Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Akorinto 14
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

Zimene Zili Mʼbuku la 1 Akorinto

      • Mphatso yonenera ndiponso yolankhula malilime (1-25)

      • Misonkhano izichitika mwadongosolo (26-40)

        • Zimene akazi ayenera kuchita mumpingo (34, 35)

1 Akorinto 14:1

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1At 5:20

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    10/15/1993, tsa. 31

1 Akorinto 14:2

Mawu a M'munsi

  • *

    Kapena kuti, “chilankhulo chachilendo.”

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1Ak 14:5
  • +1Ak 13:2

1 Akorinto 14:3

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    10/15/2010, ptsa. 24-25

1 Akorinto 14:4

Mawu a M'munsi

  • *

    Kapena kuti, “chilankhulo chachilendo.”

1 Akorinto 14:5

Mawu a M'munsi

  • *

    Kapena kuti, “zilankhulo zachilendo.”

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1Ak 12:30
  • +Yow 2:28; Mac 2:17; 21:8, 9

1 Akorinto 14:6

Mawu a M'munsi

  • *

    Kapena kuti, “zilankhulo.”

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Aga 1:11, 12; 2:2
  • +1Ak 12:8

1 Akorinto 14:8

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    12/15/2015, tsa. 21

1 Akorinto 14:9

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    12/15/2015, tsa. 21

1 Akorinto 14:12

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1Ak 12:7; 14:4, 26

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    4/15/2007, ptsa. 23-24

1 Akorinto 14:13

Mawu a M'munsi

  • *

    Kapena kuti, “chilankhulo chachilendo.”

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1Ak 12:8, 10; 14:5

1 Akorinto 14:14

Mawu a M'munsi

  • *

    Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmalilime.”

1 Akorinto 14:18

Mawu a M'munsi

  • *

    Mʼchilankhulo choyambirira, “malilime.”

1 Akorinto 14:19

Mawu a M'munsi

  • *

    Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmalilime.”

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1Ak 14:4

1 Akorinto 14:20

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Aef 4:14
  • +Aro 16:19
  • +Ahe 5:13, 14

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    2/1/2007, tsa. 11

    7/15/1993, tsa. 20

    11/15/1987, tsa. 20

1 Akorinto 14:21

Mawu a M'munsi

  • *

    Onani Zakumapeto A5.

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Yes 28:11, 12

1 Akorinto 14:22

Mawu a M'munsi

  • *

    Kutanthauza kulankhula zilankhulo zosiyanasiyana modabwitsa.

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 2:4, 13

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo,

1 Akorinto 14:24

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    11/15/1988, ptsa. 13, 15-16

1 Akorinto 14:25

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Yes 45:14; Zek 8:23

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    11/15/1988, ptsa. 15-16, 20

1 Akorinto 14:26

Mawu a M'munsi

  • *

    Kapena kuti, “nyimbo zotamanda Mulungu.”

  • *

    Kapena kuti, “chilankhulo chachilendo.”

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1Ak 12:8, 10

1 Akorinto 14:27

Mawu a M'munsi

  • *

    Kapena kuti, “chilankhulo chachilendo.”

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1Ak 14:5

1 Akorinto 14:29

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 13:1

1 Akorinto 14:31

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Ahe 10:24, 25

1 Akorinto 14:33

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1Ak 14:40; Akl 2:5

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale, lesson 20

    Ufumu wa Mulungu Ukulamulira, tsa. 120

1 Akorinto 14:34

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1Ti 2:11, 12
  • +1Ak 11:3; Aef 5:22; Akl 3:18; Tit 2:5; 1Pe 3:1

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    9/1/2012, tsa. 9

    3/1/2006, ptsa. 28-29

    Kukambitsirana, tsa. 29

1 Akorinto 14:35

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    3/1/1989, tsa. 6

1 Akorinto 14:36

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    6/1/2011, tsa. 14

1 Akorinto 14:37

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    10/15/1993, tsa. 31

1 Akorinto 14:38

Mawu a M'munsi

  • *

    Mabaibulo ena amati, “ngati wina angakhale wosadziwa, akhalebe wosadziwa.”

1 Akorinto 14:39

Mawu a M'munsi

  • *

    Kapena kuti, “chilankhulo chachilendo.”

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1At 5:20
  • +1Ak 14:27

1 Akorinto 14:40

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1Ak 14:33; Akl 2:5

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale, lesson 54

    Galamukani!,

    No. 1 2020 tsa. 10

    ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’, tsa. 49

    Nsanja ya Olonda,

    8/1/1997, tsa. 9

Mabaibulo Ena

Dinani pa nambala ya vesi kuti muone mavesi a m'Baibulo lina ofanana ndi vesilo.

