Njira Zowongolera Ulaliki Wathu wa Ufumu
1 Ntchito yathu ya kulalikira ili yofulumira kwambiri tsopano kuposa ndi kale lonse. Kukhala ndi moyo kwa anthu kapena kufa kwawo kudzadalira pa mmene iwo amachitira ndi mbiri yabwino. (1 Pet. 4:5, 6, 17; Chiv. 14:6, 7) Pachifukwa chimenechi ife nthaŵi zonse tiyenera kufunafuna njira zowongolera ulaliki wathu wa Ufumu. Kodi njira zina zochitira kuwongolerako nzotani?
2 Konzekerani Bwino: Mwa kugwiritsira ntchito kope latsopano la Utumiki Wathu Waufumu, sankhani ulaliki umene muganiza kuti udzakondweretsa anthu ochuluka m’gawo lanu. Nkofunika kugwirizanitsa mawu anu ndi mikhalidwe yakumaloko. Mwina mungafune kukonza ulaliki wanuwanu, mwakugwiritsira ntchito malingaliro ndi Malemba amene inu mwini mwapeza kukhala ogwira mtima. Mudzafunikira mawu oyamba odzutsa chikondwerero. (Onani buku la Kukambitsirana, masamba 9-15.) Mwinamwake mwalinganiza kuti mudzafunsa funso lokopa maganizo kapena kupempha mwininyumba kukambapo pa nkhani ina yakumaloko yotchulidwa panyuzi. Mutaloŵeza ulalikiwo m’maganizo, uyesezeni ndi chiŵalo cha banja kapena wofalitsa wina amene angakuuzeni pamene mufunikira kuwongolera.
3 Kambitsiranani ndi Anthu: Chifuno chathu ndicho kupereka uthenga wofunika kwambiri. Tingachite zimenezi mwa kuloŵetsa womvetsera wathu m’kukambitsirana kwatanthauzo. Ngati mwininyumba atsutsa kapena apereka lingaliro lake, mvetserani mosamalitsa zimene afuna kunena. Zokamba zake zidzakuthandizani kupereka yankho la Malemba la chiyembekezo chili mwa inu. (1 Pet. 3:15) Ngati lingaliro lake siligwirizana ndi Baibulo, munganene mwaluso kuti: “Anthu ambiri amaganiza zimenezo. Komabe, nayi njira ina yoonera nkhaniyi.” Ndiyeno ŵerengani lemba loyenera, ndi kumpempha kukambapo.
4 Khalani ndi Ndandanda Yosinthika: Kukhala wokonzekera bwino sikudzaphula kanthu ngati simukhoza kulankhula ndi anthu. Lerolino nkofala kupeza eninyumba oŵerengeka chabe panyumba pamene tiwafikira. Ngati ndimmene gawo lanu liliri, yesani kusintha ndandanda yanu kotero kuti mungathe kugwira ntchito kunyumba ndi nyumba pamene anthu ambiri ali panyumba. Mwina mungapeze kuti nthaŵi yabwino yowafikira ndi kumapeto kwa mlungu; ena angapezeke kaŵirikaŵiri mkati mwa mlungu koma chakumadzulo. M’madera ena kumawakhalira bwino ofalitsa kuchitira umboni pa maholide akudziko chifukwa chakuti amapeza anthu ambiri panyumba. Kaŵirikaŵiri anthu amakhala omasuka ndipo angakonde kwambiri kukambitsirana panthaŵi zoterozo. Kungakhale bwino kugwirizanitsa mawu anu oyamba ndi chochitikacho ndiyeno kugwirizanitsa mawu anu ndi nkhani ya Malemba.
5 Pendani Kugwira Mtima kwa Ulaliki Wanu: Mutachoka pakhomo lililonse, dzifunseni kuti: ‘Kodi ndamfika pamtima mwininyumbayo? Kodi ndinamsonkhezera kukambapo ndiyeno kumvetsera zimene anali kunena? Kodi ndamyankha mwaluso? Polingalira za mkhalidwe wake, kodi ndagwiritsira ntchito kafikidwe kabwino koposa?’ Kungakhale kothandiza kugwira ntchito nthaŵi ndi nthaŵi ndi wofalitsa wozoloŵera kapena mpainiya ndi kumvetsera mosamalitsa maulaliki ake ndi cholinga cha kuwongolera kugwira mtima kwanu mu utumiki.
6 Ngati muli ndi luso pantchito yanu, mudzakhoza kuuzako ena choonadi cha Ufumu chimene ‘chidzapulumutsa inu eni ndi iwo akumva inu.’—1 Tim. 4:16; Miy. 22:29.