Kulalikira Uthenga Wabwino Mwachangu
1 Timasonyeza kuti tikuyamikira kwambiri malonjezo a Mulungu a Ufumu mwa kukhala ndi phande ndi mtima wonse pautumiki wachikristu. Tiyenera kuchita ntchito imeneyi mwachangu. Chifukwa ninji? Chifukwa antchito ngoŵerengeka, mapeto a dongosolo ili la zinthu ali pafupi, ndipo moyo wa amene ali m’gawo lathu uli pangozi. (Ezek. 3:19; Mat. 9:37, 38) Thayo lolemera kwambiri limenelo limafuna kuti tichite zomwe tingathe mu utumiki. Kodi tingachisonyeze motani changu pantchito yathu ya utumiki wakumunda? Mwa kukonza maulaliki abwino pasadakhale, mwa kuchita khama pofunafuna anthu kulikonse kumene angapezeke, mwa kusunga cholembapo cholongosoka cha onse osonyeza chidwi, mwa kubwerera kwa iwo msanga kukakulitsa chidwi chimenecho, ndipo mwa kukumbukira kuti popeza moyo uli pangozi, tiyenera kuchita utumiki wathu mosamala. Malingaliro otsatira angatithandize pamene tikukonzekera kulalikira uthenga wabwino mwachangu m’February. Buku logaŵira lidzakhala Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha.
2 Mungayambe kukambitsirana mwa kutchula mwachidule mavuto ena amene ali m’chitaganya, ndiyeno munganene kuti:
◼ “Anthu ambiri amakhulupirira kuti Mulungu aliko, koma amafunsa kuti: ‘Kodi amatifunira mtsogolo motani?’ Kodi mungayankhe bwanji? [Yembekezerani yankho.] Kodi mudziŵa kuti Baibulo limafotokoza bwino chifuniro cha Mulungu kwa anthu ndi zimene iye akuchita kuti achikwaniritse?” Tsegulani patsamba 187 m’buku la Chidziŵitso. Ŵerengani Chivumbulutso 21:1-4 m’ndime 19 ndiyeno ŵerengani ndi kufotokoza ndimeyo. Pitani pachithunzithunzi chili pamasamba 188 ndi 189 kuti musonyeze mmene mtsogolo mwathu mudzakhalira. Ndiyeno gaŵirani bukulo pachopereka cha K12.00. Panganani nthaŵi yabwino yobweranso kudzapitiriza kukambitsirana kumeneko.
3 Mungapitirize kukambitsirana kwanu koyamba pa Chivumbulutso 21:1-4 ndi ulalikiwu wachidule:
◼ “Ulendo wapita, tinakambitsirana za makonzedwe a Mulungu odalitsira anthu. [Sonyezaninso chithunzithunzi chili patsamba 188 ndi 189 m’buku la Chidziŵitso.] Kodi mukufuna kudzaliona banja lanu likusangalala ndi mikhalidwe yotere? [Yembekezerani yankho.] Tsono funso nlakuti, ‘Kodi tiyenera kuchitanji kuti tikapeze chimwemwe cholonjezedwa chimenechi? Tamvetserani zimene buku ili likunena patsamba 191.” Ŵerengani funso losindikiza la ndime 24 ndi 25 patsamba 191, ndiyeno ŵerengani lemba limodzi kapena aŵiri m’ndime yomaliza. Mpempheni kuphunzira naye Baibulo kwaulere. Linganizani kudzamsonyeza pambuyo pake.
4 Popeza ambiri akuda nkhaŵa ndi mavuto owonjezereka amene anthu akukumana nawo, munganene zonga izi paulendo woyamba:
◼ “Ambiri amene ndakumana nawo akuda nkhaŵa ndi mavuto amene tikukumana nawo kwathu kuno. [Tchulanipo angapo.] Zaka zambiri andale alonjeza kuti adzabweretsa njira zowathetsera, ndipo ena ayesa kutero. Kodi mukuganiza chothetsera mavutowo nchiyani? [Yembekezerani yankho.] Baibulo limafotokoza chifukwa chake chimene anthu ochuluka sanachilingalirepo. Buku la Danieli limafotokoza zimene Ufumu wa Mulungu udzachita pobweretsa mtendere m’chitaganya chathu. Onani zimene udzachita, zotchulidwa pa Danieli 2:44.” Liŵerengeni vesilo, ndiyeno tsegulani buku la Chidziŵitso patsamba 95. Ŵerengani ndime 13 ndipo fotokozani Yesaya 55:11. Ndiyeno gaŵirani bukulo pachopereka cha K12.00. Panganani za kubweranso kudzakambitsirana mmene Mulungu adzathetsera mavuto a anthu.
5 Ngati munalonjeza kuti mudzafikanso kudzafotokoza njira ya Mulungu yothetsera mavuto a lerolino, mungayese kafikidwe aka:
◼ “Ndayesetsa kufikanso kuti tipitirizebe kukambitsirana za njira yeniyeni yothetsera mavuto a anthu. Ulendo watha uja, tinaona zimene Ufumu wa Mulungu udzachita pobweretsa mtendere wachikhalire m’chitaganya chathu. Popeza mikhalidwe ya dziko ikuipiraipira, kodi tingatsimikize motani kuti tidzapindula ndi madalitso ameneŵa? [Yembekezerani yankho.] Tamverani zimene Baibulo likunena.” Ŵerengani ndi kufotokoza Luka 21:34-36 patsamba 107, ndime 17. Ndiponso mwa kugwiritsira ntchito chithunzithunzi chili pamasamba 100-101 m’buku la Chidziŵitso, limbikitsani mwini nyumba kuphunzira zambiri m’Baibulo ponena za tanthauzo la mikhalidwe ya dziko lerolino. Pemphani kuphunzira naye Baibulo ndipo yesani kuyamba phunzirolo pompo.
6 Popeza anthu ambiri akuchita chidwi ndi nkhani za malo okhala, munganene zonga zotsatirazi poyambitsa kukambitsirana:
◼ “Tapeza kuti pafupifupi aliyense akuda nkhaŵa ndi kuipa kwa mpweya, madzi, ndi chakudya. Kumaiko ena mkhalidwe wa malo okhala waika kale moyo pangozi. Popeza Mulungu ndiye Mlengi wa dziko lapansi, kodi muganiza adzachitanji? [Yembekezerani yankho.] Baibulo limanena kuti Mulungu adzaŵerengera mlandu panjira imene timagwiritsira ntchito pulaneti lino. [Ŵerengani Chivumbulutso 11:18b.] Taganizani zokhala padziko lapansi lopanda zoipitsa zonse!” Tchulani lonjezo la Mulungu la paradaiso, losonyezedwa pa Chivumbulutso 21:3, 4. Sonyezani chithunzithunzi chili pamasamba 188-9 m’buku la Chidziŵitso. Gaŵirani bukulo pachopereka cha K12.00 ndi kupangana zobweranso.
7 Pobwerera kwa munthu amene anachita chidwi ndi dziko lapansi la paradaiso, munganene kuti:
◼ “Ulendo watha uja, tinavomerezana kuti pofuna kuthetsa vuto la kuipitsa dziko lapansi, Mulungu adzaloŵerera pazochita za munthu. Koma nali funso, Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tipulumuke ndi kuloŵa m’dziko latsopano lolungama lopangidwa ndi Mulungu?” Ŵerengani Yohane 17:3. Pemphani mwini nyumba kuti agwiritsire ntchito mwaŵi wa kosi yathu yaulere ya phunziro la Baibulo kuti apeze chidziŵitso chapadera chimenechi.
8 Mmene tilili amwaŵi nanga pogwiritsiridwa ntchito monga antchito yotuta amakono ndi pochita ntchito yolalikira yopulumutsa moyo! Ife tonse tikhale otanganidwa ndi kulalikira uthenga wabwino mwachangu, ‘podziŵa kuti kuchititsa kwathu sikuli chabe.’—1 Akor. 15:58.