Malemba Ena

1 Akor. 14:11At 5:20
1 Akor. 14:21Ak 14:5
1 Akor. 14:21Ak 13:2
1 Akor. 14:51Ak 12:30
1 Akor. 14:5Yow 2:28; Mac 2:17; 21:8, 9
1 Akor. 14:6Aga 1:11, 12; 2:2
1 Akor. 14:61Ak 12:8
1 Akor. 14:121Ak 12:7; 14:4, 26
1 Akor. 14:131Ak 12:8, 10; 14:5
1 Akor. 14:191Ak 14:4
1 Akor. 14:20Aef 4:14
1 Akor. 14:20Aro 16:19
1 Akor. 14:20Ahe 5:13, 14
1 Akor. 14:21Yes 28:11, 12
1 Akor. 14:22Mac 2:4, 13
1 Akor. 14:25Yes 45:14; Zek 8:23
1 Akor. 14:261Ak 12:8, 10
1 Akor. 14:271Ak 14:5
1 Akor. 14:29Mac 13:1
1 Akor. 14:31Ahe 10:24, 25
1 Akor. 14:331Ak 14:40; Akl 2:5
1 Akor. 14:341Ti 2:11, 12
1 Akor. 14:341Ak 11:3; Aef 5:22; Akl 3:18; Tit 2:5; 1Pe 3:1
1 Akor. 14:391At 5:20
1 Akor. 14:391Ak 14:27
1 Akor. 14:401Ak 14:33; Akl 2:5
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
  • Werengani mu Baibulo la Dziko Latsopano
  • 1
  • 2
  • 3
  • 4
  • 5
  • 6
  • 7
  • 8
  • 9
  • 10
  • 11
  • 12
  • 13
  • 14
  • 15
  • 16
  • 17
  • 18
  • 19
  • 20
  • 21
  • 22
  • 23
  • 24
  • 25
  • 26
  • 27
  • 28
  • 29
  • 30
  • 31
  • 32
  • 33
  • 34
  • 35
  • 36
  • 37
  • 38
  • 39
  • 40
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
1 Akorinto 14:1-40

Kalata Yoyamba Yopita kwa Akorinto

14 Mukhale ndi chikondi koma muziyesetsanso kuti mulandire mphatso za mzimu woyera, makamaka mphatso ya kunenera.+ 2 Chifukwa wolankhula malilime* salankhula ndi anthu, koma ndi Mulungu. Palibe amene amamva zonena zake,+ koma iye amalankhula zinsinsi zopatulika+ mothandizidwa ndi mzimu. 3 Komabe, wonenera amathandiza anthu ndipo amawalimbikitsa komanso kuwatonthoza ndi mawu ake. 4 Wolankhula malilime* amadzilimbikitsa yekha, koma wonenera amalimbikitsa mpingo. 5 Ndikanakondadi kuti nonsenu muzilankhula malilime,*+ koma ndikuona kuti ndi bwino kuti muzinenera.+ Kunena zoona, wonenera amaposa wolankhula malilime, kupatulapo ngati wamalilimeyo akumasulira kuti alimbikitse mpingo. 6 Abale, kodi mungapindule chiyani ngati pa nthawi ino nditabwera kwa inu ndikulankhula malilime* amene simukuwadziwa? Zingakhale zothandiza ngati ndingabwere ndi mawu amene ndalandira kuchokera kwa Mulungu,+ kapena mphatso yodziwa zinthu,+ kapena ulosi kapenanso chiphunzitso.

7 Nʼzofanana ndi zipangizo zoimbira ngati chitoliro kapena zeze. Ngati maliridwe ake atangokhala amodzi osasinthasintha, kodi nʼzotheka kudziwa nyimbo imene ikuimbidwa ndi chitoliro kapena zezeyo? 8 Ngati lipenga silikulira momveka bwino, ndani angakonzekere nkhondo? 9 Nʼchimodzimodzinso ngati mukulankhula zosamveka. Kodi munthu angadziwe bwanji zimene mukunena? Mudzakhala kuti mukulankhula kwa mphepo. 10 Padziko lapansi pali zilankhulo zambiri, koma palibe chimene chilibe tanthauzo. 11 Ngati sindikudziwa tanthauzo la chilankhulo, ndimakhala mlendo kwa wolankhulayo, ndipo wolankhulayo amakhala mlendo kwa ine. 12 Chimodzimodzinso ndi inuyo. Popeza mukufunitsitsa mphatso za mzimu, yesetsani kukhala ndi mphatso zimene zingalimbikitse mpingo.+

13 Choncho amene amalankhula malilime* apemphere kuti athe kumasulira.+ 14 Chifukwa ngati ndikupemphera mʼchilankhulo chachilendo,* mphatso yanga ya mzimu ndi imene ikupemphera, koma maganizo anga sakuchita chilichonse. 15 Ndiye chofunika nʼchiyani? Ndiyenera kupemphera ndi mphatso ya mzimu, koma ndipempherenso ndi mawu omveka. Ndiimbe nyimbo zotamanda ndi mphatso ya mzimu, koma ndiimbenso ndi mawu omveka. 16 Chifukwa ngati mothandizidwa ndi mphatso ya mzimu mukutamanda Mulungu, kodi munthu wamba anganene bwanji kuti “Ame” pa pemphero lanu loyamikira, poti sakudziwa zimene mukunena? 17 Nʼzoona kuti mukupereka pemphero loyamikira mʼnjira yabwino, koma munthu winayo sakulimbikitsidwa. 18 Ndimathokoza Mulungu kuti ndimalankhula zilankhulo zambiri* kuposa nonsenu. 19 Ngakhale zili choncho, ndi bwino kuti mumpingo ndilankhule mawu 5 omveka kuti ndiphunzitse anthu ena, kusiyana nʼkulankhula mawu 10,000 mʼchilankhulo chachilendo.*+

20 Abale, musakhale ana aangʼono pa nkhani yomvetsa zinthu.+ Koma khalani ana pa zoipa,+ ndipo pa nkhani yomvetsa zinthu khalani anthu akuluakulu.+ 21 MʼChilamulo muli mawu akuti: “‘Anthu awa ndidzawalankhula ndi malilime a anthu achilendo, ndipo ndidzawalankhula ndi milomo ya anthu achilendo, koma iwo adzakana kundimvera,’ watero Yehova.”*+ 22 Choncho malilime* ndi chizindikiro cha osakhulupirira, osati okhulupirira,+ pomwe kunenera ndi chizindikiro cha okhulupirira, osati osakhulupirira. 23 Ndiye ngati mpingo wonse wasonkhana ndipo onse akulankhula malilime, ndiyeno mwalowa anthu wamba kapena osakhulupirira, kodi sadzanena kuti mitu yanu sikugwira? 24 Koma ngati nonse mukunenera, ndiyeno mwalowa munthu wosakhulupirira kapena munthu wamba, iye amadzudzulidwa ndiponso kufufuzidwa mosamala ndi nonsenu. 25 Amadziwa zinthu zobisika zamumtima mwake, moti adzawerama nʼkulambira Mulungu, ndi kunena kuti: “Zoonadi Mulungu ali pakati panu.”+

26 Ndiyeno zizikhala bwanji abale? Mukasonkhana pamodzi, wina akhoza kukhala ndi salimo,* wina chiphunzitso, wina mawu amene walandira kuchokera kwa Mulungu komanso wina akhoza kulankhula malilime* wina nʼkumamasulira.+ Muzichita zonsezi kuti mulimbikitsane. 27 Ngati pali anthu olankhula malilime,* asapose awiri kapena atatu ndipo azipatsana mpata komanso wina azimasulira.+ 28 Koma ngati palibe womasulira, wa malilimeyo akhale chete mumpingo ndipo azilankhula ndi Mulungu chamumtima. 29 Aneneri+ awiri kapena atatu alankhule, ndipo ena onse aziyesetsa kumvetsa tanthauzo la zimene iwo akulankhulazo. 30 Koma ngati mneneri wina amene wakhala pansi walandira mawu kuchokera kwa Mulungu, woyamba uja akhale chete. 31 Nonse mukhoza kunenera, koma muyenera kupatsana mpata kuti onse aphunzire ndiponso kulimbikitsidwa.+ 32 Ndipo aneneri akamagwiritsa ntchito mphatso za mzimu ayenera kukhala odziletsa. 33 Chifukwa Mulungu si Mulungu wachisokonezo, koma wamtendere.+

Ngati mmene zilili mʼmipingo yonse ya oyerawo, 34 akazi azikhala chete mʼmipingo, chifukwa nʼzosaloleka kuti iwo azilankhula,+ koma azigonjera,+ ngati mmenenso Chilamulo chimanenera. 35 Ngati akufuna kumvetsa zinazake, akafunse amuna awo kunyumba, popeza nʼzochititsa manyazi kuti mkazi azilankhula mumpingo.

36 Kodi mawu a Mulungu anachokera kwa inu, kapena ndi inu nokha amene munauzidwa mawuwo?

37 Ngati munthu akuganiza kuti ndi mneneri kapena ali ndi mphatso ya mzimu, ayenera kuvomereza kuti zimene ndakulemberanizi ndi lamulo la Ambuye. 38 Koma ngati wina savomereza zimenezi, iyenso sadzavomerezedwa.* 39 Choncho abale anga, yesetsani kuti muzinenera,+ komabe musaletse kulankhula malilime.*+ 40 Koma zinthu zonse zizichitika moyenera ndiponso mwadongosolo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena