Dzikonzereni Ulaliki Wanu wa Magazini
1 Tikuyamikira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! chifukwa cha nkhani zawo za panthaŵi yake ndipo zopereka chidziŵitso, zimene zimanena za zilizonse kuyambira pa nkhani za m’dziko mpaka “zakuya za Mulungu.” (1 Akor. 2:10) Tonsefe tikukumbukira zinthu zambiri zatsopano ndipo zomangirira zimene taŵerenga m’magazini ameneŵa, amene Yehova akugwiritsira ntchito kuvumbulira choonadi pang’onopang’ono. (Miy. 4:18) Tiyenera kukhala ofunitsitsa kuwagaŵira kwa anthu ambiri amene tingathe.
2 Pendani Gawo Lanu: Kodi ndi anthu a mtundu wanji amene amakhala m’dera lanu? Ngati ali otanganitsidwa, mungafunikire kukonza ulaliki wachidule ndipo wolunjika. Ngati muli ndi gawo limene anthu saali otanganitsidwa kwambiri, mungathe kunena zambiri. Ngati eni nyumba ambiri amagwira ntchito usana, mungakhale ndi chipambano chachikulu kufika panyumba zawo mochedwa masana kapena madzulo dzuŵa litangoloŵa. Mungafikire ena usana mwa ulaliki wa m’khwalala kapena kugwirira ntchito kusitolo ndi sitolo. Ofalitsa ena amapeza zotulukapo zabwino mwa kufikira anthu mwamwaŵi poimika magalimoto ndi m’misika.
3 Adziŵeni Bwino Magaziniwo: Ŵerengani kope lililonse mutangolilandira. Sankhani nkhani zimene muona kuti zidzakondweretsa anthu a m’gawo lanu. Kodi ndi nkhani ziti zimene zimawakhudza? Pezani mfundo yakutiyakuti imene mungatchule m’nkhani imene mukufuna kusonyeza. Lingalirani za funso limene mungafunse kuti mudzutse chikondwerero. Sankhani lemba loyenerera limene mudzaŵerengera mwini nyumba mutakhala ndi mpata wa kuchita motero. Lingalirani mmene mungayalire maziko a ulendo wobwereza.
4 Konzani Mawu Anu Oyamba: Mosamala sankhani mawu amene mukufuna kukagwiritsira ntchito podzidziŵikitsa ndi poyambitsa makambitsirano. Ena apeza chipambano ndi mawu oyamba awa: “Ndaŵerenga nkhani yochititsa chidwi m’magaziniwa, ndipo ndikufuna kuuzako ena.” Ambiri amayamba ndi funso limene lisumika pa mfundo zokambitsiranapo zimene adzagwiritsira ntchito. Mwachitsanzo:
5 Ngati mukusonyeza nkhani yonena za kufala kwa upandu, mungafunse kuti:
◼ “Kodi padzafunikira chiyani kuti tizigona usiku mosawopa kuti adzatiloŵera kapena kutivulaza?” Fotokozani kuti muli ndi chidziŵitso chonena za njira yothetsera vutoli. Njirayo posachedwapa idzachotsaponso mtundu wina uliwonse wa chipolowe m’chitaganya. Sonyezani kanthu kena m’magazini kamene kamapereka chiyembekezo chimenechi. Pamene mubwererako, mungasonyeze mwini nyumba mutu 1 wa buku la Chidziŵitso.
6 Posonyeza nkhani yonena za moyo wa banja, munganene kuti:
◼ “Makolo ambiri amavutika kwambiri kusamalira banja masiku ano. Mabuku ambiri alembedwa ponena za nkhaniyi, koma ngakhale akatswiri sakugwirizana. Kodi pali aliyense amene angapereke chitsogozo chodalirika?” Tchulani ndemanga yakutiyakuti ya m’magaziniwo imene ikusonyeza uphungu wanzeru wopezeka m’Baibulo. Pamene mupanga ulendo wobwereza, kambitsiranani malingaliro a m’Malemba opezeka m’buku la Chidziŵitso, masamba 145-8 onena za kulera ana.
7 Posonyeza nkhani yonena za vuto la makhalidwe, munganene kuti:
◼ “Anthu ambiri ali opanikizika chifukwa cha nthaŵi zovutazi zimene tikukhalamo. Kodi muganiza kuti Mulungu anafuna kuti tizikhala motere?” Sonyezani nkhani yonena za mmene tingalimbanirane ndi mavuto a lerolino kapena imene ikupereka zifukwa zoyembekezera mtsogolo pamene sikudzakhala nkhaŵa. Paulendo wanu wotsatira, kambitsiranani chithunzi ndi mawu ake pa masamba 4-5 a buku la Chidziŵitso, ndiyeno nthaŵi yomweyo yambitsani phunziro la Baibulo lapanyumba.
8 Sinthani Malinga ndi Mwini Nyumba: Mudzakumana ndi anthu okonda zinthu zosiyanasiyana ndipo a makulidwe osiyanasiyana. Konzani ulaliki wosavuta umene mungasinthe malinga ndi mwini nyumba aliyense. Kumbukirani mmene mungasinthire zimene mudzanena kwa mwamuna, mkazi, wachikulire, kapena wachichepere. Palibe malamulo olimba a zimene muyenera kunena. Gwiritsirani ntchito mawu alionse amene mungakonde ndipo amene amakhala ndi zotulukapo. Komabe, khalani wotenthedwa maganizo, lankhulani kuchokera mumtima, ndipo khalani womvetsera wabwino. Awo amene ali “ofuna moyo” adzazindikira kuona mtima kwanu ndipo adzalabadira.—Machitidwe 13:48, NW.
9 Thandizanani: Mwa kugaŵana malingaliro, timaphunzira njira zatsopano zofotokozera malingaliro athu. Kuyesezera pamodzi maulaliki athu kumatipatsa chidziŵitso ndi chidaliro. (Miy. 27:17) Ngati muyeseza zimene mudzalankhula, mudzakhala womasuka kwambiri pakhomo. Nkofunika kuti makolo azikhala ndi nthaŵi yothandiza ana awo kukonzekera, kumvetsera pamene akuyeseza ulaliki wawo, ndi kupereka malingaliro kuti awongokere. Achatsopano angapindule mwa kugwira ntchito limodzi ndi abale achidziŵitso kwambiri.
10 Kukonza ulaliki wanuwanu wa magazini sikuyenera kukhala kovuta. Kumangofuna kukhala ndi kanthu kena m’maganizo kokanena ndi kukanena mwanjira yokopa. Mwa kugwiritsira ntchito luso ndi kukonzekera, mungapange ulaliki wabwino umene udzakhala ndi zotulukapo zabwino.
11 Kugaŵira magazini ndiko imodzi ya njira zazikulu zimene timawanditsira uthenga wa Ufumu padziko lonse lapansi. Ngati mungagaŵire Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kwa anthu oona mtima, magaziniwo adzadzilankhulira okha. Nthaŵi zonse kumbukirani kufunika kwake ndi mmene uthenga wake ungapulumutsire miyoyo. Mtundu umenewu wa ‘kuchitira chokoma ndi kugaŵana ndi ena’ ndi umene umakondweretsa kwambiri Yehova.—Aheb. 13:16.