Atsimikizira Kukhala Odalirika Kotheratu (rs-CN tsa. 65, kamutu kachiŵiri)
Nov. 20 Kuŵerenga Baibulo: Yesaya 63 mpaka 66
Na. 1: Woyang’anira Dera—Mphatso ku Mipingo ya Anthu a Mulungu (om-CN tsa. 47 ndime 1 mpaka tsa. 50 ndime 2)
Na. 2: Yesaya 65:11-25
Na. 3: Kugomeka Otsutsa Kuchiritsa pa Sabata (gt-CN mutu 79 ndime 6-9)
Na. 4: Kuchiritsa Kozizwitsa kwa Lerolino Sikumachitidwa ndi Mzimu wa Mulungu (rs-CN tsa. 166)
Nov. 27 Kuŵerenga Baibulo: Yeremiya 1 mpaka 3
Na. 1: Oyang’anira Ena Amene Amayang’anira Mwachikondi (om-CN tsa. 50 ndime 3 mpaka tsa. 54 ndime 2)
Na. 2: Yeremiya 1:4-19
Na. 3: Makola Ankhosa ndi Mbusa Wabwino (gt-CN mutu 80)
Na. 4: Kusiyana Pakati pa Kuchiritsa kwa Yesu ndi Atumwi Ake ndi kwa Lerolino (rs-CN tsa. 167, kamutu koyamba ndi kachiŵiri)
Dec. 4 Kuŵerenga Baibulo: Yeremiya 4 mpaka 6
Na. 1: Chifuno Chanzeru ndi Chachikondi cha Yehova (uw-CN mas. 184-6 ndime 1-5)
Na. 2: Yeremiya 5:1-14
Na. 3: Chifukwa Chake Akuyesayesa Kumupha Yesu (gt-CN mutu 81)
Na. 4: Mmene Akristu Oona Amadziŵikira Lerolino (rs-CN tsa. 167, kamutu kachitatu mpaka tsa. 168, kamutu koyamba)
Dec. 11 Kuŵerenga Baibulo: Yeremiya 7 mpaka 9
Na. 1: Yehova Agwirizanitsa Anthu Ake (uw-CN mas. 186-7 ndime 6-9)
Na. 2: Yeremiya 9:12-26
Na. 3: Kodi Ndani Amene Sadzapulumutsidwa? (gt-CN mutu 82 ndime 1-6)
Na. 4: Chifukwa Chake Mphatso za Kuchiritsa Zinaperekedwa m’Zaka za Zana Loyamba (rs-CN tsa. 169, kamutu koyamba)
Dec. 18 Kuŵerenga Baibulo: Yeremiya 10 mpaka 12
Na. 1: Chilengedwe Chaumunthu Chidzamasulidwa (uw-CN mas. 188-91 ndime 10-17)
Na. 2: Yeremiya 10:6-15, 22-25
Na. 3: Zochitika Paulendo Womka ku Yerusalemu (gt-CN mutu 82 ndime 7-11)
Na. 4: Kodi Nchiyembekezo Chanji Chimene Chilipo cha Kuchiritsidwa Kwenikweni kwa Mtundu Wonse wa Anthu? (rs-CN tsa. 169, kamutu kachitatu)
Dec. 25 Kupenda Kolemba. Malizani Yesaya 23 mpaka Yeremiya 12