Kodi Mukulunjika Nawo Bwino Mawu a Mulungu?
1 Yesu Kristu anali mphunzitsi wamkulu koposa amene anakhalako. Analankhula zinthu m’njira imene inakhudza mtima wa anthu, kusonkhezera malingaliro awo, ndi kuwachititsa kuchita ntchito zabwino. (Mat. 7:28, 29) Iye nthaŵi zonse anagwiritsira ntchito Mawu a Mulungu monga maziko a chiphunzitso chake. (Luka 24:44, 45) Anapereka thamo kwa Yehova Mulungu pa zonse zimene anadziŵa ndi zimene anatha kuphunzitsa. (Yoh. 7:16) Yesu anapereka chitsanzo chabwino kwambiri kwa otsatira ake mwa kulunjika nawo bwino Mawu a Mulungu.—2 Tim. 2:15.
2 Nayenso mtumwi Paulo anali chitsanzo chapadera mwa kulunjika nawo Mawu a Mulungu mogwira mtima. Anachita zoposa kungoŵerengera ena Malemba; analongosola ndi kulingalira pa zimene anali kuŵerenga, akumapereka umboni kuchokera m’Mawu a Mulungu wakuti Yesu anali Kristuyo. (Mac. 17:2-4) Chimodzimodzinso, Apolo wophunzira wolankhula mwanzeruyo anali “wamphamvu m’malembo,” ndipo analunjika nawo bwino popereka ulaliki wamphamvu wa choonadi.—Mac. 18:24, 28.
3 Khalani Mphunzitsi wa Mawu a Mulungu: Olengeza Ufumu amakono apeza chipambano chabwino kwambiri pophunzitsa anthu oona mtima mwa kuwasonyeza ndi kukambitsirana nawo za m’Baibulo. Pachochitika china, mbale wina anakhoza kugwiritsira ntchito Ezekieli 18:4 limodzi ndi malemba ena ogwirizana nalo pokambitsirana ndi pasitala wina ndi mamembala ake atatu za chotulukapo chotsimikizirika cha oipa ndi olungama. Chotulukapo chake chinali chakuti, mamembala ena a tchalitchicho anayamba kuphunzira, ndipo mmodzi wa iwo potsirizira pake analandira choonadi. Pachochitika chinanso, mlongo wina anapemphedwa kuti alongosolere mwamuna wotsutsa wa wokondwerera wina chifukwa chake Mboni za Yehova sizimakondwerera Krisimasi ndi masiku akubadwa. Pamene anali kuŵerenga mayankho a Malemba mwachindunji kuchokera m’buku la Kukambitsirana, mwamunayo anavomereza. Mkazi wake anakondwera kwambiri chifukwa cha kuvomereza kwake kwakuti anati: “Tidzayamba kufika pa misonkhano yanu.” Ndipo mwamunayo anavomereza!
4 Gwiritsirani Ntchito Thandizo Limene Lilipo: Utumiki Wathu Waufumu ndi programu ya Msonkhano Wautumiki zimagaŵira njira zabwino zotithandiza polunjika nawo Mawu a Mulungu. Ofalitsa ambiri asonyeza chiyamikiro pa maulaliki osiyanasiyana amene amafalitsidwa ndi kusonyezedwa kaamba ka phindu lathu ndi amene akhaladi apanthaŵi yake kwambiri ndi ogwira mtima. Buku la Kukambitsirana za m’Malemba lili ndi chuma cha malingaliro onena za mmene tingafotokozere bwino mitu yaikulu yoposa 70 imene imalongosoledwa m’Mawu a Mulungu. Buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha limafotokoza mwachidule ziphunzitso zonse zazikulu za Baibulo zimene atsopano afunikira kumvetsa. Maphunziro 24 ndi 25 mu Bukhu Lolangiza la Sukulu Yateokratiki amatisonyeza mmene aphunzitsi aluso moyenerera amayambira nkhani, kuŵerenga, ndi kugwiritsira ntchito malemba. Tiyenera kugwiritsira ntchito bwino thandizo lonseli limene lili lopezeka mosavuta kwa ife.
5 Pamene tilunjika nawo bwino Mawu a Mulungu, tidzapeza kuti “ali amoyo, ndi ochitachita, . . . nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima” za awo amene timawalalikira. (Aheb. 4:12) Chipambano chimene tili nacho limodzi nawo chidzatisonkhezera kulankhula choonadi molimbika mtima kwambiri!—Mac. 4:31.