Tamandani Yehova Tsiku ndi Tsiku
1 Mulungu wathu, Yehova, ndi Mlengi wodabwitsa ndi wachikondi, Magwero a moyo wonse ndi chimwemwe. Chifukwa cha ukulu wake, iye ngwofunikadi chitamando kuchokera ku zolengedwa zake zonse. Aliyense payekha, timafuna kunena monga wamasalmo kuti: “Ndidzawonjeza kukulemekezani. Pakamwa panga padzafotokozera chilungamo chanu, ndi chipulumutso chanu tsiku lonse.” (Sal. 71:14, 15) Kuti tichite zimenezi, tiyenera kufunafuna njira zotamandira Yehova tsiku ndi tsiku ndi kusonkhezeredwa kulankhula zabwino ponena za iye, chilungamo chake, ndi makonzedwe ake a chipulumutso.
2 Chitsanzo chabwino cha kutamanda Yehova chinaperekedwa ndi Akristu oyambirira. Ponena za anthu 3,000 omwe anabatizidwa pa Pentekoste timaŵerenga pa Machitidwe 2:46, 47 kuti: “Tsiku ndi tsiku anali chikhalire ndi mtima umodzi m’kachisi, . . . nalemekeza Mulungu, ndi kukhala nacho chisomo ndi anthu onse. Ndipo [Yehova, NW] anawawonjezera tsiku ndi tsiku amene akuti apulumutsidwe.” Iwo anali kuphunzira choonadi chodabwitsa ponena za Yehova ndi Mesiya wake. Chimwemwe chawo chinali choyambukira, chikumalimbikitsabe ena kumvetsera ndi kuphunzira ndi kutamanda Yehova.
3 Mwaŵi Umakhalapo Tsiku Lililonse: Ambiri lerolino amaona kuti angatamande Yehova tsiku ndi tsiku mwa kuchita ulaliki wamwamwaŵi. Kukonzekera kwa pasadakhale kumawachititsa kukhala ndi zotulukapo zabwino. Mlongo wina amene anasankha kuchita umboni wamwamwaŵi anapeza kuti munthu wina waswa madzenera aŵiri a galimoto lake ndi kubamo zinthu zina. Iye anaitanitsa wantchito yokonza nakonzekera kumlalikira wokonzayo. Kukonzekera kwake kunaphatikizapo kupempherera chitsogozo cha Yehova. Monga zotulukapo zake, analalikira kwa wokonzayo kwa ola limodzi ndi kumugaŵira buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha.
4 Mlongo winanso anali kukumana ndi mnansi wake nthaŵi zonse pamene anapita kokayenda ndi agalu awo. Nthaŵi ina pamene anakumana, anakambitsirana kwambiri za mavuto a moyo, ndipo zimenezo zinachititsa makambitsirano ena mtsogolo mwake. Posapita nthaŵi, phunziro la Baibulo linayambidwa. Modabwitsa, mnansi wakeyo anavomereza pambuyo pake kuti sakanamvetsera kwa Mboni za Yehova ngati zikanabwera panyumba pake, popeza sanakhulupirire mwa Mulungu kapena Baibulo.
5 Ena amatha kuchita umboni pamene ogulitsa zinthu kapena anthu ena abwera panyumba pawo. Mlongo wina ku Ireland analandira mwamuna wina wogulitsa inshuwalansi ya moyo. Mlongoyo anafotokoza kuti akuyembekezera kusangalala ndi moyo wosatha mtsogolo. Limeneli linali lingaliro lachilendo kotheratu kwa mwamuna ameneyu, amene analeredwa monga Mroma Katolika. Iye analandira buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha, anafika pamsonkhano mlungu wotsatira, ndipo anavomera kukhala ndi phunziro la Baibulo. Wogulitsa zinthu ameneyu ali mbale wobatizidwa tsopano.
6 Tonsefe tiyenera kukhala atcheru ndi mipata yotamandira Yehova tsiku ndi tsiku. Kuika magazini angapo kapena matrakiti pamene angaonedwe ndi kugaŵidwa mwamsanga kwa alendo kumathandiza. Kumalo ena nthaŵi yochepa imene ingatheredwe pamalo opumira ingakupatseni mwaŵi wolalikira kwa ena amene amaima kuti apume kwa kanthaŵi kochepa. Achichepere ena a Mboni m’sukulu amakhala ndi buku lofotokoza Baibulo pa desiki lawo monga njira yoyambitsira makambitsirano ndi wina wake amene aliona ndi kufunsa mafunso. Khalani ndi Lemba losonyako limodzi kapena aŵiri amene mungagwiritsire ntchito. Pemphani Yehova kuti akuthandizeni. Mudzadalitsidwa kaamba ka kuchita zimenezo.—1 Yoh. 5:14.