Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 3/1 tsamba 4-7
  • Kodi Ndani Kwenikweni Amene Ali Atumiki a Mulungu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndani Kwenikweni Amene Ali Atumiki a Mulungu?
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chikhulupiriro m’Baibulo
  • Atumiki Owona ndi Khalidwe Labwino
  • Atumiki Owona Amaphunzitsa Ziphunzitso Zowona
  • Zofunika za m’Malemba za Atumiki Owona
  • Kodi Akazi Ayenera Kuikidwa?
  • Yesu Kristu​—Chitsanzo Chowala
  • Kuthandiza Osauka, Odwala, ndi Oklamba
  • Kukwaniritsa Ulosi wa Baibulo
  • Kodi Atumiki a Mulungu Ndani Lerolino?
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Mmene Mungazindikirire Atumiki Owona a Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Kodi Akazi a Mboni za Yehova Amaphunzitsa Mawu a Mulungu?
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Gawo 1—Kodi Yesu ndi Ophunzira Ake Anaphunzitsa Chiphunzitso cha Utatu?
    Nsanja ya Olonda—1991
Nsanja ya Olonda—1989
w89 3/1 tsamba 4-7

Kodi Ndani Kwenikweni Amene Ali Atumiki a Mulungu?

“MU ORA losankha iri tikuchenjeza asilikali athu a Chikatolika kuchita ntchito yawo m’chimvero kwa Fuehrer [Hitler].”​—Abishopu a Chikatolika a ku Germany, monga momwe kunagwidwira mawu mu The New York Times, September 25, 1939.

“Mudziŵa, abambo, pa ndege yathu mmodzi wa ziwalo za gulu lathu wogwira ntchito mmenemo ali m’Katolika, ndipo mumudalitsa iye tisananyamuke kupita pa ulendo wokaphulitsa mabomba pa Germany. Tsopano, chipembedzo chimodzimodzicho cha Chikatolika mu Germany chikudalitsa chiwalo chogwira ntchito cha Chikatolika cha ndege yankhondo ya chiGerman yomwe ikubwera ndi kudzawononga mizinda yathu. Chotero funso lomwe ndikufunsa liri, ‘Kodi Mulungu ali kumbali ya ndani?’” Inalankhula tero nduna yowuluka ndi ndege ya chiBritish, David Walker, m’kukambitsirana ndi wansembe wa Chikatolika mkati mwa Nkhondo ya Dziko ya II.

Mosiyana, zikwi za Mboni za Yehova zathera zaka m’misasa ya chibalo yowopsya ya chiNazi chifukwa chokana kunena kuti heil Hitler kapena kumenya m’magulu ake ankhondo. M’maiko Ogwirizana, Mboni zambiri zinaikidwa m’ndende chifukwa chokana utumiki wankhondo.

Ndani amene ali atumiki owona a Mulungu, ndipo ndi zofunika zotani zomwe ayenera kuzikumaniza?

Chikhulupiriro m’Baibulo

Mtumiki wowona wa Mulungu ayenera mwachidziŵikire kukhala ndi chikhulupiriro cholimba m’Baibulo. Iye ayeneranso kulidziŵa bwino mokwanira kuti aliphunzitse kwa ena. Koma ambiri a atsogoleri a chipembedzo a Chikristu cha Dziko samakwaniritsa zifuno zoyambirira zimenezo. Dokotala wa zamankhwala mu South Africa ananena kuti atumiki a Tchalitchi cha Anglican, ku chimene iye anali chiwalo chake, anapanga “kugwiritsira ntchito kochepa” kwa Baibulo, ndipo maulalikiwo anawoneka kukhala lingaliro laumwini la wolalikirayo. Iye anadandaulanso ponena za ziwalo za atsogoleri a chipembedzowo, monga ngati Archbishop Tutu wa ku Cape Town, chifukwa cha kudziloŵetsa m’ndale zadziko.

Mosiyana, atumiki okhulupirika a Yehova molimba amakhulupirira Baibulo ndi kuthera yochulukira ya nthawi yawo kuphunzira ilo ndi kulongosola ilo kwa ena. Chikondwerero chawo m’Baibulo ndi chikondi kaamba ka ilo ziri zozama kotero kuti iwo atulutsa kutembenuza kofufuzidwa mosamalitsa ndi kolongosoka kotchedwa New World Translation of the Holy Scriptures, kozikidwa pa mamanusikripiti a Baibulo otsimikiziridwa a Chihebri, Aramaic, ndi Griki. Baibulo limeneli mu Reference Edition yake liri ndi zikwi za mawu a m’munsi ndi zilozero ku malemba ena kuthandiza oŵerenga kumvetsetsa Baibulo moposerapo ndi kuwatheketsa iwo kulongosola ilo kwa ena. M’kuwonjezerapo, kutembenuza Baibulo kwapadera kumeneku kwatembenuzidwa, konse kapena m’mbali yake, m’zinenero zina 10, ndipo makumi a mamiliyoni a makope agawiridwa dziko lonse.

Atumiki Owona ndi Khalidwe Labwino

Baibulo limatsutsa mwamphamvu mtundu uliwonse wa chimo la kugonana​—kuphatikizapo chigololo, dama, kugonana kwa ofanana ziwalo, ndi kugonana ndi zinyama. (Levitiko 20:10-15; Aroma 1:26, 27; Agalatiya 5:19) Atumiki owona Achikristu mwa mtima wonse amasungirira miyezo ya Mulungu ya makhalidwe abwino. Inde, Mboni za Yehova zimatenga lamulo la Mulungu mosamalitsa. Iwo amachotsa mu mpingo awo amene mosalapa amachita machimo oterowo, pamene amasonyeza chifundo kwa awo omwe mowonadi amalapa za machitidwe awo oipa ndi kuyeretsa miyoyo yawo.​—1 Akorinto 5:11-13; 2 Akorinto 2:5-8.

Mu South Africa, Mkulu wa Ansembe wa Anglican wa ku Cape Town akusimbidwa kukhala ananena kuti: “Maunansi ena a ziwalo zofanana ali abwinopo kuposa mbali inzake ya ziwalo zosiyana ndipo chifukwa cha mtundu wachikondi, ndiri wotsimikizira kuti amapanga Mulungu kukhala wokondwera koposa.” Chosiyanako chiri chowona. Mulungu amadana ndi maunansi oterowo.​—1 Akorinto 6:9, 10.

Atumiki Owona Amaphunzitsa Ziphunzitso Zowona

Atumiki owona amaphunzitsa ziphunzitso zomwe ziri zozikidwa mwamphamvu pa Mawu a Mulungu. Atumiki onyenga amaphunzitsa ziphunzitso zomwe ziribe chirikizo kapena maziko m’Baibulo. Lingalirani, mwachitsanzo, chiphunzitso cha Utatu. Monga momwe The Encyclopædia Britannica (15th Edition) ikulongosolera: “Osati ngakhale liwu lakuti Utatu kapena chiphunzitso chenichenicho chimawoneka mu Chipangano Chatsopano, ndipo Yesu ndi ophunzira ake sanafune kutsutsa Shema m’Chipangano Chakale: ‘Imvani, Israyeli: Ambuye Mulungu wathu ali Mbuye mmodzi’ (Deut. 6:4).” Utatu sunakhale chiphunzitso chalamulo cha tchalitchi kufikira zana lachinayi C.E. M’chenicheni, chinali ku mbali ina chifukwa cha kunyada ndi chisonkhezero cha wolamulira Wachiroma Constantine kuti chiphunzitso chonyengacho chinayamba kupangidwa pa Bungwe la Nicaea mu 325 B.C.E.

Chiphunzitso cha Utatu chapangitsa ziwalo zambiri za tchalitchi, ofuna chowonadi owona mtima, kutaya chidaliro mu atumiki awo. Ichi chinali chowona ponena za mkazi wachichepere mu South Africa yemwe sakanakhulupirira kuti chipembedzo chake, Dutch Reformed Church, chinaphunzitsa chiphunzitso chosokoneza monga cha Utatu kufikira pamene mmodzi wa Mboni za Yehova anapereka kwa iye umboni wolembedwa wakuti umu ndi mmene ziriridi! Loya wokalamba woleka kugwira ntchito, nayenso wa ku South Africa, anachoka ku tchalitchi chake chifukwa “ziphunzitso zosiyanasiyana zongobwerezabwereza zophunzitsidwa m’matchalitchi ziri zolakwika ndi zosokeretsa kotheratu.”

Chiphunzitso china chonyenga cha Chikristu cha Dziko chiri chija cha moto wa helo. Ngakhale kuti sichikulalikidwa mofala kapena kukhulupiridwa monga mmene chinaliri, icho chidakali chiphunzitso cholamulira cha matchalitchi ambiri. Awa amadzinenera kuti pa imfa thupi limafa koma moyo, ukumakhala wosakhoza kufa, umapitirizabe kukhala ndi moyo, ndipo awo omwe anatsogoza moyo woipa amazunzidwa mu moto woyaka kwa nthawi yonse. Kodi mumakhulupirira chimenecho? Chofunika koposa, kodi icho nchowona? Osati mogwirizana ndi Baibulo, lomwe limanena kuti: “Moyo wochimwawo ndiwo udzafa.” (Ezekieli 1:4, 20) M’kuwonjezerapo, mtumwi Paulo wowuziridwa analemba kuti: “Mphoto yake ya chimo ndi imfa”​—osati moto wa helo!​—Aroma 6:23.

Tiyeni tsopano tilingalire miyezo imene atumiki Achikristu owona ayenera kuifikiritsa.

Zofunika za m’Malemba za Atumiki Owona

Liwu la Chingelezi lakuti “minister” (mtumiki) liri matembenuzidwe a liwu la Chigriki lakuti “di·aʹko·nos,” lomwe liri ndi chiyambi chosatsimikizirika. Ilo limalozera kwa wina yemwe amachita malamulo a wina, mwachindunji mbuye. Chotero, liwu la m’Baibulo limazindikiritsa mwachindunji wantchito. Kugwiritsira ntchito kwa liwulo m’Baibulo kumasonyeza kuti wina samaleka m’kupereka mautumiki otheratu modzichepetsa m’malo mwa ena. Yesu anagogomezera chifuno kaamba ka utumiki wodzichepetsa woterowo, monga mmene chitsanzo chotsatirachi chikusonyezera.

Tsiku lina, mwamsanga imfa ya Yesu isanachitike pa mtengo wozunzirapo, amayi a Yakobo ndi Yohane anafikira iye ndi kunena kuti: “Lamulirani kuti ana anga aŵiri amenewa adzakhale, wina ku dzanja lanu lamanja, ndi wina kulamanzere, mu ufumu wanu.” Ophunzira ena anavutika mtima ndi ichi. Kenaka Yesu mwachifundo anaphunzitsa iwo phunziro lofunika koposa. Iye anasonkhanitsa iwo pamodzi ndi kunena kuti: “Amene aliyense akafuna kukhala wamkulu mwa inu, adzakhala mtumiki wanu; ndipo amene aliyense akafuna kukhala woyamba mwa inu, adzakhala kapolo wanu.”​—Mateyu 20:20, 21, 24-27.

Mu imodzi ya nkhani zake zolembedwa, zomangirira, Yesu anachenjeza khamu ponena za alembi ndi Afarisi. Iye analozanso ku zina za zolakwa zowonekera za atumiki abodza, onyenga amenewa. Iye analongosola iwo kukhala onyada ndi alamulira ndipo nthaŵi zonse ofuna malo apamwamba.​—Mateyu 23:1-7.

Lerolino, atsogoleri ambiri a chipembedzo, makamaka ansembe a Tchalitchi cha Chikatolika ndipo, mu nkhani zina, a Anglican, amafuna kuti adziitanidwa monga “Abambo.” Mwachitsanzo, wansembe mmodzi wa Tchalitchi cha England mu Mozambique, pamene anafunsidwa zaka zingapo zapitazo ndi mmodzi wa Mboni za Yehova ponena za chifukwa chimene iye anagwiritsira ntchito dzina laulemu lakuti “Abambo,” iye anayankha kuti: “Ndiri wonyada ponena za ilo!” Ndipo, ndithudi, chiri chodziŵika bwino lomwe kuti papa wa ku Rome amasangalala m’kuitanidwa monga “Atate Woyera”​—mosasamala kanthu za langizo la Yesu kwa ophunzira ake “kusatchula wina atate wanu pansi pano, pakuti alipo mmodzi ndi Atate wanu wa kumwamba.” Yesu anawonjezera prinsipulo lenileni iri kuti: “Aliyense amene adzikuza yekha adzachepetsedwa.”​—Mateyu 23:9-12, The Jerusalem Bible.

Kodi Akazi Ayenera Kuikidwa?

Nthaŵi za posachedwapa, pakhala chiwonjezeko m’chiŵerengero cha akazi oikidwa kukhala ziwalo za atsogoleri a chipembedzo. Koma Paulo analangiza Timoteo kuti: “Sindilola ine kuti mkazi aphunzitse, kapena kulamulira mwamuna.” (1 Timoteo 2:12) Ngakhale kuli tero, ichi sichitanthauza kuti mkazi Wachikristu sangaphunzitse ana ake kapena kuphunzitsa pakati pa gulu lachisawawa, koma iye safunikira kuphunzitsa mu mpingo.

Kodi akazi, chotero, sayenera kulankhula nkomwe pa misonkhano ya Chikristu? Mboni za Yehova zimaphunzira magazini ino, Nsanja ya Olonda, pa umodzi wa misonkhano yawo ya mlungu ndi mlungu, kugwiritsira ntchito nkhani zomwe zaphatikizidwa ndi mafunso pa ndimezo. Mtumiki wotsogoza phunzirolo, nthaŵi zonse mbale, amaitanira ziwalo za mpingo, kuphatikizapo alongo, kuyankha mafunso amenewa. Koma akazi amenewa sakuphunzitsa. Iwo akungolankhula kokha m’mawu awo malingaliro omwe ali mu nkhanizo. Ngakhale ana amalimbikitsidwa kugawanamo m’kupereka mayankho, ndipo kaŵirikaŵiri ndemanga zawo, mokulira zachidule ndipo zopepuka, zimafika pa nsonga kwenikweni​—kuti tilankhule kalongosoledwe kotchuka.

Paulo anapanganso ndemanga iyi ponena za akazi: “Koma ngati afuna kuphunzira kanthu afunse amuna awo a iwo okha kwawo; pakuti kunyazitsa mkazi kulankhula mu Mpingo.” (1 Akorinto 14:35) Ichi chimatanthauza kuti ngati alongo sakumvetsetsa kapena asokonezeka ndi ndemanga zina zoŵerengedwa kapena kupangidwa mkati mwa misonkhano, iwo sayenera kudzutsa nsonga zotsutsa pamaso pa mpingo. M’malomwake, iwo ayenera kufunsa amuna awo kumveketsa nkhanizo pamene ali kunyumba.

Ngakhale kuli tero, pali nthaŵi pamene akazi Achikristu angalalikire kwa amuna. Mboni za Yehova zimathera yochulukira ya nthaŵi yawo kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu kuchokera kunyumba ndi nyumba. Pamene wolalikira wamkazi apeza mwamuna, kodi iye ayenera kudzikhululukira iyemwini ndi kuchokapo? Ndithudi ayi. Mu nkhani imeneyi, iye sakulalikira ku mpingo koma kwa munthu mmodzi yemwe sangakhale wokhulupirira. Mofananamo, mtumiki wachikazi angaphunzire Baibulo ndi banja losakhala la Chikristu ngakhale ngati atate alipo.

Yesu Kristu​—Chitsanzo Chowala

Yesu anali chitsanzo chowala chomwe tiyenera kuchita bwino kuchitsanzira! Iye anali mphunzitsi wabwino koposa, mlaliki wabwino koposa, wantchito wachangu koposa, ndipo phungu wachikondi koposa yemwe anakhalapo pa dziko lapansi. Kuti titsatire m’mapazi ake uli mwawi wokulira koposa. Kodi mukuyesera kuchita chimenecho?

