Mbiri Yateokrase
Albania: Ofalitsa 600 ochitira lipoti la August anali chiŵerengero chapamwamba chinanso cha 28.
Angola: Chiŵerengero chapamwamba koposa cha ofalitsa 26,129 chinafikidwa pamapeto a chaka chautumiki. Panalinso chiŵerengero chapamwamba cha apainiya okhazikika chofika 1,309. Ofalitsa anali ndi avareji ya maola 15 ndi maphunziro a Baibulo aŵiri aliyense mu August.
Britain: Tili okondwa kusimba kuti chiŵerengero chapamwamba koposa chatsopano cha ofalitsa 132,440 chinafikidwa mu August. Zimenezi zikusonyeza chiwonjezeko cha 2 peresenti kuposa cha chaka chatha cha utumiki.
Chile: M’mwezi wa August, chiŵerengero chapamwamba koposa chatsopano cha ofalitsa chinafikidwa, chikumafika pa 50,283! Apitirira pa chiŵerengero cha 50,000 kwa nthaŵi yoyamba. Maphunziro a Baibulo apanyumba okwanira 63,732 anachititsidwa.