Misonkhano Yautumiki ya April
Mlungu Woyambira April 3
Mph. 10: Zilengezo za pamalopo ndi Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu. Lengezani madeti a msonkhano wanu wachigawo. Kambani nkhani yakuti “Konzekerani Chikumbutso.”
Mph. 15: “Oyamikira Chifukwa cha Zimene Tili Nazo.” Mafunso ndi mayankho. Ngati nthaŵi ilola, wonjezeranipo ndemanga za mu Nsanja ya Olonda ya August 1, 1990, masamba 19-20, ndime 15-20.
Mph. 20: “Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!—Magazini a Nthaŵi Zathu Zofulumira!” Kambitsiranani ndi omvetsera. Simbani chokumana nacho chosonyeza kuyamikira magazini. (g91-CN 6/8 tsa. 30) Itanani ofalitsa aŵiri kudzasonyeza mmene munthu angakonzekerere ulaliki mwa kugwiritsira ntchito malingaliro operekedwawo, ndiyeno achite chitsanzo mwa kulalikirana.
Nyimbo Na. 219 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira April 10
Mph. 10: Zilengezo za pamalopo. Lipoti la maakaunti ndi kuyamikira zopereka. Mbiri Yateokrase. Kumbutsani aliyense za kufunika kwa kuthandiza okondwerera kufika pa Chikumbutso. Limbikitsani onse kuti ayeseyese kukhala ndi phande mu utumiki wakumunda kutha kwa mlungu uno.
Mph. 15: “Kusunga Umodzi Wathu wa Ufumu.” Kambitsiranani ndi omvetsera.
Mph. 20: “Akuchuluka mu Ntchito ya Ambuye.” Nkhani ya mafunso ndi mayankho yokambidwa ndi woyang’anira utumiki. Longosolani makonzedwe ofutukulidwa a kugaŵira Uthenga wa Ufumu wapadera kunyumba ndi nyumba. Kambitsiranani za makonzedwe a kufola gawo lonse la mpingo wa kumaloko. Fotokozani zimene ziyenera kuchitidwa kuthandiza atsopano kukhala ndi phande mu utumiki kwa nthaŵi yoyamba. (Onani Utumiki Wathu Waufumu wa March 1995, tsamba 1.)
Nyimbo Na. 150 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira April 17
Mph. 13: Zilengezo za pamalopo. Simbani mfundo zolimbikitsa za pa Chikumbutso, ndipo fotokozani njira zimene tingaperekeremo thandizo lowonjezereka kwa atsopano amene anafikapo. Limbikitsani onse kudzafika pa nkhani yapadera pa April 23 ndiponso kuthandiza okondwerera atsopano kudzabweranso. Fotokozani za makonzedwe a utumiki wakumunda kaamba ka kugaŵira Uthenga wa Ufumu.
Mph. 15: “Kodi Mukuona Kusoŵako?” Mafunso ndi mayankho. Fotokozani mwachidule zonulirapo zimene zilipo zimene akulu akuyesa kukwaniritsa m’ntchito yawo yoŵeta. Fotokozani zimene munthu aliyense angachite kuti athandize.
Mph. 17: “Funafunani Amene Ali Ophunzitsika.” Fotokozani kufunika kwa kupanga maulendo obwereza. Limbikitsani kugwiritsira ntchito Baibulo. Khalani ndi ulaliki umodzi kapena maulaliki aŵiri osonyeza zimenezi mwachidule.
Nyimbo Na. 197 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira April 24
Mph. 15: Zilengezo za pamalopo. Fotokozani mmene kugaŵira Uthenga wa Ufumu kukuyendera m’gawolo. Pemphani ofalitsa kuti asimbe zokumana nazo zimene apeza pogaŵira Uthenga wa Ufumu. Sonyezani maulaliki a sabusikripishoni amene angakhale oyenera m’gawo la kumaloko. Lengezani makonzedwe alionse a mpingo a kukhala ndi phande mu umboni wa madzulo ngati mikhalidwe ilola.
Mph. 12: Zosoŵa za pamalopo. Kapena perekani nkhani yakuti, Khalani Wolimbikitsa Ena, ya mu Nsanja ya Olonda ya January 15, 1995, masamba 21-3.
Mph. 18: Chititsani Phunziro Lanu la Banja Nthaŵi Zonse. Mwamuna ndi mkazi akusonyeza nkhaŵa ponena za kusapita patsogolo kwauzimu kwa ana awo. Mwamunayo akuvomereza kuti iye wakhala akunyalanyaza nkhani ya kuchititsa phunziro la banja; nthaŵi zina milungu ingapo imapyola popanda kupereka malangizo alionse ku banjalo. Iwo akupenda chilangizo ndi chitsogozo choperekedwa mu Bukhu Lolangiza la Sukulu, tsamba 37, ndime 12-14. Onsewo akuvomerezana za kuti adzaika chisamaliro choyamba pa phunziro la banja mlungu uliwonse, osalola zochitika zina kudodometsa.
Nyimbo Na. 142 ndi pemphero lomaliza.