Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 11/96 tsamba 2
  • Misonkhano Yautumiki ya November

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Misonkhano Yautumiki ya November
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira November 4
  • Mlungu Woyambira November 11
  • Mlungu Woyambira November 18
  • Mlungu Woyambira November 25
Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
km 11/96 tsamba 2

Misonkhano Yautumiki ya November

Mlungu Woyambira November 4

Nyimbo Na. 29

Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu. Lankhulanipo pa lipoti la utumiki wakumunda la August la dziko lino ndi la mpingo wanu.

Mph. 15: “Kodi Mukulunjika Nawo Bwino Mawu a Mulungu?” Mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo ndemanga pa “Zifukwa zophunzirira Baibulo,” m’buku la Kukambitsirana, masamba 52-4.

Mph. 20: “Moyo Wosatha ndi Uwu.” (Ndime 1-5) Mutanena ndemanga zoyamba zachidule pa ndime 1, ofalitsa aŵiri okhoza bwino asonyeze chitsanzo cha ulaliki wa m’ndime 2-5. Gogomezerani cholinga cha kuyambitsa phunziro la Baibulo.

Nyimbo Na. 128 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira November 11

Nyimbo Na. 40

Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Lipoti la maakaunti.

Mph. 20: Nkumpatsiranji Yehova? Kukambitsirana kwa akulu aŵiri, sonyezani mfundo zazikulu za m’nkhani ya pa masamba 28-31 a mu Nsanja ya Olonda ya November 1, 1996. Kapena chidziŵitsocho chingaperekedwe ngati nkhani ya mkulu.

Mph. 15: “Moyo Wosatha ndi Uwu.” (Ndime 6-8) Kambitsiranani mapindu a kugwiritsira ntchito kafikidwe kachindunji poyambitsa maphunziro. Ofalitsa odziŵa bwino achite chitsanzo cha ulaliki wa m’ndime 6-7. Pemphani omvetsera kuti asimbe za nthaŵi pamene anayambitsa phunziro paulendo woyamba. Pamene mwamuna wina anapemphedwa mwachindunji kumchititsa phunziro, anayankha kuti: “Inde. Loŵani. Ndingakonde kuphunzira.” Anayamba kuphunzira naye, banja lake lonse linakhalapo mlungu wotsatira, ndipo posapita nthaŵi onse anali kufika pamisonkhano ndi kukhala ndi phande mu ntchito yopereka umboni. Limbikitsani onse kubwera ndi mphatika yawo ya mu Utumiki Wathu Waufumu wa June 1996 pa Msonkhano Wautumiki wa mlungu wamaŵa.

Nyimbo Na. 129 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira November 18

Nyimbo Na. 140

Mph. 10: Zilengezo zapamalopo.

Mph. 15: “Tili ndi Utumiki.” Mafunso ndi mayankho. Lankhulanipo mwachidule pa ndime 13-16 za mu Nsanja ya Olonda ya January 1, 1988, masamba 28-9.

Mph. 20: Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Opita Patsogolo. Nkhani ya woyang’anira utumiki. Takhala tikugwiritsira ntchito buku la Chidziŵitso mu ntchito ya maphunziro a Baibulo kwa nyengo yoposa chaka. Mwachionekere ophunzira ena alimaliza kale, pamene kuli kwakuti ena afika nalo patali. Tinalimbikitsidwa kuika mtima pa kuchititsa maphunziro olinganizidwira kuthandiza atsopano kuphunzira choonadi mwamsanga, kuchigwiritsira ntchito m’moyo wawo, ndi kukhala mbali ya mpingo. Mphatika ya Utumiki Wathu Waufumu wa June 1996 inapereka malingaliro abwino otithandiza kukhala aphunzitsi ogwira mtima. Pendani mwachidule zina za zinthu zimene tingachite pophunzitsa mwaluso ophunzira, zimene zafotokozedwa m’ndime 3-13 za mphatikayo. Ndiyeno, fotokozani zimene zifunikira kuchitidwa powathandiza kutenga kaimidwe kenikeni, monga momwe zafotokozedwera mu ndime 14-22. Ŵerengani ndime 15, 17, 20-1. Fotokozani malipoti ena abwino osonyeza mmene ofalitsa akumaloko apezera zotulukapo zabwino. Limbikitsani ambiri kukhala ndi phande mu ntchito ya maphunziro a Baibulo.

Nyimbo Na. 85 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira November 25

Nyimbo Na. 46

Mph. 5: Zilengezo zapamalopo.

Mph. 15: “Kodi Nkutsatiriranji Wotipatsa Chitsanzo Wamkulu?” Nkhani ya mkulu.

Mph. 10: Bokosi la Mafunso. Kambitsiranani ndi omvetsera.

Mph. 15: Fotokozani Mabuku Ogaŵira m’December. Gaŵirani New World Translation ndi buku lakuti Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? Mukumagwiritsira ntchito masamba 327-31 a buku la “All Scripture,” sonyezani kupambana kwa New World Translation: Imachirikiza ndi kutamanda dzina la Mulungu (ndime 1-2); mamasuliridwe ake owongoleredwa amachititsa malembo ake kumveka bwino kwambiri (ndime 6); ndiyo chiŵiya champhamvu chogwiritsira ntchito mu utumiki (ndime 22-3). Fotokozani ndi kusonyeza ulaliki wachidule, mukumagwiritsira ntchito malingaliro a patsamba 189 a Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? Muyenera kupanga makonzedwe enieni obwerera kulikonse kumene kuli munthu wosonyeza chidwi.

Nyimbo Na. 180 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena