Kusunga Umodzi Wathu wa Ufumu
1 Ufumu wa Mulungu ndiwo boma lenileni, wokhala ndi mphamvu ndi ulamuliro. Unali mutu wa nkhani wa ulaliki wa Yesu. (Mat. 4:17) Kuphunzitsa ena ndi kuchitira umboni za choonadi cha Ufumu kunali mbali yaikulu ya utumiki wa Yesu. Anatiphunzitsa kupempherera Ufumuwo ndi kupitirizabe kuufuna choyamba. (Mat. 6:9, 10, 33) Kumamatirabe kwa Yehova ndi ku gulu lake, kuchita ntchito yathu yolalikira, ndi kudzilekanitsa ndi dziko kumatikhozetsa kusunga umodzi wathu wa Ufumu. Mwa zochita zathu ndi mawu, timasonyeza kuti tili kumbali ya Ufumuwo.—Yoh. 18:37.
2 Chiyambire 1914, Ufumu wakhaladi weniweni kwa nzika zambirimbiri. Umodzi wosonyezedwa ndi nzika zimenezi za Ufumuwo ngwosiyana kwambiri ndi dziko logaŵanikali. Ife tiyenera kupanga Ufumuwo kukhala weniweni m’miyoyo yathu ngati uti ukhale mphamvu yogwirizanitsa. Kodi nchiyani chimene chimaupangitsa kukhala weniweni kwa ife?
3 Monga momwe alili maboma ena, Ufumuwo uli ndi mpambo wa malamulo. Komabe, uli wosiyana ndi ena chifukwa chakuti malamulo ake amapezeka m’Baibulo. Kuŵerenga Mawu a Mulungu nthaŵi zonse kumatipatsa zikumbutso zofunika za zimene zikufunika kwa ife monga nzika za Ufumuwo. Phunziro laumwini la zofalitsidwa zathu ndi chitsogozo chochokera kwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” zimatithandiza kugwiritsira ntchito malamulo a Mulungu m’miyoyo yathu ya tsiku ndi tsiku. (Mat. 24:45) Pamene tigwiritsira ntchito zimenezo, Ufumuwo umakhala weniweni kwambiri kwa ife, ukumatikokera pamodzi kwambiri mu ubale wa padziko lonse, kutipangitsa kukhala banja logwirizana la olambira pansi pa ulamuliro wa Yesu.
4 Umodzi Kupyolera mwa Kulalikira Ufumu: Ntchito yathu ndiyo kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu “kufikira malekezero ake a dziko.” (Mac. 1:8) Kulalikira “pamodzi” kumatigwirizanitsa pamene tikuyesetsa ‘kulemekeza’ Yehova. (Aroma 15:5, 6) Kukhala ndi phande mwachangu ndi antchito anzathu pa dziko lonse lapansi kumalimbitsa chikhulupiriro chathu ndi kulola mzimu wa Yehova kugwira ntchito pakati pathu kuti tikwaniritse chifuniro chake. “Kuchuluka mu ntchito ya Ambuye” kumatipangitsa kukhala “okhazikika, osasunthika.”—1 Akor. 15:58.
5 M’maiko ambiri Satana amayesa kusokoneza umodzi wathu mwa kudodometsa ntchito yathu yolalikira. Amagwiritsira ntchito njira zake zonse kufesa mzimu wa kusagwirizana ndi kubutsa mkhalidwe wa kusamvana, kuti ayese kuchititsa mikangano ndi nkhondo. (Miy. 6:19; Agal. 5:19-21, 26) Iye akufuna kutiloŵetsa m’mikangano ya dziko ndipo ngakhale kukhalira mbali m’nkhani za ndale ndi za kakhalidwe ka anthu. (Yak. 3:14-16) Malemba amatilimbikitsa kukana chisonkhezero chake; tikapanda kutero, angatilikwire monga nyama yake. (1 Pet. 5:8, 9) Sitiyenera kulola kutsimikizirika kwa chiyembekezo cha Ufumu kuzimiririka m’mitima ndi m’maganizo mwathu.
6 Kusunga umodzi wathu kumafuna kulama maganizo ndi nzeru ya kumwamba. Pamene mavuto abuka, makamaka ngati akhudza abale athu, tiyenera kusonyeza zipatso za mzimu kuti tisungebe mtendere. Mikhalidwe ya dziko, yonga kunyada, kaduka, ndi kudzikuza, njogaŵanitsa ndipo iyenera kuthetsedwa. (Aef. 4:1-3; Akol. 3:5-10, 12-14) Tifunikira kudzaza maganizo athu ndi malingaliro abwino, omangirira. Ufumuwo uli weniweni m’miyoyo yathu! Koma tifunikira kukhala maso kuti ukhalebe wotero!—Aef. 6:11, 13.
7 Kutsimikizirika kwa chiyembekezo chathu chabwino kwambiricho cha Ufumu kumatigwirizanitsa mumzimu wa umodzi umene sudzatha.—Sal. 133:1.