Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/97 tsamba 7
  • Bokosi la Mafunso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Bokosi la Mafunso
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mwakonzekera Masoka Achilengedwe?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Mmene Tingathandizire Pakachitika Ngozi Zadzidzidzi
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
  • Muzithandiza Ena Kupirira pa Nthawi Zovuta
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Utumiki Wothandiza Anthu pa Nthawi ya Mavuto
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulira
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
km 2/97 tsamba 7

Bokosi la Mafunso

◼ Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuchita changu kupereka lipoti la utumiki wathu wakumunda mwezi uliwonse?

Tonse timasangalala pamene timva za zinthu zabwino zimene zikuchitidwa mwa kulalikira uthenga wa Ufumu. (Onani Miyambo 25:25.) Machitidwe 2:41 akusimba kuti Petro atapereka nkhani yake yokhudza mtimayo pa tsiku la Pentekoste, “anawonjezedwa . . . anthu ngati zikwi zitatu.” Patapita nthaŵi yochepa chabe, chiŵerengero chimenecho chinakula kufika “ngati zikwi zisanu.” (Machitidwe 4:4) Ayenera kuti anali osangalatsa chotani nanga malipoti amenewo kwa Akristu a m’zaka za zana loyamba! Timamvera mofananamo lerolino pakumva malipoti otero. Timakondwa kwenikweni pakumva za chipambano chimene abale athu akukhala nacho pakulalikira uthenga wabwino padziko lonse.

Popeza kuti kuonkhetsa malipotiwo ndi ntchito yaikulu ndipo nthaŵi yochuluka imatayidwapo, kutsatira malangizo kwa wofalitsa aliyense wa Ufumu kumakhala kofunika kwambiri. Kodi mumakumbukira kupereka lipoti lanu mwachangu mwezi uliwonse?

Malipoti onena za chiwonjezeko amasangalatsa kwambiri. Ndiponso, malipoti amathandiza Sosaite kudziŵa mmene ntchito ikupitira patsogolo padziko lonse. Zigamulo ziyenera kupangidwa ponena za kumene kungafunikire chithandizo chokulirapo kapena mtundu wa mabuku ndi unyinji wa amene ayenera kufalitsidwa. Akulu mumpingo amagwiritsira ntchito malipoti kuti adziŵe mbali zofunikira kuwongolera. Malipoti abwino amamangirira, amasonkhezera tonsefe kupenda utumiki wathuwathu kuona mmene tingawongolere.

Ofalitsa onse afunikira kuzindikira thayo la munthu aliyense payekha la kupereka lipoti la utumiki wakumunda mwachangu mwezi uliwonse. Ochititsa Phunziro la Buku la Mpingo ali m’malo abwino akukumbutsa ofalitsa za thayo limeneli, pakuti amakhalanso maso kuti apereke chithandizo chaumwini kwa awo omwe angakhale ndi vuto la kusakhala ndi phande mu utumiki wakumunda mokhazikika mwezi uliwonse. Chikumbutso chimenechi chingaperekedwe paphunziro la buku lomaliza mwezi uliwonse kapena panthaŵi ina yoyenera. Ngati ena sanapeze mpata wa kupereka lipoti la utumiki wakumunda pa Nyumba ya Ufumu, wochititsa Phunziro la Buku la Mpingo angasonkhanitse malipotiwo ndi kuwapatsa kwa mlembi nthaŵi idakalipo kuti awaphatikize pa lipoti la mpingo la mwezi ndi mwezi ku Sosaite.

Khama lathu la kupereka lipoti lathu la utumiki wakumunda mokhulupirika ndi mwachangu limapeputsa mtolo wa aja amene ali ndi thayo lotisamalira mwauzimu.

◼ Kodi tiyenera kuchitanji pamene kwagwa tsoka lokhudza abale athu?

