Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/97 tsamba 7-8
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
km 2/97 tsamba 7-8

Zilengezo

◼ Mabuku ogaŵira mu February: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, kapena buku lililonse la masamba 192 limene mpingo ungakhale nalo m’stoko. March: Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. April ndi May: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! M’gawo limene limafoledwa kaŵirikaŵiri, mungagwiritsire ntchito brosha latsopano lakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?

◼ Mlembi ndi woyang’anira utumiki ayenera kupenda ntchito za apainiya onse okhazikika. Ngati ena zikuwavuta kukwanitsa maola ofunika, akulu akonze chithandizo chomwe angapereke. Kuti mupeze malingaliro, bwereranimo m’kalata ya Sosaite (S-201) ya October 1, 1993, ndi November 1, 1992. Onaninso ndime 12-20 za mphatika ya Utumiki Wathu Waufumu wa October 1986.

◼ Ofalitsa omwe akufuna kukhala apainiya othandiza mu March, April, ndi May apange makonzedwe awo tsopano ndi kupereka msanga mafomu awo ofunsirapo. Zimenezi zidzathandiza akulu kupanga makonzedwe ofunika a utumiki wakumunda ndi kukhala ndi magazini okwanira ndi mabuku ena. Maina a onse ovomerezedwa kukhala apainiya othandiza ayenera kulengezedwa kumpingo.

◼ Mipingo yonse imene maakaunti awo ali oipa iyenera kuwakonza. Iyenera kutsimikiza kuti yalipira ndalama zonse zopereŵera ndi maoda kuti itsegulenso maakaunti awo a mabuku ndi magazini. Zimenezi nzofunika kwambiri pakuti ndiyo njira yoperekera chakudya chauzimu kwa ofalitsa. Ndiponso, mipingo ija imene ili ndi mabuku alionse m’stoko iyenera kukumbutsa ofalitsa a mpingo kuti mabuku ndi magazini satengedwa pangongole kwa atumiki ake. Onse azilipira kashi. Zimenezi zidzathandiza kuti maakaunti anu asaipe.

◼ Zofalitsa Zomwe Zilipo:

Phunzirani Kuŵerenga ndi Kulemba—Chingelezi

Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo—Chipwitikizi

New World Translation of the Greek Scriptures—Chiswahili

Imbirani Yehova Zitamando (laling’ono)—Chipwitikizi

Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako—Chicheŵa, Chifrenchi, Chingelezi

Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja—Chipwitikizi

◼ Compact Disc Yatsopano Yomwe Ilipo:

Kingdom Melodies 1 (Chonde dziŵani kuti imeneyi si kaseti ayi koma disc imene imafuna makina ake. Disc imeneyo ili ndi nyimbo zimodzimodzi zimene zili pakaseti.)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena