Chikumbutso—Chochitika Chofunika Kwambiri!
1 Pa Sande, March 23, dzuŵa litaloŵa, tidzachita Chikumbutso cha imfa ya Kristu. (Luka 22:19) Chochitika chimenechi nchofunikadi kwambiri! Mwa kusunga umphumphu wake kwa Yehova mpaka imfa, Yesu anasonyeza kuti zitheka kwa munthu kukhalabe wodzipereka mwaumulungu ngakhale ali m’zipsinjo zochuluka, motero kuchirikiza kuyenera kwa uchifumu wa Yehova. (Aheb. 5:8) Ndiponso, nsembe yangwiro ya munthu yofunika kuombolera anthu inakonzeka mwa imfa ya Kristu, ndipo inatheketsa kuti aja osonyeza chikhulupiriro akhale ndi moyo kosatha. (Yoh. 3:16) Mwa kupezekapo pa Chikumbutso, timasonyeza chiyamikiro chathu chochokera mumtima kaamba ka chikondi cha Yehova ndiponso nsembe ya Yesu imene anatiperekera.
2 Ife tonse tikulimbikitsidwa kutsatira programu yoŵerenga Baibulo ya March 18-23, yosonyezedwa pa Kalenda ya Mboni za Yehova ya 1997. Ndiponso, kukambitsirana pabanja mitu 112-16 m’buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako kudzatithandiza kusumika maganizo athu pamlungu wofunika koposa m’mbiri ya munthu.
3 Kodi mungawonjeze nthaŵi imene mudzathera mu utumiki wakumunda panyengo ya Chikumbutso? Ofalitsa ambiri adzagwiritsira ntchito mwaŵi wakuchita upainiya wothandiza pamilungu isanu ya March. Bwanji osakhala mmodzi wa iwo? Ife tonse tingakhale ndi phande lalikulu pakusonyeza kufunika kwake kwa kupezeka pa Chikumbutso. Popeza padzakhala pa Sande, ambiri zidzawapepukira kupezekapo. Tsimikizani kuti mwaitana ophunzira Baibulo onse ndi ena osonyeza chidwi kuti adzasonkhane nafe. Kambitsiranani nawo zotchulidwa patsamba 127, ndime 18, m’buku la Chidziŵitso ponena za tsiku limodzi pachaka limene makamaka liyenera kusungidwa.
4 Lingalirani za chochitika chimenechi chachikulu koposa mu 1997 ndi chiyamikiro chachikulu pa zonse zimene imfa ya Yesu yatichitira. Mudzakhalepo madzulo pa March 23, pamene Akristu oona kulikonse adzachita Chikumbutso mokhulupirika.