Ngati Tsoka Lachitika Kudera Lanu: Musatekeseke. Khazikani mtima pansi, ndipo ingoganizani za chimene chilidi chamtengo wapatali—moyo, osati chuma. Samalirani zosoŵa zakuthupi za banja lanu zapanthaŵiyo. Ndiyeno dziŵitsani akulu za mkhalidwe wanu ndi kumene muli. Akulu ndi atumiki otumikira amachita zofunika kwambiri popereka thangato. Ngati chenjezo la tsokalo laperekedwa pasadakhale, monga momwe zimakhalira ndi mikuntho yaikulu, abale ameneŵa ayenera kuona kuti aliyense ali kumalo otetezereka, ndipo ngati nthaŵi ilola, ayenera kugula zofunikira ndi kuzigaŵira.

Ndiyeno, ochititsa phunziro la buku ayenera kupeza kumene kuli banja lililonse ndi kuona ngati ali bwino. Woyang’anira wotsogoza kapena mkulu wina ayenera kudziŵitsidwa za mkhalidwe wa banja lililonse, ngakhale ngati zonse zili bwino. Ngati wina wavulala, akulu adzayesa kulinganiza za mankhwala. Adzaperekanso zilizonse zofunika monga chakudya, zovala, malo, kapena zinthu zogwiritsira ntchito panyumba. (Yoh. 13:35; Agal. 6:10) Akulu akumaloko adzapereka chichirikizo chauzimu ndi chilimbikitso pampingowo ndipo adzakonza zinthu msanga kuti misonkhano ya mpingo iyambenso. Pambuyo popenda zonse mosamala, mkulu woimira bungwe la akulu ayenera kudziŵitsa woyang’anira dera, ngati angamdziŵitse mosavuta, za aliyense wovulala, kuwonongeka kwa Nyumba ya Ufumu, kapena kwa nyumba za abale, ndiponso za zosoŵa zilizonse zapadera. Woyang’anira deranso adzaimbira foni ofesi ya nthambi kupereka lipoti la mkhalidwewo. Ngati sizitheka kudziŵitsa woyang’anira dera, pamenepo woyang’anira wotsogoza, kapena mkulu wina, ayenera kudziŵitsa ofesi ya nthambi patelefoni, ngati kutheka. Ngati kulibe telefoni, chonde gwiritsirani ntchito njira iliyonse yamwamsanga yodziŵitsira Sosaite. Ofesi ya nthambi idzayang’anira ntchito iliyonse yaikulu yopereka thangato lofunikira.

Ngati Tsoka Lachitika Kwina: Kumbukirani abale ndi alongo m’mapemphero anu. (2 Akor. 1:8-11) Ngati mukufuna kupereka thandizo la ndalama, mungatumize zopereka zanu ku Sosaite, kumene kuli thumba la thangato lapadera la ntchito imeneyi. Nayi keyala yake: Watch Tower Bible & Tract Society, P.O. Box 30749, Lilongwe 3. (Mac. 2:44, 45; 1 Akor. 16:1-3; 2 Akor. 9:5-7; onani Nsanja ya Olonda ya June 15, 1986, masamba 20-2.) Musatumize zinthu kapena katundu kudera kumene kuli tsoka ngati abale oyang’anira sanakupempheni. Zimenezi zidzachititsa kuti pakhale dongosolo labwino loperekera thangato ndi kuti katunduyo agaŵiridwe moyenera. (1 Akor. 14:40) Chonde musaimbire foni Sosaite mosafunikira, pakuti zimenezi zingatsekereze mafoni ena ofunika ochokera kudera la tsokalo.

Kufufuza koyenera kutachitika, Sosaite idzaona ngati komiti yopereka chithandizo iyenera kupangidwa. Abale athayo adzadziŵitsidwa. Onse ayenera kugwirizana ndi akulu otsogolera kuti zosoŵa zofunika kwambiri za abale onse zipezeke zokwanira.—Onani Jehovah’s Witnesses—Proclaimers of God’s Kingdom, masamba 310-15.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena