Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 3/96 tsamba 6
  • Chidziŵitso Chonena za Mulungu Woona Chimatsogolera ku Moyo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chidziŵitso Chonena za Mulungu Woona Chimatsogolera ku Moyo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Nkhani Yofanana
  • “Moyo Wosatha ndi Uwu”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Thandizani Ena Kupeza Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Chidziŵitso Chochokera kwa Mulungu Chimayankha Mafunso Ambiri
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Kufalitsa Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
km 3/96 tsamba 6

Chidziŵitso Chonena za Mulungu Woona Chimatsogolera ku Moyo

“Moyo wosatha ndi uwu,” anatero Yesu m’pemphero kwa Atate wake, “kuti akadziŵe inu Mulungu woona yekha.” (Yoh. 17:3) Ha, imeneyo inali mfupo yaikulu yotani nanga! Mwa kugwiritsira ntchito buku la Knowledge That Leads to Everlasting Life, tingathandize ena kuphunzira zimene afunikira kuchita kuti akhale ndi moyo kosatha. Kodi tinganenenji kuti tidzutse chidwi ndi kuwasonkhezera kufuna kuŵerenga buku la Knowledge?

2 Mungagwiritsire ntchito ulaliki umene ukusonyeza Baibulo kukhala magwero a chitsogozo chothandiza, mwa kunena kuti:

◼ “Tikukambitsirana ndi anansi athu za kumene tingapeze magwero a chitsogozo chothandiza cholimbanirana ndi mavuto a moyo. Kale anthu ambiri ankafunafuna m’Baibulo. Koma tsopano maganizo a anthu asintha; ambiri amakayikira Baibulo, akumaliona kukhala buku longolembedwa ndi anthu. Kodi lingaliro lanu nlotani? [Yembekezerani yankho.] Pali chifukwa chabwino kwambiri chimene tinganenere kuti Baibulo nlothandiza m’tsiku lathu. [Ŵerengani 2 Timoteo 3:16, 17.] Mapulinsipulo a Baibulo amagwira ntchito kwambiri lerolino monga momwe anachitira pamene Mulungu anauzira kulembedwa kwa Baibulo.” Tsegulani patsamba 16 m’buku la Knowledge, ndi kufotokoza mwachidule za chitsogozo chopindulitsa chopezeka mu Ulaliki wa pa Phiri wa Yesu. Ŵerengani mawu ogwidwa opezeka m’ndime 11 kapena a m’ndime 13. Gaŵirani bukulo, ndipo linganizani za kudzabweranso kuti mudzayankhe funso lakuti, Kodi tingapindule motani ife enife ndi chidziŵitso chimene chili m’Baibulo?

3 Popeza kuti pemphero lili nkhani yokondedwa ndi anthu ambiri, mungakonde kukambitsirana za ilo mwa kufunsa kuti:

◼ “Pokhala ndi zovuta zonse zimene timayang’anizana nazo m’moyo wamakono, kodi muganiza kuti pemphero lingatithandizedi? [Yembekezerani yankho.] Ambiri amaganiza kuti ayandikira kwa Mulungu mwa kupemphera kwa iye ndi kuti kuchita motero kwawapatsa nyonga, imenedi Baibulo limalonjeza. [Tsegulani buku la Knowledge patsamba 156, ndi kuŵerenga Afilipi 4:6, 7.] Komabe, munthu angalingalire kuti nthaŵi zina mapemphero ake sayankhidwa. Mutu uwu ukufotokoza kuti ‘How You Can Draw Close to God.’ [Gaŵirani bukulo pachopereka chake.] Mutu umenewu ukufotokozanso mmene tingamvetsere kwa Mulungu, popeza kuti kulankhula naye sikuli kwa mbali imodzi. Tidzakambitsirana zimenezo pamene ndidzabweranso.”

4 Kodi mungakonde kafikidwe kachindunji kuti muyambitse phunziro? Nayi njira imene ingakhale yabwino kwa inu:

◼ “Tikusonyeza mochitira kosi ya phunziro la Baibulo lapanyumba laulere. Kodi munachitapo kosi ya Baibulo? [Yembekezerani yankho.] Ndiloleni ndikusonyezeni buku lothandiza kuphunzira limene timagwiritsira ntchito.” Sonyezani buku la Knowledge, tsegulani patsamba 3 kuti mwini nyumbayo aone mpambo wa zamkati, ndi kufunsa kuti, “Kodi munaganizapo ponena za zimene Baibulo limanena pa mitu iyi?” Tsegulani pa mutu umene anthu ambiri amakonda kwambiri, ndi kuŵerenga mitu yake yaing’ono. Fotokozani kuti mukufuna kumsonyeza mwachidule mmene tingalingalirire nkhaniyi m’kosi yathu ya phunziro. Kaya phunziro layambidwa kapena ayi, gaŵirani bukulo pachopereka chanthaŵi zonse.

5 Lerolino makamu a anthu akulabadira chidziŵitso cholongosoka chonena za Mulungu woona. (Yes. 2:2-4) Ndi mwaŵi wathu kuthandiza ambiri monga momwe tingathere kuti aphunzire za Yehova ndi kutsogoleredwa ku moyo.—1 Tim. 2:4.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena