Tili ndi Utumiki
1 Yesu analamula otsatira ake ‘kuphunzitsa anthu a mitundu yonse.’ (Mat. 28:19) M’maiko 232 ndi magulu a zisumbu kuzungulira dziko lonse lapansi, otamanda Yehova Mulungu oposa mamiliyoni asanu akupereka umboni wamoyo wa kukwaniritsidwa kwa lamulo la Yesu. Koma bwanji za ife patokha? Kodi timaona mwamphamvu utumiki wa kulalikira?
2 Thayo Loyenera: Utumiki ndiwo “lamulo la kuchita ntchito zofotokozedwa.” Ife tili pansi pa malamulo ochokera kwa Kristu a kulalikira. (Mac. 10:42) Mtumwi Paulo anazindikira kuti zimenezi zinamkakamiza, kapena kumpatsa thayo la kulengeza uthenga wabwino. (1 Akor. 9:16) Mwachitsanzo: Tinene kuti inu ndinu mmalinyero amene muli mu sitima yapamadzi imene ikumira. Mtsogoleri wake akulamulirani kuti muchenjeze mapasinjala ndi kuwatsogolera ku mabwato opulumukiramo. Kodi mudzanyalanyaza lamulo limenelo ndi kungoika maganizo pa kudzipulumutsa inu eni? Ndithudi ayi. Ena akudalira pa inu. Moyo wawo uli pangozi! Muli ndi thayo la kuchita utumiki wanu kuwathandiza.
3 Mulungu watipatsa ife utumiki wa kupereka chenjezo. Posachedwa Yehova adzathetsa dongosolo lonse la zinthu loipali. Miyoyo mamiliyoni ambiri ili pangozi. Kodi kungakhale bwino kwa ife kunyalanyaza ngozi ya ena ndi kungodera nkhaŵa za kudzipulumutsa ife eni? Kutalitali. Tili ndi thayo loyenera la kuthandiza kupulumutsa moyo wa ena.—1 Tim. 4:16.
4 Zitsanzo Zokhulupirika Zozitsatira: Mneneri Ezekieli anamva kukhala wamlandu wa kupereka uthenga wachenjezo kwa Aisrayeli osakhulupirika. Yehova anamchenjeza mwamphamvu za zotulukapo zake ngati akalephera kuchita utumiki wake kuti: “Ndikanena kwa woipa, Udzafa ndithu, koma iwe osamchenjeza, . . . woipa yemweyo adzafa mu mphulupulu yake; koma mwazi wake ndidzaufuna pa dzanja lako.” (Ezek. 3:18) Ezekieli anakwaniritsa mokhulupirika utumiki wake ngakhale kuti anayang’anizana ndi chitsutso cholimba. Chifukwa chake, anakondwera pamene ziweruzo za Yehova zinaperekedwa.
5 Zaka mazana ambiri pambuyo pake, mtumwi Paulo analemba za thayo lake la kulalikira. Analengeza kuti: “Ndilibe kanthu ndi mwazi wa anthu onse. Pakuti sindinakubisirani pakukulalikirani uphungu wonse wa Mulungu.” Paulo analalikira poyera ndi kunyumba ndi nyumba chifukwa chakuti anazindikira kuti kulephera kuchita motero kukanamchititsa kukhala ndi liwongo la mwazi pamaso pa Mulungu.—Mac. 20:20, 26, 27.
6 Kodi tili ndi changu cha Ezekieli? Kodi timakakamizika kulalikira monga momwe Paulo anachitira? Utumiki wathu uli monga momwe unalili wawo. Tiyenera kupitiriza kukwaniritsa thayo lathu la kuchenjeza ena, ngakhale ngati akuchita mphwayi, kapena kutsutsa. Zikwi zowonjezereka zingalabadirebe uthenga wa Ufumu ndi kulengeza kuti: “Tidzamuka nanu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi inu.” (Zek. 8:23) Chikondi chathu pa Mulungu ndi pa munthu mnzathu chitisonkhezeretu kusatopa. Tili ndi utumiki wa kulalikira!