Mamiliyoni a Mboni za Yehova akuchita kuthekera kwawo kokulira kutsanzira iye, ngakhale kuti mopanda ungwiro. Njira zake zinali zosiyana koposa ndi zija za atsogoleri achipembedzo ambiri a lerolino. Iye sanalize mabelu a tchalitchi ndi kudikira kaamba ka anthu kudza kwa iye, ngakhale kuti ambiri anabwera pa okha. M’malomwake, iye anapita kwa anthu ndi kuwaphunzitsa iwo m’nyumba zawo, m’malo apoyera, pamapiri, ndi pa gombe la Nyanja ya Galileya. Pa nthaŵi zina iye analankhula kwa magulu ofika ku chiŵerengero cha zikwi, monga momwe zasonyezeredwa pansipa.​—Mateyu 9:35; 13:36; Luka 8:1.

Kuthandiza Osauka, Odwala, ndi Oklamba

Ndi angati a awa amene alipo lerolino? Mazana a zikwi. Ndipo chiŵerengerocho chikuwonjezeka mofulumira pamene mikhalidwe ya dziko mofulumira ikunyonyotsoka ndipo dongosolo la kachitidwe ka zinthu liripoli likufikira kumapeto ake otheratu pa nkhondo ya Armagedo. (Chibvumbulutso 16:16) Matsoka a chilengedwe, njala, ndi miliri zikuwonjezera ku kusakazako ndi kuvutika. Akristu oyambirira nawonso anayenera kuchita ndi mavuto oterowo. Chifupifupi 46 C.E., pamene Klaudiyo anali wolamulira wa Roma, panali njala yofalikira. Chotero, nchiyani chimene ophunzira anachita? Iwo “yense monga anakhoza, anatsimikiza mtima kutumiza zothandiza abale akukhala m’Yudeya.”​—Machitidwe 11:27-30.

M’nthaŵi zamakono, Mboni za Yehova kaŵirikaŵiri zapereka zothandiza zaufulu kwa awo omwe akuvutika kapena ali osowa. Posachedwapa, pamene Mozambique inakanthidwa ndi nkhondo ya chiweniweni​—ndi kutulukapo kwa kupereŵera kwa chakudya kowopsya, zovala, zotumizidwa za mankhwala, ndi zosowa zina zofunika​—Mboni za Yehova mu South Africa yapafupiyo zinafika ku chithandizo cha abale awo a m’nsautso. Unyinji wokulira wa zakudya, zovala, ndi zinthu zina zinasonkhanitsidwa ndi kutumizidwa ku Maputo, mzinda waukulu, m’magalimoto aakulu.

Kukwaniritsa Ulosi wa Baibulo

Inde, atumiki owona a Mulungu lerolino akhala ndi mwaŵi wosangalatsa wa kutengamo mbali m’kukwaniritsa maulosi a Baibulo. Motani? Pa chochitika cha m’mbiri pamene ophunzira anafunsa Yesu kuti: “Zija zidzawoneka liti? ndipo chizindikiro cha kufika kwanu nchiyani, ndi cha mathedwe a nthaŵi ya pansi pano?” iye anayankha kuti mu nthaŵi ya nkhondo za dziko, njala, zivomezi, ndi kusayeruzika, “mbiri yabwino ya ufumu [idza]lalikidwa m’dziko lonse lokhalidwa ndi anthu.” (Mateyu 24:3, 14, NW) Paulo anakhazikitsa chitsanzo kaamba ka atumiki onse owona mwa kulalikira “kuchokera kunyumba ndi nyumba.”​—Machitidwe 20:20, NW.

Mboni za Yehova zikudziŵika pa dziko lonse kaamba ka changu chawo mu ntchito yolalikira imeneyi. Mwinamwake pa nthaŵi zina anafikira panyumba yanu. Kodi munayamba mwawapatsa kumvetsera kwabwino? Ngati ayi, bwanji osachita tero nthaŵi ina pamene adzafikira? Inu momvetsetseka mungadzadabwitsidwe!

[Mawu a Chithunzi patsamba 4]

Based on U.S. Army photo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena